Leviticus 11 (BOGWICC)

1 Yehova anayankhula ndi Mose ndi Aaroni kuti, 2 “Awuze Aisraeli kuti, ‘Nyama zomwe mukhoza kudya mwa nyama zonse za dziko lapansi ndi izi: 3 Nyama iliyonse imene ili ndi chipondero chogawikana pakati ndi yobzikula mukhoza kudya. 4 “ ‘Koma pali nyama zina zimene zimabzikula kokha kapena ndi zogawikana zipondero zimene simukuyenera kudya. Nyama zimenezi ndi ngamira, ngakhale imabzikula ilibe zipondero zogawikana. Choncho ndi yodetsedwa, musadye. 5 Ina ndi mbira, ngakhale imabzikula, zipondero zake nʼzosagawikana. Choncho ndi yodetsedwa, musadye. 6 Inanso ndi kalulu, ngakhale amabzikula, zipondero zake nʼzosagawikana. Choncho ndi wodetsedwa, musadye. 7 Nkhumba simabzikula ngakhale ili ndi zipondero zogawikana. Choncho ndi yodetsedwa, musadye. 8 Musamadye nyama yake kapena kukhudza imene yafa chifukwa ndi yodetsedwa. 9 “ ‘Mwa zamoyo zonse zimene zimakhala mʼmadzi a mʼnyanja ndi a mʼmitsinje mukhoza kudya chilichonse chimene chili ndi minga ya pa msana ndi mamba. 10 Koma zamoyo zonse za mʼnyanja kapena za mʼmitsinje zimene zilibe minga ya pa msana ndi mamba, kaya ndi tizirombo tonse ta mʼmadzi ndi zamoyo zonse zopezeka mʼmenemo ndi zodetsedwa kwa inu. 11 Pakuti zimenezi ndi zodetsedwa kwa inu, nyama yake musadye, ndipo zikafa zikhalebe zodetsedwa kwa inu. 12 Chamoyo chilichonse cha mʼmadzi chimene chilibe minga ya pa msana kapena mamba ndi chodetsedwa kwa inu. 13 “ ‘Mbalame zimene simukuyenera kudya chifukwa ndi zodetsedwa ndi izi: mphungu, nkhwazi, mwimba, 14 nankapakapa, akamtema a mitundu yonse, 15 akhungubwi a mitundu yonse, 16 kadzidzi wamphondo, kadzidzi wodzuma, chipudo ndi mtundu uliwonse wa akabawi 17 kadzidzi wamngʼono, chiswankhono ndi mantchichi, 18 tsekwe, vuwo, dembo, 19 indwa, zimeza za mitundu yonse, nsadzu ndi mleme. 20 “ ‘Zowuluka zonse za miyendo inayi ndi zodetsedwa. 21 Komabe mwa zowuluka zokhala ndi miyendo inayi zimene mukhoza kudya ndi zokhazo zimene zili ndi miyendo yolumphira. 22 Pa zimenezo mungathe kudya izi: dzombe la mitundu yonse, atsokonombwe a mitundu yonse, nkhululu za mitundu yonse, ndi ziwala za mitundu yonse. 23 Koma za mapiko zina zonse zokhala ndi miyendo inayi muzitenge kukhala zodetsedwa kwa inu. 24 “ ‘Zimenezi zidzakudetsani. Aliyense wozikhudza zitafa adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo. 25 Aliyense wonyamula chiwalo chilichonse cha nyama zakufazo ayenera kuchapa zovala zake, ndipo adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo. 26 “ ‘Nyama iliyonse imene ili ndi ziboda zogawikana koma mapazi ake wosagawikana, kapena imene sibzikula muyiyese yodetsedwa kwa inu ndipo munthu aliyense akakhudza nyama yakufayo, adzakhala wodetsedwa. 27 Mwa nyama zonse zoyenda ndi miyendo inayi, nyama zonse zokhala ndi zikhadabo kuphazi muzitenge kukhala zodetsedwa ndipo aliyense wozikhudza zitafa adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo. 28 Aliyense wonyamula nyamazi zitafa ayenera kuchapa zovala zake, ndipo adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo. Zimenezi ndi zodetsedwa kwa inu. 29 “ ‘Mwa nyama zokwawa, zimene zili zodetsedwa kwa inu ndi izi: likongwe, mbewa, msambulu za mitundu yonse, 30 gondwa, mngʼazi, buluzi, dududu ndi nanzikambe. 