Ezra 4 (BOGWICC)

1 Adani a Yuda ndi Benjamini anamva kuti anthu obwera ku ukapolo aja akumangira Nyumba Yehova, Mulungu wa Israeli. 2 Tsono anapita kwa Zerubabeli ndi kwa atsogoleri a mabanja awo ndi kunena kuti, “Mutilole kuti tikuthandizeni kumangaku chifukwa ife timapembedza Mulungu wanu monga momwe mumachitira inu, ndipo takhala tikupereka nsembe kwa Iye kuyambira nthawi ya Esrahadoni, mfumu ya ku Asiriya, amene anabwera nafe kuno.” 3 Koma Zerubabeli, Yesuwa ndi atsogoleri ena otsala a mabanja a Aisraeli anayankha kuti, “Inu simungatithandize kumangira Nyumba Yehova, Mulungu wathu. Tokha tidzamumangira Nyumba Yehova, Mulungu wa Aisraeli, monga mfumu Koresi, mfumu ya Perisiya inatilamulira.” 4 Tsono anthu a mʼdzikomo anayamba kuchititsa ulesi anthu a ku Yuda, ndi kuwachititsa mantha kuti aleke ntchito yomangayo. 5 Analemba alangizi ena kuti alepheretse cholinga chawo pa ntchitoyo pa nthawi yonse ya Koresi, mfumu ya ku Perisiya, ndiponso mpaka pamene Dariyo mfumu ya ku Perisiya ankalamulira dzikolo. 6 Mfumu Ahasiwero atangoyamba kulamulira dzikolo, adani aja analemba kalata yoneneza anthu a Yuda ndi Yerusalemu. 7 Ndiponso mʼnthawi ya Aritasasita mfumu ya Perisiya, Bisilamu, Mitiredati, Tabeeli ndi anzawo ena analemba kalata inanso kwa Aritasasita. Kalatayo inalembedwa mʼChiaramu ndipo ankatanthauzira poyiwerenga. 8 Rehumu mkulu wankhondo ndi Simisai mlembi, nawonso analemba kalata yawo yoneneza anthu a ku Yerusalemu kwa mfumu Aritasasita. Anayilemba motere: 9 Kalata yochokera kwa Rehumu, mkulu wa gulu lankhondo, mlembi Simisai ndi anzawo awa: oweruza, nduna, akuluakulu ena, anthu a ku Peresiya, Ereki, Babuloni, Susa mʼdziko la Elamu, 10 ndi mitundu ina imene mkulu wolemekezeka, Osanipara anayisamutsa ndi kuyikhazika mʼmizinda ya Samariya ndi mʼmadera ena apatsidya la Yufurate. 11 Mawu a mʼkalata ya kwa Aritasasita anali awa:Kwa mfumu Aritasasita:Kuchokera kwa atumiki anu, anthu a kutsidya kwa Yufurate: 12 Amfumu tati mudziwe kuti Ayuda amene anabwera kuno kuchokera kwanuko apita ku Yerusalemu ndipo akumanganso mzinda wa anthu owukira ndi oyipa uja. Akumaliza makoma ake ndipo akukonzanso maziko. 