Ezekiel 18 (BOGWICC)

1 Yehova anandiyankhula nati: 2 “Kodi anthu inu mumatanthauza chiyani mukamabwerezabwereza kunena mwambi uwu wokhudza dziko la Israeli kuti:“ ‘Nkhuyu zodya akulu zimapotandi ana omwe?’ ” 3 “Ndithu pali Ine wamoyo, akutero Ambuye Yehova, simudzanenanso mwambi umenewu mu Israeli. 4 Pakuti moyo uliwonse ndi wanga. Moyo wa abambo ndi wanga, wamwananso ndi wanga. Munthu wochimwa ndi amene adzafe. 5 “Tiyerekeze kuti pali munthu wolungamaamene amachita zolungama ndi zolondola. 6 Iye sadyera nawo pa mapiri a chipembedzokapena kupembedza mafano a Aisraeli.Iye sayipitsa mkazi wa mnzakekapena kugonana ndi mkazi pamene akusamba. 7 Iye sapondereza munthu wina aliyense,koma amabwezera wangongole nʼchigwiriro chake.Iye salanda zinthu za osauka,koma amapereka chakudya kwa anthu anjala,ndipo amapereka zovala kwa anthu ausiwa. 8 Iye sakongoletsa ndalama mwa katapira,kapena kulandira chiwongoladzanja chachikulu.Amadziletsa kuchita zoyipandipo sakondera poweruza milandu. 9 Iye amatsatira malangizo anga,ndipo amasunga malamulo anga mokhulupirika.Munthu ameneyo ndi wolungama;iye adzakhala ndithu ndi moyo,akutero Ambuye Yehova. 10 “Tiyerekeze kuti munthu wolungama chotere wabala mwana chimbalangondo amene amakhalira kupha anthu ndi kuchita zinthu zina zotere. 11 Iye nʼkumachita zinthu zimene ngakhale abambo ake sanachitepo.“Amadyera nawo ku mapiri achipembedzo.Amayipitsa mkazi wa mnzake. 12 Iye amapondereza munthu wosauka ndi wosowa.Amalanda zinthu za osauka.Sabweza chikole cha munthu wa ngongole.Iye amatembenukira ku mafanonachita zonyansa. 13 Iye amakongoletsa mwa katapira ndipo amalandira chiwongoladzanja chachikulu.Kodi munthu wotereyu nʼkukhala ndi moyo? Ayi ndithu! Chifukwa wachita zinthu zonyansa zonsezi, adzaphedwa ndipo adzalandira chilango chomuyenera. 14 “Tsono tiyerekeze kuti munthu woyipa uyu wabala mwana amene amaona machimo onse amene abambo ake ankachita. Ngakhale amaona koma osatsanzira ntchito zake zoyipazo. 15 “Sadyera nawo pa mapiri achipembedzo.Sapembedza mafano a ku Israeli.Sayipitsa mkazi wa mnzake. 16 Sapondereza munthu wina aliyense.Satenga chikole akabwereketsa chinthu. Salanda zinthu za osauka.Salanda zinthu za munthu.Amapereka chakudya kwa anthu anjala.Amapereka zovala kwa anthu aumphawi. 17 Amadziletsa kuchita zoyipa.Sakongoletsa kuti apezepo phindu. Salandira chiwongoladzanja.Amasunga malangizo anga ndi kumvera malamulo anga.Munthu wotereyo sadzafa chifukwa cha machimo a abambo ake. Adzakhala ndi moyo ndithu. 