Nehemiah 13 (BOGWICC)

1 Pa tsiku limenelo anawerenga buku la Mose anthu akumva. Ndipo anapeza mawu akuti, Mwamoni kapena Mmowabu asalowe konse mu msonkhano wa Mulungu. 2 Paja iwowa sanawachingamire Aisraeli kukawapatsa chakudya ndi madzi. Mʼmalo mwake analemba ganyu Baalamu kuti adzawatemberere. Komabe Mulungu wathu anasandutsa tembererolo kukhala mdalitso. 3 Anthu atamva lamuloli, anachotsa pakati pawo onse amene anali achilendo. 4 Izi zisanachitike, wansembe Eliyasibu anali atasankhidwa kukhala woyangʼanira zipinda zosungiramo katundu za Nyumba ya Mulungu. Iyeyu ankagwirizana kwambiri ndi Tobiya. 5 Choncho anamupatsa chipinda chachikulu chimene kale ankasungamo zopereka zakudya, lubani, ziwiya, zopereka za chakhumi za tirigu, vinyo ndi mafuta zoyenera kuperekedwa kwa Alevi, oyimba nyimbo ndi alonda a ku Nyumba ya Mulungu, komanso mphatso zoyenera kupereka kwa ansembe. 6 Koma pamene izi zonse zinkachitika mu Yerusalemu, ine kunalibe popeza mʼchaka cha 32 cha Aritasasita mfumu ya Babuloni ine ndinabwerera kwa mfumu. Patapitanso nthawi ndinapempha chilolezo kwa mfumuyo 7 ndipo ndinabwerera ku Yerusalemu. Kumeneko ndinamva za chinthu choyipa chimene Eliyasibu anachita pomupatsa Tobiya chipinda mʼbwalo la Nyumba ya Mulungu. 8 Ndinapsa mtima kwambiri ndipo ndinataya kunja katundu yense wa Tobiya amene anali mʼchipindamo. 9 Ndinalamulira kuti ayeretse zipinda, ndipo kenaka ndinabwezeramo zida za mʼNyumba ya Mulungu, pamodzi ndi chopereka cha zakudya ndi lubani. 10 Ndinapezanso kuti Alevi sankalandira magawo awo amene amayera kulandira. Chotsatira chake Alevi onse pamodzi ndi oyimba nyimbo amene ankagwira ku Nyumba ya Mulungu anathawa, aliyense kupita ku munda wake. 11 Choncho ndinadzudzula akuluakulu aja ndipo ndinawafunsa kuti, “Nʼchifukwa chiyani Nyumba ya Mulungu yasiyidwa?” Ndipo ine ndinawayitanitsa pamodzi ndi kuwayika mʼmalo awo. 12 Pambuyo pake Ayuda anayambanso kubwera ndi zopereka zawo za chakhumi cha tirigu, vinyo ndi mafuta kuti ziperekedwe ku nyumba yosungiramo chuma. 13 Ndipo ndinasankha wansembe Selemiya, mlembi Zadoki, ndi Mlevi wotchedwa Pedaya kukhala oyangʼanira zipinda zosungiramo. Ndinasankhanso Hanani mwana wa Zakuri mwana wa Mataniya kukhala wowathandizira chifukwa ndinaona kuti anthu awa anali odalirika. Ntchito yawo inali yogawira abale awo zinthu zofunika. 14 Inu Mulungu wanga, mundikumbukire pa zimenezi, ndipo musafafanize ntchito zanga zimene ndachita mokhulupirika pa Nyumba yanu pofuna kukutumikirani. 15 Nthawi imeneyo ndinaona anthu a mu Yuda akuponda ndi kufinya mphesa pa tsiku la Sabata. Ena ankawunjika tirigu milumilu ndi kumasenzetsa abulu. Enanso ankabwera ndi vinyo, mphesa, mkuyu ndi katundu wa mitundumitundu ku Yerusalemu pa tsiku la Sabata. Choncho ndinawachenjeza za kugulitsa zakudya pa tsiku la Sabata. 