2 Chronicles 25 (BOGWICC)

1 Amaziya anali wa zaka 25 pamene anakhala mfumu, ndipo analamulira mu Yerusalemu kwa zaka 29. Dzina la amayi ake linali Yehoyadini wa ku Yerusalemu. 2 Iye anachita zolungama pamaso pa Yehova, koma osati ndi mtima wonse. 3 Pamene mphamvu zonse zaufumu zinali mʼmanja mwake, iye anapha akuluakulu amene anapha abambo ake, mfumu ija. 4 Komabe iye sanaphe ana awo koma anatsatira zolembedwa mʼbuku la Mose, mʼmene Yehova analamula kuti, “Makolo sadzaphedwa chifukwa cha ana awo kapena ana kuphedwa chifukwa cha makolo awo. Aliyense adzafera machimo ake.” 5 Amaziya anasonkhanitsa anthu a ku Yuda ndipo anawapatsa zochita molingana ndi mabanja awo kukhala anthu olamulira 1,000, ndi olamulira 100 pa Ayuda onse ndi Benjamini. Ndipo iye anawerenga amene anali ndi zaka makumi awiri kapena kupitirirapo napeza kuti analipo amuna 300,000 okonzeka kugwira ntchito ya usilikali, okhoza kugwiritsa ntchito mkondo ndi chishango. 6 Iye analembanso ntchito anthu odziwa nkhondo 100,000 ochokera ku Israeli pa mtengo wa makilogalamu 3,400 a siliva. 7 Koma munthu wa Mulungu anabwera kwa iye ndipo anati, “Inu mfumu, asilikali awa ochokera ku Israeli asapite ndi inu, pakuti Yehova sali ndi Israeli kapena ndi aliyense wa anthu a Efereimu. 8 Ngakhale mupite ndi kuchita nkhondo molimba mtima, Mulungu adzakugonjetsani pamaso pa adani anu, pakuti Mulungu ali ndi mphamvu yothandiza kapena kugonjetsa.” 9 Amaziya anafunsa munthu wa Mulungu kuti, “Koma nanga za makilogalamu aja a siliva amene ndapereka kwa asilikali a Israeli?”Munthu wa Mulungu anayankha kuti, “Yehova atha kukupatsani zambiri kuposa zimenezo.” 10 Choncho Amaziya anachotsa asilikali amene anabwera kwa iye kuchokera ku Efereimu ndipo anawatumiza kwawo. Iwo anakwiyira anthu a ku Yuda ndipo anapita kwawo atapsa mtima kwambiri. 11 Ndipo Amaziya analimba mtima ndipo anatsogolera gulu lake lankhondo ku Chigwa cha Mchere, kumene anapha anthu 10,000 a ku Seiri. 12 Gulu la ankhondo la Yuda linagwiranso anthu amoyo 10,000, napita nawo pamwamba pa thanthwe ndipo anawaponya pansi kotero kuti onse ananyenyeka. 13 Pa nthawi imeneyi asilikali amene Amaziya anawabweza ndipo sanawalole kuti achite nawo nkhondo, anakathira nkhondo mizinda ya Yuda kuyambira ku Samariya mpaka ku Beti-Horoni. Iwo anapha anthu 3,000 ndipo anafunkha katundu wambiri. 14 Amaziya atabwerera kuja anakapha Aedomu, anabweretsa milungu ya anthu a ku Seiri. Ndipo anayika kuti ikhale milungu yake, ankayipembedza ndi kupereka nsembe zopsereza. 15 Yehova anakwiyira Amaziya, ndipo anamutumizira mneneri amene anati, “Nʼchifukwa chiyani mukupembedza milungu ya anthu awa, imene sinathe kupulumutsa anthu ake mʼdzanja lanu?” 16 Iye ali kuyankhula, mfumu inati, “Kodi ife takusankha iwe kuti ukhale mlangizi wa mfumu? Khala chete! Ufuna kuphedweranji?”Choncho mneneriyo analeka koma anati, “Ine ndikudziwa kuti Mulungu watsimikiza kukuwonongani chifukwa mwachita izi ndipo simunamvere uphungu wanga.” 17 Amaziya mfumu ya ku Yuda, atafunsa alangizi ake, anatumiza mawu awa kwa Yowasi mwana wa Yehowahazi mwana wa Yehu, mfumu ya Israeli: “Bwera udzakumane nane maso ndi maso.” 18 Koma Yowasi mfumu ya Israeli inayankha Amaziya mfumu ya Yuda kuti, “Nthawi ina kamtengo kaminga ka ku Lebanoni kanatumiza mawu kwa mkungudza wa ku Lebanoni kuti, ‘Pereka mwana wako wamkazi kwa mwana wanga kuti amukwatire!’ Koma chirombo cha ku Lebanoni chinabwera ndi kupondaponda mtengo wa minga uja. 19 Iwe ukuti wagonjetsa Edomu, ndipo tsopano ukudzikuza ndi kudzitamandira, koma khala kwanu komweko! Nʼchifukwa chiyani ukufuna mavuto ndi kudzichititsa kuti ugwe pamodzinso ndi Yuda?” 20 Komabe Amaziya sanamvere pakuti ndi Mulungu amene anakonzeratu kuti awapereke kwa Yehowasi, chifukwa iwo amapembedza milungu ya ku Edomu. 21 Kotero Yowasi mfumu ya Israeli inakamuthira nkhondo. Iye ndi Amaziya anayangʼanana maso ndi maso ku Beti-Semesi ku Yuda. 22 Yuda anagonjetsedwa ndi Israeli ndipo munthu aliyense anathawira kwawo. 23 Yehowahazi mfumu ya Israeli inagwira Amaziya mfumu ya Yuda, mwana wa Yowasi, mwana wa Ahaziya ku Beti-Semesi. Yehowasi anabwera naye ku Yerusalemu ndipo anagwetsa khoma la Yerusalemu kuyambira pa Chipata cha Efereimu mpaka ku Chipata Chapangodya, khoma lotalika mamita 180. 24 Iye anatenga golide ndi siliva yense ndi zida zonse zimene zimapezeka mʼNyumba ya Mulungu zimene ankazisamalira Obedi-Edomu, pamodzinso ndi chuma cha mʼnyumba yaufumu ndipo anatenga anthu ngati chikole. 25 Amaziya mwana wa Yowasi mfumu ya Yuda anakhala ndi moyo kwa zaka khumi ndi zisanu atamwalira Yehowasi mwana wa Yehowahazi mfumu ya Israeli. 26 Ntchito zina za mfumu Amaziya, kuyambira pachiyambi mpaka pa mapeto, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mafumu a Yuda ndi Israeli? 27 Kuyambira nthawi imene Amaziya analeka kutsatira Yehova anthu anamukonzera chiwembu mu Yerusalemu ndipo anathawira ku Lakisi, koma adaniwo anatumiza anthu ku Lakisiko ndipo anamupha komweko. 28 Iwo anabwera naye ali pa kavalo ndipo anayikidwa mʼmanda ndi makolo ake mu mzinda wa Yuda.

