Joshua 22 (BOGWICC)

1 Pambuyo pake Yoswa anayitanitsa fuko la Rubeni, fuko la Gadi ndi theka la fuko la Manase, 2 ndipo anawawuza kuti, “Inu mwachita zonse zimene Mose mtumiki wa Yehova anakulamulani, ndipo mwamvera mu zonse zimene ndinakulamulirani. 3 Aisraeli anzanu simunawasiye nthawi yayitali yonseyi mpaka lero lino. Inu mwaonetsetsa kuti mwachita zonse zimene Yehova anakulamulani. 4 Tsono pakuti Yehova Mulungu wanu wapereka mpumulo kwa abale anu monga anayankhulira nawo, bwererani ku nyumba zanu ku dziko limene Mose mtumiki wa Yehova anakupatsani, dziko limene lili pa tsidya la Yorodani kummawa. 5 Koma samalitsani kuti mumvere malamulo ndi malangizo amene Mose mtumiki wa Yehova anakupatsani: kukonda Yehova Mulungu wanu, kuchita zimene iye amafuna, kumvera malamulo ake, kukhala okhulupirika kwa Iye ndi kumutumikira ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse.” 6 Ndipo Yoswa anawadalitsa ndi kuwalola kuti apite ndipo anapitadi ku nyumba zawo. 7 Apa nʼkuti Mose atapereka dziko la Basani ku theka lina la fuko la Manase. Koma theka lina la fuko la Manase Yoswa analipatsa dziko la kumadzulo kwa Yorodani pamodzi ndi abale awo onse. Pamene Yoswa ankawatumiza kwawo anthu amenewa, anawadalitsa, 8 nawawuza kuti, “Mukubwerera kwanu ndi chuma chambiri. Muli ndi ngʼombe zambiri pamodzi ndi siliva, golide, mkuwa ndi chitsulo, ndiponso zovala zambiri. Izi zimene munafunkha kwa adani anu agawireni abale anu.” 9 Choncho mafuko a Rubeni, Gadi, pamodzi ndi theka la fuko la Manase anabwerera kwawo. Aisraeli ena onse anawasiya ku Silo mʼdziko la Kanaani. Tsono anapita ku dziko la Giliyadi, dziko limene linali lawo popeza analilandira potsata malamulo a Yehova kudzera mwa Mose. 10 Atafika ku Geliloti, malo amene ali mʼmbali mwa mtsinje wa Yorodani mʼdziko la Kanaani, fuko la Rubeni, fuko la Gadi ndi theka la fuko la Manase anamanga guwa lansembe lalikulu pamenepo. 11 Ndipo pamene Aisraeli ena onse anawuzidwa kuti anthu a fuko la Rubeni, fuko la Gadi ndi theka la fuko la Manase amanga guwa lansembe mʼmalire a Kanaani ku Geliloti, ku tsidya lathu lino la Yorodani, 12 gulu lonse la Aisraeli linasonkhana ku Silo kuti lipite kukachita nawo nkhondo. 13 Choncho Aisraeli anatumiza Finehasi mwana wa wansembe, Eliezara ku dziko la Giliyadi kwa mafuko a Rubeni, Gadi ndi theka la fuko la Manase. 14 Pamodzi ndi Finehasiyo anatumiza akuluakulu khumi ochokera ku fuko lililonse la Aisraeli. Aliyense mwa akuluakulu amenewa anali mtsogoleri wa banja limodzi la mafuko a Aisraeli. 15 Atafika ku Giliyadi anawuza fuko la Rubeni, Gadi ndi theka lija la fuko la Manase kuti, 16 “Gulu lonse likukufunsa kuti, ‘Chifukwa chiyani mwachita chinthu chonyansa chotere potsutsana ndi Mulungu wa Israeli? Nʼchifukwa chiyani mwapatuka ndi kuleka kutsata Yehova podzimangira nokha guwa lansembe? Mwapandukiratu Yehova! 17 Kodi tchimo lija la ku Peori ndi lochepa kwa inu? Paja Yehova analanga gulu lonse ndi mliri chifukwa cha tchimolo, ndipo mpaka lero tchimo limene lija tikanazunzika nalobe. 18 Kodi inu tsono mufuna kupatuka kuleka kumutsata Yehova?“ ‘Ngati lero mumupandukira Yehovayo, ndiye kuti mawamawali Iye adzakwiyira gulu lonse wa Israeli. 