Genesis 50 (BOGWICC)
1 Kenaka Yosefe anadzigwetsa pa nkhope ya abambo ake, nawapsompsona kwinaku akulira. 2 Ndipo Yosefe analamula antchito ake a chipatala kuti akonze thupi la Israeli ndi mankhwala kuti lisawole. Kotero antchitowo anakonzadi thupilo. 3 Antchito aja zinawatengera masiku 40 kuti akonze mtembo uja popeza ntchito ngati imeneyi inafunikira masiku monga amenewa. Ndipo Aigupto anamulira Yakobo kwa masiku makumi asanu ndi awiri. 4 Yosefe atatha kulira maliro a abambo ake, anayankhula kwa nduna za Farao nati, “Ngati mungandikomere mtima, chonde mundiyankhulire kwa Farao kumuwuza kuti, 5 ‘Abambo anga anandilumbiritsa ndipo anati, ‘Ndatsala pangʼono kumwalira, ukandiyike mʼmanda amene ndinakumba ndekha mʼdziko la Kanaani.’ Tsono mundilole ndikayike abambo anga, ndipo ndikabweranso.’ ” 6 Farao anati, “Pita ukayike abambo ako monga anakulumbiritsa kuti uchite.” 7 Kotero Yosefe anapita kukayika abambo ake. Nduna zonse za Farao, akuluakulu a bwalo lake ndi akuluakulu a ku Igupto, anapita naye pamodzi. 8 Anapitanso onse a pa banja la Yosefe ndi abale ake ndi onse amene anali a pa banja la abambo ake. Ana awo okha, nkhosa ndi ngʼombe zinatsala ku Goseni 9 Asilikali okwera pa magaleta ndi asilikali a pa akavalo anapita nayenso pamodzi. Linali gulu lalikulu. 10 Atafika pa Goreni ha-Atadi, pafupi ndi Yorodani, anachita mwambo waukulu wa maliro. Choncho Yosefe analira maliro a abambo ake masiku asanu ndi awiri. 11 Akanaani amene ankakhala ku Goreni ha-Atadi ataona mwambo wa maliro anati, “Aigupto ali ndi mwambo wa maliro a akulu.” Ndi chifukwa chake malo amenewo a pafupi ndi Yorodani amatchedwa Abeli-Mizraimu. 12 Choncho ana a Yakobo anachita monga momwe abambo awo anawalamula: 13 Ndiye kuti ana a Yakobo anamunyamula kupita naye ku Kanaani kuti akamuyike mʼphanga limene lili mʼmunda wa Makipela pafupi ndi Mamre. Abrahamu anagula mundawo kwa Efroni Mhiti kuti pakhale manda. 14 Atatha kuyika abambo ake, Yosefe anabwerera ku Igupto, pamodzi ndi abale ake ndi onse amene anapita nawo kukayika abambo ake. 15 Abale ake a Yosefe ataona kuti abambo awo amwalira, anati, “Nanga tidzatani ngati Yosefe anatisungira mangawa nafuna kutibwezera pa zoyipa zonse zimene tinamuchitira?” 16 Motero anatumiza mawu kwa Yosefe kuti, “Abambo anu anasiya malangizo asanafe nati: 17 ‘Zimene mudzayenera kunena kwa Yosefe ndi izi: Ndikukupempha kuti uwakhululukire abale ako cholakwa chawo ndi machimo awo, popeza anakuchitira zoyipa.’ Ndiye tsopano chonde tikhululukireni zolakwa zimene ife akapolo a Mulungu wa abambo anu tinachita.” Yosefe atangomva mawu amenewa anayamba kulira. 18 Kenaka abale ake anabwera nadzigwetsa pansi pamaso pake, nati, “Ife ndife akapolo anu.” 19 Koma Yosefe anawawuza kuti, “Musachite mantha. Kodi ine ndalowa mʼmalo mwa Mulungu? 20 Inu munafuna kundichitira zoyipa, koma Mulungu anasandutsa zoyipazo kuti zikhale zabwino kuti zikwaniritsidwe zimene zikuchitika panozi, zopulumutsa miyoyo yambiri. 21 Kotero, musachite mantha. Ine ndidzasamalira inu pamodzi ndi ana anu omwe.” Tsono iye anawalimbitsa mtima powayankhula moleza mtima. 22 Yosefe anakhala mu Igupto pamodzi ndi banja lonse la abambo ake. Anakhala ndi moyo zaka 110 23 ndipo anaona mʼbado wachitatu wa ana a Efereimu. Yosefe anatenganso ana a Makiri, mwana wa Manase kukhala ngati ana a mʼbanja lake. 24 Kenaka Yosefe anati kwa abale ake, “Ine ndatsala pangʼono kufa. Koma mosakayika Mulungu adzakuyangʼanirani nadzakutengani kukutulutsani mʼdziko lino kupita ku dziko limene Iye analonjeza kwa Abrahamu, Isake ndi Yakobo.” 25 Ndipo Yosefe analumbiritsa ana a Israeli lumbiro nati, “Lonjezani kuti Mulungu akadzakusungani mudzanyamula mafupa anga kuwachotsa ku malo kuno.” 26 Choncho Yosefe anafa ali ndi zaka 110. Motero iwo atakonza thupi lake ndi mankhwala kuti lisawole, analiyika mʼbokosi ku Igupto.
