Luke 22 (BOGWICC)

1 Phwando la buledi wopanda yisiti lotchedwa Paska litayandikira, 2 akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo amafunafuna mpata woti amuphere Yesu, pakuti ankachita mantha ndi anthu. 3 Kenaka Satana analowa mwa Yudasi, wotchedwa Isikarioti, mmodzi wa khumi ndi a iwiriwo. 4 Ndipo Yudasi anapita kwa akulu a ansembe ndi akulu oyangʼanira Nyumba ya Mulungu ndi kukambirana nawo za mmene iye angaperekere Yesu. 5 Iwo anakondwa ndipo anagwirizana zomupatsa ndalama. 6 Iye anavomera, ndipo anayamba kufunafuna mpata wabwino wakuti amupereke Yesu kwa iwo pamene panalibe gulu la anthu pafupi. 7 Kenaka linafika tsiku la buledi wopanda yisiti pamene mwana wankhosa wa Paska amaperekedwa nsembe. 8 Yesu anatuma Petro ndi Yohane nati, “Pitani kukatikonzera Paska kuti tikadye.” 9 Iwo anafunsa kuti, “Kodi mukufuna tikakonzere kuti?” 10 Iye anayankha kuti, “Taonani, mukamalowa mu mzinda, mudzakumana ndi mwamuna atanyamula mtsuko wamadzi. Mulondoleni ku nyumba imene akalowe, 11 ndipo mukamuwuze mwini nyumbayo kuti, ‘Aphunzitsi kufunsa kuti, chili kuti chipinda cha alendo, kumene Ine ndi ophunzira anga tikadyere Paska?’ 12 Iyeyo adzakuonetsani chipinda chachikulu chapamwamba, chokhala ndi zonse. Kachiteni zokonzekera mʼmenemo.” 13 Iwo anapita nakapeza zinthu monga mmene Yesu anawawuzira. Tsono anakonza Paska. 14 Ora litakwana, Yesu ndi ophunzira ake anakhala pa tebulo. 15 Ndipo Iye anawawuza kuti, “Ine ndakhala ndikuyembekezera kudya Paska uyu ndi inu ndisanamve zowawa. 16 Pakuti Ine ndikukuwuzani kuti sindidzadyanso Paska wina mpaka Paskayi itakwaniritsidwa mu ufumu wa Mulungu.” 17 Atanyamula chikho, Iye anayamika ndipo anati, “Tengani ndipo patsiranani pakati panu. 18 Pakuti ndikukuwuzani kuti, Ine sindidzamwanso zochokera ku chipatso cha mphesa mpaka ufumu wa Mulungu utabwera.” 19 Ndipo Iye anatenga buledi, nayamika ndipo anamunyema, nagawira iwo nati, “Ili ndi thupi langa lomwe laperekedwa kwa inu; muzichita zimenezi pokumbukira Ine.” 20 Chimodzimodzinso, utatha mgonero, anatenga chikho nati, “Chikho ichi ndi pangano latsopano la magazi anga, amene akhetsedwa chifukwa cha inu. 21 Koma dzanja la amene akundipereka Ine lili pamodzi ndi langa pa chakudya pano. 22 Mwana wa Munthu apita monga mmene zinalembedwera, koma tsoka kwa munthu amene amupereka Iye.” 23 Iwo anayamba kufunsana pakati pawo kuti ndi ndani wa iwo amene akanachita ichi. 24 Komanso mkangano unabuka pakati pawo kuti ndani mwa iwo amene amaganiziridwa kukhala wamkulu. 25 Yesu anawawuza kuti, “Mafumu a anthu a mitundu ina amaonetsa mphamvu za ufumu wawo pa anthuwo; ndipo amene ali ndi ulamuliro, amapatsidwa dzina la kuti ‘Opindula.’ 