Exodus 39 (BOGWICC)

1 Anapanga zovala za ansembe, zovala potumikira ku malo wopatulika pogwiritsa ntchito nsalu ya mtundu wa mtambo, yapepo ndi yofiira. Anapanganso zovala zopatulika za Aaroni monga momwe Yehova analamulira Mose. 2 Popanga efodi, iwo anagwiritsa ntchito golide, nsalu yamtundu wa mtambo, yapepo, yofiira, yosalala yofewa. 3 Anasula golide wopyapyala ndi kumulezaleza kuti alumikize kumodzi ndi nsalu yamtundu wa mtambo, yapepo ndi yofiira yosalala yofewa yolukidwa mwaluso. 4 Iwo anapanga efodi imene inali ndi timalamba tiwiri ta pa mapewa, tosokerera ku msonga zake ziwiri kuti azitha kumanga. 5 Lamba womangira efodi anali wolukidwa mwaluso ngati efodiyo. Anali nsalu imodzi ndi efodiyo, wopangidwa ndi golide, nsalu yamtundu wa mtambo, yapepo, yofiira, yofewa yosalala, monga momwe Yehova analamulira Mose. 6 Iwo anakonza miyala ya onikisi ndi kuyiika mu zoyikamo zake zagolide ndipo anazokota mayina a ana a Israeli monga amachitira pa chidindo. 7 Kenaka anayimangirira pa tinsalu ta mʼmapewa ta efodi tija ngati miyala ya chikumbutso cha ana a Israeli monga momwe Yehova analamulira Mose. 8 Iwo anapanga chovala chapachifuwa mwaluso kwambiri. Anachipanga ngati efodi pogwiritsa ntchito golide, nsalu yamtundu wa mtambo, yapepo, yofiira, yofewa yosalala ndi yolukidwa bwino. 9 Kutalika kwake kunali kofanana mbali zonse, mulitali masentimita 23, mulifupi masentimita 23, chinali chopinda pawiri. 10 Kenaka anayikapo mizere inayi ya miyala yokongola kwambiri. Mzere woyamba anayika miyala ya rubi, topazi ndi berili; 11 mzere wachiwiri anayikapo miyala ya emeradi, safiro ndi dayimondi; 12 mzere wachitatu anayikapo miyala ya opera, agate ndi ametisiti; 13 mzere wachinayi anayikapo miyala ya topazi, onikisi ndi yasipa. Miyalayi anayiyika mu zoyikamo zagolide. 14 Miyalayo inalipo khumi ndi iwiri, uliwonse kuyimira dzina limodzi la ana a Israeli. Mwala uliwonse unazokotedwa ngati chidindo dzina limodzi la mafuko khumi ndi awiri a Israeli. 15 Anapanga timaunyolo tagolide wabwino kwambiri ta pa chovala chapachifuwa, topota ngati chingwe. 16 Anapanganso zoyikamo zake zagolide ndi mphete ziwiri zagolide, ndipo anamangirira mphetezo pa ngodya ziwiri za chovala chapachifuwa. 17 Anamangirira timaunyolo tiwiri tagolide tija pa mphete za pa ngodya pa chovala chapachifuwacho. 18 Ndipo mbali ina ya timaunyoloto anamangirira pa zoyikapo zake ziwiri zija, ndi kulumikiza pa tinsalu takutsogolo kwa mapewa a efodi. 19 Anapanganso mphete ziwiri zagolide ndipo analumikiza ku ngodya ziwiri zamʼmunsi mwa chovala chapachifuwa, champhepete mwake, mʼkati pafupi ndi efodi ija. 20 Kenaka anapanga mphete zina ziwiri zagolide ndi kuzilumikiza kumunsi kwa tinsalu takutsogolo kwa efodi, pafupi ndi msoko, pamwamba pangʼono pa lamba wamʼchiwuno wa efodi. 