Jeremiah 22 (BOGWICC)

1 Yehova anandiwuza kuti, “Pita ku nyumba ya mfumu ya ku Yuda ndipo ukayiwuze kuti, 2 ‘Imva mawu a Yehova, iwe mfumu ya ku Yuda, amene umakhala pa mpando waufumu wa Davide; iwe, nduna zako pamodzi ndi anthu ako amene amalowera pa zipata izi. 3 Yehova akuti, uziweruza molungama ndi mosakondera. Uzipulumutsa munthu amene walandidwa katundu mʼdzanja la womuzunza. Usazunze kapena kupondereza mlendo, ana amasiye kapena akazi amasiye. Usaphe munthu wosalakwa pa malo pano. 4 Pakuti ngati udzamvera malamulo awa, ndiye kuti mafumu onse okhala pa mpando waufumu wa Davide azidzalowabe pa zipata za nyumba yaufumu ino, atakwera magaleta ndi akavalo, iwowo pamodzi ndi nduna zawo ndi anthu awo. 5 Koma ngati sumvera malamulo awa, akutero Yehova, ndikulumbira pali Ine ndemwe kuti nyumba ino yaufumu idzasanduka bwinja.’ ” 6 Pakuti zimene Yehova akunena za nyumba yaufumu ya mfumu ya ku Yuda ndi izi:“Ngakhale iwe uli ngati Giliyadi kwa Ine,ngati msonga ya phiri la Lebanoni,komabe ndidzakusandutsa chipululu,ngati mizinda yopanda anthu. 7 Ndidzatuma anthu oti adzakuwononge,munthu aliyense ali ndi zida zake,ndipo adzadula mikungudza yako yokongolanadzayiponya pa moto. 8 “Pamene anthu a mitundu ina adzadutsa pa mzinda umenewu adzafunsana kuti, ‘Chifukwa chiyani Yehova wachita chinthu chotere pa mzinda waukuluwu?’ 9 Ndipo yankho lake lidzakhala lakuti, ‘Chifukwa anasiya pangano limene anapangana ndi Yehova Mulungu wawo ndipo anapembedza ndi kutumikira milungu ina.’ ” 10 Musayilire mfumu Yosiya, musamuyimbire nyimbo womwalirayo;mʼmalo mwake, mulire kwambiri chifukwa cha Yehowahazi amene wapita ku ukapolo,chifukwa sadzabwereransokapena kuonanso dziko lake lobadwira. 11 Pakuti zimene Yehova akunena za Yehowahazi mwana wa Yosiya, amene anatenga mpando waufumu wa Yuda mʼmalo mwa abambo ake koma nʼkuwusiya ndi izi: “Iye sadzabwereranso. 12 Iyeyo adzafera ku ukapoloko. Sadzalionanso dziko lino.” 13 “Tsoka kwa munthu womanga nyumba yake mopanda chilungamo,womanga zipinda zake zosanja monyenga,pogwiritsa ntchito abale ake mwathangata,osawapatsa malipiro a ntchito yawo. 14 Munthuyo amati, ‘Ndidzadzimangira nyumba yayikuluya zipinda zikuluzikulu zamʼmwamba.’Kotero ndidzapanga mazenera akuluakulu,ndi kukhomamo matabwa a mkungudzandi kukongoletsa ndi makaka ofiira. 15 “Kodi kukhala ndi nyumba ya mkungudza wambirizingachititse iwe kukhala mfumu?Ganiza za abambo ako. Suja anali ndi zonse zakudya ndi zakumwa.Abambo ako ankaweruza molungama ndi mosakondera,ndipo zonse zinkawayendera bwino. 