Hosea 14 (BOGWICC)
1 Iwe Israeli bwerera kwa Yehova Mulungu wako.Machimo anu ndi amene akugwetsani! 2 Bweretsani zopempha zanundipo bwererani kwa Yehova.Munene kwa Iye kuti,“Tikhululukireni machimo athu onsendi kutilandira mokoma mtima,kuti tithe kukuyamikani ndi mawu a pakamwa pathu. 3 Asiriya sangatipulumutse;ife sitidzakwera pa akavalo ankhondo,sitidzanenanso kuti, ‘Milungu yathu’kwa zimene manja athu omwe anazipanga,pakuti ndinu amene mumachitira chifundo ana amasiye.” 4 Ine ndidzachiza kusakhulupirika kwawondipo ndidzawakonda mwaufulupakuti ndaleka kuwakwiyira. 5 Ndidzakhala ngati mame kwa IsraeliNdipo iye adzachita maluwa ngati kakombo.Adzazika mizu yake pansingati mkungudza wa ku Lebanoni; 6 mphukira zake zidzakula.Kukongola kwake kudzakhala ngati mtengo wa olivi,kununkhira kwake ngati mkungudza wa ku Lebanoni. 7 Anthu adzakhalanso mu mthunzi wake.Iye adzakula bwino ngati tirigu.Adzachita maluwa ngati mphesandipo kutchuka kwake kudzakhala ngati vinyo wochokera ku Lebanoni. 8 Efereimu adzati, “Ndidzachita nawonso chiyani mafano?Ine ndidzamuyankha ndi kumusamalira.Ine ndili ngati mtengo wa payini wobiriwira;zipatso zako zimachokera kwa Ine.” 9 Ndani ali ndi nzeru? Adzazindikire zinthu izi.Ndani amene amamvetsa zinthu? Adzamvetse izi.Njira za Yehova ndi zolungama;anthu olungama amayenda mʼmenemo,koma anthu owukira amapunthwamo.