2 Chronicles 24 (BOGWICC)

1 Yowasi anali wa zaka zisanu ndi ziwiri pamene anakhala mfumu, ndipo analamulira mu Yerusalemu kwa zaka makumi anayi. Dzina la amayi ake linali Zibiya wa ku Beeriseba. 2 Yowasi anachita zolungama pamaso pa Yehova nthawi yonse ya moyo wa wansembe Yehoyada. 3 Yehoyada anamupezera iye akazi awiri, ndipo anabereka ana aamuna ndi aakazi. 4 Patapita nthawi Yowasi anatsimikiza zokonzanso Nyumba ya Yehova. 5 Iye anayitanitsa pamodzi ansembe ndi Alevi ndipo anawawuza kuti, “Pitani ku mizinda ya Yuda ndi kukasonkhetsa ndalama za pa chaka kwa Aisraeli onse zokonzera Nyumba ya Mulungu wanu. Chitani zimenezi tsopano.” Koma Alevi sanachite zimenezi mwachangu. 6 Choncho mfumu inayitanitsa Yehoyada, mkulu wa ansembe ndipo inati kwa iye, “Kodi nʼchifukwa chiyani simunawuze Alevi kuti asonkhetse ndalama ku Yuda ndi Yerusalemu, msonkho umene anakhazikitsa Mose mtumiki wa Yehova ndiponso gulu lonse la Aisraeli mu tenti yaumboni?” 7 Ana a mkazi woyipa, Ataliya, anathyola chitseko cha Nyumba ya Mulungu ndipo anagwiritsa ntchito zinthu zopatulika popembedza Baala. 8 Mfumu italamulira, bokosi linapangidwa ndipo linayikidwa panja pa chipata cha Nyumba ya Yehova. 9 Ndipo analengeza kwa anthu a mu Yuda ndi mu Yerusalemu kuti abweretse kwa Yehova msonkho umene Mose mtumiki wa Mulungu analamulira Aisraeli mʼchipululu. 10 Akuluakulu onse ndi anthu onse anabweretsa zopereka zawo mokondwera ndipo anaziponya mʼbokosi mpaka linadzaza. 11 Nthawi ina iliyonse imene Alevi abweretsa bokosilo kwa akuluakulu a mfumu ndipo akaona kuti muli ndalama zambiri, mlembi waufumu ndi nduna yayikulu ya mkulu wa ansembe amabwera ndi kuchotsa ndalama mʼbokosi muja ndipo amalitenga kukaliyika pamalo pake. Iwo amachita izi nthawi ndi nthawi ndipo anapeza ndalama zambiri. 12 Mfumu pamodzi ndi Yehoyada anapereka ndalamazo kwa anthu oyangʼanira ntchito ku Nyumba ya Yehova. Analemba ntchito amisiri a miyala ndi a matabwa kuti akonzenso Nyumba ya Yehova. Analembanso ntchito amisiri a zitsulo ndi mkuwa kuti akonze Nyumba ya Mulungu. 13 Anthu amene ankagwira ntchito anali odziwa bwino, ndipo ntchitoyo inagwiridwa bwino ndi manja awo. Iwo anamanganso Nyumba ya Mulungu motsatira mapangidwe ake oyamba ndipo anayilimbitsa. 14 Atamaliza, iwo anabweretsa ndalama zotsala kwa mfumu ndi Yehoyada, ndipo anazigwiritsira ntchito popangira zida za mʼNyumba ya Yehova: ziwiya zogwiritsa ntchito potumikira ndi popereka nsembe zopsereza, komanso mbale ndi ziwiya zagolide ndi siliva. Nthawi yonse ya moyo wa Yehoyada, nsembe zopsereza zinkaperekedwa mosalekeza mʼNyumba ya Yehova. 15 Tsono Yehoyada anakalamba ndipo anali ndi zaka zambiri. Pambuyo pake iye anamwalira ali ndi zaka 130. 16 Iyeyo anayikidwa mʼmanda pamodzi ndi mafumu mu mzinda wa Davide chifukwa cha zabwino zimene anachita mu Israeli, kuchitira Mulungu ndi Nyumba yake. 17 Atamwalira Yehoyada, akuluakulu a Yuda anabwera kudzapereka ulemu kwa mfumu, ndipo mfumu inawamvera. 18 Iwo anasiya Nyumba ya Yehova, Mulungu wa makolo awo ndipo anapembedza Asera ndi mafano. Chifukwa cha kulakwa kwawo, mkwiyo wa Yehova unabwera pa Yuda ndi Yerusalemu. 19 Ngakhale Yehova anatumiza aneneri kwa anthuwo kuti awabweze kwa Iye, ngakhale aneneri ananenera mowatsutsa, anthuwo sanamvere. 20 Kenaka Mzimu wa Mulungu unabwera pa Zekariya mwana wa wansembe Yehoyada. Iye anayimirira pamaso pa anthu ndipo anati, “Zimene Mulungu akunena ndi Izi: ‘Chifukwa chiyani simukumvera Malamulo a Yehova? Simudzapindula. Chifukwa mwasiya Yehova, Iyenso wakusiyani.’ ” 21 Koma anthuwo anamuchitira chiwembu molamulidwa ndi mfumu ndipo anamugenda miyala ndi kumupha mʼbwalo la Nyumba ya Mulungu. 22 Mfumu Yowasi sinakumbukire zabwino zimene Yehoyada abambo ake a Zekariya anamuchitira, koma anapha mwana wake. Pamene amafa, iye ananena kuti, “Yehova aone zimenezi ndipo abwezere chilango.” 23 Pakutha kwa chaka, gulu lankhondo la Aramu linadzamenyana ndi Yowasi. Linalowa mu Yuda ndi mu Yerusalemu ndi kupha atsogoleri onse a anthu. Zonse zimene analanda anazitumiza kwa mfumu ya ku Damasiko. 24 Ngakhale kuti gulu lankhondo la Aramu linabwera ndi anthu ochepa okha, Yehova anapereka mʼmanja mwawo gulu lalikulu lankhondo. Chifukwa Yuda anasiya Yehova Mulungu wa makolo awo, chiweruzo chinachitika pa Yowasi. 25 Pamene Aaramu amachoka, anasiya Yowasi atavulazidwa kwambiri. Akuluakulu ake anamuchitira chiwembu chifukwa anapha mwana wa wansembe Yehoyada, ndipo anamupha ali pa bedi pake. Choncho anafa ndipo anayikidwa mʼmanda mu mzinda wa Davide, koma osati manda a mafumu. 26 Iwo amene anamuchitira chiwembu anali Zabadi mwana wa Simeati, mkazi wa ku Amoni, ndi Yehozabadi mwana wa Simiriti, mkazi wa ku Mowabu. 27 Za ana ake aamuna, uneneri wonena za iye, mbiri ya kumanganso Nyumba ya Mulungu, zalembedwa mʼbuku lofotokoza za mafumu. Ndipo Amaziya mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.

