Daniel 6 (BOGWICC)

1 Kunamukomera Dariyo kusankha akalonga 120 kuti alamulire mu ufumu wonse, 2 ndikusankha nduna zazikulu zitatu kuti ziwayangʼanire ndipo imodzi mwa ndunazo anali Danieli. Akalongawo amayangʼaniridwa ndi nduna zazikuluzo kuti zinthu za mfumu zisawonongeke. 3 Tsono Danieli anadzionetsa kuti akhoza kugwira ntchito bwino kopambana nduna zinzake chifukwa anali wanzeru kwambiri. Ndiye mfumu inaganiza zomuyika kuti akhale woyangʼanira ufumu wonse. 4 Chifukwa cha ichi, anzake ndi akalonga anayesa kupeza zifukwa zomutsutsira Danieli pa kayendetsedwe ka ntchito za dzikolo, koma sanapeze cholakwa chilichonse. Iwo sanapeze chinyengo mwa iye, chifukwa anali wokhulupirika ndipo sankachita chinyengo kapena kutayirira ntchito. 5 Pomaliza, anthu awa ananena kuti, “Sitidzapeza cholakwa chilichonse chomutsutsira Danieli kupatula chokhacho chimene chikhudza chipembedzo cha Mulungu wake.” 6 Choncho akalonga ndi nduna pamodzi anapita kwa mfumu ndipo anati: “Inu mfumu Dariyo, mukhale ndi moyo wautali! 7 Nduna zoyendetsa ufumu wanu, aphungu, akalonga ndi abwanamkubwa tonse tagwirizana kuti inu mfumu mukhazikitse lamulo ndi kulisindikiza kuti aliyense amene apemphera kwa mulungu wina kapena kwa munthu kupatula kwa inu mfumu, pa masiku makumi atatu otsatirawa, adzaponyedwa mʼdzenje la mikango. 8 Tsopano inu mfumu khazikitsani lamulo limeneli ndipo musindikizepo dzina lanu kuti lisasinthike monga mwa malamulo a Amedi ndi Aperezi, amene sasinthidwa.” 9 Choncho mfumu Dariyo anasindikizapo dzina lake pa lamuloli. 10 Danieli atamva kuti lamulo lasindikizidwa, anapita ku nyumba kwake nalowa mʼchipinda chapamwamba chimene mazenera ake anali otsekula kuloza ku Yerusalemu. Katatu pa tsiku iye ankagwada pansi pa mawondo ndipo amapemphera, kuyamika Mulungu wake, monga momwe ankachitira kale. 11 Ndipo anthu awa anapita pamodzi ndi kukapeza Danieli akupemphera ndi kupempha Mulungu wake kuti amuthandize. 12 Kotero iwo anapita kwa mfumu ndipo anayankhula naye za lamulo lake kuti, “Kodi simunasindikize lamulo lakuti pa masiku makumi atatu otsatirawa aliyense amene apemphera kwa mulungu wina aliyense kapena kwa munthu kupatula kwa inu mfumu, adzaponyedwa mʼdzenje la mikango?”Mfumu inayankha kuti, “Lamulo lilipobe monga mwa malamulo a Amedi ndi Aperezi, amene sangathe kusinthika.” 13 Kenaka iwo anati kwa mfumu, “Danieli, amene ndi mmodzi mwa akapolo ochokera ku Yuda, sakulabadira inu mfumu, kapena lamulo limene munasindikizapo dzina lanu lija. Iye akupempherabe katatu pa tsiku.” 