Jeremiah 42 (BOGWICC)
1 Atsogoleri onse a ankhondo pamodzi ndi Yohanani mwana wa Kareya ndi Azariya mwana wa Hosayia, ndiponso anthu onse, ana ndi akuluakulu omwe, anapita 2 kwa mneneri Yeremiya ndipo anamuwuza kuti, “Chonde imvani dandawulo lathu ndipo mutipempherere anthu otsalafe kwa Yehova Mulungu wanu. Pakuti monga tsopano mukuona, ngakhale kuti kale tinalipo ambiri, koma tsopano ochepa okha ndiye amene atsala. 3 Mupemphere kuti Yehova Mulungu wanu atiwuze kumene tiyenera kupita ndi chimene tiyenera kuchita.” 4 Mneneri Yeremiya anawayankha kuti, “Ndamva zimene mwanenazi. Ndithu ndidzapemphera kwa Yehova Mulungu wanu monga momwe mwandipemphera. Ndidzakuwuzani chilichonse chimene Yehova anene ndipo sindidzakubisirani kanthu kalikonse.” 5 Ndipo iwo anawuza Yeremiya kuti, “Yehova akhale mboni yoona ndi yokhulupirika yodzatitsutsa ife ngati sitichita mogwirizana ndi chilichonse chimene Yehova Mulungu adzakutumani kuti mutiwuze. 6 Kaya ndi zotikomera kapena zosatikomera, ife tidzamvera Yehova Mulungu wathu, amene takutumaniko. Tidzamvera Yehova Mulungu wathu kuti zinthu zidzatiyendere bwino.” 7 Patapita masiku khumi, Yehova anayankhula ndi Yeremiya. 8 Choncho Yeremiya anayitana Yohanani mwana wa Kareya pamodzi ndi atsogoleri onse a ankhondo amene anali naye ndiponso anthu onse, ana ndi akulu omwe. 9 Yehova, Mulungu wa Israeli amene munanditumako kuti ndikapereke madandawulo mʼdzina lanu akuti, 10 “Ngati mukhala mʼdziko muno, ndiye kuti ndidzakukhazikitsani, osakuchotsani. Inde ndidzakudzalani osakuchotsani pakuti ndi kumva chisoni kwambiri chifukwa cha mavuto amene ndabweretsa pa inu. 11 Musayiope mfumu ya ku Babuloni, imene mukuyiopa tsopano. Musachite nayo mantha, akutero Yehova, pakuti Ine ndili nanu ndipo ndidzakupulumutsani ndi kukulanditsani mʼmanja mwake. 12 Ndidzakuchitirani chifundo, ndipo mfumuyonso idzakuchitirani chifundo ndi kukulolani kuti mukhale mʼdziko mwanumwanu. 13 “Koma mwina simudzamvera Yehova Mulungu wanu nʼkumanena kuti, ‘Ayi ife sitidzakhala mʼdziko muno, 14 ndipo ngati mukunena kuti, ‘Ayi, koma tidzapita ku Igupto kumene sitidzaonako nkhondo kapena kumva kulira kwa lipenga kapenanso kusowa chakudya.’ 15 Tsono, inu otsala a ku Yuda, imvani mawu a Yehova. Iye akuti, ngati mutsimikiza zopita ku Igupto, nʼkupitadi kukakhala kumeneko, 16 ndiye nkhondo imene mukuyiopayo idzakugonjetsani ku Igupto komweko. Njala imene mukuyiopayo idzakupezani ku Igupto komweko ndipo mudzafera kumeneko. 17 Kunena zoona, onse amene atsimikiza zopita ku Igupto kuti akakhale kumeneko adzafa ndi nkhondo njala ndi mliri. Palibe ndi mmodzi yemwe amene adzapulumuke kapena kuthawa mavuto amene ndidzawagwetsera.’ 18 Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti, ‘Momwe ndinawakwiyira mwaukali anthu okhala mu Yerusalemu, koteronso ndidzakukwiyirani mukapita ku Igupto. Mudzasanduka chinthu chotembereredwa ndi chochititsa mantha, choseketsa ndi chonyozeka. Malo ano simudzawaonanso.’ 19 “Inu otsala a ku Yuda, Yehova wakuwuzani kuti, ‘Musapite ku Igupto.’ Dziwani chinthu ichi: Ine lero ndikukuchenjezani 20 kuti munalakwitsa kwambiri. Inu munandituma kwa Yehova Mulungu wanu nʼkumati ‘Mukatipempherere kwa Yehova Mulungu wathu, nʼkudzatiwuza chimene afuna kuti tichite, ndipo ife tidzachita.’ 21 Ine lero ndakuwuzani, koma inu simukumverabe zonse zimene Yehova Mulungu anandituma kuti ndikuwuzeni. 22 Tsono dziwani ichi: mudzafadi ndi nkhondo, njala ndi mliri kumalo kumene mukufuna mukakhaleko.”
