2 Samuel 11 (BOGWICC)

1 Nthawi ya mphukira, nthawi imene mafumu amapita ku nkhondo, Davide anatumiza Yowabu ndi ankhondo a mfumu pamodzi ndi gulu lonse lankhondo la Aisraeli. Iwo anawononga Aamoni ndi kuzungulira mzinda wa Raba. Koma Davide anatsala ku Yerusalemu. 2 Tsiku lina cha kumadzulo Davide anadzuka pa bedi lake ndipo ankayenda pamwamba pa nyumba yake. Ali pa dengapo anaona mkazi akusamba. Mkaziyo anali wokongola kwambiri. 3 Ndipo Davide anatuma munthu wina kuti akafufuze za iye. Munthuyo anati, “Kodi uyu si Batiseba, mwana wa Eliamu, mkazi wa Uriya Mhiti?” 4 Ndipo Davide anatumiza amithenga kwa iye kukamuyitana. Batiseba anabwera kwa Davide ndipo anagona naye. (Nʼkuti mkaziyu atayeretsedwa ku masiku ake osamba). Kenaka anabwerera ku nyumba yake. 5 Mkaziyo anakhala woyembekezera ndipo anatumiza mawu kwa Davide kunena kuti, “Ine ndine woyembekezera.” 6 Ndipo Davide anatumiza mawu awa kwa Yowabu: “Nditumizire Uriya Mhiti.” Ndipo Yowabu anamutumiza kwa Davide. 7 Uriya atafika kwa Davide, Davide anamufunsa za momwe analili Yowabu, za asilikali ndi momwe nkhondo inkayendera. 8 Kenaka Davide anati kwa Uriya, “Pita ku nyumba yako ukapumule.” Choncho Uriya anachoka ku nyumba yaufumu, ndipo mfumuyo inatumiza mphatso kwa Uriya. 9 Koma Uriya anagona pa chipata cha nyumba yaufumu pamodzi ndi antchito onse a mbuye wake ndipo sanapite ku nyumba yake. 10 Davide atawuzidwa kuti, “Uriya sanapite ku nyumba yake.” Iye anafunsa kuti, “Kodi iwe sunachokera kutali? Nʼchifukwa chiyani sunapite ku nyumba yako?” 11 Uriya anayankha Davide kuti, “Bokosi la Chipangano ndi Israeli ndiponso Yuda akukhala mʼmatenti, ndipo mbuye wanga Yowabu ndi ankhondo anu mbuye wanga amanga misasa pa mtetete. Ine ndingapite bwanji ku nyumba yanga kukadya ndi kumwa ndiponso kugona ndi mkazi wanga? Pali inu wamoyo, ine sindidzachita chinthu chimenechi.” 12 Ndipo Davide anati kwa iye, “Ukhale konkuno tsiku lina limodzi, ndipo mawa ndikulola kuti upite.” Kotero Uriya anakhala mu Yerusalemu tsiku limenelo ndi tsiku linalo. 13 Davide anayitana Uriya nadya ndi kumwa naye, ndipo Davide anamuledzeretsa. Koma madzulo Uriya anapita kukagona pa mphasa pamodzi ndi antchito a mbuye wake. Iye sanapite ku nyumba yake. 14 Mmawa Davide analemba kalata kwa Yowabu ndipo anayitumiza ndi Uriya. 15 Mʼkalatayo analembamo kuti, “Uriya mumuyike patsogolo penipeni, pamene pali nkhondo yoopsa. Ndipo mumusiye yekha kuti akanthidwe ndi kufa.” 16 Kotero Yowabu atawuzinga mzindawo, anamuyika Uriya pamalo pamene amadziwa kuti pali asilikali amphamvu. 17 Ankhondo a mu mzindawo atabwera kudzamenyana ndi Yowabu, anthu ena a gulu la ankhondo la Davide anaphedwa ndipo Uriya Mhiti uja anaphedwanso. 18 Yowabu anatumiza wamthenga kwa Davide kukafotokoza mwatsatanetsatane za nkhondoyo. 19 Iye anamulangiza wa mthengayo kuti, “Pamene ukatsiriza kufotokozera mfumu za ku nkhondozi, 20 mfumu ikapsa mtima, ndipo akakakufunsa kuti, ‘Nʼchifukwa chiyani munapita pafupi ndi mzindawo kukamenya nkhondo? Inu simunadziwe kuti atha kukuponyerani mivi kuchokera pa khoma? 21 Kodi anapha Abimeleki mwana wa Yerubeseti ndani? Kodi mkazi sanamuponyere mphero kuchokera pa khoma? Kotero kuti anakafera ku Tebezi. Nʼchifukwa chiyani munafika pafupi ndi khoma?’ Ngati iye akafunsa zimenezi, iwe ukanene kwa iye kuti, ‘Mtumiki wanunso Uriya Mhiti wafa.’ ” 22 Mthengayo ananyamuka, ndipo atafika anamuwuza Davide zonse zimene Yowabu anamutuma kuti akanene. 23 Mthengayo anati kwa Davide, “Anthuwo anatiposa mphamvu ndipo anabwera kudzalimbana nafe poyera, koma ife tinawabwezera ku chipata cha mzindawo. 24 Ndipo anthu oponya mivi anatiponyera kuchokera pa khoma, anthu ena a mfumu afa. Kuwonjezera apo, mtumiki wanu Uriya Mhiti wafanso.” 25 Davide anamuwuza mthengayo kuti, “Ukanene izi kwa Yowabu: ‘Zimenezi zisakukhumudwitse; lupanga limapha wina nthawi zinanso wina. Limbikitsa nkhondo pa mzindawo ndipo uwuwononge!’ Ukanene zimenezi pomulimbikitsa Yowabu.” 26 Mkazi wa Uriya atamva kuti mwamuna wake wafa, analira maliro. 27 Nthawi yolira maliro itatha, Davide anamubweretsa ku nyumba yake, ndipo anakhala mkazi wake nabala mwana wamwamuna. Koma Yehova sanakondwe ndi zimene Davide anachitazo.