In Other Versions

2 Chronicles 25 in the ANGEFD

2 Chronicles 25 in the ANTPNG2D

2 Chronicles 25 in the AS21

2 Chronicles 25 in the BAGH

2 Chronicles 25 in the BBPNG

2 Chronicles 25 in the BBT1E

2 Chronicles 25 in the BDS

2 Chronicles 25 in the BEV

2 Chronicles 25 in the BHAD

2 Chronicles 25 in the BIB

2 Chronicles 25 in the BLPT

2 Chronicles 25 in the BNT

2 Chronicles 25 in the BNTABOOT

2 Chronicles 25 in the BNTLV

2 Chronicles 25 in the BOATCB

2 Chronicles 25 in the BOATCB2

2 Chronicles 25 in the BOBCV

2 Chronicles 25 in the BOCNT

2 Chronicles 25 in the BOECS

2 Chronicles 25 in the BOHCB

2 Chronicles 25 in the BOHCV

2 Chronicles 25 in the BOHLNT

2 Chronicles 25 in the BOHNTLTAL

2 Chronicles 25 in the BOICB

2 Chronicles 25 in the BOILNTAP

2 Chronicles 25 in the BOITCV

2 Chronicles 25 in the BOKCV

2 Chronicles 25 in the BOKCV2

2 Chronicles 25 in the BOKHWOG

2 Chronicles 25 in the BOKSSV

2 Chronicles 25 in the BOLCB

2 Chronicles 25 in the BOLCB2

2 Chronicles 25 in the BOMCV

2 Chronicles 25 in the BONAV

2 Chronicles 25 in the BONCB

2 Chronicles 25 in the BONLT

2 Chronicles 25 in the BONUT2

2 Chronicles 25 in the BOPLNT

2 Chronicles 25 in the BOSCB

2 Chronicles 25 in the BOSNC

2 Chronicles 25 in the BOTLNT

2 Chronicles 25 in the BOVCB

2 Chronicles 25 in the BOYCB

2 Chronicles 25 in the BPBB

2 Chronicles 25 in the BPH

2 Chronicles 25 in the BSB

2 Chronicles 25 in the CCB

2 Chronicles 25 in the CUV

2 Chronicles 25 in the CUVS

2 Chronicles 25 in the DBT

2 Chronicles 25 in the DGDNT

2 Chronicles 25 in the DHNT

2 Chronicles 25 in the DNT

2 Chronicles 25 in the ELBE

2 Chronicles 25 in the EMTV

2 Chronicles 25 in the ESV

2 Chronicles 25 in the FBV

2 Chronicles 25 in the FEB

2 Chronicles 25 in the GGMNT

2 Chronicles 25 in the GNT

2 Chronicles 25 in the HARY

2 Chronicles 25 in the HNT

2 Chronicles 25 in the IRVA

2 Chronicles 25 in the IRVB

2 Chronicles 25 in the IRVG

2 Chronicles 25 in the IRVH

2 Chronicles 25 in the IRVK

2 Chronicles 25 in the IRVM

2 Chronicles 25 in the IRVM2

2 Chronicles 25 in the IRVO

2 Chronicles 25 in the IRVP

2 Chronicles 25 in the IRVT

2 Chronicles 25 in the IRVT2

2 Chronicles 25 in the IRVU

2 Chronicles 25 in the ISVN

2 Chronicles 25 in the JSNT

2 Chronicles 25 in the KAPI

2 Chronicles 25 in the KBT1ETNIK

2 Chronicles 25 in the KBV

2 Chronicles 25 in the KJV