19 Ngati dziko limene inu mwatenga ndi loyipitsidwa, bwerani ku dziko la Yehova kumene kuli chihema chake kuja, ndipo mukhale nafe limodzi. Koma inu musawukire Yehova kapena kutisandutsa ife kukhala opanduka podzimangira guwa lansembe, kuwonjezera pa guwa lansembe la Yehova Mulungu wanu. 20 Kumbukirani pamene Akani mwana wa Zera anakana kumvera lamulo la zinthu zoyenera kuwonongedwa, kodi suja mkwiyo wa Yehova unagwera gulu lonse la Israeli? Akaniyo sanafe yekha chifukwa cha tchimo lakelo.’ ” 21 Tsono mafuko a Rubeni, Gadi ndi theka la fuko la Manase anawayankha atsogoleri a mabanja a Israeli aja kuti, 22 “Wamphamvu uja, Mulungu ndiye Yehova! Wamphamvu uja Mulungu ndiye Yehova. Iyeyu ndiye akudziwa chifukwa chiyani tinachita zimenezi. Tikufunanso kuti inu mudziwe. Ngati tinachita izi mopandukira ndiponso moonetsa kusakhulupirira Yehova, lero lomwe lino musatisiye ndi moyo. 23 Ngati tinapandukira Yehova ndi kuleka kumutsata pamene tinadzimangira guwa loti tizipserezerapo nsembe kapena kupereka nsembe zaufa, kapena nsembe za mtendere, Yehova yekha ndiye atilange. 24 “Ayi! Ife tinachita izi kuopa kuti tsiku lina zidzukulu zanu zingadzanene kwa zidzukulu zathu kuti, ‘Kodi inu mukufuna chiyani kwa Yehova Mulungu wa Israeli? 25 Yehova anayika mtsinje wa Yorodani kukhala malire pakati pa ife ndi inu, anthu a fuko la Rubeni ndi Gadi. Inuyo mulibe gawo mwa Yehova.’ Tsono mwina zidzukulu zanuzo nʼkudzaletsa zathu kupembedza Yehova. 26 “Nʼchifukwa chake tinaganiza kuti, ‘Tiyeni timange guwa lansembe, koma osati kuti tiziperekapo nsembe zopsereza kapena zopereka.’ 27 Koma mosiyana ndi zimenezi, guwali likhale umboni pakati pa ife ndi inu ndiponso mibado imene ikubwerayo, kuti ife timapembedzanso Yehova ndi nsembe zathu zopsereza, zopereka, ndiponso nsembe za mtendere. Motero mʼtsogolo muno zidzukulu zanu sizidzatha kunena kwa zidzukulu zathu kuti, ‘Inu mulibe gawo mwa Yehova!’ 28 “Ndipo ife tinati kuti, ‘Ngati iwo adzatiyankhulira kapena kuyankhulira zidzukulu zathu motero mʼtsogolo muno, ife tidzayankha kuti, onani guwa lansembe, lofanana ndi lomwe makolo athu anamanga osati loperekerapo nsembe zopsereza kapena nsembe zina koma ngati umboni pakati pa inu ndi ife.’ 29 “Sizingatheke konse kuti ife lero nʼkupandukira Yehova. Ife sitingapatuke kuleka kumutsata Yehova ndi kumanga guwa lina la nsembe zopsereza, nsembe za zakudya, ndi nsembe zina zopikisana ndi guwa la Yehova, Mulungu wathu limene lili patsogolo pa Hema ya Yehova mʼmene amakhalamo.” 30 Tsono Finehasi wansembe ndi atsogoleri a gululo amene anali naye atamva zimene anthu a fuko la Rubeni, Gadi ndi theka lakummawa la fuko la Manase ananena, anakondwera kwambiri. 31 Ndipo Finehasi wansembe, mwana wa Eliezara anati kwa mafuko a Rubeni, Gadi ndi Manase, “Lero tadziwa kuti Yehova ali nafe chifukwa zimene mwachitazi simunawukire nazo Yehova. Inu mwapulumutsa Aisraeli onse ku chilango cha Yehova.” 32 Ndipo Finehasi mwana wa wansembe Eliezara, pamodzi ndi atsogoleriwo anachoka ku Giliyadi nasiya anthu a fuko la Rubeni ndi Gadi nabwerera ku Kanaani kwa Aisraeli anzawo, ndipo anakafotokoza zonsezi. 33 Mawu amenewa anakondweretsa Aisraeli onse ndipo anayamika Mulungu. Choncho sanakambenso zopita ku nkhondo kukawononga dziko limene Arubeni ndi Agadi ankakhalamo. 34 Arubeni ndi Agadi anatcha guwalo kuti Mboni: Mboni pakati pathu kuti Yehova ndi Mulungu.

