Jeremiah 38 (BOGWICC)

1 Sefatiya mwana wa Matani, Gedaliya mwana wa Pasi-Huri, Yukali mwana wa Selemiya, ndi Pasi-Huri mwana wa Malikiya anamva zimene Yeremiya ankawuza anthu onse kuti, 2 “Yehova akuti, ‘Aliyense amene akhale mu mzinda muno adzafa ndi nkhondo njala kapena mliri. Koma aliyense amene atatuluke kukadzipereka kwa Ababuloni adzapulumutsa moyo wake; iyeyo adzakhala ndi moyo. 3 Mzinda uno udzaperekedwa ndithu kwa gulu lankhondo la mfumu ya ku Babuloni, amene adzawulande.’ ” 4 Tsono akuluakuluwo anawuza mfumu kuti, “Munthu uyu ayenera kuphedwa. Iye akutayitsa mtima asilikali pamodzi ndi anthu onse amene atsala mu mzinda muno, chifukwa cha zimene akuwawuza. Munthu ameneyu sakufunira zabwino anthuwa koma chiwonongeko chawo.” 5 Mfumu Zedekiya anayankha kuti, “Munthuyu ali mʼmanja mwanu. Ine sindingakuletseni chimene mukufuna kumuchitira.” 6 Choncho iwo anatenga Yeremiya nakamuponya mʼchitsime cha Malikiya, mwana wa mfumu, chimene chinali mʼbwalo la alonda. Iwo anamutsitsira mʼdzenjemo ndi chingwe. Munalibe madzi koma matope okhaokha, ndipo Yeremiya anamira mʼmatopewo. 7 Koma Ebedi-Meleki, Mkusi, mmodzi mwa anthu ofulidwa ogwira ntchito mʼnyumba ya mfumu, anamva kuti Yeremiya anamuponya mʼchitsime. Nthawi imeneyo nʼkuti mfumu ili ku chipata cha Benjamini. 8 Ebedi-Meleki anatuluka ku nyumba ya mfumu kukayiwuza kuti, 9 “Mbuye wanga mfumu, zimene anthu awa amuchitira mneneri Yeremiya ndi zoyipa kwambiri. Iwo amuponya mʼchitsime, ndipo adzafa ndi njala chifukwa buledi watha mu mzinda muno.” 10 Tsono mfumu inalamula Ebedi-Meleki, Mkusi, kuti, “Tenga anthu makumi atatu, ndipo mukamutulutse mʼchitsimemo mneneri Yeremiya asanafe.” 11 Pamenepo Ebedi-Meleki anatenga anthuwo, napita nawo ku nyumba ya mfumu ya pansi pa chipinda chosungiramo chuma. Kumeneko anakatengako sanza ndipo anatsitsira sanzazo ndi chingwe mʼchitsime mʼmene munali Yeremiya. 12 Ebedi-Meleki, Mkusi, anawuza Yeremiya kuti, “Ika sanzazo mkwapa mwako kuti zingwe zingakupweteke.” Yeremiya anachitadi zimenezi, 13 ndipo anamukoka ndi zingwe ndi kumutulutsa mʼchitsimecho. Ndipo Yeremiya anakhalabe ku bwalo la alonda. 14 Tsiku lina Mfumu Zedekiya anayitana mneneri Yeremiya ndipo anabwera naye ku chipata chachitatu cha Nyumba ya Yehova. Mfumu inawuza Yeremiya kuti, “Ndikufuna kukufunsa kanthu kena, ndipo usandibisire chilichonse.” 