2 Chronicles 35 (BOGWICC)

1 Yosiya anachita chikondwerero cha Paska wa Yehova mu Yerusalemu, ndipo mwana wankhosa wa Paska anaphedwa pa tsiku la khumi ndi chinayi la mwezi woyamba. 2 Iye anasankha ansembe pa maudindo awo ndipo anawalimbikitsa pa ntchito ya mʼnyumba ya Yehova. 3 Iye anati kwa Alevi amene amalangiza Aisraeli onse omwe anadzipatula kwa Yehova: Ikani bokosi lopatulika mʼNyumba ya Mulungu amene Solomoni mwana wa Davide mfumu ya Israeli anamanga. Lisamanyamulidwe pa mapewa anu. Tsopano tumikirani Yehova Mulungu wanu ndi anthu ake Aisraeli. 4 Mukhale mʼmagulu anu molingana ndi mabanja anu, molingana ndi momwe analembera Davide mfumu ya Israeli ndiponso mwana wake Solomoni. 5 “Muziyima ku malo opatulika pamodzi ndi gulu la Alevi oyimira gulu lililonse lalingʼono la mabanja a abale anu amene ndi anthu wamba. 6 Muzipha ana ankhosa a Paska, muzidzipatula nokha ndi kuwakonzera abale anu ana ankhosa awo, kuchita zimene Yehova analamulira mwa Mose.” 7 Yosiya anapereka kwa anthu wamba onse ana ankhosa ndi ana ambuzi okwanira 30,000 ndi ngʼombe zazimuna 3,000, zopereka za Paska zonse zochokera pa chuma chake cha mfumu. 8 Akuluakulu akenso anapereka mwaufulu kwa anthu ndi kwa ansembe ndi Alevi. Hilikiya, Zekariya ndi Yehieli oyangʼanira ntchito ya mʼNyumba ya Mulungu anapereka kwa ansembe zopereka za Paska 2,600 ndi ngʼombe 300. 9 Konaniya nayenso pamodzi ndi Semaya ndi Netaneli, abale ake ndi Hasabiya, Yeiyeli ndi Yozabadi, atsogoleri a Alevi, anapereka nsembe za Paska 5,000 ndi ngʼombe 500 kwa Alevi. 10 Mwambo unakonzedwa ndipo ansembe anayima pamalo pawo pamodzi ndi Alevi mʼmagulu awo monga mfumu inalamulira. 11 Ana ankhosa a Paska anaphedwa ndipo ansembe anawaza magazi amene anaperekedwa kwa iwo pamene Alevi anali kusenda nyamazo. 12 Iwo anayika padera nsembe zopsereza kuti azipereke kwa magulu angʼonoangʼono a mabanja a anthu kuti apereke kwa Yehova monga zinalembedwa mʼbuku la Mose. Ndipo anachita chimodzimodzi ndi ngʼombe. 13 Anawotcha nyama za Paska monga momwe zinalembedwera ndi kuwiritsa zopereka zopatulika mʼmiphika, mʼmitsuko ndi mʼziwaya ndipo anazipereka mofulumira kwa anthu onse. 14 Izi zitatha, anakonza zawo ndi za ansembe chifukwa ansembe, zidzukulu za Aaroni, anali otanganidwa kupereka nsembe zopsereza ndi mafuta a nyama mpaka madzulo. Choncho Alevi amakonza zawo ndi za ansembe, ana a Aaroni. 15 Anthu oyimba nyimbo, zidzukulu za Asafu, anali pa malo awo potsata zomwe analemba Davide, Asafu, Hemani ndi Yedutuni mlosi wa mfumu. Alonda apazipata anali pa chipata chilichonse ndipo kunali kosafunika kuti achoke pa ntchito yawo, poti abale awo Alevi ankawakonzera zonse. 16 Kotero pa nthawi imeneyi ntchito yonse ya Yehova ya chikondwerero cha Paska ndi nsembe zopsereza pa guwa la Yehova inachitika monga analamulira mfumu Yosiya. 17 Aisraeli amene analipo anachita chikondwerero cha Paska pa nthawi imeneyi ndi kuchita mwambo wa chikondwerero cha Buledi Wopanda Yisiti, kwa masiku asanu ndi awiri. 18 Paska yofanana ndi iyi sinachitikepo ku Israeli kuyambira nthawi ya Samueli ndipo palibe mmodzi mwa mafumu a Israeli anachitapo chikondwerero cha Paska ngati anachitira Yosiya pamodzi ndi ansembe, Alevi ndi Ayuda onse ndi Aisraeli amene anali pamodzi ndi anthu a mu Yerusalemu. 19 Chikondwerero cha Paska ichi chinachitika mʼchaka cha 18 cha ulamuliro wa Yosiya. 20 Zimenezi zitachitika, pamene Yosiya anakonzanso Nyumba ya Mulungu, Neko mfumu ya Igupto inapita kukachita nkhondo ku Karikemesi ku mtsinje wa Yufurate, ndipo Yosiya anapita kukamenyana naye. 21 Koma Neko anatumiza amithenga kwa iye kunena kuti, “Kodi pali mkangano wanji pakati pa iwe ndi ine, iwe mfumu ya Yuda? Ine sindikuthira nkhondo iwe pa nthawi ino, koma nyumba imene ndili nayo pa nkhondo. Mulungu wandiwuza kuti ndifulumize choncho leka kutsutsana ndi Mulungu amene ali ndi ine, mwina adzakuwononga.” 22 Komabe Yosiya sanatembenuke kumusiya iyeyo, koma anadzizimbayitsa ndi kukalowa mʼnkhondo. Iye sanamvere zimene Neko ananena molamulidwa ndi Mulungu koma anapita kukamenyana naye ku chigwa ku Megido. 23 Anthu oponya mivi analasa mfumu Yosiya, ndipo iye anawuza akuluakulu ake, “Chotseni. Ndavulazidwa kwambiri.” 24 Choncho anamuchotsa iye mʼgaleta lake, ndipo anamuyika mʼgaleta lina limene anali nalo ndipo anabwera naye ku Yerusalemu kumene anamwalirira. Iye anayikidwa mʼmanda a makolo ake. Ndipo Ayuda ndi Yerusalemu yense anamulira. 25 Yeremiya anapeka nyimbo za maliro chifukwa cha Yosiya, ndipo mpaka lero lino amuna ndi akazi onse oyimba amakumbukira Yosiya pa nyimbo zawo za maliro. Izi zinakhala mwambo mu Israeli ndipo zinalembedwa mʼNyimbo za Maliro. 26 Zochitika zina za ulamuliro wa Yosiya ndi ntchito za kudzipereka kwake, monga zinalembedwa mʼMalamulo a Yehova, 27 zochitika zonse, kuyambira pachiyambi mpaka pa mapeto, zalembedwa mʼbuku la mafumu a Israeli ndi Yuda.

