Daniel 5 (BOGWICC)

1 Tsiku lina mfumu Belisazara anakonza phwando lalikulu la akalonga ake 1,000 ndipo anamwa vinyo pamodzi ndi iwo. 2 Pamene Belisazara ankamwa vinyo, analamula kuti ziwiya zagolide ndi zasiliva zimene Nebukadinezara abambo ake anakatenga mʼNyumba ya Mulungu ku Yerusalemu zikatengedwe kuti mfumu ndi akalonga ake, akazi ake ndi azikazi amweremo. 3 Choncho anabweretsa ziwiya zagolide zimene anazitenga mʼNyumba ya Mulungu; ndipo mfumu ndi akalonga ake, akazi ake ndi azikazi ake anamweramo. 4 Akumwa vinyo, anatamanda milungu yagolide ndi siliva, yamkuwa, chitsulo, yamtengo ndi mwala. 5 Mwadzidzidzi zala za dzanja la munthu zinaonekera ndi kulemba pa khoma, pafupi ndi choyikapo nyale mʼnyumba yaufumu. Mfumu inapenyetsetsa dzanjalo pamene limalemba. 6 Nkhope yake inasandulika ndipo inachita mantha, nkhongono zii, mawondo gwedegwede. 7 Mfumu inafuwula kuyitana owombeza, alawuli ndi amawula kuti abwere. Ndipo anawawuza anthu anzeru a ku Babuloni kuti, “Aliyense amene awerenge malembawa ndi kundiwuza tanthauzo lake adzavekedwa chovala cha pepo ndi mkanda wa golide udzavekedwa mʼkhosi mwake, ndipo adzakhala wolamulira wachitatu mu ufumuwu.” 8 Pamenepo anzeru onse a mfumu anabwera, koma sanakwanitse kuwerenga malembawo kapena kumutanthauzira mfumu. 9 Choncho mfumu Belisazara anachita mantha koposa ndipo nkhope yake inapitirira kusinthika. Akalonga ake anathedwa nzeru. 10 Mfumukazi, pakumva mawu a mfumu ndi akalonga ake, analowa mʼchipinda cha phwando ndipo anati, “Mfumu mukhale ndi moyo wautali! Musavutike! Nkhope yanu isasinthike! 11 Pali munthu wina mu ufumu wanu uno amene mwa iye muli mzimu wa milungu yoyera. Pa nthawi ya ulamuliro wa abambo anu iye anapezeka kuti ali ndi chidziwitso, luntha ndi nzeru zonga za milungu. Mfumu Nebukadinezara, abambo anu, Ine ndikukuwuzani anamusankha iye kukhala mkulu wa amatsenga, owombeza, alawuli ndi amawula. 12 Munthu ameneyu dzina lake ndi Danieli, koma mfumu inamutcha Belitesezara ndipo ali ndi nzeru zapadera, ndi wodziwa ndi kuzindikira zinthu, ndiponso luso lakutanthauzira maloto, kufotokozera miyambi ndi kuthetsa mavuto osautsa. Muyitaneni Danieli, ndipo adzakuwuzani chomwe mawuwa akutanthauza.” 13 Choncho anabwera naye Danieli pamaso pa mfumu ndipo inati kwa iye, “Kodi ndiwe Danieli, mmodzi mwa akapolo omwe abambo anga mfumu anabwera nawo kuchoka ku Yuda? 14 Ndamva kuti mzimu wa milungu uli mwa iwe ndi kuti uli ndi chidziwitso, luntha ndi nzeru zapadera. 15 Anzeru ndi owombeza anabwera pamaso panga kuti awerenge zolembedwazi ndi kundiwuza tanthauzo lake koma sanakwanitse kundifotokozera. 