Esther 2 (BOGWICC)

1 Pambuyo pake mtima wa Ahasiwero utatsika, Ahasiwero anakumbukira Vasiti ndi zimene anachita Vasitiyo. Anakumbukiranso lamulo lomukhudza limene anasindikiza. 2 Tsono anyamata a mfumu amene ankamutumikira anati, “Mfumu, akufunireni anamwali okongola. 3 Mfumu isankhe oyangʼanira pa chigawo chilichonse cha ufumu wake kuti abwere nawo pamodzi anamwali onse okongola ku nyumba yosungira akazi ku Susa. Hegai, mdindo wofulidwa wa mfumu, amene amayangʼanira amayi, akhale wosamalira anamwaliwa ndipo aziwapatsa mafuta odzola. 4 Ndipo namwali amene mfumu yakondwera naye akhale mfumukazi mʼmalo mwa Vasiti.” Mfumu inakondwera ndi uphunguwu, ndipo inachita momwemo. 5 Myuda wina wa fuko la Benjamini, dzina lake Mordekai, mwana wa Yairi, mwana wa Simei, mwana wa Kisi, anali mu mzinda wa Susa. 6 Iyeyu anali mmodzi mwa anthu amene anatengedwa ukapolo ndi Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni kuchokera ku Yerusalemu pamodzi ndi Yekoniya mfumu ya Yuda. 7 Mordekai nʼkuti atalera Hadasa, amene ankatchedwanso Estere, mwana wamkazi wa amalume ake chifukwa analibe abambo kapena amayi. Mtsikanayu anali wokongola ndi wooneka bwino ndipo Mordekai ankamutenga ngati mwana wake weniweni pamene abambo ndi amayi ake anamwalira. 8 Lamulo la mfumu atalilengeza ndi kubwera nawo pamodzi anamwali ambiri ku mzinda wa Susa kuti akasamalidwe ndi Hegai, Estere nayenso anatengedwa kupita naye ku nyumba ya mfumu kuti akasamalidwe ndi Hegai woyangʼanira nyumba yosungiramo akazi uja. 9 Hegai anasangalatsidwa naye namwaliyo ndipo anamukomera mtima. Mosataya nthawi anamupatsa mafuta ake odzola ndi chakudya chapadera. Anamusankhiranso anamwali asanu ndi awiri a ku nyumba ya mfumu kuti azimutumikira, ndipo iye pamodzi ndi anamwali omutumikira aja anawapatsa malo abwino koposa mʼnyumba yosungira akazi. 10 Estere sanawulule mtundu wake ndi abale ake chifukwa Mordekai anamuletsa kutero. 11 Tsiku ndi tsiku Mordekai ankayendayenda pafupi ndi bwalo la nyumba yosungiramo akazi ija kuti adziwe za moyo wa Estere ndi kuti zinthu zikumuyendera bwanji. 12 Tsono nthawi inkafika kuti namwali aliyense akaonekere kwa mfumu Ahasiwero, pakutha pa miyezi khumi ndi iwiri yomwe inakhazikitsidwa kuti amayi azidzikongoletsa. Pa miyezi isanu ndi umodzi ankadzola mafuta a mure ndipo pa miyezi isanu ndi umodzi inayo ankadzola zonunkhira ndi zokongoletsa. 