Genesis 48 (BOGWICC)
1 Patapita kanthawi Yosefe anawuzidwa kuti, “Abambo ako akudwala.” Choncho anatenga ana ake awiri aja Manase ndi Efereimu ndi kupita nawo kwa Yakobo. 2 Yakobo atawuzidwa kuti, “Mwana wanu Yosefe wabwera,” Israeli anadzilimbitsa nadzuka kukhala tsonga pa bedi pake. 3 Yakobo anati kwa Yosefe, “Mulungu Wamphamvuzonse anandionekera ku Luzi mʼdziko la Kanaani, ndipo anandidalitsa, 4 nati kwa ine, ‘Ndidzakupatsa ana ambiri ndipo zidzukulu zako zidzasanduka mitundu yambiri ya anthu. Ndidzapereka dziko ili kwa zidzukulu zako zobwera pambuyo pako kuti likhale lawo mpaka muyaya.’ 5 “Tsopano ana ako aamuna awiri amene anabadwa ine ndisanabwere kuno adzakhala ana anga. Efereimu ndi Manase adzakhala anga monga mmene alili Rubeni ndi Simeoni. 6 Koma amene ati adzabadwe pambuyo pa iwowa adzakhala ako ndipo cholowa chawo chidzadziwika ndi mayina a abale awo. 7 Pamene ndimabwerera kuchoka ku Parani, mwachisoni Rakele, amayi ako anamwalira mʼdziko la Kanaani, tikanali mʼnjira, mtunda wokafika ku Efurata ukanalipo. Ndipo ndinawayika kumeneko mʼmphepete mwa msewu wa ku Efurata” (amene ndi Betelehemu). 8 Israeli ataona ana a Yosefe anafunsa kuti, “Anyamatawa ndi a yani?” 9 Yosefe anati kwa abambo ake, “Awa ndi ana anga amene Mulungu wandipatsa kuno.”Ndipo Israeli anati, “Bwera nawo kuno kuti ndiwadalitse.” 10 Koma maso a Israeli anali ofowoka chifukwa cha kukalamba moti sankaona nʼkomwe. Tsono Yosefe anabwera nawo ana ake aja pafupi ndi abambo ake ndipo abambo ake anawapsompsona nawakumbatira. 11 Israeli anati kwa Yosefe, “Ine sindinali kuyembekeza kuti nʼkudzaonanso nkhope yako, ndipo tsopano Mulungu wandilola kuti ndionenso ngakhale ana ako.” 12 Tsono Yosefe anawachotsa ana aja pa mawondo a Israeli ndipo anamuweramira nkhope pansi. 13 Yosefe anawagwira ana onse awiri padzanja, Efereimu ku dzanja lake lamanja kulunjika dzanja lamanzere la Israeli ndipo Manase ku dzanja lamanzere kulunjikitsa dzanja lamanja la Israeli, ndipo anawayandikiza kwa Yakobo. 14 Koma Israeli anapinganitsa mikono motero kuti anayika dzanja lake lamanja pamutu pa Efereimu ngakhale kuti iyeyo anali wamngʼono ndi dzanja lake lakumanzere analisanjika pamutu pa Manase ngakhale kuti iyeyu ndiye anali mwana woyamba. 15 Kenaka anadalitsa Yosefe nati,“Mulungu amene makolo angaAbrahamu ndi Isake anamutumikira,Mulungu amene wakhala ali mʼbusa wangamoyo wanga wonse kufikira lero, 16 mngelo amene wandipulumutsa ine ku zovuta zonse,ameneyo adalitse anyamata awa.Kudzera mwa iwowadzina langa ndi mayina a makolo anga, Abrahamu ndi Isake, adzamveka.Iwowa adzakhala ndi ana ambiri nadzasanduka mtundu waukulupa dziko lapansi.” 17 Yosefe ataona kuti abambo ake ayika dzanja lamanja pa Efereimu, sanakondwere. Choncho anagwira dzanja la abambo ake kuti alichotse pamutu pa Efereimu ndi kuliyika pamutu pa Manase, 18 nati kwa abambo ake, “Ayi, abambo anga, uyu ndiye woyamba kubadwa, ikani dzanja lanu lamanja pamutu pake.” 19 Koma abambo ake anakana nati, “Ndikudziwa, mwana wanga, ndikudziwa. Adzukulu a iyeyunso adzakhala mtundu waukulu. Komabe mʼbale wake wamngʼonoyu adzakhala wamkulu kuposa iye, ndipo zidzukulu zake zidzakhala mitundu yayikulu ya anthu.” 20 Tsono iye anawadalitsa tsiku limenelo nati,“Aisraeli adzagwiritsa ntchito dzina lanu podalitsa nadzati:Mulungu akudalitseni monga Efereimu ndi Manase.”Choncho anayika Efereimu patsogolo pa Manase. 21 Kenaka Israeli anati kwa Yosefe, “Ine ndatsala pangʼono kufa, koma Mulungu adzakhala ndipo adzakutenganinso kubwerera nanu ku dziko la makolo anu. 22 Ndiponso iwe wekha ndikupatsa moposera abale ako, malo woonjezera, Sekemu, malo amene ndinalanda kwa Aamori ndi lupanga ndi uta wanga.”
