Ezekiel 23 (BOGWICC)

1 Yehova anandiyankhula nati: 2 “Iwe mwana wa munthu, panali atsikana awiri ana a mayi mmodzi. 3 Iwo ankachita za chiwerewere ku Igupto. Za chiwerewerezo anayamba ali achichepere. Kumeneko anthu ankangowasisita pa chifuwa ndi kuwagwiragwira mawere awo aja. 4 Wamkulu dzina lake anali Ohola, ndipo mngʼono wakeyo anali Oholiba. Ine ndinawakwatira ndipo anabereka ana aamuna ndi ana aakazi. Ohola ndiye Samariya, ndipo Yerusalemu ndiye Oholiba. 5 “Ohola anachita zachiwerewere ngakhale anali mkazi wanga; ndipo iye anakangamira abwenzi ake a ku Asiriya. 6 Amenewo anali asilikali ovala zibakuwa zamlangali, abwanamkubwa ndiponso atsogoleri a nkhondo. Onsewo anali anyamata osiririka ndipo ankakwera pa akavalo. 7 Ohola anachita zachiwerewere ndi onsewa, anthu otchuka a ku Asiriya. Iye anadziyipitsa ndi mafano a munthu aliyense amene anagona naye. 8 Iye sanaleke za chiwerewere zimene anaziphunzira ku Igupto. Paja akanali mtsikana anyamata ankagona naye. Iwo ankamusisita mawere akanali anthete nachita naye zachiwerewere. 9 “Nʼchifukwa chake Ine ndinamupereka kwa achikondi ake, Asiriya, amene iye ankawalakalaka. 10 Iwowa anamuvula, namulanda ana ake aamuna ndi aakazi ndipo anamupha ndi lupanga. Ndipo atalangidwa choncho, iye anasanduka chinthu chonyozeka pakati pa akazi. 11 “Mphwake Oholiba anaona zimenezi natengerako. Koma iye anachita zachiwerewere kuposa mkulu wake. 12 Iyenso anakangamira Asiriya, abwanamkubwa, olamulira asilikali, ankhondo ovala zovala zonse za nkhondo ndi okwera pa akavalo. Onsewa anali anyamata osiririka. 13 Ndinaona kuti iyenso anadziyipitsa; ndipo onse awiriwo anatsata njira imodzi. 14 “Koma Oholiba uja anachita chigololo kopitirira mkulu wake. Iye anaona zithunzi za amuna pa khoma, zithunzi za Ababuloni zolembedwa ndi inki yofiira, 15 atamanga malamba mʼchiwuno mwawo ndi kuvala nduwira pa mitu yawo. Onse amaoneka ngati atsogoleri a magaleta a Ababuloni, mbadwa za ku Kaldeya. 16 Oholiba atangowaona, anawalakalaka ndipo anatuma amithenga ku Kaldeya kukawayitana. 17 Ndipo Ababuloni anabwera nʼkudzagona naye. Choncho mwa chilakolako chawo anamuyipitsa. Koma atamuyipitsa choncho, iye ananyansidwa nawo. 18 Iye atachita chiwerewere chake poyera ndi kuonetsa umaliseche wake, Ine ndinamuchokera monyansidwa monga mmene ndinachitira ndi mʼbale wake. 19 Koma anachitabe zachiwerewere osalekeza. Ankakumbukira masiku a ubwana wake pamene ankachita za chiwerewere mʼdziko la Igupto. 20 Kumeneko iye ankalakalaka zibwenzi zake, amene ziwalo zawo zinali ngati za abulu ndipo kutentha kwawo kunali ngati kwa akavalo. 21 Motero, iwe Oholiba unafuna kuchitanso zadama monga unkachitira ku Igupto pamene unali mtsikana. Nthawi imene ija ankakusisita pa chifuwa ndi kugwiragwira mawere ako osagwa aja. 22 “Tsono iwe Oholiba, Ine Ambuye Yehova ndikuti: Ndidzakudzutsira zibwenzi zako zimene unkanyansidwa nazo zija kuti zilimbane nawe. Ndidzaziyitana kuti zibwere kuchokera mbali zonse. 23 Ndidzayitana anthu a ku Babuloni ndi Akaldeya onse, anthu a ku Pekodi, Sowa ndi Kowa pamodzi ndi Asiriya onse. Onsewa ndi amuna osiririka, abwanamkubwa, atsogoleri a ankhondo, oyenda pa magaleta, anthu a maudindo akuluakulu. Onsewa ndi okwera akavalo. 24 Iwo adzabwera kudzalimbana nawe ndi zida za nkhondo, magaleta ndi ngolo, pamodzi ndi anthu ambiri. Adzakuzinga mbali zonse atavala zishango zankhondo ndi zipewa zankhondo. Ndidzakupereka kwa iwo kuti akulange ndipo adzakulanga monga momwe adzafunire. 