18 Koma abambo ake, popeza kuti anazunza anthu ena ndi kubera mʼbale wawo ndiponso popeza kuti sanachitire zabwino anansi ake, adzafera machimo ake omwe. 19 “Mwina inu mukhoza kufunsa kuti, ‘Nʼchifukwa chiyani mwana salangidwa chifukwa cha kulakwa kwa abambo ake? Ayi, mwanayo adzakhala ndi moyo chifukwa ankachita zolungama ndi zolondola ndipo ankasamala kumvera malamulo anga onse. 20 Munthu wochimwa ndiye amene adzafe. Mwana sadzapezeka wolakwa chifukwa cha abambo ake, kapena abambo kupezeka wolakwa chifukwa cha mwana wawo. Chilungamo cha munthu wolungama ndicho chidzamupulutse, ndipo kuyipa kwa munthu wochimwa ndiko kudzamuwonongetse. 21 “ ‘Munthu woyipa akatembenuka mtima ndi kusiya machimo amene ankachita ndi kuyamba kumvera malamulo anga ndi kumachita zolungama ndi zokhulupirika, ndiye kuti adzakhala ndi moyo. Sadzafa ayi. 22 Zoyipa zake zonse zidzakhululukidwa. Chifukwa cha zinthu zolungama zimene anazichita adzakhala ndi moyo. 23 Kodi Ine ndimakondwera ndi imfa ya munthu woyipa? Ayi, ndimakondwera pamene woyipa watembenuka mtima kuti akhale ndi moyo. Akutero Ambuye Yehova. 24 “ ‘Koma ngati munthu wolungama apatuka kusiya zachilungamo ndi kuyamba kuchita tchimo ndi zonyansa za mtundu uliwonse zimene amachita anthu oyipa, kodi munthu wotereyu nʼkukhala ndi moyo? Ayi ndithu, zolungama zake zonse sizidzakumbukiridwa. Iye adzayenera kufa chifukwa cha machimo amene anachita. 25 “Komabe inu mukunena kuti, ‘Zimene Ambuye amachita ndi zopanda chilungamo.’ Tamvani tsono inu Aisraeli: Kodi zochita zanga ndizo zosalungama? Kodi si zochita zanu zimene ndi zosalungama? 26 Ngati munthu wolungama atembenuka kusiya chilungamo chake ndi kuchita tchimo, iye adzafa chifukwa cha tchimolo. 27 Koma ngati munthu woyipa aleka zoyipa zake zimene anazichita ndi kuyamba kuchita zimene ndi zolungama ndi zolondola, iye adzapulumutsa moyo wake. 28 Popeza waganizira za zolakwa zonse ankachita ndipo wazileka, iye adzakhala ndi moyo ndithu; sadzafa. 29 Komabe Aisraeli akunena kuti, ‘Zimene Ambuye amachita ndi zopanda chilungamo.’ Kodi zochita zanga ndizo zopanda chilungamo, inu Aisraeli? Kodi si zochita zanu zimene ndi zopanda chilungamo? 30 “Chifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti: inu Aisraeli, Ine ndidzakuweruzani aliyense wa inu molingana ndi ntchito zake. Lapani! Lekani zoyipa zanu kuti musawonongeke nazo. 31 Tayani zolakwa zanu zonse zimene munandichimwira nazo ndipo khalani ndi mtima watsopano ndi mzimu watsopano. Kodi muferanji inu Aisraeli? 32 Ine sindikondwera ndi imfa ya munthu aliyense, akutero Ambuye Yehova. Chifukwa chake, lapani kuti mukhale ndi moyo.”