In Other Versions

2 Chronicles 24 in the ANGEFD

2 Chronicles 24 in the ANTPNG2D

2 Chronicles 24 in the AS21

2 Chronicles 24 in the BAGH

2 Chronicles 24 in the BBPNG

2 Chronicles 24 in the BBT1E

2 Chronicles 24 in the BDS

2 Chronicles 24 in the BEV

2 Chronicles 24 in the BHAD

2 Chronicles 24 in the BIB

2 Chronicles 24 in the BLPT

2 Chronicles 24 in the BNT

2 Chronicles 24 in the BNTABOOT

2 Chronicles 24 in the BNTLV

2 Chronicles 24 in the BOATCB

2 Chronicles 24 in the BOATCB2

2 Chronicles 24 in the BOBCV

2 Chronicles 24 in the BOCNT

2 Chronicles 24 in the BOECS

2 Chronicles 24 in the BOHCB

2 Chronicles 24 in the BOHCV

2 Chronicles 24 in the BOHLNT

2 Chronicles 24 in the BOHNTLTAL

2 Chronicles 24 in the BOICB

2 Chronicles 24 in the BOILNTAP

2 Chronicles 24 in the BOITCV

2 Chronicles 24 in the BOKCV

2 Chronicles 24 in the BOKCV2

2 Chronicles 24 in the BOKHWOG

2 Chronicles 24 in the BOKSSV

2 Chronicles 24 in the BOLCB

2 Chronicles 24 in the BOLCB2

2 Chronicles 24 in the BOMCV

2 Chronicles 24 in the BONAV

2 Chronicles 24 in the BONCB

2 Chronicles 24 in the BONLT

2 Chronicles 24 in the BONUT2

2 Chronicles 24 in the BOPLNT

2 Chronicles 24 in the BOSCB

2 Chronicles 24 in the BOSNC

2 Chronicles 24 in the BOTLNT

2 Chronicles 24 in the BOVCB

2 Chronicles 24 in the BOYCB

2 Chronicles 24 in the BPBB

2 Chronicles 24 in the BPH

2 Chronicles 24 in the BSB

2 Chronicles 24 in the CCB

2 Chronicles 24 in the CUV

2 Chronicles 24 in the CUVS

2 Chronicles 24 in the DBT

2 Chronicles 24 in the DGDNT

2 Chronicles 24 in the DHNT

2 Chronicles 24 in the DNT

2 Chronicles 24 in the ELBE

2 Chronicles 24 in the EMTV

2 Chronicles 24 in the ESV

2 Chronicles 24 in the FBV

2 Chronicles 24 in the FEB

2 Chronicles 24 in the GGMNT

2 Chronicles 24 in the GNT

2 Chronicles 24 in the HARY

2 Chronicles 24 in the HNT

2 Chronicles 24 in the IRVA

2 Chronicles 24 in the IRVB

2 Chronicles 24 in the IRVG

2 Chronicles 24 in the IRVH

2 Chronicles 24 in the IRVK

2 Chronicles 24 in the IRVM

2 Chronicles 24 in the IRVM2

2 Chronicles 24 in the IRVO

2 Chronicles 24 in the IRVP

2 Chronicles 24 in the IRVT

2 Chronicles 24 in the IRVT2

2 Chronicles 24 in the IRVU

2 Chronicles 24 in the ISVN

2 Chronicles 24 in the JSNT

2 Chronicles 24 in the KAPI

2 Chronicles 24 in the KBT1ETNIK

2 Chronicles 24 in the KBV

2 Chronicles 24 in the KJV

