Numbers 18 (BOGWICC)

1 Yehova anawuza Aaroni kuti, “Iwe, ana ako aamuna ndi banja la abambo ako mudzasenza tchimo la malo wopatulika, koma iwe ndi ana ako aamuna okha mudzasenza tchimo lokhudza unsembe wanu. 2 Ubweretse Alevi, abale ako, kuchokera ku fuko la abambo ako kuti azikhala ndi iwe ndi kumakuthandiza pamodzi ndi ana ako amuna pamene mukutumikira mu tenti ya umboni. 3 Iwowo azikutumikirani ndipo azichita ntchito zonse za ku tenti, koma asamafike pafupi ndi zipangizo za ku malo opatulika kapena guwa lansembe, kuopa kuti iwo ndi inu mungafe. 4 Azikhala ndi inu ndipo azisamalira ntchito yonse ya mu tenti ya msonkhano koma munthu wina aliyense wapadera sayenera kufika pafupi nanu. 5 “Inuyo muzisamalira malo wopatulika ndi guwa lansembe, kuti ukali wa Yehova usawagwerenso Aisraeli. 6 Ine mwini ndasankha Alevi, abale ako, pakati pa Aisraeli ngati mphatso yako ndipo aperekedwa kwa Yehova kuti azigwira ntchito ku tenti ya msonkhano. 7 Koma iwe wekha ndi ana ako aamuna muzitumikira ngati ansembe ndi zina zonse zokhudza pa guwa lansembe ndi za mʼkati mwa malo wopatulika kwambiri. Ndikukupatsani mphatso ya utumiki wa unsembe. Aliyense woyandikira malo wopatulika ayenera kuphedwa. 8 “Kenaka Yehova anati kwa Aaroni, ona, Ine mwini ndikukuyika kuti ukhale woyangʼanira zopereka zobwera kwa Ine; zopereka zonse zopatulika za Aisraeli zimene amapereka kwa ine ndi kuzipereka kwa iwe ndi ana ako aamuna ngati gawo lanu la nthawi zonse. 9 Uzilandiranso gawo la zopereka zopatulika kwambiri zomwe sizinawotchedwe pa moto. Kuchokera pa mphatso zonse zimene amabweretsa kwa Ine ngati zopatulika kwambiri, nsembe zachakudya kapena nsembe zopepesera machimo, gawo limenelo ndi lako ndi ana ako aamuna. 10 Muzidya zimenezo ngati zinthu zopatulika kwambiri; mwamuna aliyense adyeko. Uzitenge kukhala zopatulika. 11 “Izinso ndi zako: chilichonse chopatulidwa kuchokera ku mphatso zoweyula za Aisraeli ndapereka kwa iwe ndi ana ako aamuna ndi aakazi ngati gawo lako la nthawi zonse. Aliyense wa mʼnyumba mwako amene ali woyeretsedwa monga mwa mwambo angathe kudyako. 12 “Ndikukupatsani mafuta onse abwino kwambiri a olivi ndi vinyo yense watsopano wabwino kwambiri ndi tirigu yense zomwe Aisraeli amapereka kwa Yehova ngati zipatso zoyamba pa zokolola zawo. 13 Zipatso zonse zoyamba kucha za mʼdziko lawo zomwe amapereka kwa Yehova zidzakhala zako. Aliyense mʼnyumba mwako amene ali woyeretsedwa angathe kudyako. 14 “Chilichonse mu Israeli chomwe chapatulidwira Yehova ndi chako. 15 Chilichonse choyamba kubadwa kwa munthu kaya nyama, chomwe chaperekedwa kwa Yehova ndi chako. Koma uyenera kuwombola mwana aliyense wamwamuna ndi mwana aliyense woyamba wa nyama zodetsedwa. 