Genesis 32 (BOGWICC)

1 Nayenso Yakobo analowera njira yake, ndipo angelo a Mulungu anakumana naye. 2 Pamene Yakobo anawaona anati, “Ili ndi gulu la Mulungu.” Choncho anawatcha malowo Mahanaimu. 3 Yakobo anatumiza amithenga ake kwa mʼbale wake Esau ku dera la Seiri, dziko la Edomu. 4 Anawalangiza kuti, “Zimene mukanene ndi izi kwa mbuye wanga Esau: ‘Mtumiki wanu Yakobo akuti, Ine ndakhala ndi kukhala ndi Labani mpaka tsopano. 5 Ndili ndi ngʼombe, abulu, nkhosa ndi mbuzi, antchito aamuna ndi aakazi. Tsopano ndikutumiza mawu amenewa kwa mbuye wanga, kuti mundikomere mtima.’ ” 6 Pamene amithenga aja anabwerera kwa Yakobo, anati, “Tinapita kwa mʼbale wanu Esau, ndipo tsopano iye akubwera kudzakumana nanu. Ali ndi anthu 400.” 7 Yakobo anali ndi mantha ndi nkhawa yayikulu kwambiri. Tsono anagawa anthu onse amene anali naye, ndiponso nkhosa, mbuzi, ngʼombe ndi ngamira mʼmagulu awiri. 8 Mʼmaganizo ake iye ankanena kuti, “Ngati Esau atabwera ndi kuthira nkhondo gulu limodzi, gulu lina lotsalalo likhoza kupulumuka.” 9 Pamenepo Yakobo anapemphera, “Haa, Mulungu wa kholo langa Abrahamu, Mulungu wa abambo anga Isake, Aa Yehova amene munati kwa ine, ‘Bwerera ku dziko la kwanu ndi kwa abale ako, ndipo ndidzakuchitira zabwino.’ 10 Ine siwoyenera kulandira kukoma mtima kwanu ndi kukhulupirika kwanu kumene mwaonetsa wantchito wanu. Ndinali ndi ndodo yokha pamene ndinawoloka Yorodani uyu koma tsopano ndili ndi magulu awiri. 11 Ndipulumutseni mʼdzanja la mʼbale wanga Esau, popeza ndikuopa kuti mwina akubwera kudzandithira nkhondo pamodzi ndi akazi ndi ana omwe. 12 Paja Inu munandilonjeza kuti simudzalephera kundichitira zabwino ndi kuti zidzukulu zanga zidzakhala zosawerengeka ngati mchenga wa ku nyanja.” 13 Iye anagona pomwepo usiku umenewo. Pambuyo pake anasankhula pa chuma chimene anali nacho zinthu izi ngati mphatso za Esau, mʼbale wake: 14 Anasankhula mbuzi zazikazi 200 ndi atonde makumi awiri, nkhosa zazikazi 200 ndi nkhosa zazimuna makumi awiri, 15 ngamira za mkaka 30 ndi ana awo, ngʼombe zazikazi 40 ndi zazimuna khumi, ndipo abulu aakazi makumi awiri ndi abulu aamuna khumi. 16 Iye anazipereka kwa antchito ake kuti azikuse, gulu lililonse pa lokha, ndipo anati kwa antchito akewo, “Tsogolani ndipo muonetsetse kuti pali mpata pakati pa gulu ndi gulu linzake.” 