26 Koma inu simuyenera kukhala choncho. Mʼmalo mwake, wamkulu pakati panu akhale ngati wamngʼono pa onse, ndipo iye amene alamulira akhale ngati wotumikira. 27 Pakuti wamkulu ndani, iye amene ali pa tebulo kapena iye amene akutumikira? Kodi si iye amene ali pa tebulo? Koma ndili pakati panu ngati mmodzi wokutumikirani. 28 Inu ndinu amene mwayima nane mʼmayesero. 29 Ndipo Ine ndikupatsani inu ufumu, monga momwe Atate anga anandipatsiranso Ine, 30 kuti inu muthe kudya ndi kumwa pa tebulo langa mu ufumu wanga ndi kukhala pa mipando yaufumu kuweruza mafuko khumi ndi awiri a Israeli.” 31 “Simoni, Simoni, Satana wapempha kuti akupete ngati tirigu. 32 Koma Ine ndakupempherera Simoni, kuti chikhulupiriro chako chisafowoke ndipo pamene udzabwerera kwa Ine, udzalimbikitse abale ako.” 33 Koma iye anayankha kuti, “Ambuye, ndine wokonzeka kupita nanu ku ndende ndi kufa komwe.” 34 Yesu anayankha kuti, “Ine ndikukuwuza Petro, tambala asanalire lero lino, udzandikana katatu kuti sukundidziwa Ine.” 35 Kenaka Yesu anawafunsa iwo kuti, “Ine nditakutumizani wopanda chikwama cha ndalama, thumba kapena nsapato, kodi inu munasowa kanthu?”Iwo anayankha kuti, “Palibe chimene tinasowa.” 36 Iye anawawuza kuti, “Koma tsopano ngati muli ndi chikwama cha ndalama, chitengeni, ndiponso thumba. Ndipo ngati mulibe lupanga, gulitsani mkanjo wanu ndi kugula. 37 Zalembedwa kuti, ‘Ndipo Iye anawerengedwa pamodzi ndi anthu ochimwa,’ ndipo Ine ndikuwuzani kuti izi ziyenera kukwaniritsidwa mwa Ine. Inde, zimene zinalembedwa za Ine, zikukwaniritsidwa.” 38 Ophunzira anati, “Taonani Ambuye, awa malupanga awiri.”Iye anayankha kuti, “Amenewa akwanira.” 39 Yesu anapitanso monga mwa masiku onse ku Phiri la Olivi, ndipo ophunzira ake anamutsatira Iye. 40 Atafika pamalopo, Iye anawawuza kuti, “Pempherani kuti musagwe mʼmayesero.” 41 Iye anapita patsogolo pangʼono patali ngati kuponya mwala, anagwada napephera kuti, 42 “Atate ngati mukufuna chotsereni chikho ichi. Komatu muchite zimene mukufuna osati zimene ndikufuna ine.” 43 Mngelo wochokera kumwamba anafika namulimbikitsa. 44 Ndipo mopsinjika mtima, anapemphera moona mtima, ndipo thukuta lake linali ngati madontho a magazi akugwera pansi. 45 Iye atamaliza kupemphera, ndi kubwerera kwa ophunzira ake, anawapeza atagona atafowoka ndi chisoni. 46 Iye anafunsa kuti, Nʼchifukwa chiyani mukugona? “Dzukani ndipo pempherani kuti inu musagwe mʼmayesero.” 47 Pamene Iye ankayankhulabe, gulu la anthu linabwera, ndipo munthu wotchedwa Yudasi, mmodzi wa khumi ndi awiriwo analitsogolera. Iye anamuyandikira Yesu kuti amupsompsone. 