2 Chronicles 8 (BOGWICC)

1 Patatha zaka makumi awiri, ndiye nthawi imene Solomoni anamanga Nyumba ya Mulungu ndi nyumba yake yaufumu, 2 Solomoni anamanganso midzi imene anapatsidwa ndi Hiramu, ndipo anakhazikamo Aisraeli. 3 Kenaka Solomoni anapita kukalanda Hamati-zoba. 4 Iye anamanganso Tadimori ku chipululu ndi mizinda yonse yosungiramo chuma, imene anayimanga ku Hamati. 5 Anamanganso Beti-Horoni Wakumtunda ndi Beti-Horoni Wakumunsi, mizinda yotetezedwa yokhala ndi makoma, zitseko ndi zitsulo zotchingira, 6 pamodzinso ndi Baalati ndi mizinda yake yonse yosungira chuma, ndiponso mizinda yonse yosungiramo magaleta ake ndi akavalo ndi chilichonse anafuna kumanga ku Yerusalemu, ku Lebanoni ndi ku madera onse amene iye ankalamulira. 7 Panali anthu amene anatsala pakati pa mitundu ya Ahiti, Aamori, Aperezi, Ahivi ndi Ayebusi (anthu awa sanali Aisraeli). 8 Zimenezi ndiye zinali zidzukulu zawo zotsalira mʼdzikoli, anthu amene Aisraeli sanathe kuwawononga kotheratu. Solomoni anawatenga ndi kukhala akapolo ake ogwira ntchito yathangata, monga zilili mpaka lero lino. 9 Koma Solomoni sanagwiritse ntchito ya ukapolo Aisraeli; Iwo anali anthu ake ankhondo, atsogoleri a ankhondo, olamulira magaleta ndi oyendetsa magaleta ake. 10 Amenewa ndiwo anali akuluakulu oyangʼanira ntchito za mfumu Solomoni. Onse amene ankayangʼanira anthu analipo 250. 11 Solomoni anabweretsa mwana wamkazi wa Farao mu mzinda wa Davide ku nyumba yaufumu yomwe anamumangira, pakuti iye anati, “Mkazi wanga asakhale mʼnyumba yaufumu ya Davide mfumu ya Israeli, chifukwa malo amene Bokosi la Chipangano la Yehova lafikira ndi opatulika.” 12 Solomoni anapereka nsembe zopsereza pa guwa lansembe la Yehova limene anamanga patsogolo pa khonde la polowera, 13 monga momwe zinkafunikira pa tsiku lililonse. Ankapereka nsembezo potsata malamulo a Mose okhudza chikondwerero cha Masabata, chikondwerero cha Mwezi Watsopano ndi zikondwerero zitatu za pa chaka: Chikondwerero cha Buledi Wopanda yisiti, Chikondwerero cha Masabata ndi Chikondwerero cha Misasa. 14 Potsata malangizo a Davide abambo ake, iye anayika ansembe mʼmagulumagulu monga mwa ntchito zawo ndipo anayika Alevi kukhala otsogolera matamando ndi kuthandiza ansembe pa zofunika pa tsiku lililonse. Iye anasankhanso magulumagulu a alonda a pa zipata zosiyanasiyana, chifukwa izi ndi zimene munthu wa Mulungu, Davide analamula. 15 Anthu sanapatukepo pa zimene mfumu inalamula ansembe kapena Alevi pa china chilichonse, kuphatikiza za chuma. 16 Ntchito yonse ya Solomoni inachitika kuyambira tsiku limene maziko a Nyumba ya Mulungu anakhazikitsidwa mpaka kumaliza. Kotero Nyumba ya Yehova inamalizidwa. 17 Kenaka Solomoni anapita ku Ezioni-Geberi ndi Eloti, mʼmbali mwa nyanja ku Edomu. 18 Ndipo Hiramu anatumiza sitima zapamadzi zoyendetsedwa ndi antchito ake, antchito amene ankayidziwa bwino nyanja. Awa pamodzi ndi anthu a Solomoni, anayenda pa madzi kupita ku Ofiri ndipo anakatengako golide olemera makilogalamu 18,000 amene anabwera naye kwa mfumu Solomoni.

