Jeremiah 34 (BOGWICC)

1 Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni ndi gulu lake lonse lankhondo, pamodzi ndi maufumu onse a pa dziko lapansi amene ankawalamulira ndiponso anthu a mitundu yonse ankathira nkhondo Yerusalemu ndi mizinda yonse yozungulira Yehova anayankhula ndi Yeremiya kuti, 2 “Yehova, Mulungu wa Israeli akuti: Pita kwa Zedekiya mfumu ya Yuda ndipo ukamuwuze kuti Yehova akuti mzinda uno ndidzawupereka mʼmanja mwa mfumu ya ku Babuloni ndipo adzawutentha ndi moto. 3 Iweyo sudzapulumuka mʼmanja mwake koma udzagwidwa ndithu ndipo adzakupereka mʼmanja mwake. Udzayiona mfumu ya ku Babuloni maso ndi maso ako ndipo udzayankhula nayo pakamwa ndi pakamwa. Ndipo udzapita ku Babuloni. 4 “Koma iwe Zedekiya mfumu ya Yuda, imva lonjezo ili la Yehova. Izi ndi zimene Yehova akunena za iwe: Sudzaphedwa pa nkhondo; 5 udzafera pa mtendere. Monga anthu ankafukiza lubani poyika maliro a makolo ako akale, amene anali mafumu iwe usanalowe ufumu, choncho nawenso podzayika maliro ako adzafukiza lubani ndipo polira azidzati, ‘Kalanga, mbuye wanga!’ Ine mwini ndalonjeza zimenezi, akutero Yehova.” 6 Ndipo mneneri Yeremiya anawuza zonsezi Zedekiya mfumu ya Yuda, mu Yerusalemu. 7 Nthawi imeneyi nʼkuti gulu lankhondo la mfumu ya ku Babuloni likuthira nkhondo Yerusalemu ndi mizinda ina yotsala ya Yuda, Lakisi ndi Azeka. Imeneyi yokha ndiye inali mizinda yotetezedwa yotsala ya ku Yuda. 8 Yehova anayankhulanso ndi Yeremiya. Nthawi imeneyi nʼkuti mfumu Zedekiya atachita pangano ndi anthu onse a mu Yerusalemu kuti alengeze zakuti akapolo awo adzawamasule. 9 Aliyense amene anali ndi akapolo a Chihebri, aamuna kapena aakazi awamasule; palibe amene ayenera kusunga mu ukapolo Myuda mnzake. 10 Choncho akuluakulu pamodzi ndi anthu onse amene anachita pangano ili anagwirizana kuti amasule akapolo awo aamuna ndi aakazi ndi kuti asawasungenso mu ukapolo. Iwo anachitadi zimenezi ndipo anawamasuladi. 11 Koma pambuyo pake anasintha maganizo awo ndi kuwatenganso amuna ndi akazi amene anawamasula aja ndipo anawasandutsanso akapolo. 12 Tsono Yehova anawuza Yeremiya kuti: 13 “Yehova Mulungu wa Israeli akuti: Ine ndinachita pangano ndi makolo anu pamene ndinawatulutsa ku Igupto, mʼdziko la ukapolo. Ine ndinati, 14 ‘Chaka chachisanu ndi chiwiri chilichonse aliyense wa inu ayenera kumasula mʼbale wake wa Chihebri amene anadzigulitsa yekha kwa inuyo. Iyeyo amasulidwe akagwira ntchito zaka zisanu ndi chimodzi, mumulole apite mwaufulu.’ Komatu makolo anu sanandimvere kapena kusamala konse. 15 Posachedwa pomwepa inu munalapa ndi kuchita zinthu zabwino pamaso panga: Aliyense wa inu anamasula mʼbale wake. Ndipo munachita pangano pamaso panga mʼNyumba imene imadziwika ndi dzina langa kuti mudzachitadi zimenezi. 16 Koma tsopano mwasintha maganizo anu ndipo mwayipitsa dzina langa. Mwatenganso ukapolo aamuna ndi aakazi amene munawamasula aja kuti apite kumene akufuna. Mwawakakamiza kuti akhalebe akapolo anu. 17 “Nʼchifukwa chake Yehova akuti: Inu simunandimvere Ine; simunalengeze kuti abale anu amasulidwe. Chabwino! Ine ndidzakupatsani ufulu; ufulu wake ukhala wophedwa ndi nkhondo, mliri ndi njala. Ndidzakusandutsani chinthu chochititsa mantha pakati pa maufumu onse a dziko lapansi. 18 Inu simunasunge pangano limene munachita ndi Ine. Simunasamale lonjezo limene munachita pamaso panga. Choncho ndidzakusandutsani ngati mwana wangʼombe uja amene ankamudula pawiri napita pakati pa zigawozo. 19 Amene ankadutsa pakati pa zigawozo anali atsogoleri a Yuda ndi Yerusalemu, akuluakulu a bwalo, ansembe ndi anthu onse a mʼdzikomo. 20 Onsewa ndidzawapereka kwa adani awo amene akufuna kuwapha. Mitembo yawo idzakhala chakudya cha mbalame zamlengalenga ndi zirombo za dziko lapansi. 21 “Ndidzapereka Zedekiya mfumu ya Yuda ndi nduna zake kwa adani awo amene akufuna kuwapha, kwa gulu lankhondo la mfumu ya ku Babuloni limene nthawi ino layamba kubwerera mʼmbuyo. 22 Taonani, Ine ndidzawalamula, akutero Yehova, ndipo ndidzawabweretsanso ku mzinda uno. Adzathira nkhondo mzindawu, kuwulanda ndi kuwutentha. Ndipo Ine ndidzasandutsa chipululu mizinda ya Yuda kotero kuti palibe amene adzakhalemo.”

