Genesis 15 (BOGWICC)

1 Zitatha izi, Yehova anayankhula ndi Abramu mʼmasomphenya nati:“Usaope Abramu.Ine ndili ngati chishango chokutchinjiriza.Mphotho yako idzakhala yayikulu.” 2 Koma Abramu anati, “Haa! Ambuye Yehova, mukhoza kundipatsa chiyani popeza ndikanali wopanda mwana ndipo amene adzatenge chuma changa ndi Eliezara wa ku Damasiko? 3 Inu simunandipatse ana kotero kuti wantchito wa ku nyumba kwanga ndiye amene adzalowe mʼmalo mwanga.” 4 Yehova anayankhula naye nati: “Munthu uyu sadzalowa mʼmalo mwako, koma mwana wako weniweni wamwamuna, wobereka wekha ndiye adzalowe mʼmalo mwako.” 5 Yehova anapita naye Abramu panja nati, “Tayangʼana kumwambaku, ndipo chifukwa cha chimenechi uwerenge nyenyezi ngati ungathe kuziwerenga.” Ndipo anamuwuza kuti, “Ndi mmene adzakhalire ana ako ndi zidzukulu zako.” 6 Abramu anakhulupirira Yehova, ndipo ichi chinamuchititsa kukhala wolungama. 7 Ndipo anamuwuza kuti, “Ine ndine Yehova amene ndinakuchotsa iwe ku mzinda wa Uri wa ku Akaldeya kuti ndikupatse dziko ili kuti likhale lako.” 8 Koma Abramu anati, “Haa! Ambuye Yehova, kodi ndingadziwe bwanji kuti lidzakhaladi langa?” 9 Kotero Yehova anati kwa iye, “Kanditengere kamsoti kangʼombe ka zaka zitatu, kamsoti ka mbuzi ka zaka zitatu, ndi nkhosa yayimuna ya zaka zitatu pamodzi ndi nkhunda ndi kamwana ka njiwa.” 10 Abramu anabweretsadi zonsezi nadula chilichonse pakati nʼkuzindandalika, chidutswa chilichonse kuyangʼanana ndi chinzake; koma njiwa ndi nkhunda sanazidule pakati. 11 Pamene miphamba inabwera kuti itole nyama ija, Abramu anayipirikitsa. 12 Pamene dzuwa limalowa Abramu anagona tulo tofa nato ndipo mdima wandiweyani ndi wochititsa mantha unamuphimba. 13 Tsono Yehova anati kwa iye, “Uyenera kudziwa mosakayika kuti zidzukulu zako zidzakhala alendo mʼdziko lachilendo ndipo zidzakhala akapolo ndi kuzunzidwa zaka 400. 14 Koma ndidzalanga dziko limene zidzukulu zako zidzagwireko ukapolo ndipo pambuyo pake iwo adzatulukamo ndi chuma chambiri. 15 Komabe iweyo udzamwalira mu mtendere ndi kuyikidwa mʼmanda utakalamba bwino. 16 Patapita mibado inayi, adzukulu ako adzabwereranso kuno popeza tchimo la Aamori silinafike pachimake kuti alangidwe.” 17 Dzuwa litalowa ndipo mdima utagwa, panaoneka mʼphika wofuka nthunzi ya moto ndi sakali yoyaka ndipo zinadutsa pakati pa zidutswa za nyama zija. 18 Pa tsiku limenelo, Yehova anachita pangano ndi Abramu nati, “Ndikulonjeza kuti ndidzapereka dziko ili kwa zidzukulu zako, kuchokera ku mtsinje wa ku Igupto mpaka ku mtsinje waukulu wa Yufurate. 19 Ndidzakupatsani dziko la Akeni, Akenizi, Akadimoni, 20 Ahiti, Aperezi, Arefaimu, 21 Aamori, Akanaani, Agirigasi ndi Ayebusi.”