In Other Versions

2 Samuel 11 in the ANGEFD

2 Samuel 11 in the ANTPNG2D

2 Samuel 11 in the AS21

2 Samuel 11 in the BAGH

2 Samuel 11 in the BBPNG

2 Samuel 11 in the BBT1E

2 Samuel 11 in the BDS

2 Samuel 11 in the BEV

2 Samuel 11 in the BHAD

2 Samuel 11 in the BIB

2 Samuel 11 in the BLPT

2 Samuel 11 in the BNT

2 Samuel 11 in the BNTABOOT

2 Samuel 11 in the BNTLV

2 Samuel 11 in the BOATCB

2 Samuel 11 in the BOATCB2

2 Samuel 11 in the BOBCV

2 Samuel 11 in the BOCNT

2 Samuel 11 in the BOECS

2 Samuel 11 in the BOHCB

2 Samuel 11 in the BOHCV

2 Samuel 11 in the BOHLNT

2 Samuel 11 in the BOHNTLTAL

2 Samuel 11 in the BOICB

2 Samuel 11 in the BOILNTAP

2 Samuel 11 in the BOITCV

2 Samuel 11 in the BOKCV

2 Samuel 11 in the BOKCV2

2 Samuel 11 in the BOKHWOG

2 Samuel 11 in the BOKSSV

2 Samuel 11 in the BOLCB

2 Samuel 11 in the BOLCB2

2 Samuel 11 in the BOMCV

2 Samuel 11 in the BONAV

2 Samuel 11 in the BONCB

2 Samuel 11 in the BONLT

2 Samuel 11 in the BONUT2

2 Samuel 11 in the BOPLNT

2 Samuel 11 in the BOSCB

2 Samuel 11 in the BOSNC

2 Samuel 11 in the BOTLNT

2 Samuel 11 in the BOVCB

2 Samuel 11 in the BOYCB

2 Samuel 11 in the BPBB

2 Samuel 11 in the BPH

2 Samuel 11 in the BSB

2 Samuel 11 in the CCB

2 Samuel 11 in the CUV

2 Samuel 11 in the CUVS

2 Samuel 11 in the DBT

2 Samuel 11 in the DGDNT

2 Samuel 11 in the DHNT

2 Samuel 11 in the DNT

2 Samuel 11 in the ELBE

2 Samuel 11 in the EMTV

2 Samuel 11 in the ESV

2 Samuel 11 in the FBV

2 Samuel 11 in the FEB

2 Samuel 11 in the GGMNT

2 Samuel 11 in the GNT

2 Samuel 11 in the HARY

2 Samuel 11 in the HNT

2 Samuel 11 in the IRVA

2 Samuel 11 in the IRVB

2 Samuel 11 in the IRVG

2 Samuel 11 in the IRVH

2 Samuel 11 in the IRVK

2 Samuel 11 in the IRVM

2 Samuel 11 in the IRVM2

2 Samuel 11 in the IRVO

2 Samuel 11 in the IRVP

2 Samuel 11 in the IRVT

2 Samuel 11 in the IRVT2

2 Samuel 11 in the IRVU

2 Samuel 11 in the ISVN

2 Samuel 11 in the JSNT

2 Samuel 11 in the KAPI

2 Samuel 11 in the KBT1ETNIK

2 Samuel 11 in the KBV

2 Samuel 11 in the KJV

