2 Chronicles 33 (BOGWICC)

1 Manase anali wa zaka khumi ndi ziwiri pamene anakhala mfumu, ndipo analamulira mu Yerusalemu kwa zaka 55. 2 Iye anachita zoyipa pamaso pa Yehova, potsatira machitidwe a mitundu imene Yehova anayithamangitsa pamaso pa Aisraeli. 3 Iyeyo anamanganso malo opembedzerapo mafano amene Hezekiya abambo ake anawaphwasula; anamanganso maguwa ansembe a Baala ndi kupanga mafano a Asera. Iye amagwadira zolengedwa zonse zamlengalenga ndi kumazipembedza. 4 Manase anamanga maguwa mʼNyumba ya Yehova, mʼmene Yehova ananena kuti, “Ine ndidzakhala mu Yerusalemu mpaka muyaya.” 5 Mʼmabwalo onse awiri a Nyumba ya Yehova anamangamo maguwa ansembe a zolengedwa zonse zamlengalenga. 6 Iye ankakapereka ana ake aamuna ngati nsembe yopsereza ku chigwa cha Hinomu, ankachita zamatsenga, kuwombeza ndi ufiti, ankakafunsira kwa woyankhula ndi mizimu ya anthu akufa. Iye anachita zoyipa zambiri pamaso pa Yehova, kumukwiyitsa Iyeyo. 7 Manase anatenga fano losema limene anapanga ndi kuliyika mʼNyumba ya Mulungu, zimene Mulungu ananena kwa Davide ndi kwa mwana wake Solomoni kuti, “Mʼnyumba ya Mulungu muno, mu Yerusalemu muno, malo amene ndawasankha pakati pa mafuko onse a Israeli, ndidzakhalamo mpaka muyaya. 8 Ine sindidzachotsanso phazi la Aisraeli kuchoka mʼdziko limene ndawapatsa makolo ako, ngatitu iwowa adzasamalira kuchita chilichonse chimene ndinawalamulira za malamulo onse, malangizo ndi miyambo imene inapatsidwa kudzera mwa Mose.” 9 Koma Manase anasocheretsa anthu a ku Yuda ndi Yerusalemu, kotero anachita zoyipa zambiri kupambana mitundu imene Yehova anayiwononga pamaso pa Aisraeli. 10 Yehova anayankhula kwa Manase ndi anthu ake, koma iwo sanasamaleko. 11 Kotero Yehova anawatumizira atsogoleri a ankhondo a ku Asiriya amene anagwira Manase ukapolo, anayika ngowe mʼmphuno mwake, namumanga ndi zingwe zamkuwa ndi kupita naye ku Babuloni. 12 Ali pa mavuto akewo anafunafuna kuti Yehova Mulungu wake amukomere mtima ndipo anadzichepetsa kwakukulu pamaso pa Mulungu wa makolo ake. 13 Ndipo atapemphera, Yehova anakhudzidwa ndi kupempha kwakeko ndipo anamvera madandawulo ake. Kotero anamubweretsanso ku Yerusalemu ndi ku ufumu wake. Ndipo Manase anadziwa kuti Yehova ndi Mulungu. 14 Zitapita izi iye anamanga khoma la kunja kwa Mzinda wa Davide kumadzulo kwa kasupe wa Gihoni ku chigwa mpaka polowera ku Chipata cha Nsomba kuzungulira phiri la Ofeli. Iyeyo anakweza kwambiri khomalo. Anayikanso atsogoleri a nkhondo ku mizinda yonse yotetezedwa ya Yuda. 15 Iye anachotsa milungu yonse yachilendo ndi fano mʼNyumba ya Yehova komanso maguwa ansembe onse amene anamanga pa phiri la Nyumba ya Mulungu ndi mu Yerusalemu, nazitayira kunja kwa mzinda. 16 Kenaka anabwezeretsa guwa lansembe la Yehova ndi kupereka zopereka zachiyanjano ndiponso zopereka zamatamando ndipo anawuza Yuda kuti atumikire Yehova Mulungu wa Israeli. 17 Komabe anthu anapitiriza kupereka nsembe ku malo achipembedzo, koma kwa Yehova, Mulungu wawo yekha. 18 Zina ndi zina zokhudza ulamuliro wa Manase, kuphatikiza mapemphero ake kwa Mulungu wake ndi mawu amene alosi anayankhula kwa iye mʼdzina la Yehova Mulungu wa Israeli, zalembedwa mʼmabuku a mafumu a Israeli. 19 Pemphero lake ndi momwe Mulungu anakhudzidwira ndi kupempha kwakeko, pamodzinso ndi machimo ake onse ndi kusakhulupirika kwake, ndiponso malo onse amene anamanga, malo azipembedzo ndi mafano a Asera ndi mafano asanadzichepetse, zonse zalembedwa mʼmbiri ya alosi. 20 Manase anamwalira ndipo anayikidwa mʼmanda mʼnyumba yake yaufumu. Ndipo Amoni mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake. 21 Amoni anali wa zaka 22 pamene anakhala mfumu ndipo analamulira mu Yerusalemu kwa zaka ziwiri. 22 Iye anachita zoyipa pamaso pa Yehova, monga anachitira Manase abambo ake. Amoni analambira ndi kupereka nsembe kwa mafano onse amene anapanga Manase. 23 Koma kusiyana ndi abambo ake Manase, iye sanadzichepetse pamaso pa Yehova. Amoni anawonjeza kulakwa kwake. 24 Akuluakulu a Amoni anamuchita chiwembu ndipo anamupha mʼnyumba yake yaufumu. 25 Koma anthu a mʼdzikomo anapha onse amene anakonzera chiwembu mfumu Amoni, ndipo anayika mwana wake Yosiya kukhala mfumu mʼmalo mwake.