13 Ndipo namwali ankapita kwa mfumu motere: Ankaloledwa kutenga chilichonse angafune mʼnyumba yosungiramo akazi kupita nacho ku nyumba ya mfumu. 14 Ankalowa madzulo kwa mfumu ndi kutuluka mmawa kupita ku nyumba ina yosungira akazi yomwe ankayangʼanira ndi Saasigazi, mdindo wofulidwa wa mfumu amene amayangʼanira akazi a mfumu. Namwali sankabwerera kwa mfumu pokhapokha amukomere mtima ndi kumuyitana potchula dzina lake. 15 Tsono inafika nthawi kuti Estere, mwana wamkazi wa Abihaili amenenso analeredwa ndi Mordekai amalume ake, alowe kwa mfumu. Iye sanapemphe kanthu kalikonse, koma anatenga zokhazo zimene ananena Hegai mdindo wofulidwa wa mfumu woyangʼanira nyumba yosungiramo akazi. Ndipo aliyense amene anamuona Estere, anasangalatsidwa naye. 16 Anapita naye kwa mfumu Ahasiwero ku nyumba ya ufumu pa mwezi wa khumi, mwezi wa Tebete, chaka cha chisanu ndi chiwiri cha ufumu wake. 17 Ndipo mfumu inamukonda Estere koposa wina aliyense wa akazi aja, kotero inamukonda ndi kumukomera mtima koposa wina aliyense wa anamwali aja. Choncho anamumveka chipewa chaufumu pa mutu pake nakhala mfumukazi mʼmalo mwa Vasiti. 18 Ndipo mfumu inakonza phwando lalikulu, phwando la Estere, kukonzera anthu olemekezeka ndi nduna zake zonse. Analamuliranso kuti anthu mʼzigawo zonse asapereke msonkho ndipo anapereka mphatso monga mwakukoma mtima kwa mfumu. 19 Anamwali atasonkhanitsidwa pamodzi, Mordekai anakhala pansi pa chipata cha mfumu. 20 Koma Estere anali asanawululebe za mtundu wake ndi anthu a pa banja lake monga momwe analamulira Mordekai, chifukwa anapitirira kutsata malangizo a Mordekai monga ankachitira pamene ankamulera. 21 Pa nthawi imene Mordekai ankalondera pa chipata cha mfumu, Bigitana ndi Teresi, awiri mwa adindo ofulidwa amfumu, olondera pa khomo la nyumba yake, anayipidwa mtima ndipo anakonza chiwembu chofuna kupha mfumu Ahasiwero. 22 Koma Mordekai atazindikira za chiwembuchi anawuza mfumukazi Estere ndipo iye anakawuza mfumu mʼmalo mwa Mordekai. 23 Ndipo pamene anafufuza za chiwembuchi kuti zinali zoona, adindo awiriwa anaphedwa monyongedwa. Zinthu izi zinalembedwa mʼbuku la Mbiri ndi kusungidwa ndi Mfumu.

