1 Timothy 1 (BOGWICC)

1 Paulo, mtumwi wa Khristu Yesu mwa lamulo la Mulungu, Mpulumutsi wathu ndiponso Khristu Yesu chiyembekezo chathu. 2 Kwa Timoteyo mwana wanga weniweni mʼchikhulupiriro.Chisomo, chifundo ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate ndi Khristu Yesu Ambuye athu zikhale ndi iwe. 3 Monga ndinakupempha pamene ndinkapita ku Makedoniya, khala ku Efeso komweko kuti uletse anthu ena kuphunzitsa ziphunzitso zonyenga, 4 kapena kumangoyika mitima pa nthano zopeka ndi kufufuza za mayina a makolo awo. Zinthu zotere zimapititsa mʼtsogolo mikangano mʼmalo mwa ntchito ya Mulungu yomwe ndi ya chikhulupiriro. 5 Cholinga cha lamuloli ndi chikondi, chomwe chimachokera mu mtima woyera, chikumbumtima chabwino ndi chikhulupiriro choona. 6 Anthu ena anapatuka pa zimenezi ndipo anatsata nkhani zopanda tanthauzo. 7 Iwo amafuna kukhala aphunzitsi amalamulo, koma sadziwa zimene akunena, kapena zimene akufuna kutsimikiza. 8 Tikudziwa kuti Malamulo ndi abwino ngati munthu awagwiritsa ntchito bwino. 9 Tikudziwanso kuti Malamulo sakhazikitsidwa chifukwa cha anthu olungama, koma ophwanya lamulo ndi owukira, osaopa Mulungu ndi ochimwa, wopanda chiyero ndi osapembedza; amene amapha abambo awo ndi amayi awo, kapena anthu ena. 10 Malamulo amayikidwa chifukwa cha anthu achigololo ndi ochita zadama ndi amuna anzawo, anthu ogulitsa akapolo, abodza ndi olumbira zabodza, ndi ochita chilichonse chotsutsana ndi chiphunzitso choona. 11 Chiphunzitso chimene chimagwirizana ndi Uthenga Wabwino wonena za ulemerero wa Mulungu wodala, umene Iye mwini anandisungitsa. 12 Ndikuthokoza Khristu Yesu Ambuye athu, amene anandipatsa mphamvu pa ntchitoyi. Iye ananditenga kukhala wokhulupirira, nandipatsa ntchito mu utumiki wake. 13 Ngakhale kuti kale ndinali wachipongwe, wozunza ndi wankhanza, anandichitira chifundo chifukwa ndinkachita mwaumbuli ndi mopanda chikhulupiriro. 14 Chisomo cha Ambuye athu chinatsanulidwa pa ine mochuluka, pamodzi ndi chikhulupiriro ndi chikondi zimene zili mwa Khristu Yesu. 15 Mawu odalirika ndi woyenera kuwavomereza kwathunthu ndi awa: Yesu Khristu anabwera pa dziko lapansi kudzapulumutsa ochimwa, ndipo mwa iwowo ine ndiye wochimwitsitsa. 16 Ndipo pa chifukwa chimenechi, Mulungu anandichitira chifundo, kuti mwa ine, wochimwitsitsa, Khristu Yesu aonetse kuleza mtima kwake konse kuti ndikhale chitsanzo cha omwe angathe kumukhulupirira ndi kulandira moyo wosatha. 17 Tsopano kwa Mfumu yamuyaya, yosafa, yosaoneka, amene Iye yekha ndiye Mulungu, kukhale ulemu ndi ulemerero mpaka muyaya. Ameni. 18 Mwana wanga Timoteyo, ndikukupatsa langizo ili molingana ndi maulosi amene aneneri ananena za iwe. Pamene ukumbukira mawu amenewa udzatha kumenya bwino nkhondo 19 utagwiritsitsa chikhulupiriro ndi chikumbumtima chabwino. Ena anazikana zimenezi motero chikhulupiriro chawo chinawonongeka. 20 Ena mwa amenewa ndi Humenayo ndi Alekisandro, amene ndinawapereka kwa Satana kuti aphunzire kusachita chipongwe Mulungu.