14 Mfumu itamva izi, inavutika kwambiri mu mtima mwake. Iyo inayesa kupeza njira yopulumutsira Danieli. Iyo inachita chotheka chilichonse kufikira kulowa kwa dzuwa kuti imupulumutse. 15 Ndipo anthuwo anapita pamodzi kwa mfumu ndipo anati kwa iye, “Kumbukirani, inu mfumu kuti monga mwa lamulo la Amedi ndi Aperezi, palibe chimene mfumu inalamulira kapena kukhazikitsa chimasinthidwa.” 16 Choncho mfumu inalamula, ndipo anabwera naye Danieli ndi kukamuponya mʼdzenje la mikango. Mfumu inati kwa Danieli, “Mulungu wako amene umutumikira nthawi zonse, akupulumutse!” 17 Anatenga mwala natseka pa khoma pa dzenje la mikango, ndipo mfumu inadindapo chizindikiro chake ndi cha nduna zake kuti wina asasinthepo kanthu pa za Danieli. 18 Kenaka mfumu inabwerera ku nyumba yake ndipo inakhala usiku wonse osadya kanthu, osalola chosangalatsa chilichonse. Ndipo sinagone tulo. 19 Mʼbandakucha, mfumu inanyamuka ndi kufulumira kupita ku dzenje la mikango lija. 20 Itayandikira pa dzenjelo, inayitana Danieli moonetsa nkhawa, “Danieli, mtumiki wa Mulungu wa moyo! Kodi Mulungu wako, amene umutumikira nthawi zonse, wakulanditsa ku mikango?” 21 Danieli anayankha kuti, “Inu mfumu mukhale ndi moyo wautali! 22 Mulungu wanga anatumiza mngelo wake, ndipo anatseka pakamwa pa mikango. Iyo sinandivulaze chifukwa Mulungu anaona kuti ndine wosalakwa ndi kutinso sindinakulakwireni inu mfumu.” 23 Mfumu inali ndi chimwemwe chopambana ndipo inalamulira kuti amutulutse Danieli mʼdzenjemo. Ndipo atamutulutsa Danieli mʼdzenjemo, sanapezeke ndi chilonda chilichonse pa thupi lake, chifukwa iye anadalira Mulungu wake. 24 Mwa lamulo la mfumu, anthu onse amene ananeneza Danieli aja anagwidwa ndi kukaponyedwa mʼdzenje la mikango, pamodzi ndi akazi awo ndi ana awo. Ndipo asanafike pansi pa dzenjelo, mikango inawawakha ndi mphamvu ndi kuteketa mafupa awo onse. 25 Kenaka mfumu Dariyo inalembera anthu a mitundu yonse, ndi anthu a ziyankhulo zosiyanasiyana a mʼdziko lonse kuti,“Mtendere uchuluke pakati panu! 26 “Ndikukhazikitsa lamulo kuti paliponse mʼdziko langa anthu ayenera kuopa ndi kuchitira ulemu Mulungu wa Danieli.“Popeza Iye ndi Mulungu wamoyondi wamuyaya;ufumu wake sudzawonongeka,ulamuliro wake sudzatha. 27 Iye amalanditsa ndipo amapulumutsa,amachita zizindikiro ndi zozizwitsakumwamba ndi pa dziko lapansi.Iye walanditsa Danieliku mphamvu ya mikango.” 28 Choncho Danieli anapeza ufulu pa nthawi ya ulamuliro wa Dariyo ndi ulamuliro wa Koresi wa ku Perisiya.