48 Koma Yesu anamufunsa kuti, “Yudasi, kodi ukupereka Mwana wa Munthu ndi mpsopsono?” 49 Otsatira Yesu ataona zimene zimati zichitike, anati, “Ambuye, kodi timenyane ndi malupanga athu?” 50 Ndipo mmodzi wa iwo anatema wantchito wamkulu wa ansembe, nadula khutu lake lamanja. 51 Koma Yesu anayankha kuti, “Zisachitikenso zimenezi!” Ndipo Iye anakhudza khutu la munthuyo ndi kumuchiritsa. 52 Kenaka Yesu anafunsa akulu a ansembe, akuluakulu oyangʼanira Nyumba ya Mulungu ndi akuluakulu ena amene anabwerawo kuti, “Kodi Ine ndikutsogolera gulu lowukira kuti mubwere ndi malupanga ndi zibonga? 53 Tsiku lililonse ndinali nanu mʼmabwalo a mʼNyumba ya Mulungu ndipo inu simunandigwire. Koma iyi ndi nthawi yanu pamene mdima ukulamulira.” 54 Pamenepo anamugwira Iye, napita naye ndipo anamutengera ku nyumba ya mkulu wa ansembe. Petro anamutsatira patali. 55 Koma pamene anasonkha moto pakati pa bwalo la milandu, anakhala onse pansi ndipo Petro anakhalanso pansi. 56 Mtsikana wantchito anamuona atakhala nawo pafupi ndi moto. Iye anamuyangʼanitsitsa ndipo anati, “Munthu uyu anali ndi Yesu.” 57 Koma Petro anakana nati, “Mtsikana, ine sindimudziwa ameneyu.” 58 Patatha kanthawi pangʼono, wina wake anamuona ndipo anati, “Iwenso ndiwe mmodzi mwa iwo.”Petro anayankha kuti, “Munthu iwe, ayi sindine.” 59 Patatha pafupifupi ora limodzi, munthu winanso anati, “Zoonadi, munthu uyu anali ndi Iye, pakuti ndi mu Galileya.” 60 Petro anayankha kuti, “Munthu iwe, sindikudziwa zimene ukunena apa.” Pamene iye ankayankhula, tambala analira. 61 Ambuye anachewuka namuyangʼanitsitsa Petro. Pamenepo Petro anakumbukira mawu amene Ambuye anayankhula kwa iye kuti, “Asanalire tambala lero lino, udzandikana Ine katatu.” 62 Ndipo iye anapita panja nakalira kwambiri. 63 Anthu amene ankalonda Yesu anayamba kumuchita chipongwe ndi kumumenya. 64 Anamumanga mʼmaso ndi kumufunsa kuti, “Tanenera! Wakumenya iwe ndi ndani?” 65 Ndipo iwo anamunena zachipongwe zambiri. 66 Kutacha, bungwe la akuluakulu, pamodzi ndi akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo, anakumana pamodzi, ndipo anamuyika Yesu patsogolo pawo. 67 Iwo anati, “Tiwuze, ngati ndiwe Khristu.”Yesu anayankha kuti, “Ine nditakuwuzani simungandikhulupirire. 68 Ine nditakufunsani inu, simungandiyankhe. 69 Koma kuyambira tsopano, Mwana wa Munthu adzakhala ku dzanja lamanja la Mulungu wamphamvu.” 70 Onse anafunsa kuti, “Ndiye kuti ndiwe Mwana wa Mulungu?”Iye anayankha kuti, “Mwanena ndinu kuti Ndine.” 71 Pamenepo iwo anati, “Nanga tikufuniranjinso umboni wina? Ife tamva kuchokera pa milomo yake.”