In Other Versions
Genesis 50 in the ANGEFD
Genesis 50 in the ANTPNG2D
Genesis 50 in the AS21
Genesis 50 in the BAGH
Genesis 50 in the BBPNG
Genesis 50 in the BBT1E
Genesis 50 in the BDS
Genesis 50 in the BEV
Genesis 50 in the BHAD
Genesis 50 in the BIB
Genesis 50 in the BLPT
Genesis 50 in the BNT
Genesis 50 in the BNTABOOT
Genesis 50 in the BNTLV
Genesis 50 in the BOATCB
Genesis 50 in the BOATCB2
Genesis 50 in the BOBCV
Genesis 50 in the BOCNT
Genesis 50 in the BOECS
Genesis 50 in the BOHCB
Genesis 50 in the BOHCV
Genesis 50 in the BOHLNT
Genesis 50 in the BOHNTLTAL
Genesis 50 in the BOICB
Genesis 50 in the BOILNTAP
Genesis 50 in the BOITCV
Genesis 50 in the BOKCV
Genesis 50 in the BOKCV2
Genesis 50 in the BOKHWOG
Genesis 50 in the BOKSSV
Genesis 50 in the BOLCB
Genesis 50 in the BOLCB2
Genesis 50 in the BOMCV
Genesis 50 in the BONAV
Genesis 50 in the BONCB
Genesis 50 in the BONLT
Genesis 50 in the BONUT2
Genesis 50 in the BOPLNT
Genesis 50 in the BOSCB
Genesis 50 in the BOSNC
Genesis 50 in the BOTLNT
Genesis 50 in the BOVCB
Genesis 50 in the BOYCB
Genesis 50 in the BPBB
Genesis 50 in the BPH
Genesis 50 in the BSB
Genesis 50 in the CCB
Genesis 50 in the CUV
Genesis 50 in the CUVS
Genesis 50 in the DBT
Genesis 50 in the DGDNT
Genesis 50 in the DHNT
Genesis 50 in the DNT
Genesis 50 in the ELBE
Genesis 50 in the EMTV
Genesis 50 in the ESV
Genesis 50 in the FBV
Genesis 50 in the FEB
Genesis 50 in the GGMNT
Genesis 50 in the GNT
Genesis 50 in the HARY
Genesis 50 in the HNT
Genesis 50 in the IRVA
Genesis 50 in the IRVB
Genesis 50 in the IRVG
Genesis 50 in the IRVH
Genesis 50 in the IRVK
Genesis 50 in the IRVM
Genesis 50 in the IRVM2
Genesis 50 in the IRVO
Genesis 50 in the IRVP
Genesis 50 in the IRVT
Genesis 50 in the IRVT2
Genesis 50 in the IRVU
Genesis 50 in the ISVN
Genesis 50 in the JSNT
Genesis 50 in the KAPI
Genesis 50 in the KBT1ETNIK
Genesis 50 in the KBV
Genesis 50 in the KJV
Genesis 50 in the KNFD
Genesis 50 in the LBA
Genesis 50 in the LBLA
Genesis 50 in the LNT
Genesis 50 in the LSV
Genesis 50 in the MAAL
Genesis 50 in the MBV
Genesis 50 in the MBV2
Genesis 50 in the MHNT
Genesis 50 in the MKNFD
Genesis 50 in the MNG
Genesis 50 in the MNT
Genesis 50 in the MNT2
Genesis 50 in the MRS1T
Genesis 50 in the NAA
Genesis 50 in the NASB
Genesis 50 in the NBLA
Genesis 50 in the NBS
Genesis 50 in the NBVTP
Genesis 50 in the NET2
Genesis 50 in the NIV11
Genesis 50 in the NNT
Genesis 50 in the NNT2
Genesis 50 in the NNT3
Genesis 50 in the PDDPT
Genesis 50 in the PFNT
Genesis 50 in the RMNT
Genesis 50 in the SBIAS
Genesis 50 in the SBIBS
Genesis 50 in the SBIBS2
Genesis 50 in the SBICS
Genesis 50 in the SBIDS
Genesis 50 in the SBIGS
Genesis 50 in the SBIHS
Genesis 50 in the SBIIS
Genesis 50 in the SBIIS2
Genesis 50 in the SBIIS3
Genesis 50 in the SBIKS
Genesis 50 in the SBIKS2
Genesis 50 in the SBIMS
Genesis 50 in the SBIOS
Genesis 50 in the SBIPS
Genesis 50 in the SBISS
Genesis 50 in the SBITS
Genesis 50 in the SBITS2
Genesis 50 in the SBITS3
Genesis 50 in the SBITS4
Genesis 50 in the SBIUS
Genesis 50 in the SBIVS
Genesis 50 in the SBT
Genesis 50 in the SBT1E
Genesis 50 in the SCHL
Genesis 50 in the SNT
Genesis 50 in the SUSU
Genesis 50 in the SUSU2
Genesis 50 in the SYNO
Genesis 50 in the TBIAOTANT
Genesis 50 in the TBT1E
Genesis 50 in the TBT1E2
Genesis 50 in the TFTIP
Genesis 50 in the TFTU
Genesis 50 in the TGNTATF3T
Genesis 50 in the THAI
Genesis 50 in the TNFD
Genesis 50 in the TNT
Genesis 50 in the TNTIK
Genesis 50 in the TNTIL
Genesis 50 in the TNTIN
Genesis 50 in the TNTIP
Genesis 50 in the TNTIZ
Genesis 50 in the TOMA
Genesis 50 in the TTENT
Genesis 50 in the UBG
Genesis 50 in the UGV
Genesis 50 in the UGV2
Genesis 50 in the UGV3
Genesis 50 in the VBL
Genesis 50 in the VDCC
Genesis 50 in the YALU
Genesis 50 in the YAPE
Genesis 50 in the YBVTP
Genesis 50 in the ZBP