1 Samuel 25 (BOGWICC)

1 Samueli anamwalira, ndipo Aisraeli onse anasonkhana kudzalira maliro ake ndipo anamuyika mʼmanda ku mudzi kwawo ku Rama.Ndipo Davide anapita ku chipululu cha Parani. 2 Kunali munthu wina wolemera kwambiri ku Maoni amene malo ake a ntchito anali ku Karimeli. Iyeyu anali ndi mbuzi 1,000 ndi nkhosa 3,000. 3 Dzina lake linali Nabala ndipo anali wa fuko la Kalebe. Dzina la mkazi wake linali Abigayeli. Anali mkazi wanzeru ndi wokongola, koma mwamuna wake, wa banja la Kalebe, anali wowuma mtima ndi wamwano pa zochita zake. 4 Davide anamva akanali ku chipululu kuti Nabala akumeta nkhosa. 5 Choncho anatuma anyamata khumi nawawuza kuti, “Pitani kwa Nabala ku Karimeli ndipo mukamulonjere mʼdzina langa. 6 Mukamuwuze kuti, ‘Mtendere ukhale ndi inu, banja lanu pamodzi ndi zonse zimene muli nazo. 7 “ ‘Tsono ndamva kuti muli ndi anthu ometa nkhosa. Pamene abusa anu anali nafe kuno, sitinawachite china chilichonse choyipa, ndipo sanasowe kanthu pa nthawi yonse imene anali ku Karimeli. 8 Muwafunse antchito anu ndipo akuwuzani. Kotero akomereni mtima anyamata anga, pakuti tabwera pa nthawi yachikondwerero. Chonde apatseniko antchito anuwo ndi mwana wanu Davide chilichonse chimene mungakhale nacho.’ ” 9 Anyamata a Davide aja atafika, anamuwuza Nabala zonse zimene Davide anayankhula. Ndipo anadikira yankho. 10 Nabala anayankha anyamata a Davide kuti, “Kodi Davide ndi ndani? Mwana wa Yese ndi ndani? Masiku ano pali antchito ambiri amene akuthawa kwa mabwana awo. 11 Nditengerenji buledi, madzi ndi nyama zimene ndaphera anthu anga ometa nkhosa ndi kuzipereka kwa anthu amene sindikudziwa kumene achokera?” 12 Choncho anyamata a Davide aja anatembenuka nabwerera. Atafika anafotokozera Davide mawu onse a Nabala. 13 Davide anawuza anthu ake kuti, “Aliyense amangirire lupanga lake!” Choncho aliyense anamangirira lupanga lake. Davidenso anamangirira lupanga lake. Anthu pafupifupi 400 ndiwo anapita ndi Davide, pamene anthu 200 anatsala ndi katundu. 14 Tsono mmodzi mwa antchito anawuza Abigayeli mkazi wa Nabala kuti, “Davide anatumiza amithenga kuchokera ku chipululu kudzalonjera mbuye wathu, koma iye anawalalatira. 15 Komatu anthuwa anatichitira zabwino kwambiri. Sanatizunze, ndipo nthawi yonse imene tinali nawo ku busa sitinasowe kanthu. 16 Ankatitchinjiriza ngati mpanda usiku ndi usana nthawi yonse tinkaweta nkhosa. 17 Tsono onani chimene mungachite, chifukwa zimenezi zingadzetse tsoka pa mbuye wathu pamodzi ndi nyumba yake. Paja mbuye athu aja ndi munthu wa khalidwe loyipa moti palibe amene angathe kuyankhula naye.” 18 Ndipo Abigayeli sanataye nthawi. Iye anatenga malofu a buledi 200, matumba a chikopa awiri a vinyo, nkhosa zisanu zowotcheratu, makilogalamu 17 a tirigu wokazinga, makeke a mphesa zowuma 100, ndiponso makeke a nkhuyu 200, ndipo anazisenzetsa abulu. 19 Kenaka anawuza antchito ake kuti, “Tsogolani, ine ndikutsatirani.” Koma sanawuze mwamuna wake Nabala. 20 Mayi uja atakwera pa bulu wake ndi kufika pa tsinde la phiri, anangoona Davide ndi ankhondo ake akubwera kunali iye. Choncho anakumana nawo. 21 Nthawiyi nʼkuti Davide atanena kuti, “Kani ndinalondera pachabe katundu wa munthu uyu mʼchipululu muja! Ndipotu palibe kanthu nʼkamodzi komwe kake kamene kanasowa. Tsono wandibwezera zoyipa mʼmalo mwa zabwino. 22 Mulungu andilange kwambiri ngati pofika mmawa nditakhale nditasiyako ngakhale munthu mmodzi mwa onse amene ali nawo.” 23 Abigayeli ataona Davide, anatsika pa bulu wake mofulumira ndipo anadzigwetsa pansi pamaso pa Davide. 