Jeremiah 37 (BOGWICC)
1 Nebukadinezara mfumu ya Babuloni, inakhazika pa mpando waufumu Zedekiya mwana wa Yosiya kukhala mfumu ya Yuda. Iye analowa mʼmalo mwa Yehoyakini mwana wa Yehoyakimu. 2 Koma Zedekiya kapena atumiki ake ngakhalenso anthu a mʼdzikomo sanasamalire mawu a Yehova amene anayankhula kudzera mwa mneneri Yeremiya. 3 Tsono Zedekiya anatuma Yehukali mwana wa Selemiya ndi wansembe Zefaniya mwana wa Maseya kwa mneneri Yeremiya ndi uthenga uwu: “Chonde tipempherereni kwa Yehova Mulungu wathu.” 4 Nthawi imeneyinso nʼkuti Yeremiya ali ndi ufulu woyenda pakati pa anthu chifukwa anali asanaponyedwe mʼndende. 5 Nthawi imeneyinso nʼkuti gulu lankhondo la Farao litatuluka mʼdziko la Igupto. Ndipo Ababuloni amene anali atazinga Yerusalemu atamva zimenezi, anachoka ku Yerusalemuko. 6 Tsono Yehova anawuza mneneri Yeremiya kuti, 7 “Uyiwuze mfumu ya Yuda imene inakutuma kuti udzapemphe nzeru kwa ine kuti Ine Yehova, Mulungu wa Israeli ndikuti, gulu lankhondo la Farao limene linatuluka kuti lidzakuthandize lidzabwerera kwawo ku Igupto. 8 Ndipo Ababuloni adzabwerera kudzathira nkhondo mzinda uno. Iwo adzawugonjetsa ndi kuwutentha. 9 “Yehova akuti: Musadzinyenge, nʼkumaganiza kuti, ‘Ndithu Ababuloni adzatisiya.’ Ndithudi sadzakusiyani! 10 Ngakhale mutagonjetsa gulu lonse lankhondo la Ababuloni limene likukuthirani nkhondo ndipo mʼmatenti mwawo ndikutsala anthu ovulala okhaokha, amenewo adzabwera ndi kudzatentha mzinda uno.” 11 Gulu lankhondo la Ababuloni litaleka kuthira nkhondo mzinda wa Yerusalemu chifukwa choopa gulu lankhondo la Farao, 12 Yeremiya ananyamuka kuchoka ku Yerusalemu ndi kumapita ku dziko la Benjamini kuti akalandire gawo lake la minda ya makolo ake. 13 Koma atafika pa Chipata cha Benjamini, mkulu wa alonda amene dzina lake linali Iriya mwana wa Selemiya, mwana wa Hananiya, anagwira mneneri Yeremiyayo ndipo anati, “Iwe ukuthawira kwa Ababuloni!” 14 Yeremiya anati, “Zimenezo si zoona! Ine sindikuthawira kwa Ababuloni.” Koma Iriya sanamumvere. Mʼmalo mwake anagwira Yeremiya nʼkupita naye kwa akuluakulu. 15 Akuluakuluwo anamupsera mtima Yeremiya ndipo anamukwapula ndi kumuyika mʼnyumba ya mlembi Yonatani, imene anayisandutsa ndende. 16 Yeremiya anayikidwa mʼndende ya pansi pa nthaka, kumene anakhalako nthawi yayitali. 17 Kenaka Mfumu Zedekiya inatuma anthu kuti akayitane Yeremiya ndipo anabwera naye ku nyumba ya mfumu. Atafika mfumu inamufunsa mwamseri kuti, “Kodi pali mawu ena amene Yehova wakuwuza?”Yeremiya anayankha kuti, “Inde. Inu mfumu mudzaperekedwa kwa mfumu ya ku Babuloni.” 18 Pamenepo Yeremiya anafunsa Mfumu Zedekiya kuti, “Kodi ndakulakwirani chiyani inuyo kapena akuluakulu anu kapenanso anthu awa, kuti mundiyike mʼndende? 19 Kodi ali kuti aneneri anu amene anakuloserani kuti, ‘Mfumu ya ku Babuloni sidzakuthirani nkhondo pamodzi ndi dziko lino’? 20 Koma tsopano, mbuye wanga mfumu, chonde tamverani. Loleni ndinene pempho langa pamaso panu: Musandibwezere ku nyumba ya mlembi Yonatani, kuopa kuti ndingakafere kumeneko.” 21 Tsono Mfumu Zedekiya analamula kuti Yeremiya asungidwe mʼbwalo la alonda. Ankamupatsa buledi tsiku ndi tsiku amene ankamugula kwa ophika buledi. Anapitiriza kutero mpaka buledi yense anatha mu mzindamo. Choncho Yeremiya anapitirira kukhala mʼbwalo la alonda.
