2 Kings 13 (BOGWICC)

1 Mʼchaka cha 23 cha ufumu wa Yowasi mwana wa Ahaziya mfumu ya Yuda, Yehowahazi, mwana wa Yehu anakhala mfumu ya Israeli mu Samariya, ndipo analamulira zaka 17. 2 Iye anachita zoyipa pamaso pa Yehova potsatira machimo a Yeroboamu mwana Nebati amene anachimwitsa nawo Israeli ndipo iye sanawaleke machimowo. 3 Ndipo Yehova anakwiyira Aisraeli nawayika pansi pa ulamuliro wa Hazaeli mfumu ya Siriya ndi Beni-Hadadi mwana wa Hazaeli masiku awo onse. 4 Tsono Yehowahazi anapempha Yehova kuti amuchitire chifundo ndipo Yehova anamva pempho lake chifukwa anaona momwe mfumu ya Aramu inkapsinjira Aisraeli. 5 Yehova anapatsa Aisraeli munthu woti awapulumutse ndipo anapulumuka mʼdzanja la Aramu. Choncho Aisraeli anakhala mʼnyumba zawo monga ankachitira kale. 6 Komabe Aisraeli sanaleke kuchita machimo a nyumba ya Yeroboamu, amene anachimwitsa nawo Israeli. Iwo anapitirira kuchita machimowo. Ndiponso fano la Asera linakhalabe ku Samariya. 7 Yehowahazi sanatsale ndi ankhondo ambiri koma 50 okha okwera pa akavalo, magaleta khumi ndi asilikali oyenda pansi 10,000. 8 Ntchito zina za Yehowahazi ndi zonse zimene anachita, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Israeli? 9 Yehowahazi anamwalira ndipo anayikidwa mʼmanda mu Samariya. Ndipo Yowasi mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake. 10 Mʼchaka cha 37 cha Yowasi mfumu ya Yuda, Yehowahazi anakhala mfumu ya Israeli mu Samariya, ndipo analamulira zaka 16. 11 Iye anachita zoyipa pamaso pa Yehova ndipo sanaleke kuchita tchimo la Yeroboamu mwana wa Nebati limene anachimwitsa nalo Israeli. 12 Ntchito zina za Yowasi ndi zonse zimene anachita, kuphatikizapo nkhondo yake ndi Amaziya mfumu ya Yuda, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Israeli? 13 Yowasi anayikidwa mʼmanda pamodzi ndi makolo ake ndipo Yeroboamu mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake. Yowasi anayikidwa mʼmanda mu Samariya pamodzi ndi mafumu a Israeli. 14 Tsono Elisa anadwala matenda amene anafa nawo. Yowasi mfumu ya Israeli inapita kukamuona ndipo inamulirira. Iye polira ankanena kuti, “Abambo anga! Abambo anga! Magaleta a Israeli ndi okwerapo ake a Israeli!” 15 Elisa anamuwuza kuti, “Tenga uta ndi mivi.” Ndipo anaterodi. 16 Elisa anawuza mfumu ya Israeli kuti, “Tenga uta mʼdzanja lako.” Pamene anatenga utawo, Elisa anayika manja ake pa manja a mfumuyo. 17 Elisa anamuwuza kuti, “Tsekula zenera.” Ndipo anatsekuladi. Elisa anati, “Ponya muviwo!” Ndipo anaponyadi. Elisa anati, “Muvi wa chigonjetso cha Yehova, muvi wogonjetsera Aaramu! Iwe udzawawononga kwathunthu Aaramu ku Afeki.” 18 Kenaka Elisa anati, “Tenga mivi.” Ndipo mfumu inatenga miviyo. Iye anati, “Lasa pansi.” Mfumu inalasa pansi miviyo katatu nʼkuleka. 19 Munthu wa Mulungu anapsera mtima mfumuyo ndipo anati, “Ukanalasa pansi kasanu kapena kasanu nʼkamodzi. Pamenepo ukanatha kuwagonjetsa Aaramu ndi kuwawononga kwathunthu. Koma tsopano udzawagonjetsa katatu kokha.” 20 Elisa anamwalira ndipo anayikidwa mʼmanda.Tsono magulu a ankhondo a Amowabu ankabwera kudzalowa ndi kudzathira nkhondo dzikolo nthawi ya dzinja. 21 Tsiku lina Aisraeli ena akukayika maliro mʼmanda, mwadzidzidzi anaona gulu lankhondo ndipo munthu womwalirayo anamuponyera mʼmanda a Elisa. Pamene mtembowo unakhudza mafupa a Elisa, munthu wakufayo anatsitsimuka nayimirira. 22 Hazaeli mfumu ya Aramu inazunza Aisraeli nthawi yonse ya ulamuliro wa Yehowahazi. 23 Koma Yehova anawachitira chifundo Aisraeliwo ndi kukhudzika ndi zomwe zinkawachitikira chifukwa cha pangano lake ndi Abrahamu, Isake ndi Yakobo. Mpaka lero lino Iye sanafune kuwawononga kapena kuwachotsa pamaso pake. 24 Hazaeli mfumu ya Aramu inamwalira ndipo mwana wake Beni-Hadadi analowa ufumu mʼmalo mwake. 25 Pamenepo Yowasi mwana wa Yehowahazi analandanso kwa Beni-Hadadi mwana wa Hazaeli mizinda yonse imene iye analanda Yehowahazi abambo ake. Yehowasi anagonjetsa Beni-Hadadi katatu ndipo anatenganso mizinda ya Israeli.