In Other Versions

2 Chronicles 33 in the ANGEFD

2 Chronicles 33 in the ANTPNG2D

2 Chronicles 33 in the AS21

2 Chronicles 33 in the BAGH

2 Chronicles 33 in the BBPNG

2 Chronicles 33 in the BBT1E

2 Chronicles 33 in the BDS

2 Chronicles 33 in the BEV

2 Chronicles 33 in the BHAD

2 Chronicles 33 in the BIB

2 Chronicles 33 in the BLPT

2 Chronicles 33 in the BNT

2 Chronicles 33 in the BNTABOOT

2 Chronicles 33 in the BNTLV

2 Chronicles 33 in the BOATCB

2 Chronicles 33 in the BOATCB2

2 Chronicles 33 in the BOBCV

2 Chronicles 33 in the BOCNT

2 Chronicles 33 in the BOECS

2 Chronicles 33 in the BOHCB

2 Chronicles 33 in the BOHCV

2 Chronicles 33 in the BOHLNT

2 Chronicles 33 in the BOHNTLTAL

2 Chronicles 33 in the BOICB

2 Chronicles 33 in the BOILNTAP

2 Chronicles 33 in the BOITCV

2 Chronicles 33 in the BOKCV

2 Chronicles 33 in the BOKCV2

2 Chronicles 33 in the BOKHWOG

2 Chronicles 33 in the BOKSSV

2 Chronicles 33 in the BOLCB

2 Chronicles 33 in the BOLCB2

2 Chronicles 33 in the BOMCV

2 Chronicles 33 in the BONAV

2 Chronicles 33 in the BONCB

2 Chronicles 33 in the BONLT

2 Chronicles 33 in the BONUT2

2 Chronicles 33 in the BOPLNT

2 Chronicles 33 in the BOSCB

2 Chronicles 33 in the BOSNC

2 Chronicles 33 in the BOTLNT

2 Chronicles 33 in the BOVCB

2 Chronicles 33 in the BOYCB

2 Chronicles 33 in the BPBB

2 Chronicles 33 in the BPH

2 Chronicles 33 in the BSB

2 Chronicles 33 in the CCB

2 Chronicles 33 in the CUV

2 Chronicles 33 in the CUVS

2 Chronicles 33 in the DBT

2 Chronicles 33 in the DGDNT

2 Chronicles 33 in the DHNT

2 Chronicles 33 in the DNT

2 Chronicles 33 in the ELBE

2 Chronicles 33 in the EMTV

2 Chronicles 33 in the ESV

2 Chronicles 33 in the FBV

2 Chronicles 33 in the FEB

2 Chronicles 33 in the GGMNT

2 Chronicles 33 in the GNT

2 Chronicles 33 in the HARY

2 Chronicles 33 in the HNT

2 Chronicles 33 in the IRVA

2 Chronicles 33 in the IRVB

2 Chronicles 33 in the IRVG

2 Chronicles 33 in the IRVH

2 Chronicles 33 in the IRVK

2 Chronicles 33 in the IRVM

2 Chronicles 33 in the IRVM2

2 Chronicles 33 in the IRVO

2 Chronicles 33 in the IRVP

2 Chronicles 33 in the IRVT

2 Chronicles 33 in the IRVT2

2 Chronicles 33 in the IRVU

2 Chronicles 33 in the ISVN

2 Chronicles 33 in the JSNT

2 Chronicles 33 in the KAPI

2 Chronicles 33 in the KBT1ETNIK

2 Chronicles 33 in the KBV

2 Chronicles 33 in the KJV