16 Tsopano ndamva kuti iwe ukhoza kupereka matanthauzo ndi kuthetsa mavuto. Ngati ungawerenge zolembedwazi ndi kundiwuza tanthauzo lake, udzavekedwa chovala cha pepo ndi kuyikidwa mkanda wa golide mʼkhosi mwako, ndipo udzakhala wolamulira wachitatu mu ufumu uno.” 17 Pamenepo Danieli anayankha mfumu kuti, “Inu musunge mphatso zanuzo kwa inu nokha ndipo mupereke mphothoyo kwa wina aliyense. Komabe ine ndi kuwerengerani malembawa mfumu; ndikukuwuzani tanthauzo lake. 18 “Inu mfumu, Mulungu Wammwambamwamba anapatsa abambo anu Nebukadinezara mphamvu ndi ukulu ndi ulemerero ndi ufumu. 19 Chifukwa cha udindo waukulu umene anapatsidwanso, anthu onse ndi mitundu ndi anthu aziyankhulo zosiyanasiyana ankanjenjemera ndikumuopa iye. Amene mfumu inafuna anawaphadi; amene inafuna kuwasunga, inawasunga; amene inafuna kuwakweza, inawakweza; ndipo amene inafuna kuwatsitsa, inawatsitsa. 20 Koma pamene inayamba kudzitama ndi kuwumitsa mtima wake ndi kuyamba kunyada, inachotsedwa pa mpando wake waufumu ndi kulandidwa ulemerero wake. 21 Iyo inachotsedwa pakati pa anthu ndi kupatsidwa mtima ngati wa nyama; inakhala pamodzi ndi abulu akutchire ndi kudya udzu ngati ngʼombe; ndipo thupi lake linanyowa ndi mame akumwamba, mpaka pamene anavomereza kuti Mulungu Wammwambamwamba ndiye wolamulira maufumu a anthu ndipo amawupereka kwa aliyense amene Iye wafuna. 22 “Koma inu mwana wake, Belisazara, simunadzichepetse, ngakhale kuti mumadziwa zonsezi. 23 Mʼmalo mwake, mwadzikweza nokha kutsutsana ndi Ambuye wakumwamba. Inu mwatenga ziwiya za mʼNyumba mwake, ndipo inu ndi akalonga anu, akazi anu ndi azikazi anu mwamwera vinyo mu zimenezi. Inu munatamanda milungu yasiliva ndi golide, yamkuwa, chitsulo, mtengo ndi mwala, imene singaone kapena kumva kapena kuzindikira. Koma simunamupatse ulemu Mulungu amene asunga mʼmanja mwake moyo wanu ndi njira zanu zonse. 24 Choncho Iye watumiza dzanja limene lalemba mawu amenewa. 25 “Mawu amene analembedwa ndi awa:MENE, MENE, TEKELI, PARASINI. 26 “Zimene mawuwa akutanthauza ndi izi:Mene: Mulungu wawerenga masiku a ufumu wanu ndipo wauthetsa. 27 Tekeli: Inu mwayesedwa pa sikelo ndipo mwapezeka kuti mukuperewera. 28 Parasini: Ufumu wanu wagawidwa ndi kupatsidwa kwa Amedi ndi Aperezi.” 29 Mwa lamulo la Belisazara, Danieli anavekedwa chovala cha pepo, mkanda wagolide unayikidwa mʼkhosi mwake, ndipo analengeza kuti anali wachitatu mu ulamuliro mu ufumuwo. 30 Usiku womwewo Belisazara, mfumu ya anthu a ku Babuloni, inaphedwa, 31 ndipo Dariyo Mmedi analanda ufumuwo ali ndi zaka 62.