In Other Versions

2 Kings 13 in the ANGEFD

2 Kings 13 in the ANTPNG2D

2 Kings 13 in the AS21

2 Kings 13 in the BAGH

2 Kings 13 in the BBPNG

2 Kings 13 in the BBT1E

2 Kings 13 in the BDS

2 Kings 13 in the BEV

2 Kings 13 in the BHAD

2 Kings 13 in the BIB

2 Kings 13 in the BLPT

2 Kings 13 in the BNT

2 Kings 13 in the BNTABOOT

2 Kings 13 in the BNTLV

2 Kings 13 in the BOATCB

2 Kings 13 in the BOATCB2

2 Kings 13 in the BOBCV

2 Kings 13 in the BOCNT

2 Kings 13 in the BOECS

2 Kings 13 in the BOHCB

2 Kings 13 in the BOHCV

2 Kings 13 in the BOHLNT

2 Kings 13 in the BOHNTLTAL

2 Kings 13 in the BOICB

2 Kings 13 in the BOILNTAP

2 Kings 13 in the BOITCV

2 Kings 13 in the BOKCV

2 Kings 13 in the BOKCV2

2 Kings 13 in the BOKHWOG

2 Kings 13 in the BOKSSV

2 Kings 13 in the BOLCB

2 Kings 13 in the BOLCB2

2 Kings 13 in the BOMCV

2 Kings 13 in the BONAV

2 Kings 13 in the BONCB

2 Kings 13 in the BONLT

2 Kings 13 in the BONUT2

2 Kings 13 in the BOPLNT

2 Kings 13 in the BOSCB

2 Kings 13 in the BOSNC

2 Kings 13 in the BOTLNT

2 Kings 13 in the BOVCB

2 Kings 13 in the BOYCB

2 Kings 13 in the BPBB

2 Kings 13 in the BPH

2 Kings 13 in the BSB

2 Kings 13 in the CCB

2 Kings 13 in the CUV

2 Kings 13 in the CUVS

2 Kings 13 in the DBT

2 Kings 13 in the DGDNT

2 Kings 13 in the DHNT

2 Kings 13 in the DNT

2 Kings 13 in the ELBE

2 Kings 13 in the EMTV

2 Kings 13 in the ESV

2 Kings 13 in the FBV

2 Kings 13 in the FEB

2 Kings 13 in the GGMNT

2 Kings 13 in the GNT

2 Kings 13 in the HARY

2 Kings 13 in the HNT

2 Kings 13 in the IRVA

2 Kings 13 in the IRVB

2 Kings 13 in the IRVG

2 Kings 13 in the IRVH

2 Kings 13 in the IRVK

2 Kings 13 in the IRVM

2 Kings 13 in the IRVM2

2 Kings 13 in the IRVO

2 Kings 13 in the IRVP

2 Kings 13 in the IRVT

2 Kings 13 in the IRVT2

2 Kings 13 in the IRVU

2 Kings 13 in the ISVN

2 Kings 13 in the JSNT

2 Kings 13 in the KAPI

2 Kings 13 in the KBT1ETNIK

2 Kings 13 in the KBV

2 Kings 13 in the KJV