24 Ali chigonere choncho pa mapazi a Davide anati, “Mbuye wanga, kulakwa kukhale pa ine ndekha. Chonde lolani kuti mdzakazi wanune ndiyankhule nanu, ndipo mumve mawu a ine mdzakazi wanu. 25 Mbuye wanga musasamale za mwamuna wanga Nabala, munthu wa khalidwe loyipa. Iyeyu ali monga dzina lake liliri. Monga dzina lake litanthauza kuti chitsiru, ndiye kuti zake zonse ndi zauchitsiru basi. Koma ine mdzakazi wanu, sindinawaone anthu amene mbuye wanga munawatuma. 26 Tsono mbuye wanga muli apa, ndikulumbira pali Yehova wamoyo amene wakuletsani kuti musakhetse magazi a munthu ndi kulipsira nokha, kuti adani anu amene afuna kukuchitani zoyipa adzakhale ngati Nabala. 27 Choncho, nazi mphatso zimene mdzakazi wanu ndabwera nazo kwa mbuye wanga kuti zipatsidwe kwa anyamata amene muli nawo. 28 Chonde khululukani zolakwa za ine mdzakazi wanu. Ndithu Yehova adzakhazikitsa banja la mbuye wanga mu ufumu, popeza mukumenya nkhondo ya Yehova. Choncho choyipa sichidzapezeka mwa inu masiku onse a moyo wanu. 29 Ngati munthu wina akuwukirani ndi kukulondani, Yehova Mulungu wanu adzateteza moyo wa mbuye wanga monga mmene munthu asungira chuma mʼphukusi, koma moyo wa adani anu adzawutaya kutali monga momwe munthu amaponyera mwala ndi legeni. 30 Yehova adzakuchitirani mbuye wanga zabwino zonse zimene anakulonjezani. Adzakuyikani kukhala wolamulira Aisraeli. 31 Zikadzatero, inu mbuye wanga simudzakhala ndi chikumbumtima choti munakhetsa magazi kapena kulipsira popanda chifukwa. Koma Yehova akadzakuchitirani zabwino zonsezi musadzandiyiwale ine mdzakazi wanu.” 32 Tsono Davide anawuza Abigayeli kuti, “Alemekezeke Yehova Mulungu wa Israeli, amene wakutuma iwe lero kuti ukumane nane. 33 Yehova akudalitseni chifukwa cha nzeru zanu pondiletsa lero kuti ndisakhetse magazi ndi kubwezera adani anga ndi manja anga. 34 Kunena zoona, pali Yehova Wamoyo, Mulungu wa Israeli, amene wandiletsa kuti ndisakupwetekeni, mukanapanda kubwera msanga kudzakumana nane, palibe munthu aliyense wamwamuna wa Nabala akanasiyidwa wamoyo pakucha mmawa.” 35 Ndipo Davide analandira kwa mayiyo zimene anamutengera ndipo anati, “Pitani kwanu mu mtendere. Ine ndamva mawu anu ndipo ndavomera zimene mwapempha.” 36 Abigayeli atabwerera kwa Nabala anamupeza ali mʼnyumba akuchita mphwando ngati la mfumu. Iye anali atakondwa kwambiri popeza anali ataledzera kwambiri. Choncho mkazi wakeyo sanamuwuze kalikonse mpaka mmawa kutacha. 37 Tsono mmawa, mowa utamuchoka Nabala, mkazi wake anamuwuza zonse. Pomwepo mtima wake unaleka kugunda ndipo unawuma gwaa ngati mwala. 38 Patapita masiku khumi, Yehova anakantha Nabala ndipo anafa. 39 Pamene Davide anamva kuti Nabala wamwalira, iye anati, “Alemekezeke Yehova, walipsira Nabala chipongwe chimene anandichita ndipo anandiletsa ine mtumiki wake kuti ndisachite choyipa. Yehova wabwezera pamutu pa Nabala choyipa chimene iye anachita.”Kenaka Davide anatumiza mawu kwa Abigayeli, kumupempha kuti akhale mkazi wake. 40 Anyamata a Davide atafika ku Karimeli anawuza Abigayeli kuti, “Davide watituma kwa iwe kuti tikutenge ukhale mkazi wake.” 41 Abigayeli anagwada nagunditsa nkhope yake pansi ndipo anati, “Ine mdzakazi wa mbuye wanga ndakonzeka kutumikira ngakhale kusambitsa mapazi a anyamata ake.” 42 Motero Abigayeli ananyamuka mofulumira nakwera bulu wake. Tsono iye pamodzi ndi anamwali ake asanu amene ankamutumikira, anatsagana ndi amithenga a Davide aja ndipo anakakhala mkazi wake wa Davide. 43 Davide nʼkuti atakwatiranso Ahinoamu wa ku Yezireeli ndipo onse awiri anali akazi ake. 44 Koma Sauli anali atakwatitsa Mikala, mkazi wa Davide kwa Paliti mwana wa Laisi wa ku Galimu.

