Genesis 19 (BOGWICC)

1 Angelo awiri aja anafika ku Sodomu madzulo ndipo Loti anali atakhala pansi pa chipata cha mzindawo. Loti atawaona, anayimirira ndi kukakumana nawo ndipo anaweramitsa mutu wake pansi mwaulemu. 2 Iye anati, “Ambuye wanga, chonde patukirani ku nyumba kwa mtumiki wanu. Mukhoza kusambitsa mapazi anu ndi kugona usiku uno kenaka nʼkumapitirira ndi ulendo wanu mmamawa.”Iwo anati, “Ayi, tigona panja.” 3 Koma iye anawawumiriza kwambiri kotero kuti anapita naye pamodzi ku nyumba kwake. Anawakonzera chakudya buledi wopanda yisiti ndipo anadya. 4 Alendo aja asanapite kogona, amuna onse achinyamata ndi achikulire ochokera mbali zonse za mzinda wa Sodomu anazinga nyumba ya Loti. 5 Iwo anayitana Loti namufunsa kuti, “Ali kuti amuna aja amene afika kuno usiku womwe uno? Atulutse, utipatse kuti tigone nawo malo amodzi.” 6 Loti anatuluka panja kukakumana nawo natseka chitseko 7 ndipo anati, “Ayi anzanga, musachite zinthu zoyipa zotere. 8 Taonani, ine ndili ndi ana anga akazi awiri amene sanagonepo ndi mwamuna. Mundilole ndikutulutsireni amenewo ndipo muchite nawo zimene mungafune. Koma musachite chilichonse ndi anthuwa, pakuti iwowa ndi alendo anga ndipo ndiyenera kuwatchinjiriza.” 9 Iwo anayankha kuti, “Tachoka apa tidutse.” Ndipo anati, “Munthu uyu anabwera kuno ngati mlendo chabe, tsono lero akufuna kuti akhale wotiweruza! Tikukhawulitsa kuposa iwowa.” Anapitiriza kumuwumiriza Loti uja nʼkumasunthira kutsogolo kuti athyole chitseko. 10 Koma anthu aja anali mʼkatiwa anasuzumira namukokera Loti uja mʼkati mwa nyumba nʼkutseka chitseko. 11 Kenaka anawachititsa khungu anthu amene anali panja pa nyumba aja, aangʼono ndi aakulu omwe, kuti asaone pa khomo. 12 Anthu awiri aja anati kwa Loti, “Kodi uli ndi wina aliyense pano, kaya ndi akamwini ako, kaya ndi ana ako aamuna kapena aakazi, kapena aliyense mu mzindamu amene ndi anzako? Atulutse onse muno, 13 chifukwa tiwononga malo ano. Yehova waona kuti kuyipa kwa anthu a mu mzindawu kwakulitsa. Choncho watituma kuti tiwuwononge.” 14 Choncho Loti anatuluka nayankhula ndi akamwini ake amene anali kuyembekezera kukwatira ana ake akazi nati, “Fulumirani, tiyeni tichoke pa malo ano chifukwa Yehova watsala pangʼono kuwononga mzindawu.” Koma akamwini akewo ankayesa kuti akungoselewula. 15 Mmene kumacha, angelo aja anamufulumizitsa Loti nati, “Nyamuka, tenga mkazi wako ndi ana ako aakazi awiriwo, ndipo mutuluke mu mzindawo kuopa kuti mungaphedwe pamodzi nawo.” 16 Koma Loti ankakayikabe. Koma Yehova anawachitira chifundo motero kuti anthu aja anagwira mkazi wake ndi ana ake aakazi aja nawatsogolera bwinobwino kuwatulutsa mu mzindawo. 17 Atangowatulutsa, mmodzi wa angelowo anati, “Thawani kuti mudzipulumutse, musachewuke, musayime pena paliponse mʼchigwamo! Thawirani ku mapiri kuopa kuti mungawonongeke!” 