16 Iye ankateteza anthu osauka ndi osowa,ndipo zonse zinkamuyendera bwino.Kodi zimenezi sindiye tanthauzo la kudziwa Ine?”akutero Yehova. 17 “Koma maso ako ndi mtima sizili penanso,koma zili pa phindu lachinyengo,pa zopha anthu osalakwandi pa kuzunza ndi pakulamulira mwankhanza.” 18 Nʼchifukwa chake Yehova ponena za Yehoyakimu mwana wa Yosiya mfumu ya ku Yuda akuti,“Anthu sadzamulira maliro kapena kunena kuti,‘Kalanga ine, mʼbale wanga! Kalanga ine mlongo wanga!Anthu ake sadzamulira maliro kuti,Kalanga ine, mbuye wathu! Taonani ulemerero wake wapita!’ 19 Adzayikidwa ngati bulu,kuchita kumuguguza ndi kukamutayakunja kwa zipata za Yerusalemu.” 20 “Tsono inu anthu a ku Yerusalemu, pitani ku mapiri a Lebanoni kuti mukalire mofuwula kumeneko,mawu anu akamveke mpaka ku Basani.Mulire mofuwula muli ku Abarimuchifukwa abwenzi ako onse awonongeka. 21 Ndinakuchenjezani pamene munali pa mtendere.Koma inu munati, ‘Sindidzamvera.’Umu ndi mmene mwakhala mukuchitira kuyambira mukali aangʼono.Simunandimvere Ine. 22 Mphepo idzakuchotserani abusa anu onse,ndipo abwenzi anu adzatengedwa ku ukapolo.Pamenepo mudzachita manyazi ndi kunyozedwachifukwa cha zoyipa zanu zonse. 23 Inu amene mumakhala mʼnyumba ya ku Lebanoni,amene munamanga nyumba zanu pakati pa mikungudza,mudzabuwula kwambiri pamene zowawa zidzakugwerani,zonga za mkazi pa nthawi yake yochira! 24 “Pali Ine wamoyo, akutero Yehova, ngakhale iwe, Yehoyakini mwana wa Yehoyakimu mfumu ya ku Yuda, ukanakhala ngati mphete ya ku dzanja langa lamanja, ndikanakuvula nʼkukutaya. 25 Ndidzakupereka kwa amene akufuna kukupha, amene iwe umawaopa. Ndidzakupereka kwa Nebukadinezara, mfumu ya ku Babuloni ndi anthu ake. 26 Iwe pamodzi ndi amayi ako amene anakubereka ndidzakupititsani ku dziko lachilendo. Ngakhale inu simunabadwire kumeneko, komabe mudzafera komweko. 27 Simudzabwereranso ku dziko limene mudzafuna kubwerera.” 28 Kodi Yehoyakini wakhala ngati mbiya yonyozeka,yosweka imene anthu sakuyifunanso?Kodi nʼchifukwa chake iye pamodzi ndi ana ake,achotsedwa nʼkutayidwa ku dziko limene iwo sakulidziwa? 29 Iwe dziko, dziko, dziko,Imva mawu a Yehova! 30 Yehova akuti,“Munthu ameneyu mumutenge ngati wopanda ana,munthu amene sadzakhala wochita bwino pamoyo wake wonse,pakuti palibe ndi mmodzi yemwe mwa zidzukulu zake zomwe zidzachita bwino.Palibe amene adzathe kukhala pa mpando waufumu wa Davidendi kulamulira Yuda.”

