Exodus 27 (BOGWICC)

1 “Upange guwa lansembe lamatabwa amtengo wa mkesha. Likhale lofanana mbali zonse, msinkhu wake masentimita 137, mulitali mwake masentimita 229, mulifupi mwake masentimita 229. 2 Upange nyanga imodziimodzi pa ngodya zake zinayizo kuti nyangazo ndi guwalo zikhale chinthu chimodzi, ndipo ulikute guwalo ndi mkuwa. 3 Upange ziwiya zamkuwa izi zogwirira ntchito pa guwalo: miphika yochotsera phulusa, mafosholo, mabeseni owazira magazi, ngowe zokowera nyama ndi zosonkhezera moto. 4 Upange sefa yachitsulo chamkuwa ndipo mʼngodya zake zinayizo upangiremo mphete zamkuwa. 5 Uyike sefayo mmunsi mwa khoma la guwa lansembelo, ndipo ilekezere pakati pa guwa lansembelo. 6 Upange nsichi zamtengo wa mkesha ndipo uzikutire ndi mkuwa. 7 Pamene mukunyamula guwalo, muzilowetsa nsichizo mʼmphetemo mbali zonse ziwiri za guwalo. 8 Guwalo likhale lamatabwa ndi logoba mʼkati mwake. Ulipange monga momwe ndinakuonetsera pa phiri paja. 9 “Upange bwalo la chihema. Mbali yakummwera ikhale yotalika mamita 46 ndipo ikhale ndi nsalu yotchinga yofewa yosalala yolukidwa bwino. 10 Upangenso mizati makumi awiri, matsinde makumi awiri amkuwa, ndi ngowe zasiliva ndi zingwe za mizatiyo. 11 Mbali yakumpoto ikhalenso yotalika mamita 46 ndipo ikhale ndi nsalu yotchinga. Pakhalenso mizati makumi awiri, matsinde amkuwa makumi awiri, ngowe zasiliva ndi zingwe za mizatiyo. 12 “Mbali yakumadzulo ya bwalolo ikhale yotalika mamita 23 ndipo ikhale ndi nsalu yotchinga, nsichi khumi ndi matsinde khumi. 13 Mbali yakummawa, kotulukira dzuwa, kutalika kwa bwalo kukhale mamita 23. 14 Mbali imodzi yachipata kukhale nsalu yotchinga yotalika mamita asanu ndi awiri, mizati itatu ndi matsinde atatu. 15 Ndipo ku mbali inayo kukhale nsalu yotchinga ya mamita asanu ndi awiri pamodzi ndi mizati itatu ndi matsinde atatu. 16 “Pa chipata cha bwalolo pakhale nsalu yotchinga yamtundu wa mtambo, yapepo ndi yofiira ndiponso yofewa yosalala. Nsaluyo ikhale yotalika mamita asanu ndi anayi, yopangidwa ndi anthu aluso. Pakhalenso mizati yake inayi ndi matsinde akenso anayi. 17 Mizati yonse yozungulira bwalolo ilumikizidwe ndi zingwe zasiliva. Ngowe zake zikhale zasiliva, koma matsinde ake akhale amkuwa. 18 Kutalika kwa bwalolo kukhale mamita 46, mulifupi mwake mamita 23, msinkhu wake masentimita 230. Nsalu ya katani ikhale yofewa ndi yosalala bwino. Matsinde ake akhale amkuwa. 19 Zipangizo zonse zogwiritsa ntchito zosiyanasiyana pa chihemacho, zikhomo za chihema ndi zabwalolo zikhale zamkuwa. 20 “Lamula Aisraeli kuti akupatse mafuta anyale a olivi wabwino kwambiri kuti nyalezo ziziyaka nthawi zonse. 21 Mʼchihema cha msonkhano, koma kunja kwa nsalu yotchinga Bokosi la Chipangano, Aaroni ndi ana ake azionetsetsa kuti nyale ikukhala chiyakire pamaso pa Yehova kuyambira madzulo mpaka mmawa. Limeneli ndi lamulo lamuyaya pakati pa Aisraeli pa mibado yonse.”