In Other Versions

2 Chronicles 8 in the ANGEFD

2 Chronicles 8 in the ANTPNG2D

2 Chronicles 8 in the AS21

2 Chronicles 8 in the BAGH

2 Chronicles 8 in the BBPNG

2 Chronicles 8 in the BBT1E

2 Chronicles 8 in the BDS

2 Chronicles 8 in the BEV

2 Chronicles 8 in the BHAD

2 Chronicles 8 in the BIB

2 Chronicles 8 in the BLPT

2 Chronicles 8 in the BNT

2 Chronicles 8 in the BNTABOOT

2 Chronicles 8 in the BNTLV

2 Chronicles 8 in the BOATCB

2 Chronicles 8 in the BOATCB2

2 Chronicles 8 in the BOBCV

2 Chronicles 8 in the BOCNT

2 Chronicles 8 in the BOECS

2 Chronicles 8 in the BOHCB

2 Chronicles 8 in the BOHCV

2 Chronicles 8 in the BOHLNT

2 Chronicles 8 in the BOHNTLTAL

2 Chronicles 8 in the BOICB

2 Chronicles 8 in the BOILNTAP

2 Chronicles 8 in the BOITCV

2 Chronicles 8 in the BOKCV

2 Chronicles 8 in the BOKCV2

2 Chronicles 8 in the BOKHWOG

2 Chronicles 8 in the BOKSSV

2 Chronicles 8 in the BOLCB

2 Chronicles 8 in the BOLCB2

2 Chronicles 8 in the BOMCV

2 Chronicles 8 in the BONAV

2 Chronicles 8 in the BONCB

2 Chronicles 8 in the BONLT

2 Chronicles 8 in the BONUT2

2 Chronicles 8 in the BOPLNT

2 Chronicles 8 in the BOSCB

2 Chronicles 8 in the BOSNC

2 Chronicles 8 in the BOTLNT

2 Chronicles 8 in the BOVCB

2 Chronicles 8 in the BOYCB

2 Chronicles 8 in the BPBB

2 Chronicles 8 in the BPH

2 Chronicles 8 in the BSB

2 Chronicles 8 in the CCB

2 Chronicles 8 in the CUV

2 Chronicles 8 in the CUVS

2 Chronicles 8 in the DBT

2 Chronicles 8 in the DGDNT

2 Chronicles 8 in the DHNT

2 Chronicles 8 in the DNT

2 Chronicles 8 in the ELBE

2 Chronicles 8 in the EMTV

2 Chronicles 8 in the ESV

2 Chronicles 8 in the FBV

2 Chronicles 8 in the FEB

2 Chronicles 8 in the GGMNT

2 Chronicles 8 in the GNT

2 Chronicles 8 in the HARY

2 Chronicles 8 in the HNT

2 Chronicles 8 in the IRVA

2 Chronicles 8 in the IRVB

2 Chronicles 8 in the IRVG

2 Chronicles 8 in the IRVH

2 Chronicles 8 in the IRVK

2 Chronicles 8 in the IRVM

2 Chronicles 8 in the IRVM2

2 Chronicles 8 in the IRVO

2 Chronicles 8 in the IRVP

2 Chronicles 8 in the IRVT

2 Chronicles 8 in the IRVT2

2 Chronicles 8 in the IRVU

2 Chronicles 8 in the ISVN

2 Chronicles 8 in the JSNT

2 Chronicles 8 in the KAPI

2 Chronicles 8 in the KBT1ETNIK

2 Chronicles 8 in the KBV

2 Chronicles 8 in the KJV

2 Chronicles 8 in the KNFD

2 Chronicles 8 in the LBA

2 Chronicles 8 in the LBLA

2 Chronicles 8 in the LNT

2 Chronicles 8 in the LSV

2 Chronicles 8 in the MAAL

2 Chronicles 8 in the MBV

2 Chronicles 8 in the MBV2

2 Chronicles 8 in the MHNT

2 Chronicles 8 in the MKNFD

2 Chronicles 8 in the MNG

2 Chronicles 8 in the MNT

2 Chronicles 8 in the MNT2

2 Chronicles 8 in the MRS1T

2 Chronicles 8 in the NAA

2 Chronicles 8 in the NASB

2 Chronicles 8 in the NBLA

2 Chronicles 8 in the NBS

2 Chronicles 8 in the NBVTP

2 Chronicles 8 in the NET2

2 Chronicles 8 in the NIV11

2 Chronicles 8 in the NNT

2 Chronicles 8 in the NNT2

2 Chronicles 8 in the NNT3

2 Chronicles 8 in the PDDPT

2 Chronicles 8 in the PFNT

2 Chronicles 8 in the RMNT

2 Chronicles 8 in the SBIAS

2 Chronicles 8 in the SBIBS

2 Chronicles 8 in the SBIBS2

2 Chronicles 8 in the SBICS

2 Chronicles 8 in the SBIDS

2 Chronicles 8 in the SBIGS

2 Chronicles 8 in the SBIHS

2 Chronicles 8 in the SBIIS

2 Chronicles 8 in the SBIIS2

2 Chronicles 8 in the SBIIS3

2 Chronicles 8 in the SBIKS

2 Chronicles 8 in the SBIKS2

2 Chronicles 8 in the SBIMS

2 Chronicles 8 in the SBIOS

2 Chronicles 8 in the SBIPS

2 Chronicles 8 in the SBISS

2 Chronicles 8 in the SBITS

2 Chronicles 8 in the SBITS2

2 Chronicles 8 in the SBITS3

2 Chronicles 8 in the SBITS4

2 Chronicles 8 in the SBIUS

2 Chronicles 8 in the SBIVS

2 Chronicles 8 in the SBT

2 Chronicles 8 in the SBT1E

2 Chronicles 8 in the SCHL

2 Chronicles 8 in the SNT

2 Chronicles 8 in the SUSU

2 Chronicles 8 in the SUSU2

2 Chronicles 8 in the SYNO

2 Chronicles 8 in the TBIAOTANT

2 Chronicles 8 in the TBT1E

2 Chronicles 8 in the TBT1E2

2 Chronicles 8 in the TFTIP

2 Chronicles 8 in the TFTU

2 Chronicles 8 in the TGNTATF3T

2 Chronicles 8 in the THAI

2 Chronicles 8 in the TNFD

2 Chronicles 8 in the TNT

2 Chronicles 8 in the TNTIK

2 Chronicles 8 in the TNTIL

2 Chronicles 8 in the TNTIN

2 Chronicles 8 in the TNTIP

2 Chronicles 8 in the TNTIZ

2 Chronicles 8 in the TOMA

2 Chronicles 8 in the TTENT

2 Chronicles 8 in the UBG

2 Chronicles 8 in the UGV

2 Chronicles 8 in the UGV2

2 Chronicles 8 in the UGV3

2 Chronicles 8 in the VBL

2 Chronicles 8 in the VDCC

2 Chronicles 8 in the YALU

2 Chronicles 8 in the YAPE

2 Chronicles 8 in the YBVTP

2 Chronicles 8 in the ZBP