Leviticus 5 (BOGWICC)
1 “ ‘Ngati munthu anayitanidwa ku bwalo kuti akachitire umboni pa zimene anaziona kapena kuzimva koma iye nʼkukana kuchitira umboni, munthu ameneyo wachimwa ndipo ayenera kulangidwa. 2 “ ‘Munthu akakhudza chinthu chilichonse chodetsedwa, monga nyama yakufa ya mʼthengo, kapena chiweto chakufa kapenanso chokwawa chakufa, ngakhale iyeyo wachikhudza mosadziwa, wasanduka wodetsedwa ndipo wachimwa. 3 “ ‘Munthu akakhudza choyipitsa munthu cha mtundu uliwonse, ndipo pochikhudzapo ndi kuyipitsidwa nacho mosadziwa, munthuyo adzakhala wopalamula akangodziwa chimene wachitacho. 4 “ ‘Munthu akalumbira mofulumira kapena mosasamala kuti adzachita chinthu, choyipa kapena chabwino, ngakhale kuti wachita izi mosadziwa kuti nʼkulakwa, pamene wazindira kulakwa kwake, iye adzakhalabe wopalamula akangodziwa chimene wachitacho. 5 “ ‘Pamene munthu wazindikira kuti wachimwa motere, awulule tchimo limene wachitalo. 6 Pambuyo pake, munthuyo abwere kwa Yehova ndi mwana wankhosa wamkazi kapena mbuzi kuti ikhale chopereka chopepesera tchimo ndipo wansembe achite mwambo wopepesera tchimo lomwe wachitalo. Tsono wansembe achite mwambo wopepesera tchimo la munthuyo. 7 “ ‘Ngati munthuyo alibe mwana wankhosa, abweretse njiwa ziwiri kapena nkhunda ziwiri kwa Yehova ngati chopereka chopepesera tchimo lake. Imodzi ikhale nsembe yopepesera tchimo, ndipo inayo ikhale nsembe yopsereza. 8 Tsono abwere nazo kwa wansembe, ndipo wansembeyo ayambe wapereka mbalame imodzi ngati yopepesera tchimo. Apotole khosi koma osayidula mutu, 9 kenaka awaze magazi a chopereka chopepesera tchimocho mʼmbali mwa guwa. Magazi ena onse awathire pa tsinde la guwa. Imeneyi ndi nsembe yopepesera tchimo. 10 Pambuyo pake wansembe apereke mbalame inayo kuti ikhale chopereka chopsereza potsata mwambo wake. Wansembe atatha kupereka nsembe yopepesera tchimo limene munthu uja wachita, wochimwayo adzakhululukidwa. 11 “ ‘Koma ngati munthuyo alibe njiwa ziwiri kapena nkhunda ziwiri, abweretse ufa wosalala wokwanira kilogalamu imodzi kuti ukhale chopereka chopepesera tchimo limene wachita. Asathiremo mafuta kapena lubani chifukwa ndi chopereka chopepesera tchimo. 12 Abweretse ufawo kwa wansembe ndipo wansembeyo atapeko dzanja limodzi kuti ukhale ufa wachikumbutso ndi kuwutentha pa guwa pamodzi ndi chopereka chopsereza kwa Yehova. Imeneyi ndi nsembe yopepesera tchimo. 13 Umu ndi mmene wansembe adzachitire mwambo wopepesera machimo ena aliwonse amene munthu wachita, ndipo munthuyo adzakhululukidwa. Zopereka zonse zotsala zidzakhala za wansembeyo monga momwe amachitira ndi chopereka chachakudya.’ ” 14 Yehova anawuza Mose kuti, 15 “Munthu akachita zinthu mosakhulupirika, nachimwa mosadziwa posapereka zinthu zopatulika zofunika kwa Yehova, munthuyo apereke kwa Yehova nsembe yopepesera machimo ake. Nsembeyo ikhale nkhosa yayimuna yopanda chilema ndipo mtengo wake ukhale wokwana masekeli oyenera a siliva pakawerengedwe ka ku Nyumba ya Mulungu. Imeneyi ndi nsembe yopepesera kupalamula. 16 Munthuyo ayenera kubweza zinthu zopatulika zimene sanaperekezo. Awonjezepo chimodzi mwa zigawo zisanu zilizonse ndi kuzipereka zonsezo kwa wansembe amene adzachita mwambo wopepesera machimo a munthuyo, popereka nkhosa yayimuna ija ngati nsembe yopepesera ndipo wochimwayo adzakhululukidwa. 17 “Ngati munthu wachimwa mosadziwa pochita chilichonse chimene Yehova salola, munthuyo ndi wopalamula ndithu, ndipo ayenera kulangidwa. 18 Abwere kwa wansembe ndi chopereka chopepesera kupalamula kwake. Chopereka chikhale nkhosa yayimuna yopanda chilema ndipo mtengo wake ukhale woyenera nsembe yopepesera kupalamula kumene anachimwa mosadziwako, ndipo munthuyo adzakhululukidwa. 19 Imeneyi ndi nsembe yopepesera kupalamula popeza munthuyo wapezeka wolakwa pamaso pa Yehova.”
