2 Samuel 12 (BOGWICC)

1 Tsono Yehova anatumiza Natani kwa Davide. Atafika kwa Davide anati, “Panali anthu awiri mʼmizinda ina, wina wolemera ndi wina wosauka. 2 Munthu wolemerayo anali ndi nkhosa ndi ngʼombe zambiri, 3 koma wosaukayo analibe chilichonse kupatula kankhosa kamodzi kakakazi kamene anakagula. Iye anakasunga ndipo kanakula naye pamodzi ndi ana ake. Kamadya chakudya chake, kamamwera chikho chake ndipo kamagona mʼmanja mwake. Kanali ngati mwana wamkazi kwa iyeyo. 4 “Ndipo mlendo anafika kwa munthu wolemera uja, koma munthu wolemerayo sanafune kutenga imodzi mwa nkhosa kapena ngʼombe zake kuti akonzere chakudya mlendo amene anafika kwa iye. Mʼmalo mwake anatenga mwana wankhosa wamkazi wa munthu wosauka uja nakonzera chakudya mlendo uja amene anabwera kwa iye.” 5 Davide anapsa mtima kwambiri chifukwa cha munthuyo ndipo anati kwa Natani, “Pali Yehova, munthu amene anachita zimenezi ayenera kufa basi! 6 Iye ayenera kulipira mwana wankhosa wamkaziyo kanayi, chifukwa anachita chinthu chimenechi ndipo analibe chifundo.” 7 Kenaka Natani anati kwa Davide, “Munthuyo ndinu! Yehova, Mulungu wa Israeli akuti, ‘Ine ndinakudzoza kukhala mfumu ya Israeli, ndipo ndinakupulumutsa mʼdzanja la Sauli. 8 Ndinakupatsanso banja la mbuye wako ndiponso akazi a mbuye wako mʼmanja mwako. Ine ndinakupatsanso banja la Israeli ndi Yuda. Ndipo ngati zinthu zonse izi zinali zochepa, Ine ndikanakupatsa zambiri. 9 Nʼchifukwa chiyani unanyoza mawu a Yehova pochita chimene chili choyipa pamaso pake? Iwe unakantha Uriya Mhiti ndi lupanga ndipo unatenga mkazi wake kukhala wako. Uriyayo unamupha ndi lupanga la Aamoni. 10 Ndipo tsopano lupanga silidzachoka pa nyumba yako, chifukwa unandinyoza ine ndi kutenga mkazi wa Uriya Mhiti kukhala wako.’ 11 “Yehova akuti, ‘Ine ndidzabweretsa tsoka pa iwe lochokera mʼbanja lako. Ndidzatenga akazi ako iwe ukuona ndi kuwapereka kwa wina amene ali pafupi nawe, ndipo iye adzagona ndi akazi ako masanasana Aisraeli onse akuona. 12 Iwe unachita zimenezi mwamseri koma Ine ndidzachita izi masanasana Aisraeli onse akuona.’ ” 13 Kenaka Davide anati kwa Natani, “Ine ndachimwira Yehova.”Natani anayankha kuti, “Yehova wachotsa tchimo lanu. Simufa ayi. 14 Komabe, popeza pochita zimenezi mwachititsa kuti adani a Yehova amunyoze, mwana amene akubalireniyo adzafa.” 15 Natani atapita kwawo, Yehova anakantha mwana amene mkazi wa Uriya anabereka ndipo anayamba kudwala. 16 Davide anapempherera mwanayo kwa Mulungu. Iye anasala chakudya ndipo analowa mʼnyumba mwake nagona pansi usiku wonse. 