17 Anawuza mnyamata wa gulu loyamba kuti, “Ngati ukumana naye mʼbale wanga Esau nakufunsa kuti, ‘Ndinu antchito a yani, ndipo mukupita kuti? Nanga ziweto zonse zili patsogolo pakozi ndi za yani?’ 18 Pamenepo ukayankhe kuti, ‘Zimenezi ndi za wantchito wanu, Yakobo, ndipo wazipereka kwa inu, Esau, mbuye wake ngati mphatso. Mtumiki wanuyu akubwera mʼmbuyo mwathumu.’ ” 19 Anawuza mawu omwewo kwa wachiwiri, wachitatu ndi ena onse amene ankayenda motsogoza ziwetozo kuti, “Inunso munene zomwezo kwa Esau mukakumana naye. 20 Muzikanena kuti, ‘Wantchito wanu Yakobo akubwera mʼmbuyo mwathumu.’ ” Popeza anaganiza kuti, “Ndidzamutsitsa mtima ndi mphatso ndazitsogozazi. Apo tsono ndikadzakumana naye, mwina adzandilandira bwino.” 21 Choncho mphatso za Yakobo zinatsogola, koma iye mwini anagona pa msasa pomwepo usiku umenewo. 22 Usiku umenewo Yakobo anauka natenga akazi ake awiri, antchito ake awiri ndi ana ake aamuna khumi ndi mmodzi nawoloka pa dooko la mtsinje wa Yaboki. 23 Atatha kuwawolotsa pa mtsinjewo anawolotsanso katundu wake yense. 24 Tsono Yakobo anatsala yekha. Tsono munthu wina anadzalimbana naye mpaka mʼmbandakucha. 25 Pamene munthuyo anaona kuti sangathe kumugonjetsa, anakhudza nyungʼunyu ya pa ntchafu ya Yakobo ndipo inaguluka polimbanapo. 26 Kenaka munthuyo anati, “Ndisiye ndizipita, popeza kunja kukucha.”Koma Yakobo anayankha, “Sindikulolani kupita pokhapokha mutandidalitsa.” 27 Munthu uja anamufunsa Yakobo kuti, “Kodi dzina lako ndiwe yani?”Iye anayankha, “Ndine Yakobo.” 28 Pamenepo munthuyo anati, “Dzina lako silidzakhalanso Yakobo koma Israeli, chifukwa walimbana ndi Mulungu ndi anthu ndipo wapambana.” 29 Yakobo anati, “Chonde, uzeni dzina lanu.”Koma munthuyo anati, “Chifukwa chiyani ukundifunsa dzina?” Kenaka anamudalitsa pomwepo. 30 Choncho Yakobo anawatcha malowo Penueli, popeza anati, “Ndinaonana ndi Mulungu maso ndi maso koma sindinafe.” 31 Dzuwa linamutulukira Yakobo pamene amachoka pa Penueli. Tsono ankayenda chotsimphina chifukwa cha nyungʼunyu yake ija. 32 Nʼchifukwa chake mpaka lero Aisraeli sadya nyama ya pa nyungʼunyu chifukwa Yakobo anakhudzidwa pa nyungʼunyu.