In Other Versions
Jeremiah 42 in the ANGEFD
Jeremiah 42 in the ANTPNG2D
Jeremiah 42 in the AS21
Jeremiah 42 in the BAGH
Jeremiah 42 in the BBPNG
Jeremiah 42 in the BBT1E
Jeremiah 42 in the BDS
Jeremiah 42 in the BEV
Jeremiah 42 in the BHAD
Jeremiah 42 in the BIB
Jeremiah 42 in the BLPT
Jeremiah 42 in the BNT
Jeremiah 42 in the BNTABOOT
Jeremiah 42 in the BNTLV
Jeremiah 42 in the BOATCB
Jeremiah 42 in the BOATCB2
Jeremiah 42 in the BOBCV
Jeremiah 42 in the BOCNT
Jeremiah 42 in the BOECS
Jeremiah 42 in the BOHCB
Jeremiah 42 in the BOHCV
Jeremiah 42 in the BOHLNT
Jeremiah 42 in the BOHNTLTAL
Jeremiah 42 in the BOICB
Jeremiah 42 in the BOILNTAP
Jeremiah 42 in the BOITCV
Jeremiah 42 in the BOKCV
Jeremiah 42 in the BOKCV2
Jeremiah 42 in the BOKHWOG
Jeremiah 42 in the BOKSSV
Jeremiah 42 in the BOLCB
Jeremiah 42 in the BOLCB2
Jeremiah 42 in the BOMCV
Jeremiah 42 in the BONAV
Jeremiah 42 in the BONCB
Jeremiah 42 in the BONLT
Jeremiah 42 in the BONUT2
Jeremiah 42 in the BOPLNT
Jeremiah 42 in the BOSCB
Jeremiah 42 in the BOSNC
Jeremiah 42 in the BOTLNT
Jeremiah 42 in the BOVCB
Jeremiah 42 in the BOYCB
Jeremiah 42 in the BPBB
Jeremiah 42 in the BPH
Jeremiah 42 in the BSB
Jeremiah 42 in the CCB
Jeremiah 42 in the CUV
Jeremiah 42 in the CUVS
Jeremiah 42 in the DBT
Jeremiah 42 in the DGDNT
Jeremiah 42 in the DHNT
Jeremiah 42 in the DNT
Jeremiah 42 in the ELBE
Jeremiah 42 in the EMTV
Jeremiah 42 in the ESV
Jeremiah 42 in the FBV
Jeremiah 42 in the FEB
Jeremiah 42 in the GGMNT
Jeremiah 42 in the GNT
Jeremiah 42 in the HARY
Jeremiah 42 in the HNT
Jeremiah 42 in the IRVA
Jeremiah 42 in the IRVB
Jeremiah 42 in the IRVG
Jeremiah 42 in the IRVH
Jeremiah 42 in the IRVK
Jeremiah 42 in the IRVM
Jeremiah 42 in the IRVM2
Jeremiah 42 in the IRVO
Jeremiah 42 in the IRVP
Jeremiah 42 in the IRVT
Jeremiah 42 in the IRVT2
Jeremiah 42 in the IRVU
Jeremiah 42 in the ISVN
Jeremiah 42 in the JSNT
Jeremiah 42 in the KAPI
Jeremiah 42 in the KBT1ETNIK
Jeremiah 42 in the KBV
Jeremiah 42 in the KJV
