Leviticus 26 (BOGWICC)

1 “ ‘Musadzipangire mafano ndipo musayimike chifanizo chosema kapena mwala woti mudzipembedza. Musayike mwala wosema mʼdziko mwanu kuti muziwugwadira. Ine ndine Yehova Mulungu wanu. 2 “ ‘Muzisunga Masabata anga ndipo muzilemekeza malo anga wopatulika. Ine ndine Yehova. 3 “ ‘Mukamayenda motsata malangizo anga ndi kumvera mosamalitsa malamulo anga, 4 ndidzakupatsani mvula pa nyengo yake. Nthaka yanu idzabala zokolola zake, ndipo mitengo ya mʼmunda idzabala zipatso zake. 5 Mudzakhala mukupuntha tirigu mpaka nthawi yothyola mphesa, ndipo mudzakhala mukuthyola mphesa mpaka nthawi yodzala. Mudzadya chakudya chanu mpaka kukhuta ndipo mudzakhala mʼdziko lanu mwamtendere. 6 “ ‘Ndidzabweretsa mtendere mʼdziko lanu, ndipo muzidzagona popanda wokuopsezani. Ndidzachotsa nyama zakuthengo zoopsa mʼdziko mwanu, ndipo mʼdzikomo simudzakhala nkhondo. 7 Mudzapirikitsa adani anu, ndipo mudzawagonjetsa ndi lupanga pamaso panu. 8 Anthu asanu mwa inu adzapirikitsa anthu 100, ndipo anthu 100 mwa inu adzathamangitsa anthu 10,000, ndipo adani anuwo mudzawagonjetsa ndi lupanga. 9 “ ‘Ndidzakukumbukirani ndi kukupatsani ana ambiri ndi kukuchulukitsani. Ndidzasunga pangano langa ndi inu. 10 Mudzakhala mukudyabe chakudya chogonera ndipo mudzachotse chakudyacho mʼnkhokwe kuti mupezemo malo woyika chakudya china chatsopano. 11 Ndidzakhala pakati panu, ndipo sindidzayipidwa nanu. 12 Ine ndidzayendayenda pakati panu ndipo ndidzakhala Mulungu wanu. Inu mudzakhala anthu anga. 13 Ine ndine Yehova Mulungu wanu amene ndinakutulutsani mʼdziko la Igupto kuti musakhalenso akapolo a Aigupto. Ndinadula mipiringidzo ya goli lanu ndi kukuthandizani kuti muziyenda momasuka. 14 “ ‘Koma mukadzapanda kundimvera ndi kuphwanya malamulo anga onsewa, 15 ndipo ngati mudzanyoza malangizo anga ndi kunyansidwa ndi malamulo anga, ndi kulephera kumvera zonse zimene ndakulamulani, ndi kuswa pangano langa, 16 Ine ndidzakuchitirani izi: ndidzabweretsa zoopsa zadzidzidzi monga chifuwa chachikulu chowondetsa ndiponso malungo amene adzawononga maso ndi kufowoketsa moyo wanu. Mudzangovutika kudzala mbewu zanu chifukwa adani anu adzazidya. 17 Ndidzakufulatirani, kotero kuti adani anu adzakugonjetsani. Odana nanu adzakulamulirani ndipo inu muzidzagothawa popanda wokupirikitsani. 18 “ ‘Ngati simudzandimvera mutaona zonsezi, ndidzakulanganinso mochulukitsa kasanu ndi kawiri chifukwa cha kuchimwa kwanu. 19 Ndidzathyola mphamvu zanu zimene mukunyadirazo, ndipo ndidzasandutsa mitambo kuti ikhale yowuma ngati chitsulo, ndiponso nthaka yanu kuti ikhale ngati mkuwa. 20 Mphamvu zanu zidzapita pachabe chifukwa nthaka yanu sidzabala kanthu, ngakhale mitengo yake sidzabala zipatso zake. 21 “ ‘Ngati mudzapitirira kutsutsana nane ndi kukana kundimvera, ndidzachulukitsa masautso anu kasanu ndi kawiri molingana ndi machimo anu. 22 Ndidzabweretsa zirombo zolusa pakati panu, ndipo zidzakulandani ana anu ndi kuwononga ngʼombe zanu. Choncho zidzachepetsa chiwerengero chanu kotero kuti mʼnjira mwanu simudzapita anthu. 23 “ ‘Mukadzapanda kutembenukira kwa Ine ngakhale nditakulangani motere, ndi kumachitabe zotsutsana ndi Ine, 24 Ine mwini ndidzalimbana nanu, ndipo ndidzakulangani mochulukitsa kasanu ndi kawiri chifukwa cha machimo anu. 25 Ndipo ndidzabweretsa lupanga pa inu ndi kukulangani chifukwa chophwanya pangano langa. Mukadzasonkhana mʼmizinda yanu, ndidzatumiza miliri pakati panu ndipo ndidzakuperekani mʼmanja mwa adani anu. 26 Ndikadzachepetsa buledi wanu, akazi khumi adzaphika buledi wawo mu uvuni umodzi, ndipo adzakugawirani bulediyo pangʼonopangʼono. Choncho mudzadya koma wosakhuta. 