25 Ndidzaonetsa mkwiyo wanga pa iwe ndipo iwo adzakulanga iwe mwankhanza. Adzadula mphuno zanu ndi makutu anu, ndipo amene adzatsalira mwa iwe adzaphedwa ndi lupanga. Iwo adzakulanda ana ako aamuna ndi aakazi ndipo amene adzatsalira adzaphedwa ndi moto. 26 Adzakuvulaninso zovala zanu ndikukulandani zodzikongoletsera zanu zamtengowapatali. 27 Motero ndidzathetsa zonyansa zako ndi zachigololo zomwe unaziyamba ku Igupto. Choncho sudzalakalaka za ku Igupto kapena kuzikumbukiranso. 28 “Ine Ambuye Yehova ndikuti: Ndikukupereka mʼmanja mwa amene amadana nawe, kwa iwo amene unawafulatira moyipidwa nawo. 29 Adzachita nawe mwachidani. Adzakulanda zonse zimene unagwirira ntchito. Adzakusiya wamaliseche ndiponso wausiwa. Kuyipa kwa makhalidwe ako achiwerewere kudzakhala pammbalambanda. Zonyansa zako ndi chiwerewere chako, 30 zabweretsa izi pa iwe chifukwa unachita zonyansa ndi anthu a mitundu ndi kudziyipitsa ndi mafano awo. 31 Unatsata zochita za mkulu wako; choncho Ine ndidzayika chikho cha chilango chake mʼdzanja lako. 32 “Ine Ambuye Yehova ndikuti:“Udzamwera chikho cha mkulu wako,chikho chachikulu ndi chakuya;anthu adzakuseka ndi kukunyoza,pakuti chikhocho ndi chodzaza kwambiri. 33 Udzaledzera ndipo mtima wako udzadzaza ndi chisoni.Chimenechi ndi chikho chachiwonongeko ndi chipasupasu,chikho cha mkulu wako Samariya. 34 Udzamwa chikhocho mpaka kugugudiza.Tsono udzaphwanyaphwanya chikhochondipo udzangʼamba mawere ako ndi zigoba zake.Ine ndayankhula, akutero Ambuye Yehova. 35 “Chifukwa chake, Ine Ambuye Yehova ndikuti: Popeza wandiyiwala Ine ndi kundifulatira, chomwecho uyenera kulangidwa chifukwa cha zonyansa zako ndi chiwerewere chako.” 36 Yehova anandifunsa kuti, “Iwe mwana wa munthu, kodi udzaweruza Ohola ndi Oholiba? Tsono uwayimbe mlandu chifukwa cha machitidwe awo onyansa. 37 Iwo achita chigololo ndipo anapha anthu. Anachita chigololo popembedza mafano awo. Ngakhale ana amene anandiberekera Ine anawapereka kwa mafanowo ngati chakudya chawo. 38 Anachitanso izi: Iwo anayipitsa malo anga opatulika ndi kudetsa masabata anga. 39 Atapereka ana awo kwa mafano, tsiku lomwelo anakalowanso mʼNyumba yanga yopatulika ndi kuyipitsamo. Izi ndi zimene anachita mʼNyumba mwanga. 40 “Iwo anatuma amithenga kukayitana amuna a ku mayiko akutali. Anthuwo atabwera, abale awiri aja anasambasamba, kudzola utoto wodzikometsera kumaso, kenaka ndi kuvala zovala zamakaka. 41 Anakhala pa bedi lokongola ndipo patsogolo pawo panali tebulo pamene munayikapo lubani ndi mafuta. Zonse zowapatsa Ine. 42 “Mfuwu wa chigulu cha anthu unamveka. Anthu oledzera ochokera ku chipululu anabwera pamodzi ndi anthu wamba ndipo anaveka akaziwo zibangiri kumanja ndi zipewa zaufumu zokongola ku mutu. 43 Ndipo ine ndinati za mkazi wotheratu ndi chigololoyo, ‘Tsono asiyeni kuti achite naye monga wachiwerewere, pakuti ichi ndi chimene iye ali basi.’ 44 Tsono anapita kwa iwo monga mmene anthu amapitira kwa mkazi wadama. Momwemo anapita kwa Ohola ndi kwa Oholiba kukachita nawo zadama. 45 Koma anthu olungama adzawazenga anthuwa mlandu wa chigololo ndi wa kupha anthu. Ndi iwodi anthu achigololo ndiponso mʼmanja mwawo muli magazi. 46 “Ambuye Yehova akuti: Itanitsani chigulu cha anthu kuti chidzawalange ndi kulanda chuma chawo. 47 Anthuwo adzawaponye miyala akazi awiriwo ndi kuwatema ndi malupanga awo. Ana awo aamuna ndi aakazi adzawaphe ndi kutentha nyumba zawo. 48 “Motero Ine ndidzathetsa zachigololo mʼdzikomo, ndipo akazi onse adzatengapo phunziro kuti asadzachite zachigololo monga za iwowo. 49 Ndidzawalanga chifukwa cha ntchito zawo za dama ndipo adzazunzika chifukwa cha tchimo lawo lopembedza mafano. Choncho adzadziwa kuti Ine ndine Ambuye Yehova.”