17 Akuluakulu a banja lake anayima pambali pake kuti amudzutse, koma iye anakana, ndipo sanadye chakudya chilichonse pamodzi ndi iwo. 18 Mwana anamwalira pa tsiku lachisanu ndi chiwiri. Antchito a Davide anaopa kumuwuza kuti mwanayo wamwalira, popeza ankaganiza kuti, “Pamene mwanayu anali ndi moyo, ife tinayankhula Davide koma sanatimvere. Nanga tingamuwuze bwanji kuti mwana wamwalira? Mwina atha kudzipweteka.” 19 Davide anaona kuti antchito ake amanongʼonezana pakati pawo ndipo anazindikira kuti mwanayo wamwalira. Iye anafunsa kuti, “Kodi mwanayo wamwalira?”Iwo anayankha kuti, “Inde wamwalira.” 20 Ndipo Davide anayimirira. Anakasamba nadzola mafuta ndi kusintha zovala zake. Pambuyo pake anapita ku nyumba ya Yehova kukapembedza. Kenaka anapita ku nyumba kwake ndipo atapempha chakudya anamupatsa nadya. 21 Antchito ake anamufunsa kuti, “Chifukwa chiyani mukuchita zinthu motere? Pamene mwana anali ndi moyo, munkasala chakudya ndi kulira, koma tsopano pamene mwana wamwalira inu mukudzuka ndi kudya!” 22 Iye anayankha kuti, “Pamene mwana anali ndi moyo ine ndinkasala zakudya ndi kulira. Ine ndinkaganiza kuti, ‘Akudziwa ndani? Yehova atha kundikomera mtima kuti mwanayo akhale ndi moyo.’ 23 Koma tsopano wamwalira ndisaliranji chakudya? Kodi ndingathe kumubwezanso? Ine ndidzapita kumene kuli iyeko, koma iye sadzabwerera kwa ine.” 24 Ndipo Davide anatonthoza mkazi wake Batiseba, napita kwa iye ndi kugona naye. Iye anabereka mwana wamwamuna, ndipo anamutcha dzina lake Solomoni. Yehova ankamukonda iye. 25 Ndipo chifukwa chakuti Yehova ankamukonda iyeyo, Yehovayo anatumiza mawu kwa mneneri Natani kuti akamutchule Yedidiya. 26 Pa nthawi imeneyi Yowabu anamenyana ndi Raba ku Amoni ndipo analanda nsanja yaufumu. 27 Ndipo Yowabu anatumiza amithenga kwa Davide kukanena kuti, “Ine ndamenyana ndi Raba ndipo ndatenga zitsime zake za madzi. 28 Ndipo tsopano sonkhanitsani asilikali onse ndipo muzungulire mzindawo ndi kuwulanda.” 29 Kotero Davide anasonkhanitsa ankhondo onse ndipo anapita ku Raba kukawuthira nkhondo ndi kuwulanda. 30 Davide anachotsa chipewa chaufumu pamutu pa mfumu yawo ndipo Davide anavala chipewacho. Chipewacho chinkalemera makilogalamu asanu agolide, ndiponso chinali ndi miyala yokongola. Iye anatenga katundu wambiri kuchokera mu mzindawo, 31 ndipo anatulutsa anthu amene anali mʼmenemo, nawayika kuti azigwira ntchito ya macheka, yosula makasu ndi nkhwangwa, ndiponso yowomba njerwa. Davide anachita izi ndi mizinda yonse ya Aamoni. Kenaka iye pamodzi ndi gulu lake lonse lankhondo anabwerera ku Yerusalemu.