27 “ ‘Mukadzapanda kundimvera ngakhale nditakulangani motere, ndi kumatsutsanabe ndi Ine, 28 pamenepo ndidzalimbana nanu mwaukali, ndipo Ine mwini ndidzakulangani mochulukitsa kasanu ndi kawiri chifukwa cha kuchimwa kwanu. 29 Mudzadya ana anu aamuna ndiponso mudzadya ana anu aakazi. 30 Ine ndidzawononga malo anu opembedzera mafano a ku mapiri. Ndidzagwetsa maguwa anu ofukizira lubani, ndipo ndidzawunjika pamodzi mitembo ya mafano anu wopanda moyowo, ndipo ndidzanyansidwa nanu. 31 Ndidzasandutsa mizinda yanu kukhala mabwinja ndi kuwononga malo anu wopatulika. Sindidzakondweranso ndi fungo lokoma la zopereka zanu. 32 Ndidzawononga dziko kotero kuti adani anu mʼmenemo adzadabwa. 33 Ndidzakubalalitsani pakati pa mitundu ina ya anthu ndipo ndidzasolola lupanga langa ndi kukupirikitsani. Dziko lanu lidzawonongedwa, ndipo mizinda yanu idzasanduka mabwinja. 34 Nthawi imeneyo nthaka idzasangalalira kuyipumitsa kwake nthawi yonse imene idzakhala yosalimidwa, pamene inu mudzakhala muli mʼdziko la adani anu. Pa nthawi imeneyo dziko lidzapumula ndi kukondwerera kulipumuza kwake. 35 Nthawi zonse pamene dzikolo lidzakhala lopanda anthu, nthaka idzapumula. Mpumulo umenewu udzakhala umene nthakayo sinapumulepo pa nthawi zimene inu munkapumula muli mʼdzikomo. 36 “ ‘Kunena za amene adzatsale, ndidzayika mantha mʼmitima mwawo mʼdziko la adani awo kotero kuti adzathawa ngakhale mtswatswa wa tsamba lowuluka ndi mphepo. Adzathawa ngati akuthawa lupanga, ndipo adzagwa pansi ngakhale padzakhale wopanda kuwapirikitsa. 37 Iwo adzaphunthwitsana ngati akuthawa nkhondo, ngakhale padzakhale popanda wowapirikitsa. Choncho simudzatha kuyima pamaso pa adani anu. 38 Mudzatheratu pakati pa mitundu ya anthu. Dziko la adani anu lidzakudyani. 39 Ngakhale iwo amene adzatsale adzatheratu mʼdziko la adani awo chifukwa cha machimo awo ndi machimo a makolo awo. 40 “ ‘Tsono adzawulula machimo awo ndi machimo a makolo awo, kusakhulupirika kwawo ndi mayendedwe awo otsutsana nane, 41 zomwe zinandipangitsa kuwafulatira ndi kuwapereka mʼmanja mwa adani awo. Ndipo mitima yawo yowumayo ikadzadzichepetsa ndi kuvomera kulangidwa chifukwa cha machimo awo, 42 Ine ndidzakumbukira pangano langa ndi Yakobo, pangano langa ndi Isake, pangano langa ndi Abrahamu. Ndidzakumbukiranso dzikolo. 43 Pakuti adzasiya dziko lawo lopanda anthu, nthaka idzakondwerera zaka zake zoyipumuza pamene iwo kudzakhala kulibe. Koma adzalangidwa chifukwa cha machimo awo popeza anakana malamulo anga ndipo mitima yawo inkayipidwa nawo malangizo anga. 44 Komabe ngakhale adzachite zonsezi ali mʼdziko la adani awo, Ine sindidzawakana kapena kuyipidwa nawo kwakuti nʼkuwawononga kwathunthu ndi kuthetsa pangano langa ndi iwo. Ine ndine Yehova Mulungu wawo. 45 Koma powachitira chifundo, ndidzakumbukira pangano langa ndi makolo awo amene ndinawatulutsa mʼdziko la Igupto mitundu ina ikuona kuti Ine ndikhale Mulungu wawo. Ine ndine Yehova.’ ” 46 Amenewa ndi malamulo ndi malangizo amene Yehova anawayika pakati pa Iye mwini ndi Aisraeli pa Phiri la Sinai kudzera mwa Mose.

