Deuteronomy 5 (BOGWICC)

1 Mose anayitanitsa Aisraeli onse nati:Tamverani inu Aisraeli, malangizo ndi malamulo amene ndikuwuzeni lero. Muwaphunzire ndi kuonetsetsa kuti mukuwatsata. 2 Yehova Mulungu wathu anachita pangano ndi ife ku Horebu. 3 Yehova sanachite pangano ndi makolo athu koma ndi ife, tonse amene tili moyo lero. 4 Yehova anayankhula nanu maso ndi maso kuchokera mʼmoto pa phiri paja. 5 (Pa nthawi imeneyo ine ndinayimirira pakati pa Yehova ndi inu kuti ndikuwuzeni mawu a Yehova, chifukwa inu munkachita mantha ndi moto ndipo simunakwere ku phiri). Ndipo Iye anati: 6 “Ine ndine Yehova Mulungu wako amene ndinakutulutsa ku Igupto, mʼdziko la ukapolo. 7 “Usakhale ndi milungu ina koma Ine ndekha. 8 “Usadzipangire chofanizira chinthu chilichonse chakumwamba kapena cha pa dziko lapansi kapena cha mʼmadzi a pansi pa dziko. 9 Usazigwadire kapena kuzipembedza, pakuti Ine Yehova Mulungu wako, ndine Mulungu wansanje, wolanga ana chifukwa cha tchimo la makolo awo mpaka mʼbado wachitatu ndi wachinayi wa iwo amene amadana nane, 10 koma ndimaonetsa chikondi chosasinthika ku mibado miyandamiyanda ya anthu amene amandikonda ndi kusunga malamulo anga. 11 “Usagwiritse ntchito molakwika dzina la Yehova Mulungu wako, pakuti Yehova adzamutenga kukhala wochimwa aliyense amene akugwiritsa ntchito dzina lakelo molakwika. 12 “Uzisunga tsiku la Sabata kuti likhale lopatulika monga momwe Yehova Mulungu wako anakulamulira. 13 Uzigwira ntchito zako zonse masiku asanu ndi limodzi, 14 koma tsiku lachisanu ndi chiwiri ndi Sabata, tsiku loperekedwa kwa Yehova Mulungu wako. Tsiku limeneli musagwire ntchito iliyonse, inuyo kapena mwana wanu wamwamuna kapena mwana wanu wamkazi kapena wantchito wanu wamwamuna kapena mdzakazi wanu kapena ngʼombe yanu kapena bulu wanu kapena ziweto zanu kapena mlendo amene akukhala mʼmudzi mwanu, motero ndiye kuti wantchito wanu wamwamuna ndi wantchito wanu wamkazi adzapumula monga inuyo. 15 Kumbukira kuti unali kapolo ku Igupto ndipo Yehova Mulungu wako anakutulutsa kumeneko ndi dzanja lamphamvu ndi lotambasuka. Choncho Yehova Mulungu wako akukulamula kuti uzisunga tsiku la Sabata. 16 “Lemekeza abambo ako ndi amayi ako monga Yehova Mulungu wako wakulamulira iwe kuti ukhale ndi moyo wautali ndi kuti zikuyendere bwino mʼdziko limene Yehova Mulungu wako akukupatsa. 17 “Usaphe. 18 “Usachite chigololo. 19 “Usabe. 20 “Usapereke umboni womunamizira mnzako. 21 “Usasirire mkazi wa mnzako. Usasirire nyumba ya mnzako kapena munda wake, wantchito wake wamwamuna kapena mdzakazi wake, ngʼombe yake kapena bulu wake, kapena chilichonse cha mnzako.” 22 Awa ndi malamulo amene Yehova anayankhula ndi mawu okweza kwa gulu lanu lonse pa phiri paja mʼmoto, mtambo ndi mdima woopsa, sanawonjezerepo kanthu. Ndipo anawalemba pa mapale awiri amiyala ndi kundipatsa. 23 Mutamva mawu kuchokera mu mdimawo, phiri lili moto lawilawi, atsogoleri onse a mafuko anu ndi akuluakulu anu anabwera kwa ine. 24 Ndipo munati, “Yehova Mulungu wathu wationetsa ulemerero ndi ukulu wake, ndipo tamva mawu ake kuchokera mʼmoto. Lero taona kuti munthu akhoza kukhala ndi moyo ngakhale Mulungu atayankhula naye. 25 Koma tsopano tife chifukwa chiyani? Moto waukuluwu utinyeketsa, ndipo tifa tikapitirirabe kumva mawu a Yehova Mulungu wathu. 26 Pakuti ndi munthu uti wolengedwa amene anamvapo mawu a Mulungu wamoyo akuyankhula kuchokera mʼmoto, monga tachitiramu, nakhala ndi moyo? 27 Pita pafupi kuti ukamvetsere zonse zimene Yehova Mulungu wathu akunena. Kenaka udzatiwuze chilichonse chimene Yehova Mulungu wathu akunena ndipo tidzamvera ndi kuchita.” 28 Yehova anakumvani pamene munkayankhula kwa ine ndipo Yehova anati kwa ine, “Ndamva zimene anthuwa anena kwa iwe. Chilichonse chimene anena ndi chabwino. 29 Zikanakhala bwino akanakhala ndi mtima wondiopa ndi kusunga malamulo anga nthawi zonse kuti zinthu ziziwayendera bwino, iwowo pamodzi ndi ana awo kwamuyaya. 30 “Pita uwawuze kuti abwerere ku matenti awo. 31 Koma iwe ukhale kuno ndi ine kuti ndikupatse malamulo, malangizo ndi ziphunzitso zimene azitsatira mʼdziko limene ndiwapatse kuti alitenge.” 32 Choncho samalirani kuchita zimene Yehova Mulungu wanu akukulamulirani inu, musapatukire kudzanja lamanja kapena lamanzere. 33 Muyende mʼnjira yonse imene Yehova Mulungu wanu wakulamulirani kuti mukhale ndi moyo ndi kupambana, ndi kuti masiku anu achuluke mʼdziko limene mudzatengelo.