In Other Versions

1 Samuel 25 in the ANGEFD

1 Samuel 25 in the ANTPNG2D

1 Samuel 25 in the AS21

1 Samuel 25 in the BAGH

1 Samuel 25 in the BBPNG

1 Samuel 25 in the BBT1E

1 Samuel 25 in the BDS

1 Samuel 25 in the BEV

1 Samuel 25 in the BHAD

1 Samuel 25 in the BIB

1 Samuel 25 in the BLPT

1 Samuel 25 in the BNT

1 Samuel 25 in the BNTABOOT

1 Samuel 25 in the BNTLV

1 Samuel 25 in the BOATCB

1 Samuel 25 in the BOATCB2

1 Samuel 25 in the BOBCV

1 Samuel 25 in the BOCNT

1 Samuel 25 in the BOECS

1 Samuel 25 in the BOHCB

1 Samuel 25 in the BOHCV

1 Samuel 25 in the BOHLNT

1 Samuel 25 in the BOHNTLTAL

1 Samuel 25 in the BOICB

1 Samuel 25 in the BOILNTAP

1 Samuel 25 in the BOITCV

1 Samuel 25 in the BOKCV

1 Samuel 25 in the BOKCV2

1 Samuel 25 in the BOKHWOG

1 Samuel 25 in the BOKSSV

1 Samuel 25 in the BOLCB

1 Samuel 25 in the BOLCB2

1 Samuel 25 in the BOMCV

1 Samuel 25 in the BONAV

1 Samuel 25 in the BONCB

1 Samuel 25 in the BONLT

1 Samuel 25 in the BONUT2

1 Samuel 25 in the BOPLNT

1 Samuel 25 in the BOSCB

1 Samuel 25 in the BOSNC

1 Samuel 25 in the BOTLNT

1 Samuel 25 in the BOVCB

1 Samuel 25 in the BOYCB

1 Samuel 25 in the BPBB

1 Samuel 25 in the BPH

1 Samuel 25 in the BSB

1 Samuel 25 in the CCB

1 Samuel 25 in the CUV

1 Samuel 25 in the CUVS

1 Samuel 25 in the DBT

1 Samuel 25 in the DGDNT

1 Samuel 25 in the DHNT

1 Samuel 25 in the DNT

1 Samuel 25 in the ELBE

1 Samuel 25 in the EMTV

1 Samuel 25 in the ESV

1 Samuel 25 in the FBV

1 Samuel 25 in the FEB

1 Samuel 25 in the GGMNT

1 Samuel 25 in the GNT

1 Samuel 25 in the HARY

1 Samuel 25 in the HNT

1 Samuel 25 in the IRVA

1 Samuel 25 in the IRVB

1 Samuel 25 in the IRVG

1 Samuel 25 in the IRVH

1 Samuel 25 in the IRVK

1 Samuel 25 in the IRVM

1 Samuel 25 in the IRVM2

1 Samuel 25 in the IRVO

1 Samuel 25 in the IRVP

1 Samuel 25 in the IRVT

1 Samuel 25 in the IRVT2

1 Samuel 25 in the IRVU

1 Samuel 25 in the ISVN

1 Samuel 25 in the JSNT

1 Samuel 25 in the KAPI

1 Samuel 25 in the KBT1ETNIK

1 Samuel 25 in the KBV

1 Samuel 25 in the KJV