In Other Versions

Leviticus 26 in the ANGEFD

Leviticus 26 in the ANTPNG2D

Leviticus 26 in the AS21

Leviticus 26 in the BAGH

Leviticus 26 in the BBPNG

Leviticus 26 in the BBT1E

Leviticus 26 in the BDS

Leviticus 26 in the BEV

Leviticus 26 in the BHAD

Leviticus 26 in the BIB

Leviticus 26 in the BLPT

Leviticus 26 in the BNT

Leviticus 26 in the BNTABOOT

Leviticus 26 in the BNTLV

Leviticus 26 in the BOATCB

Leviticus 26 in the BOATCB2

Leviticus 26 in the BOBCV

Leviticus 26 in the BOCNT

Leviticus 26 in the BOECS

Leviticus 26 in the BOHCB

Leviticus 26 in the BOHCV

Leviticus 26 in the BOHLNT

Leviticus 26 in the BOHNTLTAL

Leviticus 26 in the BOICB

Leviticus 26 in the BOILNTAP

Leviticus 26 in the BOITCV

Leviticus 26 in the BOKCV

Leviticus 26 in the BOKCV2

Leviticus 26 in the BOKHWOG

Leviticus 26 in the BOKSSV

Leviticus 26 in the BOLCB

Leviticus 26 in the BOLCB2

Leviticus 26 in the BOMCV

Leviticus 26 in the BONAV

Leviticus 26 in the BONCB

Leviticus 26 in the BONLT

Leviticus 26 in the BONUT2

Leviticus 26 in the BOPLNT

Leviticus 26 in the BOSCB

Leviticus 26 in the BOSNC

Leviticus 26 in the BOTLNT

Leviticus 26 in the BOVCB

Leviticus 26 in the BOYCB

Leviticus 26 in the BPBB

Leviticus 26 in the BPH

Leviticus 26 in the BSB

Leviticus 26 in the CCB

Leviticus 26 in the CUV

Leviticus 26 in the CUVS

Leviticus 26 in the DBT

Leviticus 26 in the DGDNT

Leviticus 26 in the DHNT

Leviticus 26 in the DNT

Leviticus 26 in the ELBE

Leviticus 26 in the EMTV

Leviticus 26 in the ESV

Leviticus 26 in the FBV

Leviticus 26 in the FEB

Leviticus 26 in the GGMNT

Leviticus 26 in the GNT

Leviticus 26 in the HARY

Leviticus 26 in the HNT

Leviticus 26 in the IRVA

Leviticus 26 in the IRVB

Leviticus 26 in the IRVG

Leviticus 26 in the IRVH

Leviticus 26 in the IRVK

Leviticus 26 in the IRVM

Leviticus 26 in the IRVM2

Leviticus 26 in the IRVO

Leviticus 26 in the IRVP

Leviticus 26 in the IRVT

Leviticus 26 in the IRVT2

Leviticus 26 in the IRVU

Leviticus 26 in the ISVN

Leviticus 26 in the JSNT

Leviticus 26 in the KAPI

Leviticus 26 in the KBT1ETNIK

Leviticus 26 in the KBV

Leviticus 26 in the KJV

