2 Chronicles 17 (BOGWICC)

1 Yehosafati mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake ndipo anadzilimbitsa pofuna kulimbana ndi Israeli. 2 Iye anayika magulu a asilikali mʼmizinda yonse yotetezedwa ya Yuda, ndipo anamanga maboma mu Yuda ndi mʼmizinda yonse ya Efereimu imene Asa abambo ake analanda. 3 Yehova anali ndi Yehosafati chifukwa mʼzaka zoyambirira anatsatira makhalidwe a Davide abambo ake. Iye sanafunsire kwa Abaala. 4 Koma anafunafuna Mulungu wa abambo ake ndipo anatsatira malamulo ake osati zochita za Israeli. 5 Yehova anakhazikitsa kolimba ufumuwo mʼmanja mwake ndipo Ayuda onse anabweretsa mphatso kwa Yehosafati, kotero kuti anali ndi chuma ndi ulemu wambiri. 6 Mtima wake anawupereka kutsatira Yehova, kuwonjezera apo, anachotsa malo onse achipembedzo ndi mafano a Asera mu Yuda. 7 Mʼchaka chachitatu cha ufumu wake, iye anatuma akuluakulu ake Beni-Haili, Obadiya, Zekariya, Netaneli ndi Mikaya kukaphunzitsa mʼmizinda ya Yuda. 8 Pamodzi ndi iwo panali Alevi ena: Semaya, Netaniya, Zebadiya, Asaheli, Semiramoti, Yonatani, Adoniya, Tobiya ndi Tobu-Adoniya ndiponso ansembe Elisama ndi Yehoramu. 9 Iwo anaphunzitsa mu Yuda monse atatenga Buku la Malamulo a Yehova iwo anayenda mʼmizinda yonse ya ku Yuda ndipo anaphunzitsa anthu. 10 Kuopsa kwa Yehova kunali pa maufumu onse a mayiko oyandikana ndi Yuda, kotero kuti sanachite nkhondo ndi Yehosafati. 11 Afilisti ena anabweretsa kwa Yehosafati mphatso ndi siliva ngati msonkho, ndipo Aarabu anabweretsa ziweto: nkhosa zazimuna 7,700 ndi mbuzi 7,700. 12 Mphamvu za Yehosafati zinkakulirakulira. Iye anamanga malo otetezedwa ndi mizinda yosungiramo chuma mu Yuda 13 ndipo anali ndi katundu wambiri mʼmizinda ya Yuda. Iye anayikanso asilikali odziwa bwino nkhondo mu Yerusalemu. 14 Chiwerengero chawo potsata mabanja awo chinali chotere: kuchokera ku Yuda, atsogoleri a magulu 1,000;mtsogoleri Adina, anali ndi anthu 300,000 odziwa nkhondo; 15 otsatana naye, mtsogoleri Yehohanani, anali ndi anthu 280,000; 16 otsatana naye, Amasiya mwana wa Zikiri amene anadzipereka yekha kutumikira Yehova, anali ndi anthu 200,000. 17 Kuchokera ku Benjamini:Eliada, msilikali wolimba mtima, anali ndi anthu 200,000 amene anali ndi mauta ndi zishango; 18 otsatana naye, Yehozabadi, anali ndi anthu 180,000 okonzekera nkhondo. 19 Awa ndi anthu amene ankatumikira mfumu osawerengera amene anawayika mʼmizinda yotetezedwa mʼdziko lonse la Yuda.