16 Pamene zili ndi mwezi umodzi wa kubadwa, uziwombole pa mtengo wowombolera wa ndalama zisanu zasiliva, monga mwa ndalama za ku malo wopatulika. 17 “Koma usawombole ana oyamba kubadwa a ngʼombe, nkhosa kapena mbuzi. Iwo ndi opatulika. Uwaze magazi a nyamazi pa guwa lansembe ndi kutentha mafuta ake ngati nsembe yotentha ndi moto kuti likhale fungo lokoma kwa Yehova. 18 Nyama yake ikhale yanu monga momwe chimakhalira chidale cha nsembe yoweyula ndi ntchafu za miyendo ya kumanja, zonsezi ndi zako. 19 Zonse zimene mwazichotsa ku zopereka zoyera zomwe Aisraeli anapereka kwa Yehova ndazipereka kwa iwe ndi ana ako aamuna ndi aakazi ngati gawo lanu nthawi zonse. Ili ndi pangano losatha la mchere pamaso pa Yehova kwa iwe ndi ana ako.” 20 Ndipo Yehova anati kwa Aaroni, “Iweyo sudzakhala ndi cholowa mʼdziko lawo, ndiponso sudzalandira gawo lililonse pakati pawo. Ine ndine gawo lako ndi cholowa chako pakati pa Aisraeli. 21 “Taonani, ndawapatsa Alevi chakhumi chonse mu Israeli ngati cholowa chawo chifukwa cha ntchito ya ku tenti ya msonkhano. 22 Kuyambira tsopano mpaka mʼtsogolo Aisraeli asamapite pafupi ndi tenti ya msonkhano. Ngati atero adzasenza zotsatira za tchimo lawo ndipo adzafa. 23 Alevi ndi amene azidzagwira ntchito ya ku tenti ya msonkhano ndipo adzalangidwa chilichonse chikalakwika. Ili ndi lamulo losatha kwa mibado yawo yonse. Iwowo sadzalandira cholowa pakati pa Aisraeli. 24 Mʼmalo mwake, ndikuwapatsa Aleviwo chakhumi ngati cholowa chawo chimene Aisraeli amapereka kwa Yehova. Nʼchifukwa chake zokhudza iwo ndinati: ‘Sadzakhala ndi cholowa pakati pa Aisraeli.’ ” 25 Yehova anati kwa Mose, 26 “Yankhula ndi Alevi ndi kunena nawo kuti, ‘Pamene mulandira chakhumi kuchoka kwa Aisraeli chimene ndimakupatsani ngati cholowa chanu, muyenera kupereka chakhumi cha choperekacho kwa Yehova. 27 Chopereka chanucho chidzawerengedwa kwa inu ngati tirigu wochokera kopunthira kapena ngati mphesa zopsinya kuchokera kopsinyira mphesa. 28 Mwa njira imeneyi inunso muzipereka chopereka kwa Yehova kuchokera ku chakhumi chanu chilichonse chimene mumalandira kuchokera kwa Aisraeli. Kuchokera ku chakhumicho muziperekako gawo la Yehova kwa Aaroni, wansembe. 29 Muyenera kupereka monga gawo la Yehova magawo abwino kwambiri ndi opatulika a chilichonse chimene chapatsidwa kwa inu.’ 30 “Nena kwa Alevi: ‘Pamene mupereka gawo labwino lopambana zonse, gawo limenelo lidzawerengedwa kwa inu ngati lochokera popunthira tirigu kapenanso kopsinyira mphesa. 31 Inu ndi a pa banja panu mungathe kudyera zimenezi paliponse chifukwa ndi malipiro a ntchito yanu ya ku tenti ya msonkhano. 32 Popereka gawo labwino kwambirilo simudzapezeka olakwa. Mukatero simudzadetsa zopereka zoyera za Aisraeli, ndipo simudzafa.’ ”