In Other Versions

Ezekiel 18 in the ANGEFD

Ezekiel 18 in the ANTPNG2D

Ezekiel 18 in the AS21

Ezekiel 18 in the BAGH

Ezekiel 18 in the BBPNG

Ezekiel 18 in the BBT1E

Ezekiel 18 in the BDS

Ezekiel 18 in the BEV

Ezekiel 18 in the BHAD

Ezekiel 18 in the BIB

Ezekiel 18 in the BLPT

Ezekiel 18 in the BNT

Ezekiel 18 in the BNTABOOT

Ezekiel 18 in the BNTLV

Ezekiel 18 in the BOATCB

Ezekiel 18 in the BOATCB2

Ezekiel 18 in the BOBCV

Ezekiel 18 in the BOCNT

Ezekiel 18 in the BOECS

Ezekiel 18 in the BOHCB

Ezekiel 18 in the BOHCV

Ezekiel 18 in the BOHLNT

Ezekiel 18 in the BOHNTLTAL

Ezekiel 18 in the BOICB

Ezekiel 18 in the BOILNTAP

Ezekiel 18 in the BOITCV

Ezekiel 18 in the BOKCV

Ezekiel 18 in the BOKCV2

Ezekiel 18 in the BOKHWOG

Ezekiel 18 in the BOKSSV

Ezekiel 18 in the BOLCB

Ezekiel 18 in the BOLCB2

Ezekiel 18 in the BOMCV

Ezekiel 18 in the BONAV

Ezekiel 18 in the BONCB

Ezekiel 18 in the BONLT

Ezekiel 18 in the BONUT2

Ezekiel 18 in the BOPLNT

Ezekiel 18 in the BOSCB

Ezekiel 18 in the BOSNC

Ezekiel 18 in the BOTLNT

Ezekiel 18 in the BOVCB

Ezekiel 18 in the BOYCB

Ezekiel 18 in the BPBB

Ezekiel 18 in the BPH

Ezekiel 18 in the BSB

Ezekiel 18 in the CCB

Ezekiel 18 in the CUV

Ezekiel 18 in the CUVS

Ezekiel 18 in the DBT

Ezekiel 18 in the DGDNT

Ezekiel 18 in the DHNT

Ezekiel 18 in the DNT

Ezekiel 18 in the ELBE

Ezekiel 18 in the EMTV

Ezekiel 18 in the ESV

Ezekiel 18 in the FBV

Ezekiel 18 in the FEB

Ezekiel 18 in the GGMNT

Ezekiel 18 in the GNT

Ezekiel 18 in the HARY

Ezekiel 18 in the HNT

Ezekiel 18 in the IRVA

Ezekiel 18 in the IRVB

Ezekiel 18 in the IRVG

Ezekiel 18 in the IRVH

Ezekiel 18 in the IRVK

Ezekiel 18 in the IRVM

Ezekiel 18 in the IRVM2

Ezekiel 18 in the IRVO

Ezekiel 18 in the IRVP

Ezekiel 18 in the IRVT

Ezekiel 18 in the IRVT2

Ezekiel 18 in the IRVU

Ezekiel 18 in the ISVN

Ezekiel 18 in the JSNT

Ezekiel 18 in the KAPI

Ezekiel 18 in the KBT1ETNIK

Ezekiel 18 in the KBV

Ezekiel 18 in the KJV

Ezekiel 18 in the KNFD

Ezekiel 18 in the LBA

Ezekiel 18 in the LBLA

Ezekiel 18 in the LNT

Ezekiel 18 in the LSV

Ezekiel 18 in the MAAL

Ezekiel 18 in the MBV

Ezekiel 18 in the MBV2

Ezekiel 18 in the MHNT

Ezekiel 18 in the MKNFD

Ezekiel 18 in the MNG

Ezekiel 18 in the MNT

Ezekiel 18 in the MNT2

Ezekiel 18 in the MRS1T

Ezekiel 18 in the NAA

Ezekiel 18 in the NASB

Ezekiel 18 in the NBLA

Ezekiel 18 in the NBS

Ezekiel 18 in the NBVTP

Ezekiel 18 in the NET2

Ezekiel 18 in the NIV11

Ezekiel 18 in the NNT

Ezekiel 18 in the NNT2

Ezekiel 18 in the NNT3

Ezekiel 18 in the PDDPT

Ezekiel 18 in the PFNT

Ezekiel 18 in the RMNT

Ezekiel 18 in the SBIAS

Ezekiel 18 in the SBIBS

Ezekiel 18 in the SBIBS2

Ezekiel 18 in the SBICS

Ezekiel 18 in the SBIDS

Ezekiel 18 in the SBIGS

Ezekiel 18 in the SBIHS

Ezekiel 18 in the SBIIS

Ezekiel 18 in the SBIIS2

Ezekiel 18 in the SBIIS3

Ezekiel 18 in the SBIKS

Ezekiel 18 in the SBIKS2

Ezekiel 18 in the SBIMS

Ezekiel 18 in the SBIOS

Ezekiel 18 in the SBIPS

Ezekiel 18 in the SBISS

Ezekiel 18 in the SBITS

Ezekiel 18 in the SBITS2

Ezekiel 18 in the SBITS3

Ezekiel 18 in the SBITS4

Ezekiel 18 in the SBIUS

Ezekiel 18 in the SBIVS

Ezekiel 18 in the SBT

Ezekiel 18 in the SBT1E

Ezekiel 18 in the SCHL

Ezekiel 18 in the SNT

Ezekiel 18 in the SUSU

Ezekiel 18 in the SUSU2

Ezekiel 18 in the SYNO

Ezekiel 18 in the TBIAOTANT

Ezekiel 18 in the TBT1E

Ezekiel 18 in the TBT1E2

Ezekiel 18 in the TFTIP

Ezekiel 18 in the TFTU

Ezekiel 18 in the TGNTATF3T

Ezekiel 18 in the THAI

Ezekiel 18 in the TNFD

Ezekiel 18 in the TNT

Ezekiel 18 in the TNTIK

Ezekiel 18 in the TNTIL

Ezekiel 18 in the TNTIN

Ezekiel 18 in the TNTIP

Ezekiel 18 in the TNTIZ

Ezekiel 18 in the TOMA

Ezekiel 18 in the TTENT

Ezekiel 18 in the UBG

Ezekiel 18 in the UGV

Ezekiel 18 in the UGV2

Ezekiel 18 in the UGV3

Ezekiel 18 in the VBL

Ezekiel 18 in the VDCC

Ezekiel 18 in the YALU

Ezekiel 18 in the YAPE

Ezekiel 18 in the YBVTP

Ezekiel 18 in the ZBP