2 Samuel 20 (BOGWICC)

1 Ndipo munthu wina wokonda kuyambitsa chisokonezo, dzina lake Seba, mwana wa Bikiri wa fuko la Benjamini, anali komweko. Iye analiza lipenga ndipo anafuwula kuti,“Ife tilibe chathu mu mfumu wa Davide,tilibe gawo mwa mwana wa Yese!Inu Aisraeli aliyense apite ku nyumba kwake!” 2 Kotero Aisraeli onse anamuthawa Davide ndipo anatsatira Seba mwana wa Bikiri. Koma anthu a ku Yuda anakhala ndi mfumu yawo njira yonse kuchokera ku Yorodani mpaka ku Yerusalemu. 3 Davide atabwerera ku nyumba yake yaufumu ku Yerusalemu, iye anatenga azikazi khumi aja amene anawasiya kuti aziyangʼanira nyumba yaufumu, ndipo anawayika mʼnyumba imene anayikapo mlonda. Iye ankawadyetsa koma sanagone nawonso. Anasungidwa kwa okha mpaka tsiku la kufa kwawo ndipo anakhala ngati akazi amasiye. 4 Kenaka mfumu inati kwa Amasa, “Itanitsa ankhondo a Yuda kuti abwere kwa ine pasanathe masiku atatu, ndipo iwe udzakhale nawo.” 5 Motero Amasa anakayitana Ayuda, koma anachedwa, napitirira pa nthawi imene mfumu inamuyikira. 6 Davide anati kwa Abisai, “Tsono Seba mwana wa Bikiri adzatipweteka kuposa momwe Abisalomu anatichitira. Tenga asilikali a mbuye wako ndipo umuthamangitse, mwina adzapeza mizinda yotetezedwa ndi kutithawa ife.” 7 Kotero anthu a Yowabu, Akereti ndi Apeleti ndiponso asilikali onse amphamvu anapita motsogozedwa ndi Abisai. Iwo anayenda kuchokera ku Yerusalemu kuthamangitsa Seba mwana wa Bikiri. 8 Ali pa mwala waukulu wa ku Gibiyoni, Amasa anabwera kudzakumana nawo. Yowabu anali atavala chovala chausilikali ndipo pamwamba pa malayawo, mʼchiwuno mwake anavala lamba womangirirapo lupanga lili moyikamo mwakemo. Akuyenda linasololoka kuchoka moyikamo mwake. 9 Yowabu anati kwa Amasa, “Kodi uli bwanji mʼbale wanga?” Kenaka Yowabu anamugwira ndevu Amasa uja ndi dzanja lake lamanja ndi kupsompsona. 10 Amasa sanayangʼanitsitse lupanga limene linali mʼdzanja la Yowabu, ndipo Yowabu anamubaya nalo mʼmimba ndipo matumbo ake anatuluka ndi kugwera pansi. Popanda kubayanso kachiwiri, Amasa anafa. Ndipo Yowabu ndi mʼbale wake Abisai anathamangitsa Seba mwana wa Bikiri. 11 Mmodzi mwa ankhondo a Yowabu anakayimirira pafupi ndi mtembo wa Amasa ndipo anati, “Aliyense amene amakonda Yowabu ndi aliyense amene ali wa Davide, atsatire Yowabu!” 12 Amasa anagona pakati pa msewu atasamba magazi ake, ndipo munthuyo anaona kuti asilikali onse amayima pamenepo. Atazindikira kuti aliyense amene ankafika pamene panali Amasa amayima, iye anamuchotsa mu msewu ndi kumukokera mʼmunda ndipo anamuphimba ndi nsalu. 13 Amasa atachotsedwa pa msewu anthu onse anapita ndi Yowabu kuthamangitsa Seba mwana wa Bikiri. 14 Seba anadutsa mafuko onse a Israeli mpaka ku Abeli ndi Beti-Maaka ndiponso chigawo chonse cha Abeli, amene anasonkhana pamodzi ndi kumutsata iye. 15 Ankhondo onse pamodzi ndi Yowabu anafika ndi kumuzungulira Seba mu Abeli-Beti-Maaka. Iwo anapanga mzere wa nkhondo mpaka ku mzinda, ndipo unayangʼanana ndi malo otetezera a kunja. Pamene amalimbana ndi khoma kuti aligwetse, 16 mayi wina wanzeru anafuwula kuchokera mu mzindawo, “Tamverani! Tamverani! Muwuzeni Yowabu abwere pano kuti ndiyankhule naye.” 17 Yowabu anayandikira kumene kunali mayiyo, ndipo iye anafunsa kuti, “Kodi ndinu Yowabu?”Iye anayankha kuti, “Ndine.”Mayiyo anati, “Tamverani zimene mtumiki wanu akuti anene.”Yowabu anayankha kuti, “Ndikumvetsera.” 18 Iye anapitiriza kunena kuti, “Kalekale ankanena kuti, ‘Kapeze yankho lako ku Abeli,’ ndipo nkhani imathera pamenepo. 19 Ife ndife anthu a mtendere ndi okhulupirika mu Israeli. Inu mukufuna kuwononga mzinda umene ndi mayi mu Israeli. Nʼchifukwa chiyani mukufuna kufafaniza cholowa cha Yehova?” 20 Yowabu anayankha kuti, “Ayi ndisatero. Ine sindikufuna kuwufafaniza kapena kuwuwononga. 21 Nkhani simeneyo ayi. Koma munthu wina wa ku dziko lamapiri la Efereimu, dzina lake Seba mwana wa Bikiri, wawukira mfumu Davide. Muperekeni munthuyo ndipo ine ndidzachoka pa mzinda uno.”Mayiyo anati kwa Yowabu, “Mutu wake tikuponyerani pa khoma pano.” 22 Ndipo mayiyo anapita kwa anthu onse ndi malangizo ake anzeru, ndipo anadula mutu wa Seba mwana wa Bikiri ndipo anawuponya kwa Yowabu. Kotero iye analiza lipenga ndipo anthu ake anachoka pa mzindawo, aliyense nʼkubwerera kwawo. Ndipo Yowabu anabwerera kwa mfumu ku Yerusalemu. 23 Yowabu ndiye amalamulira gulu lonse la ankhondo. Benaya mwana wa Yehoyada amalamulira Akereti ndi Apeleti. 24 Adoramu amayangʼanira anthu ogwira ntchito ya thangata, Yehosafati mwana wa Ahiludi anali mlembi wa zochitika, 25 Seva anali mlembi wa mfumu. Zadoki ndi Abiatara anali ansembe 26 ndipo Ira wa ku Yairi anali wansembe wa Davide.