In Other Versions

Deuteronomy 5 in the ANGEFD

Deuteronomy 5 in the ANTPNG2D

Deuteronomy 5 in the AS21

Deuteronomy 5 in the BAGH

Deuteronomy 5 in the BBPNG

Deuteronomy 5 in the BBT1E

Deuteronomy 5 in the BDS

Deuteronomy 5 in the BEV

Deuteronomy 5 in the BHAD

Deuteronomy 5 in the BIB

Deuteronomy 5 in the BLPT

Deuteronomy 5 in the BNT

Deuteronomy 5 in the BNTABOOT

Deuteronomy 5 in the BNTLV

Deuteronomy 5 in the BOATCB

Deuteronomy 5 in the BOATCB2

Deuteronomy 5 in the BOBCV

Deuteronomy 5 in the BOCNT

Deuteronomy 5 in the BOECS

Deuteronomy 5 in the BOHCB

Deuteronomy 5 in the BOHCV

Deuteronomy 5 in the BOHLNT

Deuteronomy 5 in the BOHNTLTAL

Deuteronomy 5 in the BOICB

Deuteronomy 5 in the BOILNTAP

Deuteronomy 5 in the BOITCV

Deuteronomy 5 in the BOKCV

Deuteronomy 5 in the BOKCV2

Deuteronomy 5 in the BOKHWOG

Deuteronomy 5 in the BOKSSV

Deuteronomy 5 in the BOLCB

Deuteronomy 5 in the BOLCB2

Deuteronomy 5 in the BOMCV

Deuteronomy 5 in the BONAV

Deuteronomy 5 in the BONCB

Deuteronomy 5 in the BONLT

Deuteronomy 5 in the BONUT2

Deuteronomy 5 in the BOPLNT

Deuteronomy 5 in the BOSCB

Deuteronomy 5 in the BOSNC

Deuteronomy 5 in the BOTLNT

Deuteronomy 5 in the BOVCB

Deuteronomy 5 in the BOYCB

Deuteronomy 5 in the BPBB

Deuteronomy 5 in the BPH

Deuteronomy 5 in the BSB

Deuteronomy 5 in the CCB

Deuteronomy 5 in the CUV

Deuteronomy 5 in the CUVS

Deuteronomy 5 in the DBT

Deuteronomy 5 in the DGDNT

Deuteronomy 5 in the DHNT

Deuteronomy 5 in the DNT

Deuteronomy 5 in the ELBE

Deuteronomy 5 in the EMTV

Deuteronomy 5 in the ESV

Deuteronomy 5 in the FBV

Deuteronomy 5 in the FEB

Deuteronomy 5 in the GGMNT

Deuteronomy 5 in the GNT

Deuteronomy 5 in the HARY

Deuteronomy 5 in the HNT

Deuteronomy 5 in the IRVA

Deuteronomy 5 in the IRVB

Deuteronomy 5 in the IRVG

Deuteronomy 5 in the IRVH

Deuteronomy 5 in the IRVK

Deuteronomy 5 in the IRVM

Deuteronomy 5 in the IRVM2

Deuteronomy 5 in the IRVO

Deuteronomy 5 in the IRVP

Deuteronomy 5 in the IRVT

Deuteronomy 5 in the IRVT2

Deuteronomy 5 in the IRVU

Deuteronomy 5 in the ISVN

Deuteronomy 5 in the JSNT

Deuteronomy 5 in the KAPI

Deuteronomy 5 in the KBT1ETNIK

Deuteronomy 5 in the KBV

Deuteronomy 5 in the KJV