In Other Versions

Jeremiah 22 in the ANGEFD

Jeremiah 22 in the ANTPNG2D

Jeremiah 22 in the AS21

Jeremiah 22 in the BAGH

Jeremiah 22 in the BBPNG

Jeremiah 22 in the BBT1E

Jeremiah 22 in the BDS

Jeremiah 22 in the BEV

Jeremiah 22 in the BHAD

Jeremiah 22 in the BIB

Jeremiah 22 in the BLPT

Jeremiah 22 in the BNT

Jeremiah 22 in the BNTABOOT

Jeremiah 22 in the BNTLV

Jeremiah 22 in the BOATCB

Jeremiah 22 in the BOATCB2

Jeremiah 22 in the BOBCV

Jeremiah 22 in the BOCNT

Jeremiah 22 in the BOECS

Jeremiah 22 in the BOHCB

Jeremiah 22 in the BOHCV

Jeremiah 22 in the BOHLNT

Jeremiah 22 in the BOHNTLTAL

Jeremiah 22 in the BOICB

Jeremiah 22 in the BOILNTAP

Jeremiah 22 in the BOITCV

Jeremiah 22 in the BOKCV

Jeremiah 22 in the BOKCV2

Jeremiah 22 in the BOKHWOG

Jeremiah 22 in the BOKSSV

Jeremiah 22 in the BOLCB

Jeremiah 22 in the BOLCB2

Jeremiah 22 in the BOMCV

Jeremiah 22 in the BONAV

Jeremiah 22 in the BONCB

Jeremiah 22 in the BONLT

Jeremiah 22 in the BONUT2

Jeremiah 22 in the BOPLNT

Jeremiah 22 in the BOSCB

Jeremiah 22 in the BOSNC

Jeremiah 22 in the BOTLNT

Jeremiah 22 in the BOVCB

Jeremiah 22 in the BOYCB

Jeremiah 22 in the BPBB

Jeremiah 22 in the BPH

Jeremiah 22 in the BSB

Jeremiah 22 in the CCB

Jeremiah 22 in the CUV

Jeremiah 22 in the CUVS

Jeremiah 22 in the DBT

Jeremiah 22 in the DGDNT

Jeremiah 22 in the DHNT

Jeremiah 22 in the DNT

Jeremiah 22 in the ELBE

Jeremiah 22 in the EMTV

Jeremiah 22 in the ESV

Jeremiah 22 in the FBV

Jeremiah 22 in the FEB

Jeremiah 22 in the GGMNT

Jeremiah 22 in the GNT

Jeremiah 22 in the HARY

Jeremiah 22 in the HNT

Jeremiah 22 in the IRVA

Jeremiah 22 in the IRVB

Jeremiah 22 in the IRVG

Jeremiah 22 in the IRVH

Jeremiah 22 in the IRVK

Jeremiah 22 in the IRVM

Jeremiah 22 in the IRVM2

Jeremiah 22 in the IRVO

Jeremiah 22 in the IRVP

Jeremiah 22 in the IRVT

Jeremiah 22 in the IRVT2

Jeremiah 22 in the IRVU

Jeremiah 22 in the ISVN

Jeremiah 22 in the JSNT

Jeremiah 22 in the KAPI

Jeremiah 22 in the KBT1ETNIK

Jeremiah 22 in the KBV

Jeremiah 22 in the KJV

Jeremiah 22 in the KNFD

Jeremiah 22 in the LBA

Jeremiah 22 in the LBLA

Jeremiah 22 in the LNT

Jeremiah 22 in the LSV

Jeremiah 22 in the MAAL

Jeremiah 22 in the MBV

Jeremiah 22 in the MBV2

Jeremiah 22 in the MHNT

Jeremiah 22 in the MKNFD

Jeremiah 22 in the MNG

Jeremiah 22 in the MNT

Jeremiah 22 in the MNT2

Jeremiah 22 in the MRS1T

Jeremiah 22 in the NAA

Jeremiah 22 in the NASB

Jeremiah 22 in the NBLA

Jeremiah 22 in the NBS

Jeremiah 22 in the NBVTP

Jeremiah 22 in the NET2

Jeremiah 22 in the NIV11

Jeremiah 22 in the NNT

Jeremiah 22 in the NNT2

Jeremiah 22 in the NNT3

Jeremiah 22 in the PDDPT

Jeremiah 22 in the PFNT

Jeremiah 22 in the RMNT

Jeremiah 22 in the SBIAS

Jeremiah 22 in the SBIBS

Jeremiah 22 in the SBIBS2

Jeremiah 22 in the SBICS

Jeremiah 22 in the SBIDS

Jeremiah 22 in the SBIGS

Jeremiah 22 in the SBIHS

Jeremiah 22 in the SBIIS

Jeremiah 22 in the SBIIS2

Jeremiah 22 in the SBIIS3

Jeremiah 22 in the SBIKS

Jeremiah 22 in the SBIKS2

Jeremiah 22 in the SBIMS

Jeremiah 22 in the SBIOS

Jeremiah 22 in the SBIPS

Jeremiah 22 in the SBISS

Jeremiah 22 in the SBITS

Jeremiah 22 in the SBITS2

Jeremiah 22 in the SBITS3

Jeremiah 22 in the SBITS4

Jeremiah 22 in the SBIUS

Jeremiah 22 in the SBIVS

Jeremiah 22 in the SBT

Jeremiah 22 in the SBT1E

Jeremiah 22 in the SCHL

Jeremiah 22 in the SNT

Jeremiah 22 in the SUSU

Jeremiah 22 in the SUSU2

Jeremiah 22 in the SYNO

Jeremiah 22 in the TBIAOTANT

Jeremiah 22 in the TBT1E

Jeremiah 22 in the TBT1E2

Jeremiah 22 in the TFTIP

Jeremiah 22 in the TFTU

Jeremiah 22 in the TGNTATF3T

Jeremiah 22 in the THAI

Jeremiah 22 in the TNFD

Jeremiah 22 in the TNT

Jeremiah 22 in the TNTIK

Jeremiah 22 in the TNTIL

Jeremiah 22 in the TNTIN

Jeremiah 22 in the TNTIP

Jeremiah 22 in the TNTIZ

Jeremiah 22 in the TOMA

Jeremiah 22 in the TTENT

Jeremiah 22 in the UBG

Jeremiah 22 in the UGV

Jeremiah 22 in the UGV2

Jeremiah 22 in the UGV3

Jeremiah 22 in the VBL

Jeremiah 22 in the VDCC

Jeremiah 22 in the YALU

Jeremiah 22 in the YAPE

Jeremiah 22 in the YBVTP

Jeremiah 22 in the ZBP