In Other Versions

2 Samuel 20 in the ANGEFD

2 Samuel 20 in the ANTPNG2D

2 Samuel 20 in the AS21

2 Samuel 20 in the BAGH

2 Samuel 20 in the BBPNG

2 Samuel 20 in the BBT1E

2 Samuel 20 in the BDS

2 Samuel 20 in the BEV

2 Samuel 20 in the BHAD

2 Samuel 20 in the BIB

2 Samuel 20 in the BLPT

2 Samuel 20 in the BNT

2 Samuel 20 in the BNTABOOT

2 Samuel 20 in the BNTLV

2 Samuel 20 in the BOATCB

2 Samuel 20 in the BOATCB2

2 Samuel 20 in the BOBCV

2 Samuel 20 in the BOCNT

2 Samuel 20 in the BOECS

2 Samuel 20 in the BOHCB

2 Samuel 20 in the BOHCV

2 Samuel 20 in the BOHLNT

2 Samuel 20 in the BOHNTLTAL

2 Samuel 20 in the BOICB

2 Samuel 20 in the BOILNTAP

2 Samuel 20 in the BOITCV

2 Samuel 20 in the BOKCV

2 Samuel 20 in the BOKCV2

2 Samuel 20 in the BOKHWOG

2 Samuel 20 in the BOKSSV

2 Samuel 20 in the BOLCB

2 Samuel 20 in the BOLCB2

2 Samuel 20 in the BOMCV

2 Samuel 20 in the BONAV

2 Samuel 20 in the BONCB

2 Samuel 20 in the BONLT

2 Samuel 20 in the BONUT2

2 Samuel 20 in the BOPLNT

2 Samuel 20 in the BOSCB

2 Samuel 20 in the BOSNC

2 Samuel 20 in the BOTLNT

2 Samuel 20 in the BOVCB

2 Samuel 20 in the BOYCB

2 Samuel 20 in the BPBB

2 Samuel 20 in the BPH

2 Samuel 20 in the BSB

2 Samuel 20 in the CCB

2 Samuel 20 in the CUV

2 Samuel 20 in the CUVS

2 Samuel 20 in the DBT

2 Samuel 20 in the DGDNT

2 Samuel 20 in the DHNT

2 Samuel 20 in the DNT

2 Samuel 20 in the ELBE

2 Samuel 20 in the EMTV

2 Samuel 20 in the ESV

2 Samuel 20 in the FBV

2 Samuel 20 in the FEB

2 Samuel 20 in the GGMNT

2 Samuel 20 in the GNT

2 Samuel 20 in the HARY

2 Samuel 20 in the HNT

2 Samuel 20 in the IRVA

2 Samuel 20 in the IRVB

2 Samuel 20 in the IRVG

2 Samuel 20 in the IRVH

2 Samuel 20 in the IRVK

2 Samuel 20 in the IRVM

2 Samuel 20 in the IRVM2

2 Samuel 20 in the IRVO

2 Samuel 20 in the IRVP

2 Samuel 20 in the IRVT

2 Samuel 20 in the IRVT2

2 Samuel 20 in the IRVU

2 Samuel 20 in the ISVN

2 Samuel 20 in the JSNT

2 Samuel 20 in the KAPI

2 Samuel 20 in the KBT1ETNIK

2 Samuel 20 in the KBV

2 Samuel 20 in the KJV