31 Mwa nyama zonse zoyenda pansi, zimenezi ndi zodetsedwa kwa inu. Munthu aliyense wozikhudza zitafa adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo. 32 Iliyonse mwa nyama zimenezi ikafa ndi kugwera pa chiwiya chilichonse, kaya chimagwira ntchito yotani, kaya ndi chopangidwa ndi mtengo, kaya ndi cha nsalu, kaya ndi cha chikopa kapena chiguduli chiwiyacho chidzakhala chodetsedwa. Muchiviyike mʼmadzi chiwiyacho komabe chidzakhala chodetsedwa mpaka madzulo, ndipo kenaka chidzakhala choyeretsedwa. 33 Tsono nyama ina iliyonse mwa zimenezi ikagwera mʼmbiya ya dothi, ndiye kuti chilichonse cha mʼmbiyamo chidzakhala chodetsedwa, ndipo muyenera kuswa mbiyayo. 34 Chakudya chilichonse chimene mungadye chikakhala kuti chathiridwa mʼmbiyamo, ndiye kuti chakudyacho chidzakhala chodetsedwa, ndipo madzi akumwa wochokera mʼmbiya zotere ndi wodetsedwa. 35 Chiwalo chilichonse cha nyama yakufa chikagwera pa chinthu chilichonse kaya pa uvuni, kapena pa mʼphika, ndiye kuti zinthuzo zidzakhala zodetsedwa, ndipo ziphwanyidwe popeza ndi zodetsedwa. 36 Koma kasupe kapena chitsime chamadzi chidzakhala choyeretsedwa ngakhale kuti chilichonse chokhudza nyama yakufayo chidzakhala chodetsedwa. Zimenezi muzitenge kukhala zodetsedwa. 37 Chiwalo chilichonse cha nyama yakufayo chikagwera pa mbewu zimene akuti adzale, mbewu zimenezo zidzakhalabe zabwino. 38 Koma mbewuzo zikakhala zonyowa ndi madzi, ndipo chiwalo chilichonse cha nyama zakufazo chikagwera pa mbewuzo, mbewuzo zikhale zodetsedwa kwa inu. 39 “ ‘Ngati nyama imene mumaloledwa kudya yafa yokha, ndiye kuti aliyense wokhudza nyama yakufayo adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo. 40 Aliyense amene adyako nyama yakufayo achape zovala zake, ndipo adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo. Aliyense amene wanyamula nyama yakufayo ayenera kuchapa zovala zake, ndipo adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo. 41 “ ‘Chinthu chilichonse chokwawa pansi ndi chonyansa, simuyenera kudya. 42 Musadye chilichonse chokwawa pansi, choyenda chamimba kapena choyenda ndi miyendo inayi kapenanso yambiri popeza ndi chodetsedwa. 43 Musadzisandutse nokha odetsedwa ndi chokwawa chilichonse. Musadziyipitse nazo, kuti mukhale odetsedwa. 44 Ine ndine Yehova Mulungu wanu, choncho dziyeretseni kuti mukhale woyera, chifukwa Ine ndine woyera. Musadzisandutse odetsedwa ndi chokwawa chilichonse. 45 Ine ndine Yehova amene ndinakutulutsani ku Igupto kuti ndikhale Mulungu wanu. Tsono mukhale woyera, chifukwa Ine ndine woyera. 46 “ ‘Amenewa ndi malamulo onena za nyama, mbalame, chamoyo chilichonse choyenda mʼmadzi ndiponso chamoyo chilichonse chokwawa. 47 Muzisiyanitsa pakati pa chodetsedwa ndi choyeretsedwa, komanso pakati pa zomwe mutha kudya ndi zomwe simuyenera kudya.’ ”