13 Kuwonjeza apo amfumu mudziwe kuti ngati amalize kumanganso mzindawu ndi kukonzanso makoma ake, adzaleka kukhoma msonkho, kulipira ndalama zakatundu olowa mʼdziko kapena msonkho wina uliwonse, ndipo chuma cha thumba la ufumu chidzachepa. 14 Popeza tsono ife timadya nawo kwa mfumu sitiyenera tizingoonerera zinthu zochititsa mfumu manyazi. Nʼchifukwa chake tikutumiza uthenga kwa inu a mfumu kuti mudziwe zonse. 15 Choncho pachitike kafukufuku mʼbuku la mbiri yakale ya makolo anu. Mʼbuku la mbiri zakale mudzapezamo ndi kuwerenga kuti mzinda umenewu ndi waupandu, wosautsa mafumu ndi nduna zamʼmadera zomwe. Kuyambira kale wakhala ukuwukira ulamuliro uliwonse. Nʼchifukwa chake mzinda umenewu anawuwononga. 16 Tsono tikukudziwitsani amfumu kuti ngati mzinda umenewu umangidwanso ndi makoma ake nʼkutsirizidwanso ndiye kuti inu simudzalamuliranso chigawo cha patsidya pa Yufurate. 17 Mfumu inatumiza yankho ili:Mkulu wa gulu lankhondo Rehumu, mlembi Simisai ndi anzanu onse amene akukhala ku Samariya ndi mʼzigawo zina zonse za Patsidya pa Yufurate.Landirani moni. 18 Kalata imene munatumiza ija yawerengedwa bwino lomwe pamaso panga. 19 Ine nditalamula kuti afufuze nkhaniyi kwapezekadi kuti mzinda umenewu uli ndi mbiri yowukira mafumu ndi kuti zaupandu ndi zowukira zinkachitikadi mʼmenemo. 20 Mafumu amphamvu akhala akulamulira Yerusalemu ndi chigawo chonse cha Patsidya pa Yufurate. Iwo ankalandira msonkho ndi kulipira ndalama zakatundu olowa mʼdziko pa kanthu kena kalikonse. 21 Tsopano inu khazikitsani lamulo kuti anthu amenewo asiye ntchitoyo, asamangenso mzindawo mpaka ine nditalamula 22 Musachedwe kuchita zimenezi. Kodi ine ndingalole bwanji kuti zowononga zotere zikule ndi kupweteka ine mfumu? 23 Kalata ya mfumu Aritasasitayi itangowerengedwa pamaso pa Rehumu ndi Simisai mlembi uja, ndi anzawo onse, iwo anapita msangamsanga ku Yerusalemu kukawaletsa Ayuda aja mwamphamvu kuti asapitirire ntchito yawo. 24 Motero ntchito yomanga Nyumba ya Mulungu ku Yerusalemu inayimitsidwa mpaka chaka cha chiwiri cha ulamuliro wa Dariyo mfumu ya ku Perisiya.

