Exodus 30 (BOGWICC)

1 Upange guwa lamatabwa amtengo wa mkesha lofukizirapo lubani. 2 Likhale lofanana mbali zonse. Mulitali masentimita 46, mulifupi masentimita 46, ndipo msinkhu masentimita 91. Nyanga zake zipangidwe kumodzi ndi guwalo. 3 Ukute guwa lonse ndi golide wabwino kwambiri, pamwamba pake, mbali zonse zinayi, pamodzi ndi nyanga zake. Ndipo upange mkombero wagolide kuzungulira guwalo. 4 Upange mphete ziwiri zagolide ndipo uzilumikize ku guwa mʼmunsi mwa mkombero, mphete ziwiri ku mbali zonse ziwiri zoyangʼanana. Mphetozo zizigwira nsichi zonyamulira guwalo. 5 Upange mizati yamtengo wa mkesha ndipo uyikute ndi golide. 6 Uyike guwalo patsogolo pa nsalu yotchinga Bokosi la Chipangano. Apa ndi pamene ndizidzakumana nawe. 7 “Aaroni ayenera kumafukiza lubani wonunkhira pa guwalo mmawa uliwonse. Pamene akukonza nyale zija afukizenso lubani. 8 Aaroni ayenera kufukizanso lubani pamene ayatsa nyale madzulo kuti lubani akhale akuyaka nthawi zonse pamaso pa Yehova kwa mibado imene ikubwera. 9 Pa guwapo usafukize lubani wachilendo kapena kuperekapo nsembe yopsereza kapena nsembe yaufa. Usathire pa guwapo ngakhale nsembe yachakumwa. 10 Aaroni azidzapereka nsembe yopepesera machimo pa nyanga za guwalo kamodzi pa chaka. Mwambowu uzidzachitika pogwiritsa ntchito magazi a nsembe yopepesera machimo, ndipo zizidzachitika mʼmibado yanu yonse. Choncho guwa lansembelo lidzakhala loyera ndi loperekedwa kwa Yehova.” 11 Ndipo Yehova anati kwa Mose, 12 “Pamene ukuchita kalembera wa Aisraeli, munthu aliyense ayenera kupereka kwa Yehova chowombolera moyo wake pamene akuwerengedwa. Motero mliri sudzabwera pa iwo pamene ukuwawerenga. 13 Izi ndi zimene aliyense wolembedwa mu kawundula ayenera kupereka: theka la sekeli, kutanthauza ndalama zolemera magalamu asanu ndi limodzi malingana ndi kawerengedwe ka ndalama za ku Nyumba ya Mulungu. Paja sekeli imodzi ikulingana ndi magera makumi awiri. Theka la sekeli chidzakhala chopereka cha kwa Yehova. 14 Aliyense wolembedwa mu kawundula amene ali ndi zaka makumi awiri kapena kupitirira ayenera kupereka chopereka kwa Yehova. 15 Anthu olemera asapereke koposa theka la sekeli ndipo osauka asapereke kuchepera theka la sekeli pamene mukupereka nsembe kwa Yehova yowombolera miyoyo yanu. 16 Ulandire ndalama zopepeserazo kuchokera kwa Aisraeli ndipo zigwiritsidwe ntchito ya ku tenti ya msonkhano. Zoperekazi zidzakhala chikumbutso cha Aisraeli pamaso pa Yehova, ndiponso zowombolera miyoyo yanu.” 17 Ndipo Yehova anati kwa Mose, 18 “Upange beseni lamkuwa lokhala ndi miyendo yamkuwanso. Uliyike pakati pa tenti ya msonkhano ndi guwa lansembe ndipo uthiremo madzi. 