In Other Versions
Leviticus 5 in the ANGEFD
Leviticus 5 in the ANTPNG2D
Leviticus 5 in the AS21
Leviticus 5 in the BAGH
Leviticus 5 in the BBPNG
Leviticus 5 in the BBT1E
Leviticus 5 in the BDS
Leviticus 5 in the BEV
Leviticus 5 in the BHAD
Leviticus 5 in the BIB
Leviticus 5 in the BLPT
Leviticus 5 in the BNT
Leviticus 5 in the BNTABOOT
Leviticus 5 in the BNTLV
Leviticus 5 in the BOATCB
Leviticus 5 in the BOATCB2
Leviticus 5 in the BOBCV
Leviticus 5 in the BOCNT
Leviticus 5 in the BOECS
Leviticus 5 in the BOHCB
Leviticus 5 in the BOHCV
Leviticus 5 in the BOHLNT
Leviticus 5 in the BOHNTLTAL
Leviticus 5 in the BOICB
Leviticus 5 in the BOILNTAP
Leviticus 5 in the BOITCV
Leviticus 5 in the BOKCV
Leviticus 5 in the BOKCV2
Leviticus 5 in the BOKHWOG
Leviticus 5 in the BOKSSV
Leviticus 5 in the BOLCB
Leviticus 5 in the BOLCB2
Leviticus 5 in the BOMCV
Leviticus 5 in the BONAV
Leviticus 5 in the BONCB
Leviticus 5 in the BONLT
Leviticus 5 in the BONUT2
Leviticus 5 in the BOPLNT
Leviticus 5 in the BOSCB
Leviticus 5 in the BOSNC
Leviticus 5 in the BOTLNT
Leviticus 5 in the BOVCB
Leviticus 5 in the BOYCB
Leviticus 5 in the BPBB
Leviticus 5 in the BPH
Leviticus 5 in the BSB
Leviticus 5 in the CCB
Leviticus 5 in the CUV
Leviticus 5 in the CUVS
Leviticus 5 in the DBT
Leviticus 5 in the DGDNT
Leviticus 5 in the DHNT
Leviticus 5 in the DNT
Leviticus 5 in the ELBE
Leviticus 5 in the EMTV
Leviticus 5 in the ESV
Leviticus 5 in the FBV
Leviticus 5 in the FEB
Leviticus 5 in the GGMNT
Leviticus 5 in the GNT
Leviticus 5 in the HARY
Leviticus 5 in the HNT
Leviticus 5 in the IRVA
Leviticus 5 in the IRVB
Leviticus 5 in the IRVG
Leviticus 5 in the IRVH
Leviticus 5 in the IRVK
Leviticus 5 in the IRVM
Leviticus 5 in the IRVM2
Leviticus 5 in the IRVO
Leviticus 5 in the IRVP
Leviticus 5 in the IRVT
Leviticus 5 in the IRVT2
Leviticus 5 in the IRVU
Leviticus 5 in the ISVN
Leviticus 5 in the JSNT
Leviticus 5 in the KAPI
Leviticus 5 in the KBT1ETNIK
Leviticus 5 in the KBV
Leviticus 5 in the KJV
Leviticus 5 in the KNFD
Leviticus 5 in the LBA
Leviticus 5 in the LBLA
Leviticus 5 in the LNT
Leviticus 5 in the LSV
Leviticus 5 in the MAAL
Leviticus 5 in the MBV
Leviticus 5 in the MBV2
Leviticus 5 in the MHNT
Leviticus 5 in the MKNFD
Leviticus 5 in the MNG
Leviticus 5 in the MNT
Leviticus 5 in the MNT2
Leviticus 5 in the MRS1T
Leviticus 5 in the NAA
Leviticus 5 in the NASB
Leviticus 5 in the NBLA
Leviticus 5 in the NBS
Leviticus 5 in the NBVTP
Leviticus 5 in the NET2
Leviticus 5 in the NIV11
Leviticus 5 in the NNT
Leviticus 5 in the NNT2
Leviticus 5 in the NNT3
Leviticus 5 in the PDDPT
Leviticus 5 in the PFNT
Leviticus 5 in the RMNT
Leviticus 5 in the SBIAS
Leviticus 5 in the SBIBS
Leviticus 5 in the SBIBS2
Leviticus 5 in the SBICS
Leviticus 5 in the SBIDS
Leviticus 5 in the SBIGS
Leviticus 5 in the SBIHS
Leviticus 5 in the SBIIS
Leviticus 5 in the SBIIS2
Leviticus 5 in the SBIIS3
Leviticus 5 in the SBIKS
Leviticus 5 in the SBIKS2
Leviticus 5 in the SBIMS
Leviticus 5 in the SBIOS
Leviticus 5 in the SBIPS
Leviticus 5 in the SBISS
Leviticus 5 in the SBITS
Leviticus 5 in the SBITS2
Leviticus 5 in the SBITS3
Leviticus 5 in the SBITS4
Leviticus 5 in the SBIUS
Leviticus 5 in the SBIVS
Leviticus 5 in the SBT
Leviticus 5 in the SBT1E
Leviticus 5 in the SCHL
Leviticus 5 in the SNT
Leviticus 5 in the SUSU
Leviticus 5 in the SUSU2
Leviticus 5 in the SYNO
Leviticus 5 in the TBIAOTANT
Leviticus 5 in the TBT1E
Leviticus 5 in the TBT1E2
Leviticus 5 in the TFTIP
Leviticus 5 in the TFTU
Leviticus 5 in the TGNTATF3T
Leviticus 5 in the THAI
Leviticus 5 in the TNFD
Leviticus 5 in the TNT
Leviticus 5 in the TNTIK
Leviticus 5 in the TNTIL
Leviticus 5 in the TNTIN
Leviticus 5 in the TNTIP
Leviticus 5 in the TNTIZ
Leviticus 5 in the TOMA
Leviticus 5 in the TTENT
Leviticus 5 in the UBG
Leviticus 5 in the UGV
Leviticus 5 in the UGV2
Leviticus 5 in the UGV3
Leviticus 5 in the VBL
Leviticus 5 in the VDCC
Leviticus 5 in the YALU
Leviticus 5 in the YAPE
Leviticus 5 in the YBVTP
Leviticus 5 in the ZBP