Joshua 9 (BOGWICC)

1 Mafumu onse okhala kumadzulo kwa Yorodani atamva zimenezi pamodzi ndi mafumu okhala ku mayiko a ku mapiri, mu zigwa, mʼmbali mwa Nyanja yayikulu mpaka ku Lebanoni (mafumu a Ahiti, Aamori, Akanaani, Aperezi, Ahivi, ndi Ayebusi), 2 anapangana kuti achite nkhondo ndi Yoswa ndi Israeli. 3 Koma Ahivi ena a ku Gibiyoni atamva zomwe Yoswa anachitira mizinda ya Yeriko ndi Ai, 4 anaganiza zochita zachinyengo. Anapita nasenzetsa abulu awo chakudya mʼmatumba akalekale ndiponso matumba a vinyo achikopa ongʼambikangʼambika. 5 Anthuwa anavala nsapato zakutha ndi zazigamba ndiponso anavala sanza. Buledi wawo yense anali wowuma ndi wowola. 6 Ndipo anapita kwa Yoswa ku msasa ku Giligala ndikumuwuza kuti, pamodzi ndi Aisraeli onse, “Ife tachokera ku dziko lakutali, ndipo tikufuna kuti muchite mgwirizano ndi ife.” 7 Koma Aisraeli anayankha Ahiviwo kuti, “Mwinatu inu mukukhala pafupi ndi ife. Tsono ife tingachite bwanji mgwirizano ndi inu?” 8 Iwo anati kwa Yoswa, “Ife ndife akapolo anu.”Tsono Yoswa anawafunsa kuti, “Inu ndinu yani ndipo mukuchokera kuti?” 9 Iwo anayankha kuti, “Akapolo anufe tachokera ku dziko lakutali chifukwa tamva za Yehova Mulungu wanu. Tamva mbiri yonse ya zimene Iye anachita ku Igupto, 10 ndi zonse zimene anachita kwa mafumu awiri a Aamori kummawa kwa Yorodani, mfumu Sihoni ya Hesiboni ndi Ogi mfumu ya Basani amene amalamulira ku Asiteroti. 11 Tsono akuluakulu athu ndi onse amene akukhala mʼdziko lathu anati kwa ife. Tengani chakudya cha pa ulendo wanu. Pitani mukakumane nawo ndipo mukati kwa iwo, ‘Ife ndife akapolo anu, ndipo tikufuna kuti mugwirizane nafe za mtendere.’ ” 12 Buledi wathuyu anali wotentha pamene timanyamuka ku mudzi kubwera kwa inu. Koma tsopano taonani ali gwaa ndiponso wawola. 13 Zikopa zimene tinathiramo vinyozi zinali zatsopano, koma taonani zathetheka. Zovala zathu ndi nsapato zathu zatha chifukwa cha kutalika kwa ulendo. 14 Aisraeli anatengako chakudya chawo koma sanafunse kwa Yehova. 15 Choncho Yoswa anapangana nawo za mtendere kuti sadzawapha, ndipo atsogoleri a gulu anavomereza pochita lumbiro. 16 Patatha masiku atatu atachita mgwirizano wa mtendere ndi Agibiyoni, Aisraeli anamva kuti anali anansi awo, anthu amene amakhala nawo pafupi. 17 Tsono Aisraeli ananyamuka ulendo ndipo tsiku lachitatu anafika ku mizinda ya Gibiyoni, Kefira, Beeroti ndi Kiriati-Yearimu. 18 Koma Aisraeli sanawaphe anthuwo chifukwa atsogoleri awo anali atalonjeza mʼdzina la Yehova Mulungu wa Israeli za Agibiyoniwo.Koma anthu onse anatsutsana ndi atsogoleriwo. 19 Koma atsogoleriwo anayankha kuti, “Ife tinawalonjeza mʼdzina la Yehova, Mulungu wa Israeli, ndipo tsopano sitingawaphe. 20 Chimene tidzachita nawo ndi ichi: Tidzawasiya akhale ndi moyo kuti mkwiyo wa Yehova usatigwere chifukwa chophwanya lonjezo limene tinawalonjeza.” 21 Anapitiriza kunena kuti “Asiyeni akhale ndi moyo, komabe akhale otidulira mitengo ndi kutitungira madzi ogwiritsa ntchito pa chipembedzo.” Lonjezo la atsogoleriwo linasungidwa. 22 Kenaka Yoswa anayitanitsa Agibiyoni aja nawafunsa kuti, “Chifukwa chiyani inu munatinyenga ponena kuti mumachokera kutali pamene zoona zake nʼzoti mumakhala pafupi pomwe pano? 23 Tsopano popeza mwachita izi, Mulungu wakutembererani ndipo palibe wina mwa inu amene akhale mfulu. Nthawi zonse inu muzidzatidulira nkhuni ndi kutitungira madzi ku Nyumba ya Yehova.” 24 Iwo anayankha Yoswa kuti, “Ife akapolo anufe tinachita zimenezi chifukwa tinamva bwino lomwe kuti Yehova Mulungu wanu analamula Mose mtumiki wake kuti adzakupatsani dziko lonseli ndi kuti anthu onse okhalamo adzaphedwe. Tsono ife tinachita mantha aakulu ndipo tinachita zimenezi pofuna kupulumutsa miyoyo yathu. 25 Tsopanotu ife tili mʼmanja mwanu, ndipo inu chitani nafe monga kukukomerani.” 26 Tsono Yoswa anawapulumutsa mʼmanja mwa Aisraeli ndipo sanawaphe. 27 Kuyambira tsiku limenelo Agibiyoni aja anasanduka odula nkhuni zaguwa lansembe la Yehova ndiponso otunga madzi. Mpaka lero lino iwo akuchitabe zimenezi kulikonse kumene Yehova anasankha.