19 Aaroni ndi ana ake azisamba mʼmanja ndi kutsuka mapazi awo ndi madzi amenewo. 20 Pamene akulowa mu tenti ya msonkhano, iwo asambe madziwa kuti asafe. Ndiponso pamene akupita kukatumikira ku guwa lansembe ndi kupereka nsembe yopsereza kwa Yehova, 21 azisamba mʼmanja mwawo ndi kutsuka mapazi kuti asadzafe. Limeneli ndi lamulo limene Aaroni, pamodzi ndi ana ndi zidzukulu zake mʼtsogolomo ayenera kumadzalitsatira mpaka muyaya.” 22 Ndipo Yehova anati kwa Mose, 23 “Utenge zonunkhira bwino kwambiri izi: makilogalamu asanu ndi limodzi a mure wamadzi, makilogalamu atatu a zonunkhira bwino za mtundu wa sinamoni, makilogalamu atatu a nzimbe yonunkhira bwino kwambiri, 24 makilogalamu asanu ndi limodzi a mkesha. Zonsezi zikhale malingana ndi muyeso wa ku Nyumba ya Mulungu. Pakhalenso malita anayi a mafuta a olivi. 25 Ugwiritse ntchito zinthu zimenezi kupanga mafuta opatulika odzozera, mafuta onunkhira, apangidwe ndi mʼmisiri waluso lopanga zonunkhiritsa. Awa adzakhala mafuta opatulika odzozera. 26 Tsono uwagwiritse ntchito podzoza tenti ya msonkhano, Bokosi la Chipangano, 27 tebulo, ndi ziwiya zake zonse, choyikapo nyale ndi zipangizo zake, guwa lofukizirapo lubani, 28 guwa lansembe yopsereza ndi ziwiya zake zonse, ndiponso beseni pamodzi ndi nsichi yake. 29 Zonsezi uzipatule kuti zidzakhale zopatulika, ndipo chilichonse chimene chidzakhudza zimenezi chidzakhala chopatulika. 30 “Udzoze Aaroni ndi ana ake aamuna ndi kuwapatula kuti akhale ansembe onditumikira. 31 Tsono awuze a Israeli kuti, mafuta wodzozera awa adzakhala wopatulika mpaka muyaya. 32 Musadzadzozere munthu wamba mafuta amenewa, ndipo musadzapange mafuta wofanana ndi amenewa. Mafutawa ndi wopatulika ndipo akhale woyera kwa inu. 33 Wina aliyense amene adzapanga mafuta wonunkhira wofanana nawo kapena kudzozera mafutawa munthu wamba osati wansembe ayenera kuchotsedwa pakati pa anthu anzake.” 34 Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Tenga muyeso wofanana wa zinthu zonunkhira izi: sitakate, onika, galibanumu pamodzi ndi lubani weniweni. 35 Uziphatikize pamodzi zonsezi ndi kupanga lubani monga amachitira mmisiri wopanga zonunkhira. Athire mchere ndipo akhale woyera ndi wopatulika. 36 Upere gawo lina mosalala kwambiri ndipo utapepo pangʼono ndi kuyika patsogolo pa Bokosi la Chipangano mu tenti ya msonkhano, kumene ine ndidzakumane nawe. Lubani ameneyu kwa inu adzakhala wopatulika kwambiri. 37 Musapange lubani wanu potsatira njira iyi. Lubani yense wopangidwa mwa njira iyi akhale wopatulika, woperekedwa kwa Yehova. 38 Aliyense amene adzapanga wofanana naye kuti asangalale ndi fungo lake ayenera kuchotsedwa pakati pa anthu anzake.”