In Other Versions

Esther 2 in the ANGEFD

Esther 2 in the ANTPNG2D

Esther 2 in the AS21

Esther 2 in the BAGH

Esther 2 in the BBPNG

Esther 2 in the BBT1E

Esther 2 in the BDS

Esther 2 in the BEV

Esther 2 in the BHAD

Esther 2 in the BIB

Esther 2 in the BLPT

Esther 2 in the BNT

Esther 2 in the BNTABOOT

Esther 2 in the BNTLV

Esther 2 in the BOATCB

Esther 2 in the BOATCB2

Esther 2 in the BOBCV

Esther 2 in the BOCNT

Esther 2 in the BOECS

Esther 2 in the BOHCB

Esther 2 in the BOHCV

Esther 2 in the BOHLNT

Esther 2 in the BOHNTLTAL

Esther 2 in the BOICB

Esther 2 in the BOILNTAP

Esther 2 in the BOITCV

Esther 2 in the BOKCV

Esther 2 in the BOKCV2

Esther 2 in the BOKHWOG

Esther 2 in the BOKSSV

Esther 2 in the BOLCB

Esther 2 in the BOLCB2

Esther 2 in the BOMCV

Esther 2 in the BONAV

Esther 2 in the BONCB

Esther 2 in the BONLT

Esther 2 in the BONUT2

Esther 2 in the BOPLNT

Esther 2 in the BOSCB

Esther 2 in the BOSNC

Esther 2 in the BOTLNT

Esther 2 in the BOVCB

Esther 2 in the BOYCB

Esther 2 in the BPBB

Esther 2 in the BPH

Esther 2 in the BSB

Esther 2 in the CCB

Esther 2 in the CUV

Esther 2 in the CUVS

Esther 2 in the DBT

Esther 2 in the DGDNT

Esther 2 in the DHNT

Esther 2 in the DNT

Esther 2 in the ELBE

Esther 2 in the EMTV

Esther 2 in the ESV

Esther 2 in the FBV

Esther 2 in the FEB

Esther 2 in the GGMNT

Esther 2 in the GNT

Esther 2 in the HARY

Esther 2 in the HNT

Esther 2 in the IRVA

Esther 2 in the IRVB

Esther 2 in the IRVG

Esther 2 in the IRVH

Esther 2 in the IRVK

Esther 2 in the IRVM

Esther 2 in the IRVM2

Esther 2 in the IRVO

Esther 2 in the IRVP

Esther 2 in the IRVT

Esther 2 in the IRVT2

Esther 2 in the IRVU

Esther 2 in the ISVN

Esther 2 in the JSNT

Esther 2 in the KAPI

Esther 2 in the KBT1ETNIK

Esther 2 in the KBV

Esther 2 in the KJV

Esther 2 in the KNFD

Esther 2 in the LBA

Esther 2 in the LBLA

Esther 2 in the LNT

Esther 2 in the LSV

Esther 2 in the MAAL

Esther 2 in the MBV

Esther 2 in the MBV2

Esther 2 in the MHNT

Esther 2 in the MKNFD

Esther 2 in the MNG

Esther 2 in the MNT

Esther 2 in the MNT2

Esther 2 in the MRS1T

Esther 2 in the NAA

Esther 2 in the NASB

Esther 2 in the NBLA

Esther 2 in the NBS

Esther 2 in the NBVTP

Esther 2 in the NET2

Esther 2 in the NIV11

Esther 2 in the NNT

Esther 2 in the NNT2

Esther 2 in the NNT3

Esther 2 in the PDDPT

Esther 2 in the PFNT

Esther 2 in the RMNT

Esther 2 in the SBIAS

Esther 2 in the SBIBS

Esther 2 in the SBIBS2

Esther 2 in the SBICS

Esther 2 in the SBIDS

Esther 2 in the SBIGS

Esther 2 in the SBIHS

Esther 2 in the SBIIS

Esther 2 in the SBIIS2

Esther 2 in the SBIIS3

Esther 2 in the SBIKS

Esther 2 in the SBIKS2

Esther 2 in the SBIMS

Esther 2 in the SBIOS

Esther 2 in the SBIPS

Esther 2 in the SBISS

Esther 2 in the SBITS

Esther 2 in the SBITS2

Esther 2 in the SBITS3

Esther 2 in the SBITS4

Esther 2 in the SBIUS

Esther 2 in the SBIVS

Esther 2 in the SBT

Esther 2 in the SBT1E

Esther 2 in the SCHL

Esther 2 in the SNT

Esther 2 in the SUSU

Esther 2 in the SUSU2

Esther 2 in the SYNO

Esther 2 in the TBIAOTANT

Esther 2 in the TBT1E

Esther 2 in the TBT1E2

Esther 2 in the TFTIP

Esther 2 in the TFTU

Esther 2 in the TGNTATF3T

Esther 2 in the THAI

Esther 2 in the TNFD

Esther 2 in the TNT

Esther 2 in the TNTIK

Esther 2 in the TNTIL

Esther 2 in the TNTIN

Esther 2 in the TNTIP

Esther 2 in the TNTIZ

Esther 2 in the TOMA

Esther 2 in the TTENT

Esther 2 in the UBG

Esther 2 in the UGV

Esther 2 in the UGV2

Esther 2 in the UGV3

Esther 2 in the VBL

Esther 2 in the VDCC

Esther 2 in the YALU

Esther 2 in the YAPE

Esther 2 in the YBVTP

Esther 2 in the ZBP