In Other Versions
Genesis 48 in the ANGEFD
Genesis 48 in the ANTPNG2D
Genesis 48 in the AS21
Genesis 48 in the BAGH
Genesis 48 in the BBPNG
Genesis 48 in the BBT1E
Genesis 48 in the BDS
Genesis 48 in the BEV
Genesis 48 in the BHAD
Genesis 48 in the BIB
Genesis 48 in the BLPT
Genesis 48 in the BNT
Genesis 48 in the BNTABOOT
Genesis 48 in the BNTLV
Genesis 48 in the BOATCB
Genesis 48 in the BOATCB2
Genesis 48 in the BOBCV
Genesis 48 in the BOCNT
Genesis 48 in the BOECS
Genesis 48 in the BOHCB
Genesis 48 in the BOHCV
Genesis 48 in the BOHLNT
Genesis 48 in the BOHNTLTAL
Genesis 48 in the BOICB
Genesis 48 in the BOILNTAP
Genesis 48 in the BOITCV
Genesis 48 in the BOKCV
Genesis 48 in the BOKCV2
Genesis 48 in the BOKHWOG
Genesis 48 in the BOKSSV
Genesis 48 in the BOLCB
Genesis 48 in the BOLCB2
Genesis 48 in the BOMCV
Genesis 48 in the BONAV
Genesis 48 in the BONCB
Genesis 48 in the BONLT
Genesis 48 in the BONUT2
Genesis 48 in the BOPLNT
Genesis 48 in the BOSCB
Genesis 48 in the BOSNC
Genesis 48 in the BOTLNT
Genesis 48 in the BOVCB
Genesis 48 in the BOYCB
Genesis 48 in the BPBB
Genesis 48 in the BPH
Genesis 48 in the BSB
Genesis 48 in the CCB
Genesis 48 in the CUV
Genesis 48 in the CUVS
Genesis 48 in the DBT
Genesis 48 in the DGDNT
Genesis 48 in the DHNT
Genesis 48 in the DNT
Genesis 48 in the ELBE
Genesis 48 in the EMTV
Genesis 48 in the ESV
Genesis 48 in the FBV
Genesis 48 in the FEB
Genesis 48 in the GGMNT
Genesis 48 in the GNT
Genesis 48 in the HARY
Genesis 48 in the HNT
Genesis 48 in the IRVA
Genesis 48 in the IRVB
Genesis 48 in the IRVG
Genesis 48 in the IRVH
Genesis 48 in the IRVK
Genesis 48 in the IRVM
Genesis 48 in the IRVM2
Genesis 48 in the IRVO
Genesis 48 in the IRVP
Genesis 48 in the IRVT
Genesis 48 in the IRVT2
Genesis 48 in the IRVU
Genesis 48 in the ISVN
Genesis 48 in the JSNT
Genesis 48 in the KAPI
Genesis 48 in the KBT1ETNIK
Genesis 48 in the KBV
Genesis 48 in the KJV
Genesis 48 in the KNFD
Genesis 48 in the LBA
Genesis 48 in the LBLA
Genesis 48 in the LNT
Genesis 48 in the LSV
Genesis 48 in the MAAL
Genesis 48 in the MBV
Genesis 48 in the MBV2
Genesis 48 in the MHNT
Genesis 48 in the MKNFD
Genesis 48 in the MNG
Genesis 48 in the MNT
Genesis 48 in the MNT2
Genesis 48 in the MRS1T
Genesis 48 in the NAA
Genesis 48 in the NASB
Genesis 48 in the NBLA
Genesis 48 in the NBS
Genesis 48 in the NBVTP
Genesis 48 in the NET2
Genesis 48 in the NIV11
Genesis 48 in the NNT
Genesis 48 in the NNT2
Genesis 48 in the NNT3
Genesis 48 in the PDDPT
Genesis 48 in the PFNT
Genesis 48 in the RMNT
Genesis 48 in the SBIAS
Genesis 48 in the SBIBS
Genesis 48 in the SBIBS2
Genesis 48 in the SBICS
Genesis 48 in the SBIDS
Genesis 48 in the SBIGS
Genesis 48 in the SBIHS
Genesis 48 in the SBIIS
Genesis 48 in the SBIIS2
Genesis 48 in the SBIIS3
Genesis 48 in the SBIKS
Genesis 48 in the SBIKS2
Genesis 48 in the SBIMS
Genesis 48 in the SBIOS
Genesis 48 in the SBIPS
Genesis 48 in the SBISS
Genesis 48 in the SBITS
Genesis 48 in the SBITS2
Genesis 48 in the SBITS3
Genesis 48 in the SBITS4
Genesis 48 in the SBIUS
Genesis 48 in the SBIVS
Genesis 48 in the SBT
Genesis 48 in the SBT1E
Genesis 48 in the SCHL
Genesis 48 in the SNT
Genesis 48 in the SUSU
Genesis 48 in the SUSU2
Genesis 48 in the SYNO
Genesis 48 in the TBIAOTANT
Genesis 48 in the TBT1E
Genesis 48 in the TBT1E2
Genesis 48 in the TFTIP
Genesis 48 in the TFTU
Genesis 48 in the TGNTATF3T
Genesis 48 in the THAI
Genesis 48 in the TNFD
Genesis 48 in the TNT
Genesis 48 in the TNTIK
Genesis 48 in the TNTIL
Genesis 48 in the TNTIN
Genesis 48 in the TNTIP
Genesis 48 in the TNTIZ
Genesis 48 in the TOMA
Genesis 48 in the TTENT
Genesis 48 in the UBG
Genesis 48 in the UGV
Genesis 48 in the UGV2
Genesis 48 in the UGV3
Genesis 48 in the VBL
Genesis 48 in the VDCC
Genesis 48 in the YALU
Genesis 48 in the YAPE
Genesis 48 in the YBVTP
Genesis 48 in the ZBP