In Other Versions

2 Chronicles 35 in the ANGEFD

2 Chronicles 35 in the ANTPNG2D

2 Chronicles 35 in the AS21

2 Chronicles 35 in the BAGH

2 Chronicles 35 in the BBPNG

2 Chronicles 35 in the BBT1E

2 Chronicles 35 in the BDS

2 Chronicles 35 in the BEV

2 Chronicles 35 in the BHAD

2 Chronicles 35 in the BIB

2 Chronicles 35 in the BLPT

2 Chronicles 35 in the BNT

2 Chronicles 35 in the BNTABOOT

2 Chronicles 35 in the BNTLV

2 Chronicles 35 in the BOATCB

2 Chronicles 35 in the BOATCB2

2 Chronicles 35 in the BOBCV

2 Chronicles 35 in the BOCNT

2 Chronicles 35 in the BOECS

2 Chronicles 35 in the BOHCB

2 Chronicles 35 in the BOHCV

2 Chronicles 35 in the BOHLNT

2 Chronicles 35 in the BOHNTLTAL

2 Chronicles 35 in the BOICB

2 Chronicles 35 in the BOILNTAP

2 Chronicles 35 in the BOITCV

2 Chronicles 35 in the BOKCV

2 Chronicles 35 in the BOKCV2

2 Chronicles 35 in the BOKHWOG

2 Chronicles 35 in the BOKSSV

2 Chronicles 35 in the BOLCB

2 Chronicles 35 in the BOLCB2

2 Chronicles 35 in the BOMCV

2 Chronicles 35 in the BONAV

2 Chronicles 35 in the BONCB

2 Chronicles 35 in the BONLT

2 Chronicles 35 in the BONUT2

2 Chronicles 35 in the BOPLNT

2 Chronicles 35 in the BOSCB

2 Chronicles 35 in the BOSNC

2 Chronicles 35 in the BOTLNT

2 Chronicles 35 in the BOVCB

2 Chronicles 35 in the BOYCB

2 Chronicles 35 in the BPBB

2 Chronicles 35 in the BPH

2 Chronicles 35 in the BSB

2 Chronicles 35 in the CCB

2 Chronicles 35 in the CUV

2 Chronicles 35 in the CUVS

2 Chronicles 35 in the DBT

2 Chronicles 35 in the DGDNT

2 Chronicles 35 in the DHNT

2 Chronicles 35 in the DNT

2 Chronicles 35 in the ELBE

2 Chronicles 35 in the EMTV

2 Chronicles 35 in the ESV

2 Chronicles 35 in the FBV

2 Chronicles 35 in the FEB

2 Chronicles 35 in the GGMNT

2 Chronicles 35 in the GNT

2 Chronicles 35 in the HARY

2 Chronicles 35 in the HNT

2 Chronicles 35 in the IRVA

2 Chronicles 35 in the IRVB

2 Chronicles 35 in the IRVG

2 Chronicles 35 in the IRVH

2 Chronicles 35 in the IRVK

2 Chronicles 35 in the IRVM

2 Chronicles 35 in the IRVM2

2 Chronicles 35 in the IRVO

2 Chronicles 35 in the IRVP

2 Chronicles 35 in the IRVT

2 Chronicles 35 in the IRVT2

2 Chronicles 35 in the IRVU

2 Chronicles 35 in the ISVN

2 Chronicles 35 in the JSNT

2 Chronicles 35 in the KAPI

2 Chronicles 35 in the KBT1ETNIK

2 Chronicles 35 in the KBV

2 Chronicles 35 in the KJV