Deuteronomy 5 in the KNFD

Deuteronomy 5 in the LBA

Deuteronomy 5 in the LBLA

Deuteronomy 5 in the LNT

Deuteronomy 5 in the LSV

Deuteronomy 5 in the MAAL

Deuteronomy 5 in the MBV

Deuteronomy 5 in the MBV2

Deuteronomy 5 in the MHNT

Deuteronomy 5 in the MKNFD

Deuteronomy 5 in the MNG

Deuteronomy 5 in the MNT

Deuteronomy 5 in the MNT2

Deuteronomy 5 in the MRS1T

Deuteronomy 5 in the NAA

Deuteronomy 5 in the NASB

Deuteronomy 5 in the NBLA

Deuteronomy 5 in the NBS

Deuteronomy 5 in the NBVTP

Deuteronomy 5 in the NET2

Deuteronomy 5 in the NIV11

Deuteronomy 5 in the NNT

Deuteronomy 5 in the NNT2

Deuteronomy 5 in the NNT3

Deuteronomy 5 in the PDDPT

Deuteronomy 5 in the PFNT

Deuteronomy 5 in the RMNT

Deuteronomy 5 in the SBIAS

Deuteronomy 5 in the SBIBS

Deuteronomy 5 in the SBIBS2

Deuteronomy 5 in the SBICS

Deuteronomy 5 in the SBIDS

Deuteronomy 5 in the SBIGS

Deuteronomy 5 in the SBIHS

Deuteronomy 5 in the SBIIS

Deuteronomy 5 in the SBIIS2

Deuteronomy 5 in the SBIIS3

Deuteronomy 5 in the SBIKS

Deuteronomy 5 in the SBIKS2

Deuteronomy 5 in the SBIMS

Deuteronomy 5 in the SBIOS

Deuteronomy 5 in the SBIPS

Deuteronomy 5 in the SBISS

Deuteronomy 5 in the SBITS

Deuteronomy 5 in the SBITS2

Deuteronomy 5 in the SBITS3

Deuteronomy 5 in the SBITS4

Deuteronomy 5 in the SBIUS

Deuteronomy 5 in the SBIVS

Deuteronomy 5 in the SBT

Deuteronomy 5 in the SBT1E

Deuteronomy 5 in the SCHL

Deuteronomy 5 in the SNT

Deuteronomy 5 in the SUSU

Deuteronomy 5 in the SUSU2

Deuteronomy 5 in the SYNO

Deuteronomy 5 in the TBIAOTANT

Deuteronomy 5 in the TBT1E

Deuteronomy 5 in the TBT1E2

Deuteronomy 5 in the TFTIP

Deuteronomy 5 in the TFTU

Deuteronomy 5 in the TGNTATF3T

Deuteronomy 5 in the THAI

Deuteronomy 5 in the TNFD

Deuteronomy 5 in the TNT

Deuteronomy 5 in the TNTIK

Deuteronomy 5 in the TNTIL

Deuteronomy 5 in the TNTIN

Deuteronomy 5 in the TNTIP

Deuteronomy 5 in the TNTIZ

Deuteronomy 5 in the TOMA

Deuteronomy 5 in the TTENT

Deuteronomy 5 in the UBG

Deuteronomy 5 in the UGV

Deuteronomy 5 in the UGV2

Deuteronomy 5 in the UGV3

Deuteronomy 5 in the VBL

Deuteronomy 5 in the VDCC

Deuteronomy 5 in the YALU

Deuteronomy 5 in the YAPE

Deuteronomy 5 in the YBVTP

Deuteronomy 5 in the ZBP