Exodus 3 (BOGWICC)

1 Tsono Mose amaweta ziweto za mpongozi wake Yetero, wansembe uja wa ku Midiyani. Tsiku lina iye anazitsogolera kupita ku chipululu ndipo anafika ku phiri la Mulungu lotchedwa Horebu. 2 Kumeneko mngelo wa Yehova anaonekera kwa iye mʼmalawi amoto mʼchitsamba. Mose anaona kuti ngakhale chitsambacho chimayaka koma sichimanyeka. 3 Tsono Mose anati mu mtima mwake, “Ine ndipita komweko ndikaone zodabwitsazi, chitsamba sichikunyeka chifukwa chiyani?” 4 Yehova ataona kuti Mose anapatuka kuti adzaonetsetse, Mulungu anamuyitana Mose kuchokera mʼchitsambamo nati, “Mose! Mose!”Ndipo anayankha, “Wawa.” 5 Mulungu anati, “Usayandikire kuno. Vula nsapato zako, pakuti malo amene wayimapo ndi opatulika.” 6 Mulungu anati, “Ine ndine Mulungu wa makolo ako, Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isake, ndi Mulungu wa Yakobo.” Atamva zimenezi, Mose anaphimba nkhope yake chifukwa anaopa kuona Mulungu. 7 Yehova anati, “Ine ndaona ndithu mazunzo a anthu anga amene ali ku Igupto. Ndamva kulira kwawo chifukwa cha anthu amene akuwapsinja, ndipo ndakhudzidwa ndi masautso awo. 8 Choncho ndabwera kuti ndiwapulumutse mʼdzanja la Aigupto, kuwatulutsa mʼdzikolo ndi kukawalowetsa mʼdziko labwino ndi lalikulu, dziko loyenda mkaka ndi uchi, kwawo kwa Akanaani, Ahiti, Aamori, Aperezi, Ahivi ndi Ayebusi. 9 Ine ndamva ndithu kulira kwa Aisraeli, ndipo ndaona mmene Aigupto akuwazunzira. 10 Kotero tsopano, pita. Ine ndikukutuma kwa Farao kuti ukatulutse anthu anga, Aisraeli mʼdziko la Igupto.” 11 Koma Mose anafunsa Mulungu, “Ine ndine yani kuti ndipite kwa Farao ndi kukatulutsa Aisraeli mʼdziko la Igupto?” 12 Ndipo Mulungu anati, “Ine ndidzakhala nawe, ndipo ichi chidzakhala chizindikiro kwa iwe kuti ndine amene ndakutuma; Ukadzatulutsa anthu anga mʼdziko la Igupto, udzapembedza Mulungu pa phiri lino.” 13 Mose anati kwa Mulungu, “Ngati ndipita kwa Aisraeli ndi kukawawuza kuti, ‘Mulungu wa makolo anu wandituma kwa inu,’ ndipo iwo nʼkukandifunsa kuti ‘Dzina lake ndi ndani?’ Tsono ine ndikawawuze chiyani?” 14 Mulungu anati kwa Mose, “NDINE AMENE NDILI. Izi ndi zimene ukanene kwa Aisraeli: ‘NDINE wandituma kwa inu.’ ” 15 Mulungu anatinso kwa Mose, “Ukanene kwa Aisraeli kuti ‘Yehova, Mulungu wa makolo anu, Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isake, ndi Mulungu wa Yakobo, wandituma kwa inu.’ Ili ndilo dzina langa mpaka muyaya, ndipo mibado ya mʼtsogolomo izidzanditchula ndi dzina limeneli. 16 “Pita, ukawasonkhanitse akuluakulu a Israeli ndipo ukati kwa iwo, ‘Yehova, Mulungu wa makolo anu, Mulungu wa Abrahamu, Isake ndi Yakobo, anandionekera ndipo akuti Iye wadzakuyenderani ndipo waona mmene Aigupto akukuzunzirani. 17 Choncho wanenetsa kuti adzakutulutsani mʼdziko la Igupto, dziko la masautsoli kupita ku dziko la Akanaani, Ahiti, Aamori Aperezi, Ahivi ndi Ayebusi, dziko loyenda mkaka ndi uchi.’ 18 “Akuluakulu a Israeli akakumvera. Kenaka iwe ndi akuluakuluwo mukapite kwa mfumu ya Igupto ndipo mukanene kuti, ‘Yehova, Mulungu wa Ahebri, wakumana nafe. Tsono tikukupemphani kuti mutilole tipite pa ulendo wa masiku atatu mʼchipululu kuti tikapereke nsembe kwa Yehova Mulungu wathu.’ 19 Koma Ine ndikudziwa kuti mfumu ya Igupto sikakulolani kuti mupite pokhapokha Ine nditayikakamiza. 20 Tsono Ine ndidzatambasula dzanja langa ndi kukantha Aigupto ndi zodabwitsa zanga zimene ndidzazichita pakati pawo. Zikadzatha izi, Iye adzakulolani kuti mupite. 21 “Ndipo ine ndidzafewetsa mtima wa Aigupto pa anthu anga, kotero kuti mukadzatuluka simudzapita wopanda kanthu. 22 Mkazi aliyense adzapemphe Mwigupto woyandikana naye ndiponso mkazi amene akukhala mʼnyumba yake, kuti amupatse ziwiya za siliva ndi golide ndiponso zovala zimene mudzaveka ana anu aamuna ndi aakazi. Ndipo potero mudzawalanda zonse Aiguptowo.”