1 Samuel 25 in the KNFD

1 Samuel 25 in the LBA

1 Samuel 25 in the LBLA

1 Samuel 25 in the LNT

1 Samuel 25 in the LSV

1 Samuel 25 in the MAAL

1 Samuel 25 in the MBV

1 Samuel 25 in the MBV2

1 Samuel 25 in the MHNT

1 Samuel 25 in the MKNFD

1 Samuel 25 in the MNG

1 Samuel 25 in the MNT

1 Samuel 25 in the MNT2

1 Samuel 25 in the MRS1T

1 Samuel 25 in the NAA

1 Samuel 25 in the NASB

1 Samuel 25 in the NBLA

1 Samuel 25 in the NBS

1 Samuel 25 in the NBVTP

1 Samuel 25 in the NET2

1 Samuel 25 in the NIV11

1 Samuel 25 in the NNT

1 Samuel 25 in the NNT2

1 Samuel 25 in the NNT3

1 Samuel 25 in the PDDPT

1 Samuel 25 in the PFNT

1 Samuel 25 in the RMNT

1 Samuel 25 in the SBIAS

1 Samuel 25 in the SBIBS

1 Samuel 25 in the SBIBS2

1 Samuel 25 in the SBICS

1 Samuel 25 in the SBIDS

1 Samuel 25 in the SBIGS

1 Samuel 25 in the SBIHS

1 Samuel 25 in the SBIIS

1 Samuel 25 in the SBIIS2

1 Samuel 25 in the SBIIS3

1 Samuel 25 in the SBIKS

1 Samuel 25 in the SBIKS2

1 Samuel 25 in the SBIMS

1 Samuel 25 in the SBIOS

1 Samuel 25 in the SBIPS

1 Samuel 25 in the SBISS

1 Samuel 25 in the SBITS

1 Samuel 25 in the SBITS2

1 Samuel 25 in the SBITS3

1 Samuel 25 in the SBITS4

1 Samuel 25 in the SBIUS

1 Samuel 25 in the SBIVS

1 Samuel 25 in the SBT

1 Samuel 25 in the SBT1E

1 Samuel 25 in the SCHL

1 Samuel 25 in the SNT

1 Samuel 25 in the SUSU

1 Samuel 25 in the SUSU2

1 Samuel 25 in the SYNO

1 Samuel 25 in the TBIAOTANT

1 Samuel 25 in the TBT1E

1 Samuel 25 in the TBT1E2

1 Samuel 25 in the TFTIP

1 Samuel 25 in the TFTU

1 Samuel 25 in the TGNTATF3T

1 Samuel 25 in the THAI

1 Samuel 25 in the TNFD

1 Samuel 25 in the TNT

1 Samuel 25 in the TNTIK

1 Samuel 25 in the TNTIL

1 Samuel 25 in the TNTIN

1 Samuel 25 in the TNTIP

1 Samuel 25 in the TNTIZ

1 Samuel 25 in the TOMA

1 Samuel 25 in the TTENT

1 Samuel 25 in the UBG

1 Samuel 25 in the UGV

1 Samuel 25 in the UGV2

1 Samuel 25 in the UGV3

1 Samuel 25 in the VBL

1 Samuel 25 in the VDCC

1 Samuel 25 in the YALU

1 Samuel 25 in the YAPE

1 Samuel 25 in the YBVTP

1 Samuel 25 in the ZBP