21 Anamangirira mphete za pa chovala chapachifuwa zija ku mphete za efodi ndi chingwe chamtundu wa mtambo, kulumikiza lamba ndi chovala chapachifuwacho kuti chovala chapachifuwacho chisalekane ndi efodi ija monga Yehova analamulira Mose. 22 Anayipangira efodiyo mkanjo wamtundu wa mtambo, wolukidwa ndi mmisiri waluso. 23 Mkanjowo unali ndi malo opisapo mutu pakati pakepo. Pa chibowopo panali chibandi chosokedwa mochita ngati kuluka monga muja akhalira malaya kuti chibowocho chilimbe, chisangʼambike. 24 Pa mpendero wamʼmunsi wa mkanjowo, analumikiza mphonje zokhala ngati makangadza za nsalu yamtundu wa mtambo, yapepo ndi yofiira yofewa yosalala ndi yopetedwa bwino yomwe inazungulira mkanjo. 25 Ndipo anapanga maberu agolide wabwino kwambiri ndipo analumikiza mozungulira mpendero pakati pa makangadzawo. 26 Kotero panali mphonje imodzi ndi belu limodzi kuzungulira mpendero wa mkanjo wovala potumikira monga momwe Yehova analamulira Mose. 27 Kwa Aaroni ndi ana ake anawapangira minjiro ya nsalu yofewa yosalala, yolukidwa bwino ndi munthu waluso, 28 nduwira ya nsalu yofewa yosalala, lamba wa nsalu yofewa yosalala, womanga mʼmutu, ndi makabudula amʼkati a nsalu yofewa yosalala olukidwa bwino. 29 Anapanga lamba wolukidwa bwino wa nsalu yofewa ndi yosalala ya mtundu wa mtambo yapepo ndi yofiira. Ili linaliluso la munthu wopanga zokometsera monga Yehova analamulira Mose. 30 Iwo anapanga duwa lagolide wabwino kwambiri ngati chidindo ndipo anazokotapo mawu akuti, WOPATULIKIRA YEHOVA. 31 Kenaka analimangira ndi chingwe cha nsalu yamtundu wa mtambo pa nduwira, monga momwe Yehova analamulira Mose. 32 Tsopano ntchito yonse ya tenti ya msonkhano inatha. Aisraeli anachita zonse monga momwe Yehova analamulira Mose. 33 Kenaka anabweretsa chihema kwa Mose. Tenti ndi zipangizo zake, ngowe zake, maferemu ake, mitanda yake, mizati yake ndi matsinde ake; 34 chophimba cha chikopa cha nkhosa yayimuna chonyikidwa mu utoto ofiira, chophimba cha chikopa cha akatumbu ndi nsalu zophimba; 35 bokosi la umboni pamodzi ndi mitengo yake yonyamulira ndiponso chovundikira chake; 36 tebulo pamodzi ndi zipangizo zake ndiponso buledi wokhala pamaso pa Yehova; 37 choyikapo nyale chagolide wabwino kwambiri pamodzi ndi nyale zake ndi zipangizo zake zonse, ndiponso mafuta anyalezo; 38 guwa lagolide, mafuta odzozera, lubani onunkhira ndi nsalu yotchinga pa khomo lolowera mu tenti; 39 guwa lamkuwa ndi sefa yamkuwa, mitengo yake yonyamulira ndi zipangizo zake zonse; beseni ndi miyendo yake; 40 nsalu yotchingira bwalo pamodzi ndi mizati yake ndi matsinde ake ndiponso nsalu yotchingira pa khomo lolowera ku bwalo; zingwe zake ndi zikhomo za tenti; zipangizo zonse za chihema, tenti ya msonkhano; 41 ndiponso zovala zolukidwa zovala potumikira kumalo opatulika, zovala zopatulika za wansembe, Aaroni pamodzi ndi za ana ake aamuna pamene akutumikira monga ansembe. 42 Aisraeli anagwira ntchito yonse monga momwe Yehova analamulira Mose. 43 Mose anayendera ntchitoyo ndipo anaona kuti anayichita monga momwe Yehova analamulira. Kotero Mose anawadalitsa.