In Other Versions

Exodus 3 in the ANGEFD

Exodus 3 in the ANTPNG2D

Exodus 3 in the AS21

Exodus 3 in the BAGH

Exodus 3 in the BBPNG

Exodus 3 in the BBT1E

Exodus 3 in the BDS

Exodus 3 in the BEV

Exodus 3 in the BHAD

Exodus 3 in the BIB

Exodus 3 in the BLPT

Exodus 3 in the BNT

Exodus 3 in the BNTABOOT

Exodus 3 in the BNTLV

Exodus 3 in the BOATCB

Exodus 3 in the BOATCB2

Exodus 3 in the BOBCV

Exodus 3 in the BOCNT

Exodus 3 in the BOECS

Exodus 3 in the BOHCB

Exodus 3 in the BOHCV

Exodus 3 in the BOHLNT

Exodus 3 in the BOHNTLTAL

Exodus 3 in the BOICB

Exodus 3 in the BOILNTAP

Exodus 3 in the BOITCV

Exodus 3 in the BOKCV

Exodus 3 in the BOKCV2

Exodus 3 in the BOKHWOG

Exodus 3 in the BOKSSV

Exodus 3 in the BOLCB

Exodus 3 in the BOLCB2

Exodus 3 in the BOMCV

Exodus 3 in the BONAV

Exodus 3 in the BONCB

Exodus 3 in the BONLT

Exodus 3 in the BONUT2

Exodus 3 in the BOPLNT

Exodus 3 in the BOSCB

Exodus 3 in the BOSNC

Exodus 3 in the BOTLNT

Exodus 3 in the BOVCB

Exodus 3 in the BOYCB

Exodus 3 in the BPBB

Exodus 3 in the BPH

Exodus 3 in the BSB

Exodus 3 in the CCB

Exodus 3 in the CUV

Exodus 3 in the CUVS

Exodus 3 in the DBT

Exodus 3 in the DGDNT

Exodus 3 in the DHNT

Exodus 3 in the DNT

Exodus 3 in the ELBE

Exodus 3 in the EMTV

Exodus 3 in the ESV

Exodus 3 in the FBV

Exodus 3 in the FEB

Exodus 3 in the GGMNT

Exodus 3 in the GNT

Exodus 3 in the HARY

Exodus 3 in the HNT

Exodus 3 in the IRVA

Exodus 3 in the IRVB

Exodus 3 in the IRVG

Exodus 3 in the IRVH

Exodus 3 in the IRVK

Exodus 3 in the IRVM

Exodus 3 in the IRVM2

Exodus 3 in the IRVO

Exodus 3 in the IRVP

Exodus 3 in the IRVT

Exodus 3 in the IRVT2

Exodus 3 in the IRVU

Exodus 3 in the ISVN

Exodus 3 in the JSNT

Exodus 3 in the KAPI

Exodus 3 in the KBT1ETNIK

Exodus 3 in the KBV

Exodus 3 in the KJV

Exodus 3 in the KNFD

Exodus 3 in the LBA

Exodus 3 in the LBLA

Exodus 3 in the LNT

Exodus 3 in the LSV

Exodus 3 in the MAAL

Exodus 3 in the MBV

Exodus 3 in the MBV2

Exodus 3 in the MHNT

Exodus 3 in the MKNFD

Exodus 3 in the MNG

Exodus 3 in the MNT

Exodus 3 in the MNT2

Exodus 3 in the MRS1T

Exodus 3 in the NAA

Exodus 3 in the NASB

Exodus 3 in the NBLA

Exodus 3 in the NBS

Exodus 3 in the NBVTP

Exodus 3 in the NET2

Exodus 3 in the NIV11

Exodus 3 in the NNT

Exodus 3 in the NNT2

Exodus 3 in the NNT3

Exodus 3 in the PDDPT

Exodus 3 in the PFNT

Exodus 3 in the RMNT

Exodus 3 in the SBIAS

Exodus 3 in the SBIBS

Exodus 3 in the SBIBS2

Exodus 3 in the SBICS

Exodus 3 in the SBIDS

Exodus 3 in the SBIGS

Exodus 3 in the SBIHS

Exodus 3 in the SBIIS

Exodus 3 in the SBIIS2

Exodus 3 in the SBIIS3

Exodus 3 in the SBIKS

Exodus 3 in the SBIKS2

Exodus 3 in the SBIMS

Exodus 3 in the SBIOS

Exodus 3 in the SBIPS

Exodus 3 in the SBISS

Exodus 3 in the SBITS

Exodus 3 in the SBITS2

Exodus 3 in the SBITS3

Exodus 3 in the SBITS4

Exodus 3 in the SBIUS

Exodus 3 in the SBIVS

Exodus 3 in the SBT

Exodus 3 in the SBT1E

Exodus 3 in the SCHL

Exodus 3 in the SNT

Exodus 3 in the SUSU

Exodus 3 in the SUSU2

Exodus 3 in the SYNO

Exodus 3 in the TBIAOTANT

Exodus 3 in the TBT1E

Exodus 3 in the TBT1E2

Exodus 3 in the TFTIP

Exodus 3 in the TFTU

Exodus 3 in the TGNTATF3T

Exodus 3 in the THAI

Exodus 3 in the TNFD

Exodus 3 in the TNT

Exodus 3 in the TNTIK

Exodus 3 in the TNTIL

Exodus 3 in the TNTIN

Exodus 3 in the TNTIP

Exodus 3 in the TNTIZ

Exodus 3 in the TOMA

Exodus 3 in the TTENT

Exodus 3 in the UBG

Exodus 3 in the UGV

Exodus 3 in the UGV2

Exodus 3 in the UGV3

Exodus 3 in the VBL

Exodus 3 in the VDCC

Exodus 3 in the YALU

Exodus 3 in the YAPE

Exodus 3 in the YBVTP

Exodus 3 in the ZBP