2 Chronicles 25 in the KNFD

2 Chronicles 25 in the LBA

2 Chronicles 25 in the LBLA

2 Chronicles 25 in the LNT

2 Chronicles 25 in the LSV

2 Chronicles 25 in the MAAL

2 Chronicles 25 in the MBV

2 Chronicles 25 in the MBV2

2 Chronicles 25 in the MHNT

2 Chronicles 25 in the MKNFD

2 Chronicles 25 in the MNG

2 Chronicles 25 in the MNT

2 Chronicles 25 in the MNT2

2 Chronicles 25 in the MRS1T

2 Chronicles 25 in the NAA

2 Chronicles 25 in the NASB

2 Chronicles 25 in the NBLA

2 Chronicles 25 in the NBS

2 Chronicles 25 in the NBVTP

2 Chronicles 25 in the NET2

2 Chronicles 25 in the NIV11

2 Chronicles 25 in the NNT

2 Chronicles 25 in the NNT2

2 Chronicles 25 in the NNT3

2 Chronicles 25 in the PDDPT

2 Chronicles 25 in the PFNT

2 Chronicles 25 in the RMNT

2 Chronicles 25 in the SBIAS

2 Chronicles 25 in the SBIBS

2 Chronicles 25 in the SBIBS2

2 Chronicles 25 in the SBICS

2 Chronicles 25 in the SBIDS

2 Chronicles 25 in the SBIGS

2 Chronicles 25 in the SBIHS

2 Chronicles 25 in the SBIIS

2 Chronicles 25 in the SBIIS2

2 Chronicles 25 in the SBIIS3

2 Chronicles 25 in the SBIKS

2 Chronicles 25 in the SBIKS2

2 Chronicles 25 in the SBIMS

2 Chronicles 25 in the SBIOS

2 Chronicles 25 in the SBIPS

2 Chronicles 25 in the SBISS

2 Chronicles 25 in the SBITS

2 Chronicles 25 in the SBITS2

2 Chronicles 25 in the SBITS3

2 Chronicles 25 in the SBITS4

2 Chronicles 25 in the SBIUS

2 Chronicles 25 in the SBIVS

2 Chronicles 25 in the SBT

2 Chronicles 25 in the SBT1E

2 Chronicles 25 in the SCHL

2 Chronicles 25 in the SNT

2 Chronicles 25 in the SUSU

2 Chronicles 25 in the SUSU2

2 Chronicles 25 in the SYNO

2 Chronicles 25 in the TBIAOTANT

2 Chronicles 25 in the TBT1E

2 Chronicles 25 in the TBT1E2

2 Chronicles 25 in the TFTIP

2 Chronicles 25 in the TFTU

2 Chronicles 25 in the TGNTATF3T

2 Chronicles 25 in the THAI

2 Chronicles 25 in the TNFD

2 Chronicles 25 in the TNT

2 Chronicles 25 in the TNTIK

2 Chronicles 25 in the TNTIL

2 Chronicles 25 in the TNTIN

2 Chronicles 25 in the TNTIP

2 Chronicles 25 in the TNTIZ

2 Chronicles 25 in the TOMA

2 Chronicles 25 in the TTENT

2 Chronicles 25 in the UBG

2 Chronicles 25 in the UGV

2 Chronicles 25 in the UGV2

2 Chronicles 25 in the UGV3

2 Chronicles 25 in the VBL

2 Chronicles 25 in the VDCC

2 Chronicles 25 in the YALU

2 Chronicles 25 in the YAPE

2 Chronicles 25 in the YBVTP

2 Chronicles 25 in the ZBP