In Other Versions

Luke 22 in the ANGEFD

Luke 22 in the ANTPNG2D

Luke 22 in the AS21

Luke 22 in the BAGH

Luke 22 in the BBPNG

Luke 22 in the BBT1E

Luke 22 in the BDS

Luke 22 in the BEV

Luke 22 in the BHAD

Luke 22 in the BIB

Luke 22 in the BLPT

Luke 22 in the BNT

Luke 22 in the BNTABOOT

Luke 22 in the BNTLV

Luke 22 in the BOATCB

Luke 22 in the BOATCB2

Luke 22 in the BOBCV

Luke 22 in the BOCNT

Luke 22 in the BOECS

Luke 22 in the BOHCB

Luke 22 in the BOHCV

Luke 22 in the BOHLNT

Luke 22 in the BOHNTLTAL

Luke 22 in the BOICB

Luke 22 in the BOILNTAP

Luke 22 in the BOITCV

Luke 22 in the BOKCV

Luke 22 in the BOKCV2

Luke 22 in the BOKHWOG

Luke 22 in the BOKSSV

Luke 22 in the BOLCB

Luke 22 in the BOLCB2

Luke 22 in the BOMCV

Luke 22 in the BONAV

Luke 22 in the BONCB

Luke 22 in the BONLT

Luke 22 in the BONUT2

Luke 22 in the BOPLNT

Luke 22 in the BOSCB

Luke 22 in the BOSNC

Luke 22 in the BOTLNT

Luke 22 in the BOVCB

Luke 22 in the BOYCB

Luke 22 in the BPBB

Luke 22 in the BPH

Luke 22 in the BSB

Luke 22 in the CCB

Luke 22 in the CUV

Luke 22 in the CUVS

Luke 22 in the DBT

Luke 22 in the DGDNT

Luke 22 in the DHNT

Luke 22 in the DNT

Luke 22 in the ELBE

Luke 22 in the EMTV

Luke 22 in the ESV

Luke 22 in the FBV

Luke 22 in the FEB

Luke 22 in the GGMNT

Luke 22 in the GNT

Luke 22 in the HARY

Luke 22 in the HNT

Luke 22 in the IRVA

Luke 22 in the IRVB

Luke 22 in the IRVG

Luke 22 in the IRVH

Luke 22 in the IRVK

Luke 22 in the IRVM

Luke 22 in the IRVM2

Luke 22 in the IRVO

Luke 22 in the IRVP

Luke 22 in the IRVT

Luke 22 in the IRVT2

Luke 22 in the IRVU

Luke 22 in the ISVN

Luke 22 in the JSNT

Luke 22 in the KAPI

Luke 22 in the KBT1ETNIK

Luke 22 in the KBV

Luke 22 in the KJV

Luke 22 in the KNFD

Luke 22 in the LBA

Luke 22 in the LBLA

Luke 22 in the LNT

Luke 22 in the LSV

Luke 22 in the MAAL

Luke 22 in the MBV

Luke 22 in the MBV2

Luke 22 in the MHNT

Luke 22 in the MKNFD

Luke 22 in the MNG

Luke 22 in the MNT

Luke 22 in the MNT2

Luke 22 in the MRS1T

Luke 22 in the NAA

Luke 22 in the NASB

Luke 22 in the NBLA

Luke 22 in the NBS

Luke 22 in the NBVTP

Luke 22 in the NET2

Luke 22 in the NIV11

Luke 22 in the NNT

Luke 22 in the NNT2

Luke 22 in the NNT3

Luke 22 in the PDDPT

Luke 22 in the PFNT

Luke 22 in the RMNT

Luke 22 in the SBIAS

Luke 22 in the SBIBS

Luke 22 in the SBIBS2

Luke 22 in the SBICS

Luke 22 in the SBIDS

Luke 22 in the SBIGS

Luke 22 in the SBIHS

Luke 22 in the SBIIS

Luke 22 in the SBIIS2

Luke 22 in the SBIIS3

Luke 22 in the SBIKS

Luke 22 in the SBIKS2

Luke 22 in the SBIMS

Luke 22 in the SBIOS

Luke 22 in the SBIPS

Luke 22 in the SBISS

Luke 22 in the SBITS

Luke 22 in the SBITS2

Luke 22 in the SBITS3

Luke 22 in the SBITS4

Luke 22 in the SBIUS

Luke 22 in the SBIVS

Luke 22 in the SBT

Luke 22 in the SBT1E

Luke 22 in the SCHL

Luke 22 in the SNT

Luke 22 in the SUSU

Luke 22 in the SUSU2

Luke 22 in the SYNO

Luke 22 in the TBIAOTANT

Luke 22 in the TBT1E

Luke 22 in the TBT1E2

Luke 22 in the TFTIP

Luke 22 in the TFTU

Luke 22 in the TGNTATF3T

Luke 22 in the THAI

Luke 22 in the TNFD

Luke 22 in the TNT

Luke 22 in the TNTIK

Luke 22 in the TNTIL

Luke 22 in the TNTIN

Luke 22 in the TNTIP

Luke 22 in the TNTIZ

Luke 22 in the TOMA

Luke 22 in the TTENT

Luke 22 in the UBG

Luke 22 in the UGV

Luke 22 in the UGV2

Luke 22 in the UGV3

Luke 22 in the VBL

Luke 22 in the VDCC

Luke 22 in the YALU

Luke 22 in the YAPE

Luke 22 in the YBVTP

Luke 22 in the ZBP