In Other Versions

Ezekiel 23 in the ANGEFD

Ezekiel 23 in the ANTPNG2D

Ezekiel 23 in the AS21

Ezekiel 23 in the BAGH

Ezekiel 23 in the BBPNG

Ezekiel 23 in the BBT1E

Ezekiel 23 in the BDS

Ezekiel 23 in the BEV

Ezekiel 23 in the BHAD

Ezekiel 23 in the BIB

Ezekiel 23 in the BLPT

Ezekiel 23 in the BNT

Ezekiel 23 in the BNTABOOT

Ezekiel 23 in the BNTLV

Ezekiel 23 in the BOATCB

Ezekiel 23 in the BOATCB2

Ezekiel 23 in the BOBCV

Ezekiel 23 in the BOCNT

Ezekiel 23 in the BOECS

Ezekiel 23 in the BOHCB

Ezekiel 23 in the BOHCV

Ezekiel 23 in the BOHLNT

Ezekiel 23 in the BOHNTLTAL

Ezekiel 23 in the BOICB

Ezekiel 23 in the BOILNTAP

Ezekiel 23 in the BOITCV

Ezekiel 23 in the BOKCV

Ezekiel 23 in the BOKCV2

Ezekiel 23 in the BOKHWOG

Ezekiel 23 in the BOKSSV

Ezekiel 23 in the BOLCB

Ezekiel 23 in the BOLCB2

Ezekiel 23 in the BOMCV

Ezekiel 23 in the BONAV

Ezekiel 23 in the BONCB

Ezekiel 23 in the BONLT

Ezekiel 23 in the BONUT2

Ezekiel 23 in the BOPLNT

Ezekiel 23 in the BOSCB

Ezekiel 23 in the BOSNC

Ezekiel 23 in the BOTLNT

Ezekiel 23 in the BOVCB

Ezekiel 23 in the BOYCB

Ezekiel 23 in the BPBB

Ezekiel 23 in the BPH

Ezekiel 23 in the BSB

Ezekiel 23 in the CCB

Ezekiel 23 in the CUV

Ezekiel 23 in the CUVS

Ezekiel 23 in the DBT

Ezekiel 23 in the DGDNT

Ezekiel 23 in the DHNT

Ezekiel 23 in the DNT

Ezekiel 23 in the ELBE

Ezekiel 23 in the EMTV

Ezekiel 23 in the ESV

Ezekiel 23 in the FBV

Ezekiel 23 in the FEB

Ezekiel 23 in the GGMNT

Ezekiel 23 in the GNT

Ezekiel 23 in the HARY

Ezekiel 23 in the HNT

Ezekiel 23 in the IRVA

Ezekiel 23 in the IRVB

Ezekiel 23 in the IRVG

Ezekiel 23 in the IRVH

Ezekiel 23 in the IRVK

Ezekiel 23 in the IRVM

Ezekiel 23 in the IRVM2

Ezekiel 23 in the IRVO

Ezekiel 23 in the IRVP

Ezekiel 23 in the IRVT

Ezekiel 23 in the IRVT2

Ezekiel 23 in the IRVU

Ezekiel 23 in the ISVN

Ezekiel 23 in the JSNT

Ezekiel 23 in the KAPI

Ezekiel 23 in the KBT1ETNIK

Ezekiel 23 in the KBV

Ezekiel 23 in the KJV