In Other Versions

Ezra 4 in the ANGEFD

Ezra 4 in the ANTPNG2D

Ezra 4 in the AS21

Ezra 4 in the BAGH

Ezra 4 in the BBPNG

Ezra 4 in the BBT1E

Ezra 4 in the BDS

Ezra 4 in the BEV

Ezra 4 in the BHAD

Ezra 4 in the BIB

Ezra 4 in the BLPT

Ezra 4 in the BNT

Ezra 4 in the BNTABOOT

Ezra 4 in the BNTLV

Ezra 4 in the BOATCB

Ezra 4 in the BOATCB2

Ezra 4 in the BOBCV

Ezra 4 in the BOCNT

Ezra 4 in the BOECS

Ezra 4 in the BOHCB

Ezra 4 in the BOHCV

Ezra 4 in the BOHLNT

Ezra 4 in the BOHNTLTAL

Ezra 4 in the BOICB

Ezra 4 in the BOILNTAP

Ezra 4 in the BOITCV

Ezra 4 in the BOKCV

Ezra 4 in the BOKCV2

Ezra 4 in the BOKHWOG

Ezra 4 in the BOKSSV

Ezra 4 in the BOLCB

Ezra 4 in the BOLCB2

Ezra 4 in the BOMCV

Ezra 4 in the BONAV

Ezra 4 in the BONCB

Ezra 4 in the BONLT

Ezra 4 in the BONUT2

Ezra 4 in the BOPLNT

Ezra 4 in the BOSCB

Ezra 4 in the BOSNC

Ezra 4 in the BOTLNT

Ezra 4 in the BOVCB

Ezra 4 in the BOYCB

Ezra 4 in the BPBB

Ezra 4 in the BPH

Ezra 4 in the BSB

Ezra 4 in the CCB

Ezra 4 in the CUV

Ezra 4 in the CUVS

Ezra 4 in the DBT

Ezra 4 in the DGDNT

Ezra 4 in the DHNT

Ezra 4 in the DNT

Ezra 4 in the ELBE

Ezra 4 in the EMTV

Ezra 4 in the ESV

Ezra 4 in the FBV

Ezra 4 in the FEB

Ezra 4 in the GGMNT

Ezra 4 in the GNT

Ezra 4 in the HARY

Ezra 4 in the HNT

Ezra 4 in the IRVA

Ezra 4 in the IRVB

Ezra 4 in the IRVG

Ezra 4 in the IRVH

Ezra 4 in the IRVK

Ezra 4 in the IRVM

Ezra 4 in the IRVM2

Ezra 4 in the IRVO

Ezra 4 in the IRVP

Ezra 4 in the IRVT

Ezra 4 in the IRVT2

Ezra 4 in the IRVU

Ezra 4 in the ISVN

Ezra 4 in the JSNT

Ezra 4 in the KAPI

Ezra 4 in the KBT1ETNIK

Ezra 4 in the KBV

Ezra 4 in the KJV

Ezra 4 in the KNFD

Ezra 4 in the LBA

Ezra 4 in the LBLA

Ezra 4 in the LNT

Ezra 4 in the LSV

Ezra 4 in the MAAL

Ezra 4 in the MBV

Ezra 4 in the MBV2

Ezra 4 in the MHNT

Ezra 4 in the MKNFD

Ezra 4 in the MNG

Ezra 4 in the MNT

Ezra 4 in the MNT2

Ezra 4 in the MRS1T

Ezra 4 in the NAA

Ezra 4 in the NASB

Ezra 4 in the NBLA

Ezra 4 in the NBS

Ezra 4 in the NBVTP

Ezra 4 in the NET2

Ezra 4 in the NIV11

Ezra 4 in the NNT

Ezra 4 in the NNT2

Ezra 4 in the NNT3

Ezra 4 in the PDDPT

Ezra 4 in the PFNT

Ezra 4 in the RMNT

Ezra 4 in the SBIAS

Ezra 4 in the SBIBS

Ezra 4 in the SBIBS2

Ezra 4 in the SBICS

Ezra 4 in the SBIDS

Ezra 4 in the SBIGS

Ezra 4 in the SBIHS

Ezra 4 in the SBIIS

Ezra 4 in the SBIIS2

Ezra 4 in the SBIIS3

Ezra 4 in the SBIKS

Ezra 4 in the SBIKS2

Ezra 4 in the SBIMS

Ezra 4 in the SBIOS

Ezra 4 in the SBIPS

Ezra 4 in the SBISS

Ezra 4 in the SBITS

Ezra 4 in the SBITS2

Ezra 4 in the SBITS3

Ezra 4 in the SBITS4

Ezra 4 in the SBIUS

Ezra 4 in the SBIVS

Ezra 4 in the SBT

Ezra 4 in the SBT1E

Ezra 4 in the SCHL

Ezra 4 in the SNT

Ezra 4 in the SUSU

Ezra 4 in the SUSU2

Ezra 4 in the SYNO

Ezra 4 in the TBIAOTANT

Ezra 4 in the TBT1E

Ezra 4 in the TBT1E2

Ezra 4 in the TFTIP

Ezra 4 in the TFTU

Ezra 4 in the TGNTATF3T

Ezra 4 in the THAI

Ezra 4 in the TNFD

Ezra 4 in the TNT

Ezra 4 in the TNTIK

Ezra 4 in the TNTIL

Ezra 4 in the TNTIN

Ezra 4 in the TNTIP

Ezra 4 in the TNTIZ

Ezra 4 in the TOMA

Ezra 4 in the TTENT

Ezra 4 in the UBG

Ezra 4 in the UGV

Ezra 4 in the UGV2

Ezra 4 in the UGV3

Ezra 4 in the VBL

Ezra 4 in the VDCC

Ezra 4 in the YALU

Ezra 4 in the YAPE

Ezra 4 in the YBVTP

Ezra 4 in the ZBP