In Other Versions

Jeremiah 34 in the ANGEFD

Jeremiah 34 in the ANTPNG2D

Jeremiah 34 in the AS21

Jeremiah 34 in the BAGH

Jeremiah 34 in the BBPNG

Jeremiah 34 in the BBT1E

Jeremiah 34 in the BDS

Jeremiah 34 in the BEV

Jeremiah 34 in the BHAD

Jeremiah 34 in the BIB

Jeremiah 34 in the BLPT

Jeremiah 34 in the BNT

Jeremiah 34 in the BNTABOOT

Jeremiah 34 in the BNTLV

Jeremiah 34 in the BOATCB

Jeremiah 34 in the BOATCB2

Jeremiah 34 in the BOBCV

Jeremiah 34 in the BOCNT

Jeremiah 34 in the BOECS

Jeremiah 34 in the BOHCB

Jeremiah 34 in the BOHCV

Jeremiah 34 in the BOHLNT

Jeremiah 34 in the BOHNTLTAL

Jeremiah 34 in the BOICB

Jeremiah 34 in the BOILNTAP

Jeremiah 34 in the BOITCV

Jeremiah 34 in the BOKCV

Jeremiah 34 in the BOKCV2

Jeremiah 34 in the BOKHWOG

Jeremiah 34 in the BOKSSV

Jeremiah 34 in the BOLCB

Jeremiah 34 in the BOLCB2

Jeremiah 34 in the BOMCV

Jeremiah 34 in the BONAV

Jeremiah 34 in the BONCB

Jeremiah 34 in the BONLT

Jeremiah 34 in the BONUT2

Jeremiah 34 in the BOPLNT

Jeremiah 34 in the BOSCB

Jeremiah 34 in the BOSNC

Jeremiah 34 in the BOTLNT

Jeremiah 34 in the BOVCB

Jeremiah 34 in the BOYCB

Jeremiah 34 in the BPBB

Jeremiah 34 in the BPH

Jeremiah 34 in the BSB

Jeremiah 34 in the CCB

Jeremiah 34 in the CUV

Jeremiah 34 in the CUVS

Jeremiah 34 in the DBT

Jeremiah 34 in the DGDNT

Jeremiah 34 in the DHNT

Jeremiah 34 in the DNT

Jeremiah 34 in the ELBE

Jeremiah 34 in the EMTV

Jeremiah 34 in the ESV

Jeremiah 34 in the FBV

Jeremiah 34 in the FEB

Jeremiah 34 in the GGMNT

Jeremiah 34 in the GNT

Jeremiah 34 in the HARY

Jeremiah 34 in the HNT

Jeremiah 34 in the IRVA

Jeremiah 34 in the IRVB

Jeremiah 34 in the IRVG

Jeremiah 34 in the IRVH

Jeremiah 34 in the IRVK

Jeremiah 34 in the IRVM

Jeremiah 34 in the IRVM2

Jeremiah 34 in the IRVO

Jeremiah 34 in the IRVP

Jeremiah 34 in the IRVT

Jeremiah 34 in the IRVT2

Jeremiah 34 in the IRVU

Jeremiah 34 in the ISVN

Jeremiah 34 in the JSNT

Jeremiah 34 in the KAPI

Jeremiah 34 in the KBT1ETNIK

Jeremiah 34 in the KBV

Jeremiah 34 in the KJV