In Other Versions
Jeremiah 37 in the ANGEFD
Jeremiah 37 in the ANTPNG2D
Jeremiah 37 in the AS21
Jeremiah 37 in the BAGH
Jeremiah 37 in the BBPNG
Jeremiah 37 in the BBT1E
Jeremiah 37 in the BDS
Jeremiah 37 in the BEV
Jeremiah 37 in the BHAD
Jeremiah 37 in the BIB
Jeremiah 37 in the BLPT
Jeremiah 37 in the BNT
Jeremiah 37 in the BNTABOOT
Jeremiah 37 in the BNTLV
Jeremiah 37 in the BOATCB
Jeremiah 37 in the BOATCB2
Jeremiah 37 in the BOBCV
Jeremiah 37 in the BOCNT
Jeremiah 37 in the BOECS
Jeremiah 37 in the BOHCB
Jeremiah 37 in the BOHCV
Jeremiah 37 in the BOHLNT
Jeremiah 37 in the BOHNTLTAL
Jeremiah 37 in the BOICB
Jeremiah 37 in the BOILNTAP
Jeremiah 37 in the BOITCV
Jeremiah 37 in the BOKCV
Jeremiah 37 in the BOKCV2
Jeremiah 37 in the BOKHWOG
Jeremiah 37 in the BOKSSV
Jeremiah 37 in the BOLCB
Jeremiah 37 in the BOLCB2
Jeremiah 37 in the BOMCV
Jeremiah 37 in the BONAV
Jeremiah 37 in the BONCB
Jeremiah 37 in the BONLT
Jeremiah 37 in the BONUT2
Jeremiah 37 in the BOPLNT
Jeremiah 37 in the BOSCB
Jeremiah 37 in the BOSNC
Jeremiah 37 in the BOTLNT
Jeremiah 37 in the BOVCB
Jeremiah 37 in the BOYCB
Jeremiah 37 in the BPBB
Jeremiah 37 in the BPH
Jeremiah 37 in the BSB
Jeremiah 37 in the CCB
Jeremiah 37 in the CUV
Jeremiah 37 in the CUVS
Jeremiah 37 in the DBT
Jeremiah 37 in the DGDNT
Jeremiah 37 in the DHNT
Jeremiah 37 in the DNT
Jeremiah 37 in the ELBE
Jeremiah 37 in the EMTV
Jeremiah 37 in the ESV
Jeremiah 37 in the FBV
Jeremiah 37 in the FEB
Jeremiah 37 in the GGMNT
Jeremiah 37 in the GNT
Jeremiah 37 in the HARY
Jeremiah 37 in the HNT
Jeremiah 37 in the IRVA
Jeremiah 37 in the IRVB
Jeremiah 37 in the IRVG
Jeremiah 37 in the IRVH
Jeremiah 37 in the IRVK
Jeremiah 37 in the IRVM
Jeremiah 37 in the IRVM2
Jeremiah 37 in the IRVO
Jeremiah 37 in the IRVP
Jeremiah 37 in the IRVT
Jeremiah 37 in the IRVT2
Jeremiah 37 in the IRVU
Jeremiah 37 in the ISVN
Jeremiah 37 in the JSNT
Jeremiah 37 in the KAPI
Jeremiah 37 in the KBT1ETNIK
Jeremiah 37 in the KBV
Jeremiah 37 in the KJV
Jeremiah 37 in the KNFD
Jeremiah 37 in the LBA
Jeremiah 37 in the LBLA
Jeremiah 37 in the LNT
Jeremiah 37 in the LSV
Jeremiah 37 in the MAAL
Jeremiah 37 in the MBV
Jeremiah 37 in the MBV2
Jeremiah 37 in the MHNT
Jeremiah 37 in the MKNFD
Jeremiah 37 in the MNG
Jeremiah 37 in the MNT
Jeremiah 37 in the MNT2
Jeremiah 37 in the MRS1T
Jeremiah 37 in the NAA
Jeremiah 37 in the NASB
Jeremiah 37 in the NBLA
Jeremiah 37 in the NBS
Jeremiah 37 in the NBVTP
Jeremiah 37 in the NET2
Jeremiah 37 in the NIV11
Jeremiah 37 in the NNT
Jeremiah 37 in the NNT2
Jeremiah 37 in the NNT3
Jeremiah 37 in the PDDPT
Jeremiah 37 in the PFNT
Jeremiah 37 in the RMNT
Jeremiah 37 in the SBIAS
Jeremiah 37 in the SBIBS
Jeremiah 37 in the SBIBS2
Jeremiah 37 in the SBICS
Jeremiah 37 in the SBIDS
Jeremiah 37 in the SBIGS
Jeremiah 37 in the SBIHS
Jeremiah 37 in the SBIIS
Jeremiah 37 in the SBIIS2
Jeremiah 37 in the SBIIS3
Jeremiah 37 in the SBIKS
Jeremiah 37 in the SBIKS2
Jeremiah 37 in the SBIMS
Jeremiah 37 in the SBIOS
Jeremiah 37 in the SBIPS
Jeremiah 37 in the SBISS
Jeremiah 37 in the SBITS
Jeremiah 37 in the SBITS2
Jeremiah 37 in the SBITS3
Jeremiah 37 in the SBITS4
Jeremiah 37 in the SBIUS
Jeremiah 37 in the SBIVS
Jeremiah 37 in the SBT
Jeremiah 37 in the SBT1E
Jeremiah 37 in the SCHL
Jeremiah 37 in the SNT
Jeremiah 37 in the SUSU
Jeremiah 37 in the SUSU2
Jeremiah 37 in the SYNO
Jeremiah 37 in the TBIAOTANT
Jeremiah 37 in the TBT1E
Jeremiah 37 in the TBT1E2
Jeremiah 37 in the TFTIP
Jeremiah 37 in the TFTU
Jeremiah 37 in the TGNTATF3T
Jeremiah 37 in the THAI
Jeremiah 37 in the TNFD
Jeremiah 37 in the TNT
Jeremiah 37 in the TNTIK
Jeremiah 37 in the TNTIL
Jeremiah 37 in the TNTIN
Jeremiah 37 in the TNTIP
Jeremiah 37 in the TNTIZ
Jeremiah 37 in the TOMA
Jeremiah 37 in the TTENT
Jeremiah 37 in the UBG
Jeremiah 37 in the UGV
Jeremiah 37 in the UGV2
Jeremiah 37 in the UGV3
Jeremiah 37 in the VBL
Jeremiah 37 in the VDCC
Jeremiah 37 in the YALU
Jeremiah 37 in the YAPE
Jeremiah 37 in the YBVTP
Jeremiah 37 in the ZBP