18 Koma Loti anawawuza kuti, “Ayi, ambuye anga chonde musatero! 19 Taonani, Inu mwachitira mtumiki wanu chifundo, ndipo mwaonetsa kukoma mtima kwanu pondipulumutsa. Sindingathawire ku mapiri chifukwa chiwonongekochi chikhoza kundipeza ndisanafike ku mapiriko ndipo ndingafe. 20 Koma, chapafupi pomwepa pali mudzi woti ndikhoza kuthamanga nʼkukafikako. Mundilole ndithawireko, ndi waungʼono kwambiri, si choncho? Mukatero, moyo wanga upulumuka.” 21 Mngeloyo anati kwa iye, “Chabwino, ndavomeranso pempho lako, sindiwononga mudzi ukunenawo. 22 Koma uthawireko mofulumira chifukwa sindichita kena kalikonse mpaka utafikako.” (Nʼchifukwa chake mudziwo unatchedwa Zowari). 23 Pamene Loti amafika ku Zowari, nʼkuti dzuwa litatuluka. 24 Ndiye Yehova anathira sulufule wamoto wochokera kumwamba kwa Yehova pa Sodomu ndi Gomora. 25 Kotero, anawononga mizindayo, chigwa chonse pamodzi ndi onse okhala mʼmizindayo. Anawononganso zomera zonse za mʼdzikolo. 26 Koma mkazi wa Loti anachewuka ndipo anasanduka mwala wa mchere. 27 Mmawa mwake, Abrahamu ananyamuka nabwerera kumalo kumene anakumana ndi Yehova kuja. 28 Anayangʼana kumunsi ku Sodomu, Gomora ndi ku dziko lonse la ku chigwa, ndipo anaona chiwutsi chikufuka mʼdzikolo ngati chikuchokera mʼngʼanjo. 29 Choncho Mulungu anawononga mizinda ya ku chigwa, koma anakumbukira pemphero la Abrahamu natulutsa Loti ku sulufule ndi moto zimene zinawononga mizinda ya kumene Loti amakhalako. 30 Loti ndi ana ake awiri aakazi anachoka ku Zowari nakakhala ku mapiri, chifukwa amachita mantha kukhala ku Zowari. Iye ndi ana ake awiri ankakhala mʼphanga. 31 Tsiku lina mwana wake wamkazi wamkulu anawuza mngʼono wake kuti, “Abambo athu ndi wokalamba ndipo palibe mwamuna aliyense pano woti atikwatire ndi kubereka ana monga mwa chikhalidwe cha pa dziko lonse lapansi. 32 Tiye tiwamwetse vinyo ndipo tigone nawo. Tikatero mtundu wathu udzakhalapobe.” 33 Usiku umenewo analedzeretsa vinyo abambo awo, ndipo wamkuluyo analowa nagona naye. Abambo awo samadziwa kanthu pamene mwanayo anagona naye kapena pamene anadzuka. 34 Tsiku linali mwana wamkazi wamkulu uja anati kwa mngʼono wake, “Usiku wathawu ine ndinagona ndi abambo anga. Tiye tiwaledzeretsenso vinyo usiku uno ndipo iwe upite ndi kugona nawo ndipo mtundu wathu udzakhalapobe.” 35 Choncho analedzeranso vinyo abambo awo usiku umenewonso, ndipo mwana wamkazi wamngʼono anapita nagona nawo. Abambo awo sanadziwenso kanthu pamene mwanayo anagona naye kapena pamene anadzuka. 36 Choncho ana onse awiri a Loti aja anatenga pathupi pa abambo awo. 37 Mwana wamkazi wamkulu uja anabereka mwana wa mwamuna ndipo anamutcha Mowabu. Iyeyo ndiye kholo la Amowabu onse. 38 Mwana wamkazi wamngʼono naye anabereka mwana wamwamuna, ndipo anamutcha iye Beni-Ammi. Iyeyu ndiye kholo la Aamoni onse.