In Other Versions

Exodus 30 in the ANGEFD

Exodus 30 in the ANTPNG2D

Exodus 30 in the AS21

Exodus 30 in the BAGH

Exodus 30 in the BBPNG

Exodus 30 in the BBT1E

Exodus 30 in the BDS

Exodus 30 in the BEV

Exodus 30 in the BHAD

Exodus 30 in the BIB

Exodus 30 in the BLPT

Exodus 30 in the BNT

Exodus 30 in the BNTABOOT

Exodus 30 in the BNTLV

Exodus 30 in the BOATCB

Exodus 30 in the BOATCB2

Exodus 30 in the BOBCV

Exodus 30 in the BOCNT

Exodus 30 in the BOECS

Exodus 30 in the BOHCB

Exodus 30 in the BOHCV

Exodus 30 in the BOHLNT

Exodus 30 in the BOHNTLTAL

Exodus 30 in the BOICB

Exodus 30 in the BOILNTAP

Exodus 30 in the BOITCV

Exodus 30 in the BOKCV

Exodus 30 in the BOKCV2

Exodus 30 in the BOKHWOG

Exodus 30 in the BOKSSV

Exodus 30 in the BOLCB

Exodus 30 in the BOLCB2

Exodus 30 in the BOMCV

Exodus 30 in the BONAV

Exodus 30 in the BONCB

Exodus 30 in the BONLT

Exodus 30 in the BONUT2

Exodus 30 in the BOPLNT

Exodus 30 in the BOSCB

Exodus 30 in the BOSNC

Exodus 30 in the BOTLNT

Exodus 30 in the BOVCB

Exodus 30 in the BOYCB

Exodus 30 in the BPBB

Exodus 30 in the BPH

Exodus 30 in the BSB

Exodus 30 in the CCB

Exodus 30 in the CUV

Exodus 30 in the CUVS

Exodus 30 in the DBT

Exodus 30 in the DGDNT

Exodus 30 in the DHNT

Exodus 30 in the DNT

Exodus 30 in the ELBE

Exodus 30 in the EMTV

Exodus 30 in the ESV

Exodus 30 in the FBV

Exodus 30 in the FEB

Exodus 30 in the GGMNT

Exodus 30 in the GNT

Exodus 30 in the HARY

Exodus 30 in the HNT

Exodus 30 in the IRVA

Exodus 30 in the IRVB

Exodus 30 in the IRVG

Exodus 30 in the IRVH

Exodus 30 in the IRVK

Exodus 30 in the IRVM

Exodus 30 in the IRVM2

Exodus 30 in the IRVO

Exodus 30 in the IRVP

Exodus 30 in the IRVT

Exodus 30 in the IRVT2

Exodus 30 in the IRVU

Exodus 30 in the ISVN

Exodus 30 in the JSNT

Exodus 30 in the KAPI

Exodus 30 in the KBT1ETNIK

Exodus 30 in the KBV

Exodus 30 in the KJV

Exodus 30 in the KNFD

Exodus 30 in the LBA

Exodus 30 in the LBLA

Exodus 30 in the LNT

Exodus 30 in the LSV

Exodus 30 in the MAAL

Exodus 30 in the MBV

Exodus 30 in the MBV2

Exodus 30 in the MHNT

Exodus 30 in the MKNFD

Exodus 30 in the MNG

Exodus 30 in the MNT

Exodus 30 in the MNT2

Exodus 30 in the MRS1T

Exodus 30 in the NAA

Exodus 30 in the NASB

Exodus 30 in the NBLA

Exodus 30 in the NBS

Exodus 30 in the NBVTP

Exodus 30 in the NET2

Exodus 30 in the NIV11

Exodus 30 in the NNT

Exodus 30 in the NNT2

Exodus 30 in the NNT3

Exodus 30 in the PDDPT

Exodus 30 in the PFNT

Exodus 30 in the RMNT

Exodus 30 in the SBIAS

Exodus 30 in the SBIBS

Exodus 30 in the SBIBS2

Exodus 30 in the SBICS

Exodus 30 in the SBIDS

Exodus 30 in the SBIGS

Exodus 30 in the SBIHS

Exodus 30 in the SBIIS

Exodus 30 in the SBIIS2

Exodus 30 in the SBIIS3

Exodus 30 in the SBIKS

Exodus 30 in the SBIKS2

Exodus 30 in the SBIMS

Exodus 30 in the SBIOS

Exodus 30 in the SBIPS

Exodus 30 in the SBISS

Exodus 30 in the SBITS

Exodus 30 in the SBITS2

Exodus 30 in the SBITS3

Exodus 30 in the SBITS4

Exodus 30 in the SBIUS

Exodus 30 in the SBIVS

Exodus 30 in the SBT

Exodus 30 in the SBT1E

Exodus 30 in the SCHL

Exodus 30 in the SNT

Exodus 30 in the SUSU

Exodus 30 in the SUSU2

Exodus 30 in the SYNO

Exodus 30 in the TBIAOTANT

Exodus 30 in the TBT1E

Exodus 30 in the TBT1E2

Exodus 30 in the TFTIP

Exodus 30 in the TFTU

Exodus 30 in the TGNTATF3T

Exodus 30 in the THAI

Exodus 30 in the TNFD

Exodus 30 in the TNT

Exodus 30 in the TNTIK

Exodus 30 in the TNTIL

Exodus 30 in the TNTIN

Exodus 30 in the TNTIP

Exodus 30 in the TNTIZ

Exodus 30 in the TOMA

Exodus 30 in the TTENT

Exodus 30 in the UBG

Exodus 30 in the UGV

Exodus 30 in the UGV2

Exodus 30 in the UGV3

Exodus 30 in the VBL

Exodus 30 in the VDCC

Exodus 30 in the YALU

Exodus 30 in the YAPE

Exodus 30 in the YBVTP

Exodus 30 in the ZBP