2 Chronicles 24 in the KNFD

2 Chronicles 24 in the LBA

2 Chronicles 24 in the LBLA

2 Chronicles 24 in the LNT

2 Chronicles 24 in the LSV

2 Chronicles 24 in the MAAL

2 Chronicles 24 in the MBV

2 Chronicles 24 in the MBV2

2 Chronicles 24 in the MHNT

2 Chronicles 24 in the MKNFD

2 Chronicles 24 in the MNG

2 Chronicles 24 in the MNT

2 Chronicles 24 in the MNT2

2 Chronicles 24 in the MRS1T

2 Chronicles 24 in the NAA

2 Chronicles 24 in the NASB

2 Chronicles 24 in the NBLA

2 Chronicles 24 in the NBS

2 Chronicles 24 in the NBVTP

2 Chronicles 24 in the NET2

2 Chronicles 24 in the NIV11

2 Chronicles 24 in the NNT

2 Chronicles 24 in the NNT2

2 Chronicles 24 in the NNT3

2 Chronicles 24 in the PDDPT

2 Chronicles 24 in the PFNT

2 Chronicles 24 in the RMNT

2 Chronicles 24 in the SBIAS

2 Chronicles 24 in the SBIBS

2 Chronicles 24 in the SBIBS2

2 Chronicles 24 in the SBICS

2 Chronicles 24 in the SBIDS

2 Chronicles 24 in the SBIGS

2 Chronicles 24 in the SBIHS

2 Chronicles 24 in the SBIIS

2 Chronicles 24 in the SBIIS2

2 Chronicles 24 in the SBIIS3

2 Chronicles 24 in the SBIKS

2 Chronicles 24 in the SBIKS2

2 Chronicles 24 in the SBIMS

2 Chronicles 24 in the SBIOS

2 Chronicles 24 in the SBIPS

2 Chronicles 24 in the SBISS

2 Chronicles 24 in the SBITS

2 Chronicles 24 in the SBITS2

2 Chronicles 24 in the SBITS3

2 Chronicles 24 in the SBITS4

2 Chronicles 24 in the SBIUS

2 Chronicles 24 in the SBIVS

2 Chronicles 24 in the SBT

2 Chronicles 24 in the SBT1E

2 Chronicles 24 in the SCHL

2 Chronicles 24 in the SNT

2 Chronicles 24 in the SUSU

2 Chronicles 24 in the SUSU2

2 Chronicles 24 in the SYNO

2 Chronicles 24 in the TBIAOTANT

2 Chronicles 24 in the TBT1E

2 Chronicles 24 in the TBT1E2

2 Chronicles 24 in the TFTIP

2 Chronicles 24 in the TFTU

2 Chronicles 24 in the TGNTATF3T

2 Chronicles 24 in the THAI

2 Chronicles 24 in the TNFD

2 Chronicles 24 in the TNT

2 Chronicles 24 in the TNTIK

2 Chronicles 24 in the TNTIL

2 Chronicles 24 in the TNTIN

2 Chronicles 24 in the TNTIP

2 Chronicles 24 in the TNTIZ

2 Chronicles 24 in the TOMA

2 Chronicles 24 in the TTENT

2 Chronicles 24 in the UBG

2 Chronicles 24 in the UGV

2 Chronicles 24 in the UGV2

2 Chronicles 24 in the UGV3

2 Chronicles 24 in the VBL

2 Chronicles 24 in the VDCC

2 Chronicles 24 in the YALU

2 Chronicles 24 in the YAPE

2 Chronicles 24 in the YBVTP

2 Chronicles 24 in the ZBP