In Other Versions

Joshua 22 in the ANGEFD

Joshua 22 in the ANTPNG2D

Joshua 22 in the AS21

Joshua 22 in the BAGH

Joshua 22 in the BBPNG

Joshua 22 in the BBT1E

Joshua 22 in the BDS

Joshua 22 in the BEV

Joshua 22 in the BHAD

Joshua 22 in the BIB

Joshua 22 in the BLPT

Joshua 22 in the BNT

Joshua 22 in the BNTABOOT

Joshua 22 in the BNTLV

Joshua 22 in the BOATCB

Joshua 22 in the BOATCB2

Joshua 22 in the BOBCV

Joshua 22 in the BOCNT

Joshua 22 in the BOECS

Joshua 22 in the BOHCB

Joshua 22 in the BOHCV

Joshua 22 in the BOHLNT

Joshua 22 in the BOHNTLTAL

Joshua 22 in the BOICB

Joshua 22 in the BOILNTAP

Joshua 22 in the BOITCV

Joshua 22 in the BOKCV

Joshua 22 in the BOKCV2

Joshua 22 in the BOKHWOG

Joshua 22 in the BOKSSV

Joshua 22 in the BOLCB

Joshua 22 in the BOLCB2

Joshua 22 in the BOMCV

Joshua 22 in the BONAV

Joshua 22 in the BONCB

Joshua 22 in the BONLT

Joshua 22 in the BONUT2

Joshua 22 in the BOPLNT

Joshua 22 in the BOSCB

Joshua 22 in the BOSNC

Joshua 22 in the BOTLNT

Joshua 22 in the BOVCB

Joshua 22 in the BOYCB

Joshua 22 in the BPBB

Joshua 22 in the BPH

Joshua 22 in the BSB

Joshua 22 in the CCB

Joshua 22 in the CUV

Joshua 22 in the CUVS

Joshua 22 in the DBT

Joshua 22 in the DGDNT

Joshua 22 in the DHNT

Joshua 22 in the DNT

Joshua 22 in the ELBE

Joshua 22 in the EMTV

Joshua 22 in the ESV

Joshua 22 in the FBV

Joshua 22 in the FEB

Joshua 22 in the GGMNT

Joshua 22 in the GNT

Joshua 22 in the HARY

Joshua 22 in the HNT

Joshua 22 in the IRVA

Joshua 22 in the IRVB

Joshua 22 in the IRVG

Joshua 22 in the IRVH

Joshua 22 in the IRVK

Joshua 22 in the IRVM

Joshua 22 in the IRVM2

Joshua 22 in the IRVO

Joshua 22 in the IRVP

Joshua 22 in the IRVT

Joshua 22 in the IRVT2

Joshua 22 in the IRVU

Joshua 22 in the ISVN

Joshua 22 in the JSNT

Joshua 22 in the KAPI

Joshua 22 in the KBT1ETNIK

Joshua 22 in the KBV

Joshua 22 in the KJV

Joshua 22 in the KNFD

Joshua 22 in the LBA

Joshua 22 in the LBLA

Joshua 22 in the LNT

Joshua 22 in the LSV

Joshua 22 in the MAAL

Joshua 22 in the MBV

Joshua 22 in the MBV2

Joshua 22 in the MHNT

Joshua 22 in the MKNFD

Joshua 22 in the MNG

Joshua 22 in the MNT

Joshua 22 in the MNT2

Joshua 22 in the MRS1T

Joshua 22 in the NAA

Joshua 22 in the NASB

Joshua 22 in the NBLA

Joshua 22 in the NBS

Joshua 22 in the NBVTP

Joshua 22 in the NET2

Joshua 22 in the NIV11

Joshua 22 in the NNT

Joshua 22 in the NNT2

Joshua 22 in the NNT3

Joshua 22 in the PDDPT

Joshua 22 in the PFNT

Joshua 22 in the RMNT

Joshua 22 in the SBIAS

Joshua 22 in the SBIBS

Joshua 22 in the SBIBS2

Joshua 22 in the SBICS

Joshua 22 in the SBIDS

Joshua 22 in the SBIGS

Joshua 22 in the SBIHS

Joshua 22 in the SBIIS

Joshua 22 in the SBIIS2

Joshua 22 in the SBIIS3

Joshua 22 in the SBIKS

Joshua 22 in the SBIKS2

Joshua 22 in the SBIMS

Joshua 22 in the SBIOS

Joshua 22 in the SBIPS

Joshua 22 in the SBISS

Joshua 22 in the SBITS

Joshua 22 in the SBITS2

Joshua 22 in the SBITS3

Joshua 22 in the SBITS4

Joshua 22 in the SBIUS

Joshua 22 in the SBIVS

Joshua 22 in the SBT

Joshua 22 in the SBT1E

Joshua 22 in the SCHL

Joshua 22 in the SNT

Joshua 22 in the SUSU

Joshua 22 in the SUSU2

Joshua 22 in the SYNO

Joshua 22 in the TBIAOTANT

Joshua 22 in the TBT1E

Joshua 22 in the TBT1E2

Joshua 22 in the TFTIP

Joshua 22 in the TFTU

Joshua 22 in the TGNTATF3T

Joshua 22 in the THAI

Joshua 22 in the TNFD

Joshua 22 in the TNT

Joshua 22 in the TNTIK

Joshua 22 in the TNTIL

Joshua 22 in the TNTIN

Joshua 22 in the TNTIP

Joshua 22 in the TNTIZ

Joshua 22 in the TOMA

Joshua 22 in the TTENT

Joshua 22 in the UBG

Joshua 22 in the UGV

Joshua 22 in the UGV2

Joshua 22 in the UGV3

Joshua 22 in the VBL

Joshua 22 in the VDCC

Joshua 22 in the YALU

Joshua 22 in the YAPE

Joshua 22 in the YBVTP

Joshua 22 in the ZBP