2 Samuel 11 in the KNFD

2 Samuel 11 in the LBA

2 Samuel 11 in the LBLA

2 Samuel 11 in the LNT

2 Samuel 11 in the LSV

2 Samuel 11 in the MAAL

2 Samuel 11 in the MBV

2 Samuel 11 in the MBV2

2 Samuel 11 in the MHNT

2 Samuel 11 in the MKNFD

2 Samuel 11 in the MNG

2 Samuel 11 in the MNT

2 Samuel 11 in the MNT2

2 Samuel 11 in the MRS1T

2 Samuel 11 in the NAA

2 Samuel 11 in the NASB

2 Samuel 11 in the NBLA

2 Samuel 11 in the NBS

2 Samuel 11 in the NBVTP

2 Samuel 11 in the NET2

2 Samuel 11 in the NIV11

2 Samuel 11 in the NNT

2 Samuel 11 in the NNT2

2 Samuel 11 in the NNT3

2 Samuel 11 in the PDDPT

2 Samuel 11 in the PFNT

2 Samuel 11 in the RMNT

2 Samuel 11 in the SBIAS

2 Samuel 11 in the SBIBS

2 Samuel 11 in the SBIBS2

2 Samuel 11 in the SBICS

2 Samuel 11 in the SBIDS

2 Samuel 11 in the SBIGS

2 Samuel 11 in the SBIHS

2 Samuel 11 in the SBIIS

2 Samuel 11 in the SBIIS2

2 Samuel 11 in the SBIIS3

2 Samuel 11 in the SBIKS

2 Samuel 11 in the SBIKS2

2 Samuel 11 in the SBIMS

2 Samuel 11 in the SBIOS

2 Samuel 11 in the SBIPS

2 Samuel 11 in the SBISS

2 Samuel 11 in the SBITS

2 Samuel 11 in the SBITS2

2 Samuel 11 in the SBITS3

2 Samuel 11 in the SBITS4

2 Samuel 11 in the SBIUS

2 Samuel 11 in the SBIVS

2 Samuel 11 in the SBT

2 Samuel 11 in the SBT1E

2 Samuel 11 in the SCHL

2 Samuel 11 in the SNT

2 Samuel 11 in the SUSU

2 Samuel 11 in the SUSU2

2 Samuel 11 in the SYNO

2 Samuel 11 in the TBIAOTANT

2 Samuel 11 in the TBT1E

2 Samuel 11 in the TBT1E2

2 Samuel 11 in the TFTIP

2 Samuel 11 in the TFTU

2 Samuel 11 in the TGNTATF3T

2 Samuel 11 in the THAI

2 Samuel 11 in the TNFD

2 Samuel 11 in the TNT

2 Samuel 11 in the TNTIK

2 Samuel 11 in the TNTIL

2 Samuel 11 in the TNTIN

2 Samuel 11 in the TNTIP

2 Samuel 11 in the TNTIZ

2 Samuel 11 in the TOMA

2 Samuel 11 in the TTENT

2 Samuel 11 in the UBG

2 Samuel 11 in the UGV

2 Samuel 11 in the UGV2

2 Samuel 11 in the UGV3

2 Samuel 11 in the VBL

2 Samuel 11 in the VDCC

2 Samuel 11 in the YALU

2 Samuel 11 in the YAPE

2 Samuel 11 in the YBVTP

2 Samuel 11 in the ZBP