Ezekiel 4 (BOGWICC)
1 Mulungu anati, “Iwe mwana wa munthu, tsopano tenga njerwa, uliyike pamaso pako ndipo ujambulepo chithunzi cha mzinda wa Yerusalemu. 2 Ndipo uwuzinge mzindawo motere: uwumangire nsanja zowuzinga, uwumbire mitumbira ya nkhondo, uwumangire misasa ya nkhondo ndipo uyike zida zogumulira kuzungulira mzindawo. 3 Kenaka utenge chiwaya chachitsulo uchiyike ngati khoma lachitsulo pakati pa iwe ndi mzindawo. Uyangʼanitsitse mzindawo ndipo udzakhala wozingidwa ndi nsanja za nkhondo. Choncho umangire nsanja zankhondo. Chimenechi chidzakhala chizindikiro kwa Aisraeli. 4 “Tsono iwe ugonere kumanzere kwako ndipo ndidzayika pa iwe tchimo la Aisraeli. Iwe udzasenza tchimolo masiku onse amene udzagonere mbali imeneyo. 5 Ine ndakuyikira masiku okwana 390 malingana ndi zaka za machimo awo. Umu ndi mmene udzasenzere machimo a Aisraeli. 6 “Utatha zimenezo udzagonerenso mbali ya kudzanja lamanja, ndipo udzasenza machimo a anthu a ku Yuda masiku makumi anayi, tsiku lililonse kuyimira chaka chimodzi. 7 Tsono udzayangʼanitsitse nsanja za nkhondo zozinga. Dzanja la mkanjo wako utalikwinya ndi dzanja lako utakweza, udzalosere modzudzula Yerusalemu. 8 Ine ndidzakumanga ndi zingwe kotero kuti sudzatha kutembenukira uku ndi uku mpaka utatsiriza masiku akuzingidwa ako. 9 “Tsono tenga tirigu ndi barele, nyemba ndi mphodza, mapira ndi mchewere; ndipo uyike zonsezi mʼmbale imodzi ndipo upange buledi wako. Uzidya pa masiku 390 amene udzakhala ukugonera mbali imodzi. 10 Uyeze theka la kilogalamu la chakudyacho kuti uzidya tsiku lililonse kamodzi kokha. 11 Uyezenso zikho ziwiri zamadzi ndipo uzimwa tsiku ndi tsiku. 12 Uzidya chakudya chako ngati momwe amadyera keke ya barele. Uzidzaphika chakudyacho anthu akuona pogwiritsa ntchito ndowe ya munthu ngati nkhuni.” 13 Yehova anati, “Chimodzimodzi anthu a Israeli adzadya chakudya chodetsedwa ku mayiko achilendo kumene Ine ndidzawapirikitsira.” 14 Koma ine ndinati, “Zisatero, Ambuye Yehova! Ine sindinadziyipitsepo pa zachipembedzo. Kuyambira ubwana wanga mpaka tsopano, sindinadyepo kanthu kalikonse kopezeka katafa kapena kophedwa ndi zirombo za kutchire. Palibe nyama yodetsedwa pa zachipembedzo imene inalowa pakamwa panga.” 15 Iye anati, “Chabwino, ndidzakulola kuti uphike buledi wako ndi ndowe za ngʼombe mʼmalo mwa ndowe za munthu.” 16 Pambuyo pake anandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, anthu a ku Yerusalemu ndidzawachepetsera chakudya. Anthuwo adzadya chakudya chochita kuyeza ndipo azidzadya mwa nkhawa. Azidzamwanso madzi ochita kuyeza ndiponso mwa mantha. 17 Ndidzachita zimenezi kuti adzasowe chakudya ndi madzi. Choncho adzachita nkhawa akumapenyana ndipo adzatheratu ndi kuwonda chifukwa cha machimo awo.”