In Other Versions

1 Timothy 1 in the ANGEFD

1 Timothy 1 in the ANTPNG2D

1 Timothy 1 in the AS21

1 Timothy 1 in the BAGH

1 Timothy 1 in the BBPNG

1 Timothy 1 in the BBT1E

1 Timothy 1 in the BDS

1 Timothy 1 in the BEV

1 Timothy 1 in the BHAD

1 Timothy 1 in the BIB

1 Timothy 1 in the BLPT

1 Timothy 1 in the BNT

1 Timothy 1 in the BNTABOOT

1 Timothy 1 in the BNTLV

1 Timothy 1 in the BOATCB

1 Timothy 1 in the BOATCB2

1 Timothy 1 in the BOBCV

1 Timothy 1 in the BOCNT

1 Timothy 1 in the BOECS

1 Timothy 1 in the BOHCB

1 Timothy 1 in the BOHCV

1 Timothy 1 in the BOHLNT

1 Timothy 1 in the BOHNTLTAL

1 Timothy 1 in the BOICB

1 Timothy 1 in the BOILNTAP

1 Timothy 1 in the BOITCV

1 Timothy 1 in the BOKCV

1 Timothy 1 in the BOKCV2

1 Timothy 1 in the BOKHWOG

1 Timothy 1 in the BOKSSV

1 Timothy 1 in the BOLCB

1 Timothy 1 in the BOLCB2

1 Timothy 1 in the BOMCV

1 Timothy 1 in the BONAV

1 Timothy 1 in the BONCB

1 Timothy 1 in the BONLT

1 Timothy 1 in the BONUT2

1 Timothy 1 in the BOPLNT

1 Timothy 1 in the BOSCB

1 Timothy 1 in the BOSNC

1 Timothy 1 in the BOTLNT

1 Timothy 1 in the BOVCB

1 Timothy 1 in the BOYCB

1 Timothy 1 in the BPBB

1 Timothy 1 in the BPH

1 Timothy 1 in the BSB

1 Timothy 1 in the CCB

1 Timothy 1 in the CUV

1 Timothy 1 in the CUVS

1 Timothy 1 in the DBT

1 Timothy 1 in the DGDNT

1 Timothy 1 in the DHNT

1 Timothy 1 in the DNT

1 Timothy 1 in the ELBE

1 Timothy 1 in the EMTV

1 Timothy 1 in the ESV

1 Timothy 1 in the FBV

1 Timothy 1 in the FEB

1 Timothy 1 in the GGMNT

1 Timothy 1 in the GNT

1 Timothy 1 in the HARY

1 Timothy 1 in the HNT

1 Timothy 1 in the IRVA

1 Timothy 1 in the IRVB

1 Timothy 1 in the IRVG

1 Timothy 1 in the IRVH

1 Timothy 1 in the IRVK

1 Timothy 1 in the IRVM

1 Timothy 1 in the IRVM2

1 Timothy 1 in the IRVO

1 Timothy 1 in the IRVP

1 Timothy 1 in the IRVT

1 Timothy 1 in the IRVT2

1 Timothy 1 in the IRVU

1 Timothy 1 in the ISVN

1 Timothy 1 in the JSNT

1 Timothy 1 in the KAPI

1 Timothy 1 in the KBT1ETNIK

1 Timothy 1 in the KBV

1 Timothy 1 in the KJV

1 Timothy 1 in the KNFD

1 Timothy 1 in the LBA

1 Timothy 1 in the LBLA

1 Timothy 1 in the LNT

1 Timothy 1 in the LSV

1 Timothy 1 in the MAAL

1 Timothy 1 in the MBV

1 Timothy 1 in the MBV2

1 Timothy 1 in the MHNT

1 Timothy 1 in the MKNFD

1 Timothy 1 in the MNG

1 Timothy 1 in the MNT

1 Timothy 1 in the MNT2

1 Timothy 1 in the MRS1T

1 Timothy 1 in the NAA

1 Timothy 1 in the NASB

1 Timothy 1 in the NBLA

1 Timothy 1 in the NBS

1 Timothy 1 in the NBVTP

1 Timothy 1 in the NET2

1 Timothy 1 in the NIV11

1 Timothy 1 in the NNT

1 Timothy 1 in the NNT2

1 Timothy 1 in the NNT3

1 Timothy 1 in the PDDPT

1 Timothy 1 in the PFNT

1 Timothy 1 in the RMNT

1 Timothy 1 in the SBIAS

1 Timothy 1 in the SBIBS

1 Timothy 1 in the SBIBS2

1 Timothy 1 in the SBICS

1 Timothy 1 in the SBIDS

1 Timothy 1 in the SBIGS

1 Timothy 1 in the SBIHS

1 Timothy 1 in the SBIIS

1 Timothy 1 in the SBIIS2

1 Timothy 1 in the SBIIS3

1 Timothy 1 in the SBIKS

1 Timothy 1 in the SBIKS2

1 Timothy 1 in the SBIMS

1 Timothy 1 in the SBIOS

1 Timothy 1 in the SBIPS

1 Timothy 1 in the SBISS

1 Timothy 1 in the SBITS

1 Timothy 1 in the SBITS2

1 Timothy 1 in the SBITS3

1 Timothy 1 in the SBITS4

1 Timothy 1 in the SBIUS

1 Timothy 1 in the SBIVS

1 Timothy 1 in the SBT

1 Timothy 1 in the SBT1E

1 Timothy 1 in the SCHL

1 Timothy 1 in the SNT

1 Timothy 1 in the SUSU

1 Timothy 1 in the SUSU2

1 Timothy 1 in the SYNO

1 Timothy 1 in the TBIAOTANT

1 Timothy 1 in the TBT1E

1 Timothy 1 in the TBT1E2

1 Timothy 1 in the TFTIP

1 Timothy 1 in the TFTU

1 Timothy 1 in the TGNTATF3T

1 Timothy 1 in the THAI

1 Timothy 1 in the TNFD

1 Timothy 1 in the TNT

1 Timothy 1 in the TNTIK

1 Timothy 1 in the TNTIL

1 Timothy 1 in the TNTIN

1 Timothy 1 in the TNTIP

1 Timothy 1 in the TNTIZ

1 Timothy 1 in the TOMA

1 Timothy 1 in the TTENT

1 Timothy 1 in the UBG

1 Timothy 1 in the UGV

1 Timothy 1 in the UGV2

1 Timothy 1 in the UGV3

1 Timothy 1 in the VBL

1 Timothy 1 in the VDCC

1 Timothy 1 in the YALU

1 Timothy 1 in the YAPE

1 Timothy 1 in the YBVTP

1 Timothy 1 in the ZBP