In Other Versions

Genesis 19 in the ANGEFD

Genesis 19 in the ANTPNG2D

Genesis 19 in the AS21

Genesis 19 in the BAGH

Genesis 19 in the BBPNG

Genesis 19 in the BBT1E

Genesis 19 in the BDS

Genesis 19 in the BEV

Genesis 19 in the BHAD

Genesis 19 in the BIB

Genesis 19 in the BLPT

Genesis 19 in the BNT

Genesis 19 in the BNTABOOT

Genesis 19 in the BNTLV

Genesis 19 in the BOATCB

Genesis 19 in the BOATCB2

Genesis 19 in the BOBCV

Genesis 19 in the BOCNT

Genesis 19 in the BOECS

Genesis 19 in the BOHCB

Genesis 19 in the BOHCV

Genesis 19 in the BOHLNT

Genesis 19 in the BOHNTLTAL

Genesis 19 in the BOICB

Genesis 19 in the BOILNTAP

Genesis 19 in the BOITCV

Genesis 19 in the BOKCV

Genesis 19 in the BOKCV2

Genesis 19 in the BOKHWOG

Genesis 19 in the BOKSSV

Genesis 19 in the BOLCB

Genesis 19 in the BOLCB2

Genesis 19 in the BOMCV

Genesis 19 in the BONAV

Genesis 19 in the BONCB

Genesis 19 in the BONLT

Genesis 19 in the BONUT2

Genesis 19 in the BOPLNT

Genesis 19 in the BOSCB

Genesis 19 in the BOSNC

Genesis 19 in the BOTLNT

Genesis 19 in the BOVCB

Genesis 19 in the BOYCB

Genesis 19 in the BPBB

Genesis 19 in the BPH

Genesis 19 in the BSB

Genesis 19 in the CCB

Genesis 19 in the CUV

Genesis 19 in the CUVS

Genesis 19 in the DBT

Genesis 19 in the DGDNT

Genesis 19 in the DHNT

Genesis 19 in the DNT

Genesis 19 in the ELBE

Genesis 19 in the EMTV

Genesis 19 in the ESV

Genesis 19 in the FBV

Genesis 19 in the FEB

Genesis 19 in the GGMNT

Genesis 19 in the GNT

Genesis 19 in the HARY

Genesis 19 in the HNT

Genesis 19 in the IRVA

Genesis 19 in the IRVB

Genesis 19 in the IRVG

Genesis 19 in the IRVH

Genesis 19 in the IRVK

Genesis 19 in the IRVM

Genesis 19 in the IRVM2

Genesis 19 in the IRVO

Genesis 19 in the IRVP

Genesis 19 in the IRVT

Genesis 19 in the IRVT2

Genesis 19 in the IRVU

Genesis 19 in the ISVN

Genesis 19 in the JSNT

Genesis 19 in the KAPI

Genesis 19 in the KBT1ETNIK

Genesis 19 in the KBV

Genesis 19 in the KJV

Genesis 19 in the KNFD

Genesis 19 in the LBA

Genesis 19 in the LBLA

Genesis 19 in the LNT

Genesis 19 in the LSV

Genesis 19 in the MAAL

Genesis 19 in the MBV

Genesis 19 in the MBV2

Genesis 19 in the MHNT

Genesis 19 in the MKNFD

Genesis 19 in the MNG

Genesis 19 in the MNT

Genesis 19 in the MNT2

Genesis 19 in the MRS1T

Genesis 19 in the NAA

Genesis 19 in the NASB

Genesis 19 in the NBLA

Genesis 19 in the NBS

Genesis 19 in the NBVTP

Genesis 19 in the NET2

Genesis 19 in the NIV11

Genesis 19 in the NNT

Genesis 19 in the NNT2

Genesis 19 in the NNT3

Genesis 19 in the PDDPT

Genesis 19 in the PFNT

Genesis 19 in the RMNT

Genesis 19 in the SBIAS

Genesis 19 in the SBIBS

Genesis 19 in the SBIBS2

Genesis 19 in the SBICS

Genesis 19 in the SBIDS

Genesis 19 in the SBIGS

Genesis 19 in the SBIHS

Genesis 19 in the SBIIS

Genesis 19 in the SBIIS2

Genesis 19 in the SBIIS3

Genesis 19 in the SBIKS

Genesis 19 in the SBIKS2

Genesis 19 in the SBIMS

Genesis 19 in the SBIOS

Genesis 19 in the SBIPS

Genesis 19 in the SBISS

Genesis 19 in the SBITS

Genesis 19 in the SBITS2

Genesis 19 in the SBITS3

Genesis 19 in the SBITS4

Genesis 19 in the SBIUS

Genesis 19 in the SBIVS

Genesis 19 in the SBT

Genesis 19 in the SBT1E

Genesis 19 in the SCHL

Genesis 19 in the SNT

Genesis 19 in the SUSU

Genesis 19 in the SUSU2

Genesis 19 in the SYNO

Genesis 19 in the TBIAOTANT

Genesis 19 in the TBT1E

Genesis 19 in the TBT1E2

Genesis 19 in the TFTIP

Genesis 19 in the TFTU

Genesis 19 in the TGNTATF3T

Genesis 19 in the THAI

Genesis 19 in the TNFD

Genesis 19 in the TNT

Genesis 19 in the TNTIK

Genesis 19 in the TNTIL

Genesis 19 in the TNTIN

Genesis 19 in the TNTIP

Genesis 19 in the TNTIZ

Genesis 19 in the TOMA

Genesis 19 in the TTENT

Genesis 19 in the UBG

Genesis 19 in the UGV

Genesis 19 in the UGV2

Genesis 19 in the UGV3

Genesis 19 in the VBL

Genesis 19 in the VDCC

Genesis 19 in the YALU

Genesis 19 in the YAPE

Genesis 19 in the YBVTP

Genesis 19 in the ZBP