In Other Versions

Genesis 32 in the ANGEFD

Genesis 32 in the ANTPNG2D

Genesis 32 in the AS21

Genesis 32 in the BAGH

Genesis 32 in the BBPNG

Genesis 32 in the BBT1E

Genesis 32 in the BDS

Genesis 32 in the BEV

Genesis 32 in the BHAD

Genesis 32 in the BIB

Genesis 32 in the BLPT

Genesis 32 in the BNT

Genesis 32 in the BNTABOOT

Genesis 32 in the BNTLV

Genesis 32 in the BOATCB

Genesis 32 in the BOATCB2

Genesis 32 in the BOBCV

Genesis 32 in the BOCNT

Genesis 32 in the BOECS

Genesis 32 in the BOHCB

Genesis 32 in the BOHCV

Genesis 32 in the BOHLNT

Genesis 32 in the BOHNTLTAL

Genesis 32 in the BOICB

Genesis 32 in the BOILNTAP

Genesis 32 in the BOITCV

Genesis 32 in the BOKCV

Genesis 32 in the BOKCV2

Genesis 32 in the BOKHWOG

Genesis 32 in the BOKSSV

Genesis 32 in the BOLCB

Genesis 32 in the BOLCB2

Genesis 32 in the BOMCV

Genesis 32 in the BONAV

Genesis 32 in the BONCB

Genesis 32 in the BONLT

Genesis 32 in the BONUT2

Genesis 32 in the BOPLNT

Genesis 32 in the BOSCB

Genesis 32 in the BOSNC

Genesis 32 in the BOTLNT

Genesis 32 in the BOVCB

Genesis 32 in the BOYCB

Genesis 32 in the BPBB

Genesis 32 in the BPH

Genesis 32 in the BSB

Genesis 32 in the CCB

Genesis 32 in the CUV

Genesis 32 in the CUVS

Genesis 32 in the DBT

Genesis 32 in the DGDNT

Genesis 32 in the DHNT

Genesis 32 in the DNT

Genesis 32 in the ELBE

Genesis 32 in the EMTV

Genesis 32 in the ESV

Genesis 32 in the FBV

Genesis 32 in the FEB

Genesis 32 in the GGMNT

Genesis 32 in the GNT

Genesis 32 in the HARY

Genesis 32 in the HNT

Genesis 32 in the IRVA

Genesis 32 in the IRVB

Genesis 32 in the IRVG

Genesis 32 in the IRVH

Genesis 32 in the IRVK

Genesis 32 in the IRVM

Genesis 32 in the IRVM2

Genesis 32 in the IRVO

Genesis 32 in the IRVP

Genesis 32 in the IRVT

Genesis 32 in the IRVT2

Genesis 32 in the IRVU

Genesis 32 in the ISVN

Genesis 32 in the JSNT

Genesis 32 in the KAPI

Genesis 32 in the KBT1ETNIK

Genesis 32 in the KBV

Genesis 32 in the KJV

Genesis 32 in the KNFD

Genesis 32 in the LBA

Genesis 32 in the LBLA

Genesis 32 in the LNT

Genesis 32 in the LSV

Genesis 32 in the MAAL

Genesis 32 in the MBV

Genesis 32 in the MBV2

Genesis 32 in the MHNT

Genesis 32 in the MKNFD

Genesis 32 in the MNG

Genesis 32 in the MNT

Genesis 32 in the MNT2

Genesis 32 in the MRS1T

Genesis 32 in the NAA

Genesis 32 in the NASB

Genesis 32 in the NBLA

Genesis 32 in the NBS

Genesis 32 in the NBVTP

Genesis 32 in the NET2

Genesis 32 in the NIV11

Genesis 32 in the NNT

Genesis 32 in the NNT2

Genesis 32 in the NNT3

Genesis 32 in the PDDPT

Genesis 32 in the PFNT

Genesis 32 in the RMNT

Genesis 32 in the SBIAS

Genesis 32 in the SBIBS

Genesis 32 in the SBIBS2

Genesis 32 in the SBICS

Genesis 32 in the SBIDS

Genesis 32 in the SBIGS

Genesis 32 in the SBIHS

Genesis 32 in the SBIIS

Genesis 32 in the SBIIS2

Genesis 32 in the SBIIS3

Genesis 32 in the SBIKS

Genesis 32 in the SBIKS2

Genesis 32 in the SBIMS

Genesis 32 in the SBIOS

Genesis 32 in the SBIPS

Genesis 32 in the SBISS

Genesis 32 in the SBITS

Genesis 32 in the SBITS2

Genesis 32 in the SBITS3

Genesis 32 in the SBITS4

Genesis 32 in the SBIUS

Genesis 32 in the SBIVS

Genesis 32 in the SBT

Genesis 32 in the SBT1E

Genesis 32 in the SCHL

Genesis 32 in the SNT

Genesis 32 in the SUSU

Genesis 32 in the SUSU2

Genesis 32 in the SYNO

Genesis 32 in the TBIAOTANT

Genesis 32 in the TBT1E

Genesis 32 in the TBT1E2

Genesis 32 in the TFTIP

Genesis 32 in the TFTU

Genesis 32 in the TGNTATF3T

Genesis 32 in the THAI

Genesis 32 in the TNFD

Genesis 32 in the TNT

Genesis 32 in the TNTIK

Genesis 32 in the TNTIL

Genesis 32 in the TNTIN

Genesis 32 in the TNTIP

Genesis 32 in the TNTIZ

Genesis 32 in the TOMA

Genesis 32 in the TTENT

Genesis 32 in the UBG

Genesis 32 in the UGV

Genesis 32 in the UGV2

Genesis 32 in the UGV3

Genesis 32 in the VBL

Genesis 32 in the VDCC

Genesis 32 in the YALU

Genesis 32 in the YAPE

Genesis 32 in the YBVTP

Genesis 32 in the ZBP