Jeremiah 34 in the KNFD

Jeremiah 34 in the LBA

Jeremiah 34 in the LBLA

Jeremiah 34 in the LNT

Jeremiah 34 in the LSV

Jeremiah 34 in the MAAL

Jeremiah 34 in the MBV

Jeremiah 34 in the MBV2

Jeremiah 34 in the MHNT

Jeremiah 34 in the MKNFD

Jeremiah 34 in the MNG

Jeremiah 34 in the MNT

Jeremiah 34 in the MNT2

Jeremiah 34 in the MRS1T

Jeremiah 34 in the NAA

Jeremiah 34 in the NASB

Jeremiah 34 in the NBLA

Jeremiah 34 in the NBS

Jeremiah 34 in the NBVTP

Jeremiah 34 in the NET2

Jeremiah 34 in the NIV11

Jeremiah 34 in the NNT

Jeremiah 34 in the NNT2

Jeremiah 34 in the NNT3

Jeremiah 34 in the PDDPT

Jeremiah 34 in the PFNT

Jeremiah 34 in the RMNT

Jeremiah 34 in the SBIAS

Jeremiah 34 in the SBIBS

Jeremiah 34 in the SBIBS2

Jeremiah 34 in the SBICS

Jeremiah 34 in the SBIDS

Jeremiah 34 in the SBIGS

Jeremiah 34 in the SBIHS

Jeremiah 34 in the SBIIS

Jeremiah 34 in the SBIIS2

Jeremiah 34 in the SBIIS3

Jeremiah 34 in the SBIKS

Jeremiah 34 in the SBIKS2

Jeremiah 34 in the SBIMS

Jeremiah 34 in the SBIOS

Jeremiah 34 in the SBIPS

Jeremiah 34 in the SBISS

Jeremiah 34 in the SBITS

Jeremiah 34 in the SBITS2

Jeremiah 34 in the SBITS3

Jeremiah 34 in the SBITS4

Jeremiah 34 in the SBIUS

Jeremiah 34 in the SBIVS

Jeremiah 34 in the SBT

Jeremiah 34 in the SBT1E

Jeremiah 34 in the SCHL

Jeremiah 34 in the SNT

Jeremiah 34 in the SUSU

Jeremiah 34 in the SUSU2

Jeremiah 34 in the SYNO

Jeremiah 34 in the TBIAOTANT

Jeremiah 34 in the TBT1E

Jeremiah 34 in the TBT1E2

Jeremiah 34 in the TFTIP

Jeremiah 34 in the TFTU

Jeremiah 34 in the TGNTATF3T

Jeremiah 34 in the THAI

Jeremiah 34 in the TNFD

Jeremiah 34 in the TNT

Jeremiah 34 in the TNTIK

Jeremiah 34 in the TNTIL

Jeremiah 34 in the TNTIN

Jeremiah 34 in the TNTIP

Jeremiah 34 in the TNTIZ

Jeremiah 34 in the TOMA

Jeremiah 34 in the TTENT

Jeremiah 34 in the UBG

Jeremiah 34 in the UGV

Jeremiah 34 in the UGV2

Jeremiah 34 in the UGV3

Jeremiah 34 in the VBL

Jeremiah 34 in the VDCC

Jeremiah 34 in the YALU

Jeremiah 34 in the YAPE

Jeremiah 34 in the YBVTP

Jeremiah 34 in the ZBP