In Other Versions

Numbers 18 in the ANGEFD

Numbers 18 in the ANTPNG2D

Numbers 18 in the AS21

Numbers 18 in the BAGH

Numbers 18 in the BBPNG

Numbers 18 in the BBT1E

Numbers 18 in the BDS

Numbers 18 in the BEV

Numbers 18 in the BHAD

Numbers 18 in the BIB

Numbers 18 in the BLPT

Numbers 18 in the BNT

Numbers 18 in the BNTABOOT

Numbers 18 in the BNTLV

Numbers 18 in the BOATCB

Numbers 18 in the BOATCB2

Numbers 18 in the BOBCV

Numbers 18 in the BOCNT

Numbers 18 in the BOECS

Numbers 18 in the BOHCB

Numbers 18 in the BOHCV

Numbers 18 in the BOHLNT

Numbers 18 in the BOHNTLTAL

Numbers 18 in the BOICB

Numbers 18 in the BOILNTAP

Numbers 18 in the BOITCV

Numbers 18 in the BOKCV

Numbers 18 in the BOKCV2

Numbers 18 in the BOKHWOG

Numbers 18 in the BOKSSV

Numbers 18 in the BOLCB

Numbers 18 in the BOLCB2

Numbers 18 in the BOMCV

Numbers 18 in the BONAV

Numbers 18 in the BONCB

Numbers 18 in the BONLT

Numbers 18 in the BONUT2

Numbers 18 in the BOPLNT

Numbers 18 in the BOSCB

Numbers 18 in the BOSNC

Numbers 18 in the BOTLNT

Numbers 18 in the BOVCB

Numbers 18 in the BOYCB

Numbers 18 in the BPBB

Numbers 18 in the BPH

Numbers 18 in the BSB

Numbers 18 in the CCB

Numbers 18 in the CUV

Numbers 18 in the CUVS

Numbers 18 in the DBT

Numbers 18 in the DGDNT

Numbers 18 in the DHNT

Numbers 18 in the DNT

Numbers 18 in the ELBE

Numbers 18 in the EMTV

Numbers 18 in the ESV

Numbers 18 in the FBV

Numbers 18 in the FEB

Numbers 18 in the GGMNT

Numbers 18 in the GNT

Numbers 18 in the HARY

Numbers 18 in the HNT

Numbers 18 in the IRVA

Numbers 18 in the IRVB

Numbers 18 in the IRVG

Numbers 18 in the IRVH

Numbers 18 in the IRVK

Numbers 18 in the IRVM

Numbers 18 in the IRVM2

Numbers 18 in the IRVO

Numbers 18 in the IRVP

Numbers 18 in the IRVT

Numbers 18 in the IRVT2

Numbers 18 in the IRVU

Numbers 18 in the ISVN

Numbers 18 in the JSNT

Numbers 18 in the KAPI

Numbers 18 in the KBT1ETNIK

Numbers 18 in the KBV

Numbers 18 in the KJV

Numbers 18 in the KNFD

Numbers 18 in the LBA

Numbers 18 in the LBLA

Numbers 18 in the LNT

Numbers 18 in the LSV

Numbers 18 in the MAAL

Numbers 18 in the MBV

Numbers 18 in the MBV2

Numbers 18 in the MHNT

Numbers 18 in the MKNFD

Numbers 18 in the MNG

Numbers 18 in the MNT

Numbers 18 in the MNT2

Numbers 18 in the MRS1T

Numbers 18 in the NAA

Numbers 18 in the NASB

Numbers 18 in the NBLA

Numbers 18 in the NBS

Numbers 18 in the NBVTP

Numbers 18 in the NET2

Numbers 18 in the NIV11

Numbers 18 in the NNT

Numbers 18 in the NNT2

Numbers 18 in the NNT3

Numbers 18 in the PDDPT

Numbers 18 in the PFNT

Numbers 18 in the RMNT

Numbers 18 in the SBIAS

Numbers 18 in the SBIBS

Numbers 18 in the SBIBS2

Numbers 18 in the SBICS

Numbers 18 in the SBIDS

Numbers 18 in the SBIGS

Numbers 18 in the SBIHS

Numbers 18 in the SBIIS

Numbers 18 in the SBIIS2

Numbers 18 in the SBIIS3

Numbers 18 in the SBIKS

Numbers 18 in the SBIKS2

Numbers 18 in the SBIMS

Numbers 18 in the SBIOS

Numbers 18 in the SBIPS

Numbers 18 in the SBISS

Numbers 18 in the SBITS

Numbers 18 in the SBITS2

Numbers 18 in the SBITS3

Numbers 18 in the SBITS4

Numbers 18 in the SBIUS

Numbers 18 in the SBIVS

Numbers 18 in the SBT

Numbers 18 in the SBT1E

Numbers 18 in the SCHL

Numbers 18 in the SNT

Numbers 18 in the SUSU

Numbers 18 in the SUSU2

Numbers 18 in the SYNO

Numbers 18 in the TBIAOTANT

Numbers 18 in the TBT1E

Numbers 18 in the TBT1E2

Numbers 18 in the TFTIP

Numbers 18 in the TFTU

Numbers 18 in the TGNTATF3T

Numbers 18 in the THAI

Numbers 18 in the TNFD

Numbers 18 in the TNT

Numbers 18 in the TNTIK

Numbers 18 in the TNTIL

Numbers 18 in the TNTIN

Numbers 18 in the TNTIP

Numbers 18 in the TNTIZ

Numbers 18 in the TOMA

Numbers 18 in the TTENT

Numbers 18 in the UBG

Numbers 18 in the UGV

Numbers 18 in the UGV2

Numbers 18 in the UGV3

Numbers 18 in the VBL

Numbers 18 in the VDCC

Numbers 18 in the YALU

Numbers 18 in the YAPE

Numbers 18 in the YBVTP

Numbers 18 in the ZBP