Jeremiah 42 in the KNFD
Jeremiah 42 in the LBA
Jeremiah 42 in the LBLA
Jeremiah 42 in the LNT
Jeremiah 42 in the LSV
Jeremiah 42 in the MAAL
Jeremiah 42 in the MBV
Jeremiah 42 in the MBV2
Jeremiah 42 in the MHNT
Jeremiah 42 in the MKNFD
Jeremiah 42 in the MNG
Jeremiah 42 in the MNT
Jeremiah 42 in the MNT2
Jeremiah 42 in the MRS1T
Jeremiah 42 in the NAA
Jeremiah 42 in the NASB
Jeremiah 42 in the NBLA
Jeremiah 42 in the NBS
Jeremiah 42 in the NBVTP
Jeremiah 42 in the NET2
Jeremiah 42 in the NIV11
Jeremiah 42 in the NNT
Jeremiah 42 in the NNT2
Jeremiah 42 in the NNT3
Jeremiah 42 in the PDDPT
Jeremiah 42 in the PFNT
Jeremiah 42 in the RMNT
Jeremiah 42 in the SBIAS
Jeremiah 42 in the SBIBS
Jeremiah 42 in the SBIBS2
Jeremiah 42 in the SBICS
Jeremiah 42 in the SBIDS
Jeremiah 42 in the SBIGS
Jeremiah 42 in the SBIHS
Jeremiah 42 in the SBIIS
Jeremiah 42 in the SBIIS2
Jeremiah 42 in the SBIIS3
Jeremiah 42 in the SBIKS
Jeremiah 42 in the SBIKS2
Jeremiah 42 in the SBIMS
Jeremiah 42 in the SBIOS
Jeremiah 42 in the SBIPS
Jeremiah 42 in the SBISS
Jeremiah 42 in the SBITS
Jeremiah 42 in the SBITS2
Jeremiah 42 in the SBITS3
Jeremiah 42 in the SBITS4
Jeremiah 42 in the SBIUS
Jeremiah 42 in the SBIVS
Jeremiah 42 in the SBT
Jeremiah 42 in the SBT1E
Jeremiah 42 in the SCHL
Jeremiah 42 in the SNT
Jeremiah 42 in the SUSU
Jeremiah 42 in the SUSU2
Jeremiah 42 in the SYNO
Jeremiah 42 in the TBIAOTANT
Jeremiah 42 in the TBT1E
Jeremiah 42 in the TBT1E2
Jeremiah 42 in the TFTIP
Jeremiah 42 in the TFTU
Jeremiah 42 in the TGNTATF3T
Jeremiah 42 in the THAI
Jeremiah 42 in the TNFD
Jeremiah 42 in the TNT
Jeremiah 42 in the TNTIK
Jeremiah 42 in the TNTIL
Jeremiah 42 in the TNTIN
Jeremiah 42 in the TNTIP
Jeremiah 42 in the TNTIZ
Jeremiah 42 in the TOMA
Jeremiah 42 in the TTENT
Jeremiah 42 in the UBG
Jeremiah 42 in the UGV
Jeremiah 42 in the UGV2
Jeremiah 42 in the UGV3
Jeremiah 42 in the VBL
Jeremiah 42 in the VDCC
Jeremiah 42 in the YALU
Jeremiah 42 in the YAPE
Jeremiah 42 in the YBVTP
Jeremiah 42 in the ZBP