15 Yeremiya anati kwa Zedekiya, “Ndikakuyankhani, kodi simundipha? Ngakhaletu ine nditakulangizani, inu simudzandimvera.” 16 Koma Mfumu Zedekiya mwachinsinsi inalumbira kwa Yeremiya kuti, “Pali Yehova wamoyo, amene amatipatsa moyo, sindidzakupha ngakhalenso kukupereka kwa amene akufuna kukuphawa.” 17 Pamenepo Yeremiya anati kwa Zedekiya, “Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti, ‘Ngati mutuluka kukadzipereka kwa ankhondo a mfumu ya ku Babuloni, mudzakhala ndi moyo ndipo mzinda uno sadzawutentha, inu pamodzi ndi banja lanu mudzakhala ndi moyo. 18 Koma ngati simutuluka kukadzipereka kwa ankhondo a mfumu ya ku Babuloni, mzinda uno udzaperekedwa kwa Ababuloni ndipo adzawutentha; inuyo simudzapulumuka mʼdzanja mwawo.’ ” 19 Mfumu Zedekiya inati kwa Yeremiya, “Ine ndikuopa Ayuda amene anathawira kale kwa Ababuloni, pakuti mwina Ababuloniwo adzandipereka kwa Ayudawo ndipo iwowo adzandizunza.” 20 Yeremiya anayankha kuti, “Ngati mumvera Yehova ndi kuchita zimene ndakuwuzani, ndiye kuti zinthu zidzakuyenderani bwino. Inu simudzaphedwa. 21 Koma mukakana kudzipereka, chimene Yehova wandiwululira ndi ichi: 22 Akazi onse amene atsala mʼnyumba ya mfumu ya Yuda adzaperekedwa kwa akuluakulu a mfumu ya ku Babuloni. Akazi amenewo adzakuwuzani kuti,“ ‘Abwenzi ako okhulupirika aja anakusokeretsa,ndipo anakugonjetsa.Poti tsopano miyendo yako yazama mʼmatope;abwenzi ako aja akusiya.’ 23 “Akazi pamodzi ndi ana anu adzaperekedwa kwa Ababuloni. Inuyo simudzapulumuka mʼmanja mwawo koma mfumu ya ku Babuloni idzakugwirani; mzinda uno adzawutentha.” 24 Pamenepo Zedekiya anati kwa Yeremiya, “Usawuze munthu wina aliyense zimene takambiranazi, ukatero udzaphedwa. 25 Akuluakulu akamva kuti ndinayankhula nawe ndipo akabwera kwa iwe nʼkudzakufunsa kuti, ‘Tiwuze zimene unanena kwa mfumu ndi zimene mfumu inanena kwa iwe; usatibisire, ukatero tidzakupha,’ 26 udzawawuze kuti, ‘Ine ndimapempha mfumu kuti isandibwezerenso ku nyumba ya Yonatani kuti ndikafere kumeneko.’ ” 27 Akuluakulu onse anabweradi kwa Yeremiya kudzamufunsa. Iye anawayankha monga momwe mfumu inamulamula. Choncho palibe amene ananenanso kanthu, pakuti palibe amene anamva zomwe anakambirana ndi mfumu. 28 Ndipo Yeremiya anakhalabe mʼbwalo la alonda mpaka tsiku limene mzinda wa Yerusalemu unalandidwa.