In Other Versions

2 Samuel 12 in the ANGEFD

2 Samuel 12 in the ANTPNG2D

2 Samuel 12 in the AS21

2 Samuel 12 in the BAGH

2 Samuel 12 in the BBPNG

2 Samuel 12 in the BBT1E

2 Samuel 12 in the BDS

2 Samuel 12 in the BEV

2 Samuel 12 in the BHAD

2 Samuel 12 in the BIB

2 Samuel 12 in the BLPT

2 Samuel 12 in the BNT

2 Samuel 12 in the BNTABOOT

2 Samuel 12 in the BNTLV

2 Samuel 12 in the BOATCB

2 Samuel 12 in the BOATCB2

2 Samuel 12 in the BOBCV

2 Samuel 12 in the BOCNT

2 Samuel 12 in the BOECS

2 Samuel 12 in the BOHCB

2 Samuel 12 in the BOHCV

2 Samuel 12 in the BOHLNT

2 Samuel 12 in the BOHNTLTAL

2 Samuel 12 in the BOICB

2 Samuel 12 in the BOILNTAP

2 Samuel 12 in the BOITCV

2 Samuel 12 in the BOKCV

2 Samuel 12 in the BOKCV2

2 Samuel 12 in the BOKHWOG

2 Samuel 12 in the BOKSSV

2 Samuel 12 in the BOLCB

2 Samuel 12 in the BOLCB2

2 Samuel 12 in the BOMCV

2 Samuel 12 in the BONAV

2 Samuel 12 in the BONCB

2 Samuel 12 in the BONLT

2 Samuel 12 in the BONUT2

2 Samuel 12 in the BOPLNT

2 Samuel 12 in the BOSCB

2 Samuel 12 in the BOSNC

2 Samuel 12 in the BOTLNT

2 Samuel 12 in the BOVCB

2 Samuel 12 in the BOYCB

2 Samuel 12 in the BPBB

2 Samuel 12 in the BPH

2 Samuel 12 in the BSB

2 Samuel 12 in the CCB

2 Samuel 12 in the CUV

2 Samuel 12 in the CUVS

2 Samuel 12 in the DBT

2 Samuel 12 in the DGDNT

2 Samuel 12 in the DHNT

2 Samuel 12 in the DNT

2 Samuel 12 in the ELBE

2 Samuel 12 in the EMTV

2 Samuel 12 in the ESV

2 Samuel 12 in the FBV

2 Samuel 12 in the FEB

2 Samuel 12 in the GGMNT

2 Samuel 12 in the GNT

2 Samuel 12 in the HARY

2 Samuel 12 in the HNT

2 Samuel 12 in the IRVA

2 Samuel 12 in the IRVB

2 Samuel 12 in the IRVG

2 Samuel 12 in the IRVH

2 Samuel 12 in the IRVK

2 Samuel 12 in the IRVM

2 Samuel 12 in the IRVM2

2 Samuel 12 in the IRVO

2 Samuel 12 in the IRVP

2 Samuel 12 in the IRVT

2 Samuel 12 in the IRVT2

2 Samuel 12 in the IRVU

2 Samuel 12 in the ISVN

2 Samuel 12 in the JSNT

2 Samuel 12 in the KAPI

2 Samuel 12 in the KBT1ETNIK

2 Samuel 12 in the KBV

2 Samuel 12 in the KJV

2 Samuel 12 in the KNFD

2 Samuel 12 in the LBA

2 Samuel 12 in the LBLA

2 Samuel 12 in the LNT

2 Samuel 12 in the LSV

2 Samuel 12 in the MAAL

2 Samuel 12 in the MBV

2 Samuel 12 in the MBV2

2 Samuel 12 in the MHNT

2 Samuel 12 in the MKNFD

2 Samuel 12 in the MNG

2 Samuel 12 in the MNT

2 Samuel 12 in the MNT2

2 Samuel 12 in the MRS1T

2 Samuel 12 in the NAA

2 Samuel 12 in the NASB

2 Samuel 12 in the NBLA

2 Samuel 12 in the NBS

2 Samuel 12 in the NBVTP

2 Samuel 12 in the NET2

2 Samuel 12 in the NIV11

2 Samuel 12 in the NNT

2 Samuel 12 in the NNT2

2 Samuel 12 in the NNT3

2 Samuel 12 in the PDDPT

2 Samuel 12 in the PFNT

2 Samuel 12 in the RMNT

2 Samuel 12 in the SBIAS

2 Samuel 12 in the SBIBS

2 Samuel 12 in the SBIBS2

2 Samuel 12 in the SBICS

2 Samuel 12 in the SBIDS

2 Samuel 12 in the SBIGS

2 Samuel 12 in the SBIHS

2 Samuel 12 in the SBIIS

2 Samuel 12 in the SBIIS2

2 Samuel 12 in the SBIIS3

2 Samuel 12 in the SBIKS

2 Samuel 12 in the SBIKS2

2 Samuel 12 in the SBIMS

2 Samuel 12 in the SBIOS

2 Samuel 12 in the SBIPS

2 Samuel 12 in the SBISS

2 Samuel 12 in the SBITS

2 Samuel 12 in the SBITS2

2 Samuel 12 in the SBITS3

2 Samuel 12 in the SBITS4

2 Samuel 12 in the SBIUS

2 Samuel 12 in the SBIVS

2 Samuel 12 in the SBT

2 Samuel 12 in the SBT1E

2 Samuel 12 in the SCHL

2 Samuel 12 in the SNT

2 Samuel 12 in the SUSU

2 Samuel 12 in the SUSU2

2 Samuel 12 in the SYNO

2 Samuel 12 in the TBIAOTANT

2 Samuel 12 in the TBT1E

2 Samuel 12 in the TBT1E2

2 Samuel 12 in the TFTIP

2 Samuel 12 in the TFTU

2 Samuel 12 in the TGNTATF3T

2 Samuel 12 in the THAI

2 Samuel 12 in the TNFD

2 Samuel 12 in the TNT

2 Samuel 12 in the TNTIK

2 Samuel 12 in the TNTIL

2 Samuel 12 in the TNTIN

2 Samuel 12 in the TNTIP

2 Samuel 12 in the TNTIZ

2 Samuel 12 in the TOMA

2 Samuel 12 in the TTENT

2 Samuel 12 in the UBG

2 Samuel 12 in the UGV

2 Samuel 12 in the UGV2

2 Samuel 12 in the UGV3

2 Samuel 12 in the VBL

2 Samuel 12 in the VDCC

2 Samuel 12 in the YALU

2 Samuel 12 in the YAPE

2 Samuel 12 in the YBVTP

2 Samuel 12 in the ZBP