Leviticus 26 in the KNFD

Leviticus 26 in the LBA

Leviticus 26 in the LBLA

Leviticus 26 in the LNT

Leviticus 26 in the LSV

Leviticus 26 in the MAAL

Leviticus 26 in the MBV

Leviticus 26 in the MBV2

Leviticus 26 in the MHNT

Leviticus 26 in the MKNFD

Leviticus 26 in the MNG

Leviticus 26 in the MNT

Leviticus 26 in the MNT2

Leviticus 26 in the MRS1T

Leviticus 26 in the NAA

Leviticus 26 in the NASB

Leviticus 26 in the NBLA

Leviticus 26 in the NBS

Leviticus 26 in the NBVTP

Leviticus 26 in the NET2

Leviticus 26 in the NIV11

Leviticus 26 in the NNT

Leviticus 26 in the NNT2

Leviticus 26 in the NNT3

Leviticus 26 in the PDDPT

Leviticus 26 in the PFNT

Leviticus 26 in the RMNT

Leviticus 26 in the SBIAS

Leviticus 26 in the SBIBS

Leviticus 26 in the SBIBS2

Leviticus 26 in the SBICS

Leviticus 26 in the SBIDS

Leviticus 26 in the SBIGS

Leviticus 26 in the SBIHS

Leviticus 26 in the SBIIS

Leviticus 26 in the SBIIS2

Leviticus 26 in the SBIIS3

Leviticus 26 in the SBIKS

Leviticus 26 in the SBIKS2

Leviticus 26 in the SBIMS

Leviticus 26 in the SBIOS

Leviticus 26 in the SBIPS

Leviticus 26 in the SBISS

Leviticus 26 in the SBITS

Leviticus 26 in the SBITS2

Leviticus 26 in the SBITS3

Leviticus 26 in the SBITS4

Leviticus 26 in the SBIUS

Leviticus 26 in the SBIVS

Leviticus 26 in the SBT

Leviticus 26 in the SBT1E

Leviticus 26 in the SCHL

Leviticus 26 in the SNT

Leviticus 26 in the SUSU

Leviticus 26 in the SUSU2

Leviticus 26 in the SYNO

Leviticus 26 in the TBIAOTANT

Leviticus 26 in the TBT1E

Leviticus 26 in the TBT1E2

Leviticus 26 in the TFTIP

Leviticus 26 in the TFTU

Leviticus 26 in the TGNTATF3T

Leviticus 26 in the THAI

Leviticus 26 in the TNFD

Leviticus 26 in the TNT

Leviticus 26 in the TNTIK

Leviticus 26 in the TNTIL

Leviticus 26 in the TNTIN

Leviticus 26 in the TNTIP

Leviticus 26 in the TNTIZ

Leviticus 26 in the TOMA

Leviticus 26 in the TTENT

Leviticus 26 in the UBG

Leviticus 26 in the UGV

Leviticus 26 in the UGV2

Leviticus 26 in the UGV3

Leviticus 26 in the VBL

Leviticus 26 in the VDCC

Leviticus 26 in the YALU

Leviticus 26 in the YAPE

Leviticus 26 in the YBVTP

Leviticus 26 in the ZBP