In Other Versions

Genesis 15 in the ANGEFD

Genesis 15 in the ANTPNG2D

Genesis 15 in the AS21

Genesis 15 in the BAGH

Genesis 15 in the BBPNG

Genesis 15 in the BBT1E

Genesis 15 in the BDS

Genesis 15 in the BEV

Genesis 15 in the BHAD

Genesis 15 in the BIB

Genesis 15 in the BLPT

Genesis 15 in the BNT

Genesis 15 in the BNTABOOT

Genesis 15 in the BNTLV

Genesis 15 in the BOATCB

Genesis 15 in the BOATCB2

Genesis 15 in the BOBCV

Genesis 15 in the BOCNT

Genesis 15 in the BOECS

Genesis 15 in the BOHCB

Genesis 15 in the BOHCV

Genesis 15 in the BOHLNT

Genesis 15 in the BOHNTLTAL

Genesis 15 in the BOICB

Genesis 15 in the BOILNTAP

Genesis 15 in the BOITCV

Genesis 15 in the BOKCV

Genesis 15 in the BOKCV2

Genesis 15 in the BOKHWOG

Genesis 15 in the BOKSSV

Genesis 15 in the BOLCB

Genesis 15 in the BOLCB2

Genesis 15 in the BOMCV

Genesis 15 in the BONAV

Genesis 15 in the BONCB

Genesis 15 in the BONLT

Genesis 15 in the BONUT2

Genesis 15 in the BOPLNT

Genesis 15 in the BOSCB

Genesis 15 in the BOSNC

Genesis 15 in the BOTLNT

Genesis 15 in the BOVCB

Genesis 15 in the BOYCB

Genesis 15 in the BPBB

Genesis 15 in the BPH

Genesis 15 in the BSB

Genesis 15 in the CCB

Genesis 15 in the CUV

Genesis 15 in the CUVS

Genesis 15 in the DBT

Genesis 15 in the DGDNT

Genesis 15 in the DHNT

Genesis 15 in the DNT

Genesis 15 in the ELBE

Genesis 15 in the EMTV

Genesis 15 in the ESV

Genesis 15 in the FBV

Genesis 15 in the FEB

Genesis 15 in the GGMNT

Genesis 15 in the GNT

Genesis 15 in the HARY

Genesis 15 in the HNT

Genesis 15 in the IRVA

Genesis 15 in the IRVB

Genesis 15 in the IRVG

Genesis 15 in the IRVH

Genesis 15 in the IRVK

Genesis 15 in the IRVM

Genesis 15 in the IRVM2

Genesis 15 in the IRVO

Genesis 15 in the IRVP

Genesis 15 in the IRVT

Genesis 15 in the IRVT2

Genesis 15 in the IRVU

Genesis 15 in the ISVN

Genesis 15 in the JSNT

Genesis 15 in the KAPI

Genesis 15 in the KBT1ETNIK

Genesis 15 in the KBV

Genesis 15 in the KJV

Genesis 15 in the KNFD

Genesis 15 in the LBA

Genesis 15 in the LBLA

Genesis 15 in the LNT

Genesis 15 in the LSV

Genesis 15 in the MAAL

Genesis 15 in the MBV

Genesis 15 in the MBV2

Genesis 15 in the MHNT

Genesis 15 in the MKNFD

Genesis 15 in the MNG

Genesis 15 in the MNT

Genesis 15 in the MNT2

Genesis 15 in the MRS1T

Genesis 15 in the NAA

Genesis 15 in the NASB

Genesis 15 in the NBLA

Genesis 15 in the NBS

Genesis 15 in the NBVTP

Genesis 15 in the NET2

Genesis 15 in the NIV11

Genesis 15 in the NNT

Genesis 15 in the NNT2

Genesis 15 in the NNT3

Genesis 15 in the PDDPT

Genesis 15 in the PFNT

Genesis 15 in the RMNT

Genesis 15 in the SBIAS

Genesis 15 in the SBIBS

Genesis 15 in the SBIBS2

Genesis 15 in the SBICS

Genesis 15 in the SBIDS

Genesis 15 in the SBIGS

Genesis 15 in the SBIHS

Genesis 15 in the SBIIS

Genesis 15 in the SBIIS2

Genesis 15 in the SBIIS3

Genesis 15 in the SBIKS

Genesis 15 in the SBIKS2

Genesis 15 in the SBIMS

Genesis 15 in the SBIOS

Genesis 15 in the SBIPS

Genesis 15 in the SBISS

Genesis 15 in the SBITS

Genesis 15 in the SBITS2

Genesis 15 in the SBITS3

Genesis 15 in the SBITS4

Genesis 15 in the SBIUS

Genesis 15 in the SBIVS

Genesis 15 in the SBT

Genesis 15 in the SBT1E

Genesis 15 in the SCHL

Genesis 15 in the SNT

Genesis 15 in the SUSU

Genesis 15 in the SUSU2

Genesis 15 in the SYNO

Genesis 15 in the TBIAOTANT

Genesis 15 in the TBT1E

Genesis 15 in the TBT1E2

Genesis 15 in the TFTIP

Genesis 15 in the TFTU

Genesis 15 in the TGNTATF3T

Genesis 15 in the THAI

Genesis 15 in the TNFD

Genesis 15 in the TNT

Genesis 15 in the TNTIK

Genesis 15 in the TNTIL

Genesis 15 in the TNTIN

Genesis 15 in the TNTIP

Genesis 15 in the TNTIZ

Genesis 15 in the TOMA

Genesis 15 in the TTENT

Genesis 15 in the UBG

Genesis 15 in the UGV

Genesis 15 in the UGV2

Genesis 15 in the UGV3

Genesis 15 in the VBL

Genesis 15 in the VDCC

Genesis 15 in the YALU

Genesis 15 in the YAPE

Genesis 15 in the YBVTP

Genesis 15 in the ZBP