Ezekiel 23 in the KNFD

Ezekiel 23 in the LBA

Ezekiel 23 in the LBLA

Ezekiel 23 in the LNT

Ezekiel 23 in the LSV

Ezekiel 23 in the MAAL

Ezekiel 23 in the MBV

Ezekiel 23 in the MBV2

Ezekiel 23 in the MHNT

Ezekiel 23 in the MKNFD

Ezekiel 23 in the MNG

Ezekiel 23 in the MNT

Ezekiel 23 in the MNT2

Ezekiel 23 in the MRS1T

Ezekiel 23 in the NAA

Ezekiel 23 in the NASB

Ezekiel 23 in the NBLA

Ezekiel 23 in the NBS

Ezekiel 23 in the NBVTP

Ezekiel 23 in the NET2

Ezekiel 23 in the NIV11

Ezekiel 23 in the NNT

Ezekiel 23 in the NNT2

Ezekiel 23 in the NNT3

Ezekiel 23 in the PDDPT

Ezekiel 23 in the PFNT

Ezekiel 23 in the RMNT

Ezekiel 23 in the SBIAS

Ezekiel 23 in the SBIBS

Ezekiel 23 in the SBIBS2

Ezekiel 23 in the SBICS

Ezekiel 23 in the SBIDS

Ezekiel 23 in the SBIGS

Ezekiel 23 in the SBIHS

Ezekiel 23 in the SBIIS

Ezekiel 23 in the SBIIS2

Ezekiel 23 in the SBIIS3

Ezekiel 23 in the SBIKS

Ezekiel 23 in the SBIKS2

Ezekiel 23 in the SBIMS

Ezekiel 23 in the SBIOS

Ezekiel 23 in the SBIPS

Ezekiel 23 in the SBISS

Ezekiel 23 in the SBITS

Ezekiel 23 in the SBITS2

Ezekiel 23 in the SBITS3

Ezekiel 23 in the SBITS4

Ezekiel 23 in the SBIUS

Ezekiel 23 in the SBIVS

Ezekiel 23 in the SBT

Ezekiel 23 in the SBT1E

Ezekiel 23 in the SCHL

Ezekiel 23 in the SNT

Ezekiel 23 in the SUSU

Ezekiel 23 in the SUSU2

Ezekiel 23 in the SYNO

Ezekiel 23 in the TBIAOTANT

Ezekiel 23 in the TBT1E

Ezekiel 23 in the TBT1E2

Ezekiel 23 in the TFTIP

Ezekiel 23 in the TFTU

Ezekiel 23 in the TGNTATF3T

Ezekiel 23 in the THAI

Ezekiel 23 in the TNFD

Ezekiel 23 in the TNT

Ezekiel 23 in the TNTIK

Ezekiel 23 in the TNTIL

Ezekiel 23 in the TNTIN

Ezekiel 23 in the TNTIP

Ezekiel 23 in the TNTIZ

Ezekiel 23 in the TOMA

Ezekiel 23 in the TTENT

Ezekiel 23 in the UBG

Ezekiel 23 in the UGV

Ezekiel 23 in the UGV2

Ezekiel 23 in the UGV3

Ezekiel 23 in the VBL

Ezekiel 23 in the VDCC

Ezekiel 23 in the YALU

Ezekiel 23 in the YAPE

Ezekiel 23 in the YBVTP

Ezekiel 23 in the ZBP