In Other Versions

Exodus 39 in the ANGEFD

Exodus 39 in the ANTPNG2D

Exodus 39 in the AS21

Exodus 39 in the BAGH

Exodus 39 in the BBPNG

Exodus 39 in the BBT1E

Exodus 39 in the BDS

Exodus 39 in the BEV

Exodus 39 in the BHAD

Exodus 39 in the BIB

Exodus 39 in the BLPT

Exodus 39 in the BNT

Exodus 39 in the BNTABOOT

Exodus 39 in the BNTLV

Exodus 39 in the BOATCB

Exodus 39 in the BOATCB2

Exodus 39 in the BOBCV

Exodus 39 in the BOCNT

Exodus 39 in the BOECS

Exodus 39 in the BOHCB

Exodus 39 in the BOHCV

Exodus 39 in the BOHLNT

Exodus 39 in the BOHNTLTAL

Exodus 39 in the BOICB

Exodus 39 in the BOILNTAP

Exodus 39 in the BOITCV

Exodus 39 in the BOKCV

Exodus 39 in the BOKCV2

Exodus 39 in the BOKHWOG

Exodus 39 in the BOKSSV

Exodus 39 in the BOLCB

Exodus 39 in the BOLCB2

Exodus 39 in the BOMCV

Exodus 39 in the BONAV

Exodus 39 in the BONCB

Exodus 39 in the BONLT

Exodus 39 in the BONUT2

Exodus 39 in the BOPLNT

Exodus 39 in the BOSCB

Exodus 39 in the BOSNC

Exodus 39 in the BOTLNT

Exodus 39 in the BOVCB

Exodus 39 in the BOYCB

Exodus 39 in the BPBB

Exodus 39 in the BPH

Exodus 39 in the BSB

Exodus 39 in the CCB

Exodus 39 in the CUV

Exodus 39 in the CUVS

Exodus 39 in the DBT

Exodus 39 in the DGDNT

Exodus 39 in the DHNT

Exodus 39 in the DNT

Exodus 39 in the ELBE

Exodus 39 in the EMTV

Exodus 39 in the ESV

Exodus 39 in the FBV

Exodus 39 in the FEB

Exodus 39 in the GGMNT

Exodus 39 in the GNT

Exodus 39 in the HARY

Exodus 39 in the HNT

Exodus 39 in the IRVA

Exodus 39 in the IRVB

Exodus 39 in the IRVG

Exodus 39 in the IRVH

Exodus 39 in the IRVK

Exodus 39 in the IRVM

Exodus 39 in the IRVM2

Exodus 39 in the IRVO

Exodus 39 in the IRVP

Exodus 39 in the IRVT

Exodus 39 in the IRVT2

Exodus 39 in the IRVU

Exodus 39 in the ISVN

Exodus 39 in the JSNT

Exodus 39 in the KAPI

Exodus 39 in the KBT1ETNIK

Exodus 39 in the KBV

Exodus 39 in the KJV

Exodus 39 in the KNFD

Exodus 39 in the LBA

Exodus 39 in the LBLA

Exodus 39 in the LNT

Exodus 39 in the LSV

Exodus 39 in the MAAL

Exodus 39 in the MBV

Exodus 39 in the MBV2

Exodus 39 in the MHNT

Exodus 39 in the MKNFD

Exodus 39 in the MNG

Exodus 39 in the MNT

Exodus 39 in the MNT2

Exodus 39 in the MRS1T

Exodus 39 in the NAA

Exodus 39 in the NASB

Exodus 39 in the NBLA

Exodus 39 in the NBS

Exodus 39 in the NBVTP

Exodus 39 in the NET2

Exodus 39 in the NIV11

Exodus 39 in the NNT

Exodus 39 in the NNT2

Exodus 39 in the NNT3

Exodus 39 in the PDDPT

Exodus 39 in the PFNT

Exodus 39 in the RMNT

Exodus 39 in the SBIAS

Exodus 39 in the SBIBS

Exodus 39 in the SBIBS2

Exodus 39 in the SBICS

Exodus 39 in the SBIDS

Exodus 39 in the SBIGS

Exodus 39 in the SBIHS

Exodus 39 in the SBIIS

Exodus 39 in the SBIIS2

Exodus 39 in the SBIIS3

Exodus 39 in the SBIKS

Exodus 39 in the SBIKS2

Exodus 39 in the SBIMS

Exodus 39 in the SBIOS

Exodus 39 in the SBIPS

Exodus 39 in the SBISS

Exodus 39 in the SBITS

Exodus 39 in the SBITS2

Exodus 39 in the SBITS3

Exodus 39 in the SBITS4

Exodus 39 in the SBIUS

Exodus 39 in the SBIVS

Exodus 39 in the SBT

Exodus 39 in the SBT1E

Exodus 39 in the SCHL

Exodus 39 in the SNT

Exodus 39 in the SUSU

Exodus 39 in the SUSU2

Exodus 39 in the SYNO

Exodus 39 in the TBIAOTANT

Exodus 39 in the TBT1E

Exodus 39 in the TBT1E2

Exodus 39 in the TFTIP

Exodus 39 in the TFTU

Exodus 39 in the TGNTATF3T

Exodus 39 in the THAI

Exodus 39 in the TNFD

Exodus 39 in the TNT

Exodus 39 in the TNTIK

Exodus 39 in the TNTIL

Exodus 39 in the TNTIN

Exodus 39 in the TNTIP

Exodus 39 in the TNTIZ

Exodus 39 in the TOMA

Exodus 39 in the TTENT

Exodus 39 in the UBG

Exodus 39 in the UGV

Exodus 39 in the UGV2

Exodus 39 in the UGV3

Exodus 39 in the VBL

Exodus 39 in the VDCC

Exodus 39 in the YALU

Exodus 39 in the YAPE

Exodus 39 in the YBVTP

Exodus 39 in the ZBP