In Other Versions

Daniel 5 in the ANGEFD

Daniel 5 in the ANTPNG2D

Daniel 5 in the AS21

Daniel 5 in the BAGH

Daniel 5 in the BBPNG

Daniel 5 in the BBT1E

Daniel 5 in the BDS

Daniel 5 in the BEV

Daniel 5 in the BHAD

Daniel 5 in the BIB

Daniel 5 in the BLPT

Daniel 5 in the BNT

Daniel 5 in the BNTABOOT

Daniel 5 in the BNTLV

Daniel 5 in the BOATCB

Daniel 5 in the BOATCB2

Daniel 5 in the BOBCV

Daniel 5 in the BOCNT

Daniel 5 in the BOECS

Daniel 5 in the BOHCB

Daniel 5 in the BOHCV

Daniel 5 in the BOHLNT

Daniel 5 in the BOHNTLTAL

Daniel 5 in the BOICB

Daniel 5 in the BOILNTAP

Daniel 5 in the BOITCV

Daniel 5 in the BOKCV

Daniel 5 in the BOKCV2

Daniel 5 in the BOKHWOG

Daniel 5 in the BOKSSV

Daniel 5 in the BOLCB

Daniel 5 in the BOLCB2

Daniel 5 in the BOMCV

Daniel 5 in the BONAV

Daniel 5 in the BONCB

Daniel 5 in the BONLT

Daniel 5 in the BONUT2

Daniel 5 in the BOPLNT

Daniel 5 in the BOSCB

Daniel 5 in the BOSNC

Daniel 5 in the BOTLNT

Daniel 5 in the BOVCB

Daniel 5 in the BOYCB

Daniel 5 in the BPBB

Daniel 5 in the BPH

Daniel 5 in the BSB

Daniel 5 in the CCB

Daniel 5 in the CUV

Daniel 5 in the CUVS

Daniel 5 in the DBT

Daniel 5 in the DGDNT

Daniel 5 in the DHNT

Daniel 5 in the DNT

Daniel 5 in the ELBE

Daniel 5 in the EMTV

Daniel 5 in the ESV

Daniel 5 in the FBV

Daniel 5 in the FEB

Daniel 5 in the GGMNT

Daniel 5 in the GNT

Daniel 5 in the HARY

Daniel 5 in the HNT

Daniel 5 in the IRVA

Daniel 5 in the IRVB

Daniel 5 in the IRVG

Daniel 5 in the IRVH

Daniel 5 in the IRVK

Daniel 5 in the IRVM

Daniel 5 in the IRVM2

Daniel 5 in the IRVO

Daniel 5 in the IRVP

Daniel 5 in the IRVT

Daniel 5 in the IRVT2

Daniel 5 in the IRVU

Daniel 5 in the ISVN

Daniel 5 in the JSNT

Daniel 5 in the KAPI

Daniel 5 in the KBT1ETNIK

Daniel 5 in the KBV

Daniel 5 in the KJV

Daniel 5 in the KNFD

Daniel 5 in the LBA

Daniel 5 in the LBLA

Daniel 5 in the LNT

Daniel 5 in the LSV

Daniel 5 in the MAAL

Daniel 5 in the MBV

Daniel 5 in the MBV2

Daniel 5 in the MHNT

Daniel 5 in the MKNFD

Daniel 5 in the MNG

Daniel 5 in the MNT

Daniel 5 in the MNT2

Daniel 5 in the MRS1T

Daniel 5 in the NAA

Daniel 5 in the NASB

Daniel 5 in the NBLA

Daniel 5 in the NBS

Daniel 5 in the NBVTP

Daniel 5 in the NET2

Daniel 5 in the NIV11

Daniel 5 in the NNT

Daniel 5 in the NNT2

Daniel 5 in the NNT3

Daniel 5 in the PDDPT

Daniel 5 in the PFNT

Daniel 5 in the RMNT

Daniel 5 in the SBIAS

Daniel 5 in the SBIBS

Daniel 5 in the SBIBS2

Daniel 5 in the SBICS

Daniel 5 in the SBIDS

Daniel 5 in the SBIGS

Daniel 5 in the SBIHS

Daniel 5 in the SBIIS

Daniel 5 in the SBIIS2

Daniel 5 in the SBIIS3

Daniel 5 in the SBIKS

Daniel 5 in the SBIKS2

Daniel 5 in the SBIMS

Daniel 5 in the SBIOS

Daniel 5 in the SBIPS

Daniel 5 in the SBISS

Daniel 5 in the SBITS

Daniel 5 in the SBITS2

Daniel 5 in the SBITS3

Daniel 5 in the SBITS4

Daniel 5 in the SBIUS

Daniel 5 in the SBIVS

Daniel 5 in the SBT

Daniel 5 in the SBT1E

Daniel 5 in the SCHL

Daniel 5 in the SNT

Daniel 5 in the SUSU

Daniel 5 in the SUSU2

Daniel 5 in the SYNO

Daniel 5 in the TBIAOTANT

Daniel 5 in the TBT1E

Daniel 5 in the TBT1E2

Daniel 5 in the TFTIP

Daniel 5 in the TFTU

Daniel 5 in the TGNTATF3T

Daniel 5 in the THAI

Daniel 5 in the TNFD

Daniel 5 in the TNT

Daniel 5 in the TNTIK

Daniel 5 in the TNTIL

Daniel 5 in the TNTIN

Daniel 5 in the TNTIP

Daniel 5 in the TNTIZ

Daniel 5 in the TOMA

Daniel 5 in the TTENT

Daniel 5 in the UBG

Daniel 5 in the UGV

Daniel 5 in the UGV2

Daniel 5 in the UGV3

Daniel 5 in the VBL

Daniel 5 in the VDCC

Daniel 5 in the YALU

Daniel 5 in the YAPE

Daniel 5 in the YBVTP

Daniel 5 in the ZBP