2 Chronicles 33 in the KNFD

2 Chronicles 33 in the LBA

2 Chronicles 33 in the LBLA

2 Chronicles 33 in the LNT

2 Chronicles 33 in the LSV

2 Chronicles 33 in the MAAL

2 Chronicles 33 in the MBV

2 Chronicles 33 in the MBV2

2 Chronicles 33 in the MHNT

2 Chronicles 33 in the MKNFD

2 Chronicles 33 in the MNG

2 Chronicles 33 in the MNT

2 Chronicles 33 in the MNT2

2 Chronicles 33 in the MRS1T

2 Chronicles 33 in the NAA

2 Chronicles 33 in the NASB

2 Chronicles 33 in the NBLA

2 Chronicles 33 in the NBS

2 Chronicles 33 in the NBVTP

2 Chronicles 33 in the NET2

2 Chronicles 33 in the NIV11

2 Chronicles 33 in the NNT

2 Chronicles 33 in the NNT2

2 Chronicles 33 in the NNT3

2 Chronicles 33 in the PDDPT

2 Chronicles 33 in the PFNT

2 Chronicles 33 in the RMNT

2 Chronicles 33 in the SBIAS

2 Chronicles 33 in the SBIBS

2 Chronicles 33 in the SBIBS2

2 Chronicles 33 in the SBICS

2 Chronicles 33 in the SBIDS

2 Chronicles 33 in the SBIGS

2 Chronicles 33 in the SBIHS

2 Chronicles 33 in the SBIIS

2 Chronicles 33 in the SBIIS2

2 Chronicles 33 in the SBIIS3

2 Chronicles 33 in the SBIKS

2 Chronicles 33 in the SBIKS2

2 Chronicles 33 in the SBIMS

2 Chronicles 33 in the SBIOS

2 Chronicles 33 in the SBIPS

2 Chronicles 33 in the SBISS

2 Chronicles 33 in the SBITS

2 Chronicles 33 in the SBITS2

2 Chronicles 33 in the SBITS3

2 Chronicles 33 in the SBITS4

2 Chronicles 33 in the SBIUS

2 Chronicles 33 in the SBIVS

2 Chronicles 33 in the SBT

2 Chronicles 33 in the SBT1E

2 Chronicles 33 in the SCHL

2 Chronicles 33 in the SNT

2 Chronicles 33 in the SUSU

2 Chronicles 33 in the SUSU2

2 Chronicles 33 in the SYNO

2 Chronicles 33 in the TBIAOTANT

2 Chronicles 33 in the TBT1E

2 Chronicles 33 in the TBT1E2

2 Chronicles 33 in the TFTIP

2 Chronicles 33 in the TFTU

2 Chronicles 33 in the TGNTATF3T

2 Chronicles 33 in the THAI

2 Chronicles 33 in the TNFD

2 Chronicles 33 in the TNT

2 Chronicles 33 in the TNTIK

2 Chronicles 33 in the TNTIL

2 Chronicles 33 in the TNTIN

2 Chronicles 33 in the TNTIP

2 Chronicles 33 in the TNTIZ

2 Chronicles 33 in the TOMA

2 Chronicles 33 in the TTENT

2 Chronicles 33 in the UBG

2 Chronicles 33 in the UGV

2 Chronicles 33 in the UGV2

2 Chronicles 33 in the UGV3

2 Chronicles 33 in the VBL

2 Chronicles 33 in the VDCC

2 Chronicles 33 in the YALU

2 Chronicles 33 in the YAPE

2 Chronicles 33 in the YBVTP

2 Chronicles 33 in the ZBP