In Other Versions

Joshua 9 in the ANGEFD

Joshua 9 in the ANTPNG2D

Joshua 9 in the AS21

Joshua 9 in the BAGH

Joshua 9 in the BBPNG

Joshua 9 in the BBT1E

Joshua 9 in the BDS

Joshua 9 in the BEV

Joshua 9 in the BHAD

Joshua 9 in the BIB

Joshua 9 in the BLPT

Joshua 9 in the BNT

Joshua 9 in the BNTABOOT

Joshua 9 in the BNTLV

Joshua 9 in the BOATCB

Joshua 9 in the BOATCB2

Joshua 9 in the BOBCV

Joshua 9 in the BOCNT

Joshua 9 in the BOECS

Joshua 9 in the BOHCB

Joshua 9 in the BOHCV

Joshua 9 in the BOHLNT

Joshua 9 in the BOHNTLTAL

Joshua 9 in the BOICB

Joshua 9 in the BOILNTAP

Joshua 9 in the BOITCV

Joshua 9 in the BOKCV

Joshua 9 in the BOKCV2

Joshua 9 in the BOKHWOG

Joshua 9 in the BOKSSV

Joshua 9 in the BOLCB

Joshua 9 in the BOLCB2

Joshua 9 in the BOMCV

Joshua 9 in the BONAV

Joshua 9 in the BONCB

Joshua 9 in the BONLT

Joshua 9 in the BONUT2

Joshua 9 in the BOPLNT

Joshua 9 in the BOSCB

Joshua 9 in the BOSNC

Joshua 9 in the BOTLNT

Joshua 9 in the BOVCB

Joshua 9 in the BOYCB

Joshua 9 in the BPBB

Joshua 9 in the BPH

Joshua 9 in the BSB

Joshua 9 in the CCB

Joshua 9 in the CUV

Joshua 9 in the CUVS

Joshua 9 in the DBT

Joshua 9 in the DGDNT

Joshua 9 in the DHNT

Joshua 9 in the DNT

Joshua 9 in the ELBE

Joshua 9 in the EMTV

Joshua 9 in the ESV

Joshua 9 in the FBV

Joshua 9 in the FEB

Joshua 9 in the GGMNT

Joshua 9 in the GNT

Joshua 9 in the HARY

Joshua 9 in the HNT

Joshua 9 in the IRVA

Joshua 9 in the IRVB

Joshua 9 in the IRVG

Joshua 9 in the IRVH

Joshua 9 in the IRVK

Joshua 9 in the IRVM

Joshua 9 in the IRVM2

Joshua 9 in the IRVO

Joshua 9 in the IRVP

Joshua 9 in the IRVT

Joshua 9 in the IRVT2

Joshua 9 in the IRVU

Joshua 9 in the ISVN

Joshua 9 in the JSNT

Joshua 9 in the KAPI

Joshua 9 in the KBT1ETNIK

Joshua 9 in the KBV

Joshua 9 in the KJV