2 Kings 13 in the KNFD

2 Kings 13 in the LBA

2 Kings 13 in the LBLA

2 Kings 13 in the LNT

2 Kings 13 in the LSV

2 Kings 13 in the MAAL

2 Kings 13 in the MBV

2 Kings 13 in the MBV2

2 Kings 13 in the MHNT

2 Kings 13 in the MKNFD

2 Kings 13 in the MNG

2 Kings 13 in the MNT

2 Kings 13 in the MNT2

2 Kings 13 in the MRS1T

2 Kings 13 in the NAA

2 Kings 13 in the NASB

2 Kings 13 in the NBLA

2 Kings 13 in the NBS

2 Kings 13 in the NBVTP

2 Kings 13 in the NET2

2 Kings 13 in the NIV11

2 Kings 13 in the NNT

2 Kings 13 in the NNT2

2 Kings 13 in the NNT3

2 Kings 13 in the PDDPT

2 Kings 13 in the PFNT

2 Kings 13 in the RMNT

2 Kings 13 in the SBIAS

2 Kings 13 in the SBIBS

2 Kings 13 in the SBIBS2

2 Kings 13 in the SBICS

2 Kings 13 in the SBIDS

2 Kings 13 in the SBIGS

2 Kings 13 in the SBIHS

2 Kings 13 in the SBIIS

2 Kings 13 in the SBIIS2

2 Kings 13 in the SBIIS3

2 Kings 13 in the SBIKS

2 Kings 13 in the SBIKS2

2 Kings 13 in the SBIMS

2 Kings 13 in the SBIOS

2 Kings 13 in the SBIPS

2 Kings 13 in the SBISS

2 Kings 13 in the SBITS

2 Kings 13 in the SBITS2

2 Kings 13 in the SBITS3

2 Kings 13 in the SBITS4

2 Kings 13 in the SBIUS

2 Kings 13 in the SBIVS

2 Kings 13 in the SBT

2 Kings 13 in the SBT1E

2 Kings 13 in the SCHL

2 Kings 13 in the SNT

2 Kings 13 in the SUSU

2 Kings 13 in the SUSU2

2 Kings 13 in the SYNO

2 Kings 13 in the TBIAOTANT

2 Kings 13 in the TBT1E

2 Kings 13 in the TBT1E2

2 Kings 13 in the TFTIP

2 Kings 13 in the TFTU

2 Kings 13 in the TGNTATF3T

2 Kings 13 in the THAI

2 Kings 13 in the TNFD

2 Kings 13 in the TNT

2 Kings 13 in the TNTIK

2 Kings 13 in the TNTIL

2 Kings 13 in the TNTIN

2 Kings 13 in the TNTIP

2 Kings 13 in the TNTIZ

2 Kings 13 in the TOMA

2 Kings 13 in the TTENT

2 Kings 13 in the UBG

2 Kings 13 in the UGV

2 Kings 13 in the UGV2

2 Kings 13 in the UGV3

2 Kings 13 in the VBL

2 Kings 13 in the VDCC

2 Kings 13 in the YALU

2 Kings 13 in the YAPE

2 Kings 13 in the YBVTP

2 Kings 13 in the ZBP