In Other Versions

2 Chronicles 17 in the ANGEFD

2 Chronicles 17 in the ANTPNG2D

2 Chronicles 17 in the AS21

2 Chronicles 17 in the BAGH

2 Chronicles 17 in the BBPNG

2 Chronicles 17 in the BBT1E

2 Chronicles 17 in the BDS

2 Chronicles 17 in the BEV

2 Chronicles 17 in the BHAD

2 Chronicles 17 in the BIB

2 Chronicles 17 in the BLPT

2 Chronicles 17 in the BNT

2 Chronicles 17 in the BNTABOOT

2 Chronicles 17 in the BNTLV

2 Chronicles 17 in the BOATCB

2 Chronicles 17 in the BOATCB2

2 Chronicles 17 in the BOBCV

2 Chronicles 17 in the BOCNT

2 Chronicles 17 in the BOECS

2 Chronicles 17 in the BOHCB

2 Chronicles 17 in the BOHCV

2 Chronicles 17 in the BOHLNT

2 Chronicles 17 in the BOHNTLTAL

2 Chronicles 17 in the BOICB

2 Chronicles 17 in the BOILNTAP

2 Chronicles 17 in the BOITCV

2 Chronicles 17 in the BOKCV

2 Chronicles 17 in the BOKCV2

2 Chronicles 17 in the BOKHWOG

2 Chronicles 17 in the BOKSSV

2 Chronicles 17 in the BOLCB

2 Chronicles 17 in the BOLCB2

2 Chronicles 17 in the BOMCV

2 Chronicles 17 in the BONAV

2 Chronicles 17 in the BONCB

2 Chronicles 17 in the BONLT

2 Chronicles 17 in the BONUT2

2 Chronicles 17 in the BOPLNT

2 Chronicles 17 in the BOSCB

2 Chronicles 17 in the BOSNC

2 Chronicles 17 in the BOTLNT

2 Chronicles 17 in the BOVCB

2 Chronicles 17 in the BOYCB

2 Chronicles 17 in the BPBB

2 Chronicles 17 in the BPH

2 Chronicles 17 in the BSB

2 Chronicles 17 in the CCB

2 Chronicles 17 in the CUV

2 Chronicles 17 in the CUVS

2 Chronicles 17 in the DBT

2 Chronicles 17 in the DGDNT

2 Chronicles 17 in the DHNT

2 Chronicles 17 in the DNT

2 Chronicles 17 in the ELBE

2 Chronicles 17 in the EMTV

2 Chronicles 17 in the ESV

2 Chronicles 17 in the FBV

2 Chronicles 17 in the FEB

2 Chronicles 17 in the GGMNT

2 Chronicles 17 in the GNT

2 Chronicles 17 in the HARY

2 Chronicles 17 in the HNT

2 Chronicles 17 in the IRVA

2 Chronicles 17 in the IRVB

2 Chronicles 17 in the IRVG

2 Chronicles 17 in the IRVH

2 Chronicles 17 in the IRVK

2 Chronicles 17 in the IRVM

2 Chronicles 17 in the IRVM2

2 Chronicles 17 in the IRVO

2 Chronicles 17 in the IRVP

2 Chronicles 17 in the IRVT

2 Chronicles 17 in the IRVT2

2 Chronicles 17 in the IRVU

2 Chronicles 17 in the ISVN

2 Chronicles 17 in the JSNT

2 Chronicles 17 in the KAPI

2 Chronicles 17 in the KBT1ETNIK

2 Chronicles 17 in the KBV

2 Chronicles 17 in the KJV

2 Chronicles 17 in the KNFD

2 Chronicles 17 in the LBA

2 Chronicles 17 in the LBLA

2 Chronicles 17 in the LNT

2 Chronicles 17 in the LSV

2 Chronicles 17 in the MAAL

2 Chronicles 17 in the MBV

2 Chronicles 17 in the MBV2

2 Chronicles 17 in the MHNT

2 Chronicles 17 in the MKNFD

2 Chronicles 17 in the MNG

2 Chronicles 17 in the MNT

2 Chronicles 17 in the MNT2

2 Chronicles 17 in the MRS1T

2 Chronicles 17 in the NAA

2 Chronicles 17 in the NASB

2 Chronicles 17 in the NBLA

2 Chronicles 17 in the NBS

2 Chronicles 17 in the NBVTP

2 Chronicles 17 in the NET2

2 Chronicles 17 in the NIV11

2 Chronicles 17 in the NNT

2 Chronicles 17 in the NNT2

2 Chronicles 17 in the NNT3

2 Chronicles 17 in the PDDPT

2 Chronicles 17 in the PFNT

2 Chronicles 17 in the RMNT

2 Chronicles 17 in the SBIAS

2 Chronicles 17 in the SBIBS

2 Chronicles 17 in the SBIBS2

2 Chronicles 17 in the SBICS

2 Chronicles 17 in the SBIDS

2 Chronicles 17 in the SBIGS

2 Chronicles 17 in the SBIHS

2 Chronicles 17 in the SBIIS

2 Chronicles 17 in the SBIIS2

2 Chronicles 17 in the SBIIS3

2 Chronicles 17 in the SBIKS

2 Chronicles 17 in the SBIKS2

2 Chronicles 17 in the SBIMS

2 Chronicles 17 in the SBIOS

2 Chronicles 17 in the SBIPS

2 Chronicles 17 in the SBISS

2 Chronicles 17 in the SBITS

2 Chronicles 17 in the SBITS2

2 Chronicles 17 in the SBITS3

2 Chronicles 17 in the SBITS4

2 Chronicles 17 in the SBIUS

2 Chronicles 17 in the SBIVS

2 Chronicles 17 in the SBT

2 Chronicles 17 in the SBT1E

2 Chronicles 17 in the SCHL

2 Chronicles 17 in the SNT

2 Chronicles 17 in the SUSU

2 Chronicles 17 in the SUSU2

2 Chronicles 17 in the SYNO

2 Chronicles 17 in the TBIAOTANT

2 Chronicles 17 in the TBT1E

2 Chronicles 17 in the TBT1E2

2 Chronicles 17 in the TFTIP

2 Chronicles 17 in the TFTU

2 Chronicles 17 in the TGNTATF3T

2 Chronicles 17 in the THAI

2 Chronicles 17 in the TNFD

2 Chronicles 17 in the TNT

2 Chronicles 17 in the TNTIK

2 Chronicles 17 in the TNTIL

2 Chronicles 17 in the TNTIN

2 Chronicles 17 in the TNTIP

2 Chronicles 17 in the TNTIZ

2 Chronicles 17 in the TOMA

2 Chronicles 17 in the TTENT

2 Chronicles 17 in the UBG

2 Chronicles 17 in the UGV

2 Chronicles 17 in the UGV2

2 Chronicles 17 in the UGV3

2 Chronicles 17 in the VBL

2 Chronicles 17 in the VDCC

2 Chronicles 17 in the YALU

2 Chronicles 17 in the YAPE

2 Chronicles 17 in the YBVTP

2 Chronicles 17 in the ZBP