2 Samuel 20 in the KNFD

2 Samuel 20 in the LBA

2 Samuel 20 in the LBLA

2 Samuel 20 in the LNT

2 Samuel 20 in the LSV

2 Samuel 20 in the MAAL

2 Samuel 20 in the MBV

2 Samuel 20 in the MBV2

2 Samuel 20 in the MHNT

2 Samuel 20 in the MKNFD

2 Samuel 20 in the MNG

2 Samuel 20 in the MNT

2 Samuel 20 in the MNT2

2 Samuel 20 in the MRS1T

2 Samuel 20 in the NAA

2 Samuel 20 in the NASB

2 Samuel 20 in the NBLA

2 Samuel 20 in the NBS

2 Samuel 20 in the NBVTP

2 Samuel 20 in the NET2

2 Samuel 20 in the NIV11

2 Samuel 20 in the NNT

2 Samuel 20 in the NNT2

2 Samuel 20 in the NNT3

2 Samuel 20 in the PDDPT

2 Samuel 20 in the PFNT

2 Samuel 20 in the RMNT

2 Samuel 20 in the SBIAS

2 Samuel 20 in the SBIBS

2 Samuel 20 in the SBIBS2

2 Samuel 20 in the SBICS

2 Samuel 20 in the SBIDS

2 Samuel 20 in the SBIGS

2 Samuel 20 in the SBIHS

2 Samuel 20 in the SBIIS

2 Samuel 20 in the SBIIS2

2 Samuel 20 in the SBIIS3

2 Samuel 20 in the SBIKS

2 Samuel 20 in the SBIKS2

2 Samuel 20 in the SBIMS

2 Samuel 20 in the SBIOS

2 Samuel 20 in the SBIPS

2 Samuel 20 in the SBISS

2 Samuel 20 in the SBITS

2 Samuel 20 in the SBITS2

2 Samuel 20 in the SBITS3

2 Samuel 20 in the SBITS4

2 Samuel 20 in the SBIUS

2 Samuel 20 in the SBIVS

2 Samuel 20 in the SBT

2 Samuel 20 in the SBT1E

2 Samuel 20 in the SCHL

2 Samuel 20 in the SNT

2 Samuel 20 in the SUSU

2 Samuel 20 in the SUSU2

2 Samuel 20 in the SYNO

2 Samuel 20 in the TBIAOTANT

2 Samuel 20 in the TBT1E

2 Samuel 20 in the TBT1E2

2 Samuel 20 in the TFTIP

2 Samuel 20 in the TFTU

2 Samuel 20 in the TGNTATF3T

2 Samuel 20 in the THAI

2 Samuel 20 in the TNFD

2 Samuel 20 in the TNT

2 Samuel 20 in the TNTIK

2 Samuel 20 in the TNTIL

2 Samuel 20 in the TNTIN

2 Samuel 20 in the TNTIP

2 Samuel 20 in the TNTIZ

2 Samuel 20 in the TOMA

2 Samuel 20 in the TTENT

2 Samuel 20 in the UBG

2 Samuel 20 in the UGV

2 Samuel 20 in the UGV2

2 Samuel 20 in the UGV3

2 Samuel 20 in the VBL

2 Samuel 20 in the VDCC

2 Samuel 20 in the YALU

2 Samuel 20 in the YAPE

2 Samuel 20 in the YBVTP

2 Samuel 20 in the ZBP