In Other Versions

Jeremiah 38 in the ANGEFD

Jeremiah 38 in the ANTPNG2D

Jeremiah 38 in the AS21

Jeremiah 38 in the BAGH

Jeremiah 38 in the BBPNG

Jeremiah 38 in the BBT1E

Jeremiah 38 in the BDS

Jeremiah 38 in the BEV

Jeremiah 38 in the BHAD

Jeremiah 38 in the BIB

Jeremiah 38 in the BLPT

Jeremiah 38 in the BNT

Jeremiah 38 in the BNTABOOT

Jeremiah 38 in the BNTLV

Jeremiah 38 in the BOATCB

Jeremiah 38 in the BOATCB2

Jeremiah 38 in the BOBCV

Jeremiah 38 in the BOCNT

Jeremiah 38 in the BOECS

Jeremiah 38 in the BOHCB

Jeremiah 38 in the BOHCV

Jeremiah 38 in the BOHLNT

Jeremiah 38 in the BOHNTLTAL

Jeremiah 38 in the BOICB

Jeremiah 38 in the BOILNTAP

Jeremiah 38 in the BOITCV

Jeremiah 38 in the BOKCV

Jeremiah 38 in the BOKCV2

Jeremiah 38 in the BOKHWOG

Jeremiah 38 in the BOKSSV

Jeremiah 38 in the BOLCB

Jeremiah 38 in the BOLCB2

Jeremiah 38 in the BOMCV

Jeremiah 38 in the BONAV

Jeremiah 38 in the BONCB

Jeremiah 38 in the BONLT

Jeremiah 38 in the BONUT2

Jeremiah 38 in the BOPLNT

Jeremiah 38 in the BOSCB

Jeremiah 38 in the BOSNC

Jeremiah 38 in the BOTLNT

Jeremiah 38 in the BOVCB

Jeremiah 38 in the BOYCB

Jeremiah 38 in the BPBB

Jeremiah 38 in the BPH

Jeremiah 38 in the BSB

Jeremiah 38 in the CCB

Jeremiah 38 in the CUV

Jeremiah 38 in the CUVS

Jeremiah 38 in the DBT

Jeremiah 38 in the DGDNT

Jeremiah 38 in the DHNT

Jeremiah 38 in the DNT

Jeremiah 38 in the ELBE

Jeremiah 38 in the EMTV

Jeremiah 38 in the ESV

Jeremiah 38 in the FBV

Jeremiah 38 in the FEB

Jeremiah 38 in the GGMNT

Jeremiah 38 in the GNT

Jeremiah 38 in the HARY

Jeremiah 38 in the HNT

Jeremiah 38 in the IRVA

Jeremiah 38 in the IRVB

Jeremiah 38 in the IRVG

Jeremiah 38 in the IRVH

Jeremiah 38 in the IRVK

Jeremiah 38 in the IRVM

Jeremiah 38 in the IRVM2

Jeremiah 38 in the IRVO

Jeremiah 38 in the IRVP

Jeremiah 38 in the IRVT

Jeremiah 38 in the IRVT2

Jeremiah 38 in the IRVU

Jeremiah 38 in the ISVN

Jeremiah 38 in the JSNT

Jeremiah 38 in the KAPI

Jeremiah 38 in the KBT1ETNIK

Jeremiah 38 in the KBV

Jeremiah 38 in the KJV

Jeremiah 38 in the KNFD

Jeremiah 38 in the LBA

Jeremiah 38 in the LBLA

Jeremiah 38 in the LNT

Jeremiah 38 in the LSV

Jeremiah 38 in the MAAL

Jeremiah 38 in the MBV

Jeremiah 38 in the MBV2

Jeremiah 38 in the MHNT

Jeremiah 38 in the MKNFD

Jeremiah 38 in the MNG

Jeremiah 38 in the MNT

Jeremiah 38 in the MNT2

Jeremiah 38 in the MRS1T

Jeremiah 38 in the NAA

Jeremiah 38 in the NASB

Jeremiah 38 in the NBLA

Jeremiah 38 in the NBS

Jeremiah 38 in the NBVTP

Jeremiah 38 in the NET2

Jeremiah 38 in the NIV11

Jeremiah 38 in the NNT

Jeremiah 38 in the NNT2

Jeremiah 38 in the NNT3

Jeremiah 38 in the PDDPT

Jeremiah 38 in the PFNT

Jeremiah 38 in the RMNT

Jeremiah 38 in the SBIAS

Jeremiah 38 in the SBIBS

Jeremiah 38 in the SBIBS2

Jeremiah 38 in the SBICS

Jeremiah 38 in the SBIDS

Jeremiah 38 in the SBIGS

Jeremiah 38 in the SBIHS

Jeremiah 38 in the SBIIS

Jeremiah 38 in the SBIIS2

Jeremiah 38 in the SBIIS3

Jeremiah 38 in the SBIKS

Jeremiah 38 in the SBIKS2

Jeremiah 38 in the SBIMS

Jeremiah 38 in the SBIOS

Jeremiah 38 in the SBIPS

Jeremiah 38 in the SBISS

Jeremiah 38 in the SBITS

Jeremiah 38 in the SBITS2

Jeremiah 38 in the SBITS3

Jeremiah 38 in the SBITS4

Jeremiah 38 in the SBIUS

Jeremiah 38 in the SBIVS

Jeremiah 38 in the SBT

Jeremiah 38 in the SBT1E

Jeremiah 38 in the SCHL

Jeremiah 38 in the SNT

Jeremiah 38 in the SUSU

Jeremiah 38 in the SUSU2

Jeremiah 38 in the SYNO

Jeremiah 38 in the TBIAOTANT

Jeremiah 38 in the TBT1E

Jeremiah 38 in the TBT1E2

Jeremiah 38 in the TFTIP

Jeremiah 38 in the TFTU

Jeremiah 38 in the TGNTATF3T

Jeremiah 38 in the THAI

Jeremiah 38 in the TNFD

Jeremiah 38 in the TNT

Jeremiah 38 in the TNTIK

Jeremiah 38 in the TNTIL

Jeremiah 38 in the TNTIN

Jeremiah 38 in the TNTIP

Jeremiah 38 in the TNTIZ

Jeremiah 38 in the TOMA

Jeremiah 38 in the TTENT

Jeremiah 38 in the UBG

Jeremiah 38 in the UGV

Jeremiah 38 in the UGV2

Jeremiah 38 in the UGV3

Jeremiah 38 in the VBL

Jeremiah 38 in the VDCC

Jeremiah 38 in the YALU

Jeremiah 38 in the YAPE

Jeremiah 38 in the YBVTP

Jeremiah 38 in the ZBP