In Other Versions
Ezekiel 4 in the ANGEFD
Ezekiel 4 in the ANTPNG2D
Ezekiel 4 in the AS21
Ezekiel 4 in the BAGH
Ezekiel 4 in the BBPNG
Ezekiel 4 in the BBT1E
Ezekiel 4 in the BDS
Ezekiel 4 in the BEV
Ezekiel 4 in the BHAD
Ezekiel 4 in the BIB
Ezekiel 4 in the BLPT
Ezekiel 4 in the BNT
Ezekiel 4 in the BNTABOOT
Ezekiel 4 in the BNTLV
Ezekiel 4 in the BOATCB
Ezekiel 4 in the BOATCB2
Ezekiel 4 in the BOBCV
Ezekiel 4 in the BOCNT
Ezekiel 4 in the BOECS
Ezekiel 4 in the BOHCB
Ezekiel 4 in the BOHCV
Ezekiel 4 in the BOHLNT
Ezekiel 4 in the BOHNTLTAL
Ezekiel 4 in the BOICB
Ezekiel 4 in the BOILNTAP
Ezekiel 4 in the BOITCV
Ezekiel 4 in the BOKCV
Ezekiel 4 in the BOKCV2
Ezekiel 4 in the BOKHWOG
Ezekiel 4 in the BOKSSV
Ezekiel 4 in the BOLCB
Ezekiel 4 in the BOLCB2
Ezekiel 4 in the BOMCV
Ezekiel 4 in the BONAV
Ezekiel 4 in the BONCB
Ezekiel 4 in the BONLT
Ezekiel 4 in the BONUT2
Ezekiel 4 in the BOPLNT
Ezekiel 4 in the BOSCB
Ezekiel 4 in the BOSNC
Ezekiel 4 in the BOTLNT
Ezekiel 4 in the BOVCB
Ezekiel 4 in the BOYCB
Ezekiel 4 in the BPBB
Ezekiel 4 in the BPH
Ezekiel 4 in the BSB
Ezekiel 4 in the CCB
Ezekiel 4 in the CUV
Ezekiel 4 in the CUVS
Ezekiel 4 in the DBT
Ezekiel 4 in the DGDNT
Ezekiel 4 in the DHNT
Ezekiel 4 in the DNT
Ezekiel 4 in the ELBE
Ezekiel 4 in the EMTV
Ezekiel 4 in the ESV
Ezekiel 4 in the FBV
Ezekiel 4 in the FEB
Ezekiel 4 in the GGMNT
Ezekiel 4 in the GNT
Ezekiel 4 in the HARY
Ezekiel 4 in the HNT
Ezekiel 4 in the IRVA
Ezekiel 4 in the IRVB
Ezekiel 4 in the IRVG
Ezekiel 4 in the IRVH
Ezekiel 4 in the IRVK
Ezekiel 4 in the IRVM
Ezekiel 4 in the IRVM2
Ezekiel 4 in the IRVO
Ezekiel 4 in the IRVP
Ezekiel 4 in the IRVT
Ezekiel 4 in the IRVT2
Ezekiel 4 in the IRVU
Ezekiel 4 in the ISVN
Ezekiel 4 in the JSNT
Ezekiel 4 in the KAPI
Ezekiel 4 in the KBT1ETNIK
Ezekiel 4 in the KBV
Ezekiel 4 in the KJV
Ezekiel 4 in the KNFD
Ezekiel 4 in the LBA
Ezekiel 4 in the LBLA
Ezekiel 4 in the LNT
Ezekiel 4 in the LSV
Ezekiel 4 in the MAAL
Ezekiel 4 in the MBV
Ezekiel 4 in the MBV2
Ezekiel 4 in the MHNT
Ezekiel 4 in the MKNFD
Ezekiel 4 in the MNG
Ezekiel 4 in the MNT
Ezekiel 4 in the MNT2
Ezekiel 4 in the MRS1T
Ezekiel 4 in the NAA
Ezekiel 4 in the NASB
Ezekiel 4 in the NBLA
Ezekiel 4 in the NBS
Ezekiel 4 in the NBVTP
Ezekiel 4 in the NET2
Ezekiel 4 in the NIV11
Ezekiel 4 in the NNT
Ezekiel 4 in the NNT2
Ezekiel 4 in the NNT3
Ezekiel 4 in the PDDPT
Ezekiel 4 in the PFNT
Ezekiel 4 in the RMNT
Ezekiel 4 in the SBIAS
Ezekiel 4 in the SBIBS
Ezekiel 4 in the SBIBS2
Ezekiel 4 in the SBICS
Ezekiel 4 in the SBIDS
Ezekiel 4 in the SBIGS
Ezekiel 4 in the SBIHS
Ezekiel 4 in the SBIIS
Ezekiel 4 in the SBIIS2
Ezekiel 4 in the SBIIS3
Ezekiel 4 in the SBIKS
Ezekiel 4 in the SBIKS2
Ezekiel 4 in the SBIMS
Ezekiel 4 in the SBIOS
Ezekiel 4 in the SBIPS
Ezekiel 4 in the SBISS
Ezekiel 4 in the SBITS
Ezekiel 4 in the SBITS2
Ezekiel 4 in the SBITS3
Ezekiel 4 in the SBITS4
Ezekiel 4 in the SBIUS
Ezekiel 4 in the SBIVS
Ezekiel 4 in the SBT
Ezekiel 4 in the SBT1E
Ezekiel 4 in the SCHL
Ezekiel 4 in the SNT
Ezekiel 4 in the SUSU
Ezekiel 4 in the SUSU2
Ezekiel 4 in the SYNO
Ezekiel 4 in the TBIAOTANT
Ezekiel 4 in the TBT1E
Ezekiel 4 in the TBT1E2
Ezekiel 4 in the TFTIP
Ezekiel 4 in the TFTU
Ezekiel 4 in the TGNTATF3T
Ezekiel 4 in the THAI
Ezekiel 4 in the TNFD
Ezekiel 4 in the TNT
Ezekiel 4 in the TNTIK
Ezekiel 4 in the TNTIL
Ezekiel 4 in the TNTIN
Ezekiel 4 in the TNTIP
Ezekiel 4 in the TNTIZ
Ezekiel 4 in the TOMA
Ezekiel 4 in the TTENT
Ezekiel 4 in the UBG
Ezekiel 4 in the UGV
Ezekiel 4 in the UGV2
Ezekiel 4 in the UGV3
Ezekiel 4 in the VBL
Ezekiel 4 in the VDCC
Ezekiel 4 in the YALU
Ezekiel 4 in the YAPE
Ezekiel 4 in the YBVTP
Ezekiel 4 in the ZBP