2 Chronicles 35 in the KNFD

2 Chronicles 35 in the LBA

2 Chronicles 35 in the LBLA

2 Chronicles 35 in the LNT

2 Chronicles 35 in the LSV

2 Chronicles 35 in the MAAL

2 Chronicles 35 in the MBV

2 Chronicles 35 in the MBV2

2 Chronicles 35 in the MHNT

2 Chronicles 35 in the MKNFD

2 Chronicles 35 in the MNG

2 Chronicles 35 in the MNT

2 Chronicles 35 in the MNT2

2 Chronicles 35 in the MRS1T

2 Chronicles 35 in the NAA

2 Chronicles 35 in the NASB

2 Chronicles 35 in the NBLA

2 Chronicles 35 in the NBS

2 Chronicles 35 in the NBVTP

2 Chronicles 35 in the NET2

2 Chronicles 35 in the NIV11

2 Chronicles 35 in the NNT

2 Chronicles 35 in the NNT2

2 Chronicles 35 in the NNT3

2 Chronicles 35 in the PDDPT

2 Chronicles 35 in the PFNT

2 Chronicles 35 in the RMNT

2 Chronicles 35 in the SBIAS

2 Chronicles 35 in the SBIBS

2 Chronicles 35 in the SBIBS2

2 Chronicles 35 in the SBICS

2 Chronicles 35 in the SBIDS

2 Chronicles 35 in the SBIGS

2 Chronicles 35 in the SBIHS

2 Chronicles 35 in the SBIIS

2 Chronicles 35 in the SBIIS2

2 Chronicles 35 in the SBIIS3

2 Chronicles 35 in the SBIKS

2 Chronicles 35 in the SBIKS2

2 Chronicles 35 in the SBIMS

2 Chronicles 35 in the SBIOS

2 Chronicles 35 in the SBIPS

2 Chronicles 35 in the SBISS

2 Chronicles 35 in the SBITS

2 Chronicles 35 in the SBITS2

2 Chronicles 35 in the SBITS3

2 Chronicles 35 in the SBITS4

2 Chronicles 35 in the SBIUS

2 Chronicles 35 in the SBIVS

2 Chronicles 35 in the SBT

2 Chronicles 35 in the SBT1E

2 Chronicles 35 in the SCHL

2 Chronicles 35 in the SNT

2 Chronicles 35 in the SUSU

2 Chronicles 35 in the SUSU2

2 Chronicles 35 in the SYNO

2 Chronicles 35 in the TBIAOTANT

2 Chronicles 35 in the TBT1E

2 Chronicles 35 in the TBT1E2

2 Chronicles 35 in the TFTIP

2 Chronicles 35 in the TFTU

2 Chronicles 35 in the TGNTATF3T

2 Chronicles 35 in the THAI

2 Chronicles 35 in the TNFD

2 Chronicles 35 in the TNT

2 Chronicles 35 in the TNTIK

2 Chronicles 35 in the TNTIL

2 Chronicles 35 in the TNTIN

2 Chronicles 35 in the TNTIP

2 Chronicles 35 in the TNTIZ

2 Chronicles 35 in the TOMA

2 Chronicles 35 in the TTENT

2 Chronicles 35 in the UBG

2 Chronicles 35 in the UGV

2 Chronicles 35 in the UGV2

2 Chronicles 35 in the UGV3

2 Chronicles 35 in the VBL

2 Chronicles 35 in the VDCC

2 Chronicles 35 in the YALU

2 Chronicles 35 in the YAPE

2 Chronicles 35 in the YBVTP

2 Chronicles 35 in the ZBP