In Other Versions

Leviticus 11 in the ANGEFD

Leviticus 11 in the ANTPNG2D

Leviticus 11 in the AS21

Leviticus 11 in the BAGH

Leviticus 11 in the BBPNG

Leviticus 11 in the BBT1E

Leviticus 11 in the BDS

Leviticus 11 in the BEV

Leviticus 11 in the BHAD

Leviticus 11 in the BIB

Leviticus 11 in the BLPT

Leviticus 11 in the BNT

Leviticus 11 in the BNTABOOT

Leviticus 11 in the BNTLV

Leviticus 11 in the BOATCB

Leviticus 11 in the BOATCB2

Leviticus 11 in the BOBCV

Leviticus 11 in the BOCNT

Leviticus 11 in the BOECS

Leviticus 11 in the BOHCB

Leviticus 11 in the BOHCV

Leviticus 11 in the BOHLNT

Leviticus 11 in the BOHNTLTAL

Leviticus 11 in the BOICB

Leviticus 11 in the BOILNTAP

Leviticus 11 in the BOITCV

Leviticus 11 in the BOKCV

Leviticus 11 in the BOKCV2

Leviticus 11 in the BOKHWOG

Leviticus 11 in the BOKSSV

Leviticus 11 in the BOLCB

Leviticus 11 in the BOLCB2

Leviticus 11 in the BOMCV

Leviticus 11 in the BONAV

Leviticus 11 in the BONCB

Leviticus 11 in the BONLT

Leviticus 11 in the BONUT2

Leviticus 11 in the BOPLNT

Leviticus 11 in the BOSCB

Leviticus 11 in the BOSNC

Leviticus 11 in the BOTLNT

Leviticus 11 in the BOVCB

Leviticus 11 in the BOYCB

Leviticus 11 in the BPBB

Leviticus 11 in the BPH

Leviticus 11 in the BSB

Leviticus 11 in the CCB

Leviticus 11 in the CUV

Leviticus 11 in the CUVS

Leviticus 11 in the DBT

Leviticus 11 in the DGDNT

Leviticus 11 in the DHNT

Leviticus 11 in the DNT

Leviticus 11 in the ELBE

Leviticus 11 in the EMTV

Leviticus 11 in the ESV

Leviticus 11 in the FBV

Leviticus 11 in the FEB

Leviticus 11 in the GGMNT

Leviticus 11 in the GNT

Leviticus 11 in the HARY

Leviticus 11 in the HNT

Leviticus 11 in the IRVA

Leviticus 11 in the IRVB

Leviticus 11 in the IRVG

Leviticus 11 in the IRVH

Leviticus 11 in the IRVK

Leviticus 11 in the IRVM

Leviticus 11 in the IRVM2

Leviticus 11 in the IRVO

Leviticus 11 in the IRVP

Leviticus 11 in the IRVT

Leviticus 11 in the IRVT2

Leviticus 11 in the IRVU

Leviticus 11 in the ISVN

Leviticus 11 in the JSNT

Leviticus 11 in the KAPI

Leviticus 11 in the KBT1ETNIK

Leviticus 11 in the KBV

Leviticus 11 in the KJV

Leviticus 11 in the KNFD

Leviticus 11 in the LBA

Leviticus 11 in the LBLA

Leviticus 11 in the LNT

Leviticus 11 in the LSV

Leviticus 11 in the MAAL

Leviticus 11 in the MBV

Leviticus 11 in the MBV2

Leviticus 11 in the MHNT

Leviticus 11 in the MKNFD

Leviticus 11 in the MNG

Leviticus 11 in the MNT

Leviticus 11 in the MNT2

Leviticus 11 in the MRS1T

Leviticus 11 in the NAA

Leviticus 11 in the NASB

Leviticus 11 in the NBLA

Leviticus 11 in the NBS

Leviticus 11 in the NBVTP

Leviticus 11 in the NET2

Leviticus 11 in the NIV11

Leviticus 11 in the NNT

Leviticus 11 in the NNT2

Leviticus 11 in the NNT3

Leviticus 11 in the PDDPT

Leviticus 11 in the PFNT

Leviticus 11 in the RMNT

Leviticus 11 in the SBIAS

Leviticus 11 in the SBIBS

Leviticus 11 in the SBIBS2

Leviticus 11 in the SBICS

Leviticus 11 in the SBIDS

Leviticus 11 in the SBIGS

Leviticus 11 in the SBIHS

Leviticus 11 in the SBIIS

Leviticus 11 in the SBIIS2

Leviticus 11 in the SBIIS3

Leviticus 11 in the SBIKS

Leviticus 11 in the SBIKS2

Leviticus 11 in the SBIMS

Leviticus 11 in the SBIOS

Leviticus 11 in the SBIPS

Leviticus 11 in the SBISS

Leviticus 11 in the SBITS

Leviticus 11 in the SBITS2

Leviticus 11 in the SBITS3

Leviticus 11 in the SBITS4

Leviticus 11 in the SBIUS

Leviticus 11 in the SBIVS

Leviticus 11 in the SBT

Leviticus 11 in the SBT1E

Leviticus 11 in the SCHL

Leviticus 11 in the SNT

Leviticus 11 in the SUSU

Leviticus 11 in the SUSU2

Leviticus 11 in the SYNO

Leviticus 11 in the TBIAOTANT

Leviticus 11 in the TBT1E

Leviticus 11 in the TBT1E2

Leviticus 11 in the TFTIP

Leviticus 11 in the TFTU

Leviticus 11 in the TGNTATF3T

Leviticus 11 in the THAI

Leviticus 11 in the TNFD

Leviticus 11 in the TNT

Leviticus 11 in the TNTIK

Leviticus 11 in the TNTIL

Leviticus 11 in the TNTIN

Leviticus 11 in the TNTIP

Leviticus 11 in the TNTIZ

Leviticus 11 in the TOMA

Leviticus 11 in the TTENT

Leviticus 11 in the UBG

Leviticus 11 in the UGV

Leviticus 11 in the UGV2

Leviticus 11 in the UGV3

Leviticus 11 in the VBL

Leviticus 11 in the VDCC

Leviticus 11 in the YALU

Leviticus 11 in the YAPE

Leviticus 11 in the YBVTP

Leviticus 11 in the ZBP