Joshua 9 in the KNFD

Joshua 9 in the LBA

Joshua 9 in the LBLA

Joshua 9 in the LNT

Joshua 9 in the LSV

Joshua 9 in the MAAL

Joshua 9 in the MBV

Joshua 9 in the MBV2

Joshua 9 in the MHNT

Joshua 9 in the MKNFD

Joshua 9 in the MNG

Joshua 9 in the MNT

Joshua 9 in the MNT2

Joshua 9 in the MRS1T

Joshua 9 in the NAA

Joshua 9 in the NASB

Joshua 9 in the NBLA

Joshua 9 in the NBS

Joshua 9 in the NBVTP

Joshua 9 in the NET2

Joshua 9 in the NIV11

Joshua 9 in the NNT

Joshua 9 in the NNT2

Joshua 9 in the NNT3

Joshua 9 in the PDDPT

Joshua 9 in the PFNT

Joshua 9 in the RMNT

Joshua 9 in the SBIAS

Joshua 9 in the SBIBS

Joshua 9 in the SBIBS2

Joshua 9 in the SBICS

Joshua 9 in the SBIDS

Joshua 9 in the SBIGS

Joshua 9 in the SBIHS

Joshua 9 in the SBIIS

Joshua 9 in the SBIIS2

Joshua 9 in the SBIIS3

Joshua 9 in the SBIKS

Joshua 9 in the SBIKS2

Joshua 9 in the SBIMS

Joshua 9 in the SBIOS

Joshua 9 in the SBIPS

Joshua 9 in the SBISS

Joshua 9 in the SBITS

Joshua 9 in the SBITS2

Joshua 9 in the SBITS3

Joshua 9 in the SBITS4

Joshua 9 in the SBIUS

Joshua 9 in the SBIVS

Joshua 9 in the SBT

Joshua 9 in the SBT1E

Joshua 9 in the SCHL

Joshua 9 in the SNT

Joshua 9 in the SUSU

Joshua 9 in the SUSU2

Joshua 9 in the SYNO

Joshua 9 in the TBIAOTANT

Joshua 9 in the TBT1E

Joshua 9 in the TBT1E2

Joshua 9 in the TFTIP

Joshua 9 in the TFTU

Joshua 9 in the TGNTATF3T

Joshua 9 in the THAI

Joshua 9 in the TNFD

Joshua 9 in the TNT

Joshua 9 in the TNTIK

Joshua 9 in the TNTIL

Joshua 9 in the TNTIN

Joshua 9 in the TNTIP

Joshua 9 in the TNTIZ

Joshua 9 in the TOMA

Joshua 9 in the TTENT

Joshua 9 in the UBG

Joshua 9 in the UGV

Joshua 9 in the UGV2

Joshua 9 in the UGV3

Joshua 9 in the VBL

Joshua 9 in the VDCC

Joshua 9 in the YALU

Joshua 9 in the YAPE

Joshua 9 in the YBVTP

Joshua 9 in the ZBP