16 Nawonso anthu a ku Turo amene ankakhala mu Yerusalemu ankabweretsa nsomba ndi akatundu ena onse amalonda kudzagulitsa pa Sabata kwa anthu a mʼdziko la Yuda ndi a mu Yerusalemu. 17 Ndipo ndinadzudzula anthu olemekezeka a dziko la Yuda. Ndinawafunsa kuti, “Nʼchoyipa chanji mukuchitachi, kumayipitsa tsiku la Sabata chotere? 18 Makolo anu anachita zomwezi ndipo Mulungu wathu anadzetsa mavuto pa ife ndi pa mzinda uwu. Kodi inu mukufuna kuwutsanso mkwiyo wa Mulungu pa Israeli pamene mukudetsa tsiku la Sabata?” 19 Nʼchifukwa chake ndikulamula kuti pamene kuyamba kuda, tsiku la Sabata lisanayambe, azitseka zipata zonse za Yerusalemu ndipo asazitsekule mpaka sabata litatha. Ndinayika ena mwa antchito anga oyangʼanira pa zipata kuti katundu aliyense asalowe mu Yerusalemu pa tsiku la Sabata. 20 Choncho kamodzi kapena kawiri anthu amalonda ndi anthu ogulitsa katundu osiyanasiyana ankagona usiku wonse kunja kwa Yerusalemu. 21 Koma ndinawachenjeza ndi kuwafunsa kuti, “Nʼchifukwa chiyani mukugona pafupi ndi khoma? Ngati muchitanso zimenezi, ine ndidzakugwirani.” Kuyambira nthawi imeneyo, sanabwerenso pa tsiku la Sabata. 22 Ndipo ndinalamulira Alevi kuti adziyeretse okha ndi kubwera kudzalonda pa zipata ndi cholinga choti tsiku la Sabata likhale tsiku loyera. Inu Mulungu wanga, kumbukireninso ine pa zimenezi ndipo mundisunge malingana ndi chikondi chanu chachikulu chosasinthika. 23 Masiku amenewo ndinaonanso anthu a ku Yuda amene anakwatira akazi ochokera ku Asidodi, Amoni ndi Mowabu. 24 Theka la ana awo linkayankhula chiyankhulo cha Asidodi kapena chiyankhulo chimodzi cha anthu ena, ndipo sankathanso kuyankhula chiyankhulo cha Ayuda. 25 Tsono ndinakangana nawo ndi kuwatemberera. Ndinamenya ena mwa anthuwo ndi kuzula tsitsi lawo. Ine ndinawalumbiritsa mʼdzina la Mulungu kuti, “Inu musapereke ana anu aakazi kuti akwatiwe ndi ana awo aamuna kapena inuyo ngakhale ana anu aamuna kukwatira ana awo aakazi. 26 Kodi Solomoni mfumu ya Israeli suja anachimwa chifukwa cha ukwati ngati umenewu. Pakati pa mitundu yambiri panalibe mfumu ngati iyi. Iye anakondedwa ndi Mulungu wake, ndipo Mulungu anamuyika kukhala mfumu ya Israeli yense, koma iyeyo anachimwa chifukwa cha akazi achilendo. 27 Kodi tsopano ife tizimva inu kuti mukuchita choyipa chachikulu chimenechi, kupandukira Yehova Mulungu wathu pomakwatira akazi achilendo?” 28 Mmodzi mwa ana aamuna a Yehoyada mwana Eliyasibu mkulu wa ansembe nʼkuti nthawi imeneyi ali mpongozi wa Sanibalati wa ku Horoni. Choncho ndinamuthamangitsa pamaso panga. 29 Inu Mulungu wanga, mukumbukire mmene iwo anayipitsira unsembe, pangano la unsembe komanso la Alevi. 30 Motero ndinayeretsa ansembe ndi Alevi powachotsera kalikonse kachilendo. Ndipo ndinakhazikitsa ntchito zawo, kuti aliyense akhale pa ntchito yake. 31 Ndiponso kupereka nkhuni ndi zipatso zoyamba kucha pa nthawi yake. Ndikumbukireni pondikomera mtima, Inu Mulungu wanga.