In Other Versions

Exodus 27 in the ANGEFD

Exodus 27 in the ANTPNG2D

Exodus 27 in the AS21

Exodus 27 in the BAGH

Exodus 27 in the BBPNG

Exodus 27 in the BBT1E

Exodus 27 in the BDS

Exodus 27 in the BEV

Exodus 27 in the BHAD

Exodus 27 in the BIB

Exodus 27 in the BLPT

Exodus 27 in the BNT

Exodus 27 in the BNTABOOT

Exodus 27 in the BNTLV

Exodus 27 in the BOATCB

Exodus 27 in the BOATCB2

Exodus 27 in the BOBCV

Exodus 27 in the BOCNT

Exodus 27 in the BOECS

Exodus 27 in the BOHCB

Exodus 27 in the BOHCV

Exodus 27 in the BOHLNT

Exodus 27 in the BOHNTLTAL

Exodus 27 in the BOICB

Exodus 27 in the BOILNTAP

Exodus 27 in the BOITCV

Exodus 27 in the BOKCV

Exodus 27 in the BOKCV2

Exodus 27 in the BOKHWOG

Exodus 27 in the BOKSSV

Exodus 27 in the BOLCB

Exodus 27 in the BOLCB2

Exodus 27 in the BOMCV

Exodus 27 in the BONAV

Exodus 27 in the BONCB

Exodus 27 in the BONLT

Exodus 27 in the BONUT2

Exodus 27 in the BOPLNT

Exodus 27 in the BOSCB

Exodus 27 in the BOSNC

Exodus 27 in the BOTLNT

Exodus 27 in the BOVCB

Exodus 27 in the BOYCB

Exodus 27 in the BPBB

Exodus 27 in the BPH

Exodus 27 in the BSB

Exodus 27 in the CCB

Exodus 27 in the CUV

Exodus 27 in the CUVS

Exodus 27 in the DBT

Exodus 27 in the DGDNT

Exodus 27 in the DHNT

Exodus 27 in the DNT

Exodus 27 in the ELBE

Exodus 27 in the EMTV

Exodus 27 in the ESV

Exodus 27 in the FBV

Exodus 27 in the FEB

Exodus 27 in the GGMNT

Exodus 27 in the GNT

Exodus 27 in the HARY

Exodus 27 in the HNT

Exodus 27 in the IRVA

Exodus 27 in the IRVB

Exodus 27 in the IRVG

Exodus 27 in the IRVH

Exodus 27 in the IRVK

Exodus 27 in the IRVM

Exodus 27 in the IRVM2

Exodus 27 in the IRVO

Exodus 27 in the IRVP

Exodus 27 in the IRVT

Exodus 27 in the IRVT2

Exodus 27 in the IRVU

Exodus 27 in the ISVN

Exodus 27 in the JSNT

Exodus 27 in the KAPI

Exodus 27 in the KBT1ETNIK

Exodus 27 in the KBV

Exodus 27 in the KJV

Exodus 27 in the KNFD

Exodus 27 in the LBA

Exodus 27 in the LBLA

Exodus 27 in the LNT

Exodus 27 in the LSV

Exodus 27 in the MAAL

Exodus 27 in the MBV

Exodus 27 in the MBV2

Exodus 27 in the MHNT

Exodus 27 in the MKNFD

Exodus 27 in the MNG

Exodus 27 in the MNT

Exodus 27 in the MNT2

Exodus 27 in the MRS1T

Exodus 27 in the NAA

Exodus 27 in the NASB

Exodus 27 in the NBLA

Exodus 27 in the NBS

Exodus 27 in the NBVTP

Exodus 27 in the NET2

Exodus 27 in the NIV11

Exodus 27 in the NNT

Exodus 27 in the NNT2

Exodus 27 in the NNT3

Exodus 27 in the PDDPT

Exodus 27 in the PFNT

Exodus 27 in the RMNT

Exodus 27 in the SBIAS

Exodus 27 in the SBIBS

Exodus 27 in the SBIBS2

Exodus 27 in the SBICS

Exodus 27 in the SBIDS

Exodus 27 in the SBIGS

Exodus 27 in the SBIHS

Exodus 27 in the SBIIS

Exodus 27 in the SBIIS2

Exodus 27 in the SBIIS3

Exodus 27 in the SBIKS

Exodus 27 in the SBIKS2

Exodus 27 in the SBIMS

Exodus 27 in the SBIOS

Exodus 27 in the SBIPS

Exodus 27 in the SBISS

Exodus 27 in the SBITS

Exodus 27 in the SBITS2

Exodus 27 in the SBITS3

Exodus 27 in the SBITS4

Exodus 27 in the SBIUS

Exodus 27 in the SBIVS

Exodus 27 in the SBT

Exodus 27 in the SBT1E

Exodus 27 in the SCHL

Exodus 27 in the SNT

Exodus 27 in the SUSU

Exodus 27 in the SUSU2

Exodus 27 in the SYNO

Exodus 27 in the TBIAOTANT

Exodus 27 in the TBT1E

Exodus 27 in the TBT1E2

Exodus 27 in the TFTIP

Exodus 27 in the TFTU

Exodus 27 in the TGNTATF3T

Exodus 27 in the THAI

Exodus 27 in the TNFD

Exodus 27 in the TNT

Exodus 27 in the TNTIK

Exodus 27 in the TNTIL

Exodus 27 in the TNTIN

Exodus 27 in the TNTIP

Exodus 27 in the TNTIZ

Exodus 27 in the TOMA

Exodus 27 in the TTENT

Exodus 27 in the UBG

Exodus 27 in the UGV

Exodus 27 in the UGV2

Exodus 27 in the UGV3

Exodus 27 in the VBL

Exodus 27 in the VDCC

Exodus 27 in the YALU

Exodus 27 in the YAPE

Exodus 27 in the YBVTP

Exodus 27 in the ZBP