In Other Versions

Daniel 6 in the ANGEFD

Daniel 6 in the ANTPNG2D

Daniel 6 in the AS21

Daniel 6 in the BAGH

Daniel 6 in the BBPNG

Daniel 6 in the BBT1E

Daniel 6 in the BDS

Daniel 6 in the BEV

Daniel 6 in the BHAD

Daniel 6 in the BIB

Daniel 6 in the BLPT

Daniel 6 in the BNT

Daniel 6 in the BNTABOOT

Daniel 6 in the BNTLV

Daniel 6 in the BOATCB

Daniel 6 in the BOATCB2

Daniel 6 in the BOBCV

Daniel 6 in the BOCNT

Daniel 6 in the BOECS

Daniel 6 in the BOHCB

Daniel 6 in the BOHCV

Daniel 6 in the BOHLNT

Daniel 6 in the BOHNTLTAL

Daniel 6 in the BOICB

Daniel 6 in the BOILNTAP

Daniel 6 in the BOITCV

Daniel 6 in the BOKCV

Daniel 6 in the BOKCV2

Daniel 6 in the BOKHWOG

Daniel 6 in the BOKSSV

Daniel 6 in the BOLCB

Daniel 6 in the BOLCB2

Daniel 6 in the BOMCV

Daniel 6 in the BONAV

Daniel 6 in the BONCB

Daniel 6 in the BONLT

Daniel 6 in the BONUT2

Daniel 6 in the BOPLNT

Daniel 6 in the BOSCB

Daniel 6 in the BOSNC

Daniel 6 in the BOTLNT

Daniel 6 in the BOVCB

Daniel 6 in the BOYCB

Daniel 6 in the BPBB

Daniel 6 in the BPH

Daniel 6 in the BSB

Daniel 6 in the CCB

Daniel 6 in the CUV

Daniel 6 in the CUVS

Daniel 6 in the DBT

Daniel 6 in the DGDNT

Daniel 6 in the DHNT

Daniel 6 in the DNT

Daniel 6 in the ELBE

Daniel 6 in the EMTV

Daniel 6 in the ESV

Daniel 6 in the FBV

Daniel 6 in the FEB

Daniel 6 in the GGMNT

Daniel 6 in the GNT

Daniel 6 in the HARY

Daniel 6 in the HNT

Daniel 6 in the IRVA

Daniel 6 in the IRVB

Daniel 6 in the IRVG

Daniel 6 in the IRVH

Daniel 6 in the IRVK

Daniel 6 in the IRVM

Daniel 6 in the IRVM2

Daniel 6 in the IRVO

Daniel 6 in the IRVP

Daniel 6 in the IRVT

Daniel 6 in the IRVT2

Daniel 6 in the IRVU

Daniel 6 in the ISVN

Daniel 6 in the JSNT

Daniel 6 in the KAPI

Daniel 6 in the KBT1ETNIK

Daniel 6 in the KBV

Daniel 6 in the KJV

Daniel 6 in the KNFD

Daniel 6 in the LBA

Daniel 6 in the LBLA

Daniel 6 in the LNT

Daniel 6 in the LSV

Daniel 6 in the MAAL

Daniel 6 in the MBV

Daniel 6 in the MBV2

Daniel 6 in the MHNT

Daniel 6 in the MKNFD

Daniel 6 in the MNG

Daniel 6 in the MNT

Daniel 6 in the MNT2

Daniel 6 in the MRS1T

Daniel 6 in the NAA

Daniel 6 in the NASB

Daniel 6 in the NBLA

Daniel 6 in the NBS

Daniel 6 in the NBVTP

Daniel 6 in the NET2

Daniel 6 in the NIV11

Daniel 6 in the NNT

Daniel 6 in the NNT2

Daniel 6 in the NNT3

Daniel 6 in the PDDPT

Daniel 6 in the PFNT

Daniel 6 in the RMNT

Daniel 6 in the SBIAS

Daniel 6 in the SBIBS

Daniel 6 in the SBIBS2

Daniel 6 in the SBICS

Daniel 6 in the SBIDS

Daniel 6 in the SBIGS

Daniel 6 in the SBIHS

Daniel 6 in the SBIIS

Daniel 6 in the SBIIS2

Daniel 6 in the SBIIS3

Daniel 6 in the SBIKS

Daniel 6 in the SBIKS2

Daniel 6 in the SBIMS

Daniel 6 in the SBIOS

Daniel 6 in the SBIPS

Daniel 6 in the SBISS

Daniel 6 in the SBITS

Daniel 6 in the SBITS2

Daniel 6 in the SBITS3

Daniel 6 in the SBITS4

Daniel 6 in the SBIUS

Daniel 6 in the SBIVS

Daniel 6 in the SBT

Daniel 6 in the SBT1E

Daniel 6 in the SCHL

Daniel 6 in the SNT

Daniel 6 in the SUSU

Daniel 6 in the SUSU2

Daniel 6 in the SYNO

Daniel 6 in the TBIAOTANT

Daniel 6 in the TBT1E

Daniel 6 in the TBT1E2

Daniel 6 in the TFTIP

Daniel 6 in the TFTU

Daniel 6 in the TGNTATF3T

Daniel 6 in the THAI

Daniel 6 in the TNFD

Daniel 6 in the TNT

Daniel 6 in the TNTIK

Daniel 6 in the TNTIL

Daniel 6 in the TNTIN

Daniel 6 in the TNTIP

Daniel 6 in the TNTIZ

Daniel 6 in the TOMA

Daniel 6 in the TTENT

Daniel 6 in the UBG

Daniel 6 in the UGV

Daniel 6 in the UGV2

Daniel 6 in the UGV3

Daniel 6 in the VBL

Daniel 6 in the VDCC

Daniel 6 in the YALU

Daniel 6 in the YAPE

Daniel 6 in the YBVTP

Daniel 6 in the ZBP