In Other Versions

Nehemiah 13 in the ANGEFD

Nehemiah 13 in the ANTPNG2D

Nehemiah 13 in the AS21

Nehemiah 13 in the BAGH

Nehemiah 13 in the BBPNG

Nehemiah 13 in the BBT1E

Nehemiah 13 in the BDS

Nehemiah 13 in the BEV

Nehemiah 13 in the BHAD

Nehemiah 13 in the BIB

Nehemiah 13 in the BLPT

Nehemiah 13 in the BNT

Nehemiah 13 in the BNTABOOT

Nehemiah 13 in the BNTLV

Nehemiah 13 in the BOATCB

Nehemiah 13 in the BOATCB2

Nehemiah 13 in the BOBCV

Nehemiah 13 in the BOCNT

Nehemiah 13 in the BOECS

Nehemiah 13 in the BOHCB

Nehemiah 13 in the BOHCV

Nehemiah 13 in the BOHLNT

Nehemiah 13 in the BOHNTLTAL

Nehemiah 13 in the BOICB

Nehemiah 13 in the BOILNTAP

Nehemiah 13 in the BOITCV

Nehemiah 13 in the BOKCV

Nehemiah 13 in the BOKCV2

Nehemiah 13 in the BOKHWOG

Nehemiah 13 in the BOKSSV

Nehemiah 13 in the BOLCB

Nehemiah 13 in the BOLCB2

Nehemiah 13 in the BOMCV

Nehemiah 13 in the BONAV

Nehemiah 13 in the BONCB

Nehemiah 13 in the BONLT

Nehemiah 13 in the BONUT2

Nehemiah 13 in the BOPLNT

Nehemiah 13 in the BOSCB

Nehemiah 13 in the BOSNC

Nehemiah 13 in the BOTLNT

Nehemiah 13 in the BOVCB

Nehemiah 13 in the BOYCB

Nehemiah 13 in the BPBB

Nehemiah 13 in the BPH

Nehemiah 13 in the BSB

Nehemiah 13 in the CCB

Nehemiah 13 in the CUV

Nehemiah 13 in the CUVS

Nehemiah 13 in the DBT

Nehemiah 13 in the DGDNT

Nehemiah 13 in the DHNT

Nehemiah 13 in the DNT

Nehemiah 13 in the ELBE

Nehemiah 13 in the EMTV

Nehemiah 13 in the ESV

Nehemiah 13 in the FBV

Nehemiah 13 in the FEB

Nehemiah 13 in the GGMNT

Nehemiah 13 in the GNT

Nehemiah 13 in the HARY

Nehemiah 13 in the HNT

Nehemiah 13 in the IRVA

Nehemiah 13 in the IRVB

Nehemiah 13 in the IRVG

Nehemiah 13 in the IRVH

Nehemiah 13 in the IRVK

Nehemiah 13 in the IRVM

Nehemiah 13 in the IRVM2

Nehemiah 13 in the IRVO

Nehemiah 13 in the IRVP

Nehemiah 13 in the IRVT

Nehemiah 13 in the IRVT2

Nehemiah 13 in the IRVU

Nehemiah 13 in the ISVN

Nehemiah 13 in the JSNT

Nehemiah 13 in the KAPI

Nehemiah 13 in the KBT1ETNIK

Nehemiah 13 in the KBV

Nehemiah 13 in the KJV

Nehemiah 13 in the KNFD

Nehemiah 13 in the LBA

Nehemiah 13 in the LBLA

Nehemiah 13 in the LNT

Nehemiah 13 in the LSV

Nehemiah 13 in the MAAL

Nehemiah 13 in the MBV

Nehemiah 13 in the MBV2

Nehemiah 13 in the MHNT

Nehemiah 13 in the MKNFD

Nehemiah 13 in the MNG

Nehemiah 13 in the MNT

Nehemiah 13 in the MNT2

Nehemiah 13 in the MRS1T

Nehemiah 13 in the NAA

Nehemiah 13 in the NASB

Nehemiah 13 in the NBLA

Nehemiah 13 in the NBS

Nehemiah 13 in the NBVTP

Nehemiah 13 in the NET2

Nehemiah 13 in the NIV11

Nehemiah 13 in the NNT

Nehemiah 13 in the NNT2

Nehemiah 13 in the NNT3

Nehemiah 13 in the PDDPT

Nehemiah 13 in the PFNT

Nehemiah 13 in the RMNT

Nehemiah 13 in the SBIAS

Nehemiah 13 in the SBIBS

Nehemiah 13 in the SBIBS2

Nehemiah 13 in the SBICS

Nehemiah 13 in the SBIDS

Nehemiah 13 in the SBIGS

Nehemiah 13 in the SBIHS

Nehemiah 13 in the SBIIS

Nehemiah 13 in the SBIIS2

Nehemiah 13 in the SBIIS3

Nehemiah 13 in the SBIKS

Nehemiah 13 in the SBIKS2

Nehemiah 13 in the SBIMS

Nehemiah 13 in the SBIOS

Nehemiah 13 in the SBIPS

Nehemiah 13 in the SBISS

Nehemiah 13 in the SBITS

Nehemiah 13 in the SBITS2

Nehemiah 13 in the SBITS3

Nehemiah 13 in the SBITS4

Nehemiah 13 in the SBIUS

Nehemiah 13 in the SBIVS

Nehemiah 13 in the SBT

Nehemiah 13 in the SBT1E

Nehemiah 13 in the SCHL

Nehemiah 13 in the SNT

Nehemiah 13 in the SUSU

Nehemiah 13 in the SUSU2

Nehemiah 13 in the SYNO

Nehemiah 13 in the TBIAOTANT

Nehemiah 13 in the TBT1E

Nehemiah 13 in the TBT1E2

Nehemiah 13 in the TFTIP

Nehemiah 13 in the TFTU

Nehemiah 13 in the TGNTATF3T

Nehemiah 13 in the THAI

Nehemiah 13 in the TNFD

Nehemiah 13 in the TNT

Nehemiah 13 in the TNTIK

Nehemiah 13 in the TNTIL

Nehemiah 13 in the TNTIN

Nehemiah 13 in the TNTIP

Nehemiah 13 in the TNTIZ

Nehemiah 13 in the TOMA

Nehemiah 13 in the TTENT

Nehemiah 13 in the UBG

Nehemiah 13 in the UGV

Nehemiah 13 in the UGV2

Nehemiah 13 in the UGV3

Nehemiah 13 in the VBL

Nehemiah 13 in the VDCC

Nehemiah 13 in the YALU

Nehemiah 13 in the YAPE

Nehemiah 13 in the YBVTP

Nehemiah 13 in the ZBP