Numbers 21 (BOGWICC)

1 Mfumu ya Akanaani ya ku Aradi, imene inkakhala ku Negevi, itamva kuti Aisraeli akubwera kudzera msewu wopita ku Atarimu, inachita nkhondo ndi Aisraeli nigwira ena mwa iwo. 2 Ndipo Israeli anachita lonjezo ili kwa Yehova: “Mukapereka anthu awa mʼdzanja lathu ife tidzawonongeratu mizinda yawo.” 3 Yehova anamva pempho la Aisraeli ndipo anapereka Akanaaniwo kwa iwo. Anawawononga pamodzi ndi mizinda yawo. Kotero malowo anatchedwa Horima. 4 Aisraeli anayenda kuchokera ku phiri la Hori kudzera njira ya ku Nyanja Yofiira kuzungulira dziko la Edomu. Koma anthu anataya mtima mʼnjiramo 5 ndipo anayankhula motsutsana ndi Mulungu ndi Mose, nati, “Chifukwa chiyani munatitulutsa kuchoka mʼdziko la Igupto kuti tidzafere mʼchipululu muno? Kuno kulibe chakudya, kulibe madzi ndipo chakudya cha chabechabechi tatopa nacho.” 6 Choncho Yehova anatumiza njoka zaululu pakati pawo. Zinaluma anthu ndipo Aisraeli ambiri anafa. 7 Anthuwo anabwera kwa Mose ndi kunena kuti, “Tachimwa chifukwa tayankhula motsutsana ndi Yehova komanso inu. Pempherani kwa Yehova kuti atichotsere njokazi.” Tsono Mose anapempherera anthuwo. 8 Yehova anati kwa Mose, “Upange njoka yaululu ndipo uyipachike pa mtengo. Aliyense amene walumidwa akangoyangʼana njokayo adzakhala ndi moyo.” 9 Pamenepo Mose anapanga njoka yamkuwa ndi kuyipachika pa mtengo. Ndipo aliyense wolumidwa akayangʼana njoka yamkuwayo ankakhala ndi moyo. 10 Aisraeli anayendabe nakamanga misasa yawo ku Oboti. 11 Kenaka anasamuka ku Oboti nakamanga misasa yawo ku Iye-Abarimu, mʼchipululu chimene chili kummawa kwa Mowabu, kotulukira dzuwa. 12 Kuchoka kumeneko anayendabe nakamanga misasa yawo mʼchigwa cha Zeredi. 13 Anasamukanso kumeneko nakamanga moyandikana ndi Arinoni mʼdera limene lili mʼchipululu chimene chimafika mʼdziko la Aamori. Arinoni ndiwo malire a Mowabu ndi Aamori. 14 Nʼchifukwa chake Buku la Nkhondo za Yehova limati,“Mzinda wa Wahebu uli mu Sufa,mu zigwa za Arinoni, 15 ku matsitso a zigwaamene afika mpaka ku Arinakhudza malire a dziko la Mowabu.” 16 Kuchokera kumeneko anapitirira mpaka ku Beeri, pa chitsime chomwe Yehova anawuza Mose kuti, “Sonkhanitsa anthu pamodzi ndipo ndidzawapatsa madzi.” 17 Pamenepo Aisraeli anayimba nyimbo iyi:“Tulutsa madzi, chitsime iwe!Chiyimbireni nyimbo, 18 chitsime chomwe anakumba mafumu,chomwe anakumba anthu omveka,ndi ndodo zawo zaufumu ndi ndodo zawo zoyendera.”Kenaka anachoka ku chipululu ndi kupita ku Matana. 19 Kuchoka ku Matana anapita ku Nahalieli, kuchoka ku Nahalieli anapita ku Bamoti, 20 ndipo atachoka ku Bamoti anapita ku chigwa cha dziko la Mowabu kudzera njira ya pamwamba pa phiri la Pisiga, moyangʼanana ndi Yesimoni. 21 Aisraeli anatumiza amithenga kwa Sihoni mfumu ya Aamori, kuti, 22 “Tiloleni kuti tidutse mʼdziko mwanu. Sitidzapatukira mʼminda mwanu kapena mu mpesa wanu kapena kumwa madzi mʼchitsime chili chonse. Tidzayenda mu msewu waukulu wa mfumu mpaka titadutsa malire a dziko lanu.” 23 Koma Sihoni sanalole kuti Aisraeli adutse mʼdziko mwake. Iye anasonkhanitsa pamodzi ankhondo ake onse kuti akamenyane ndi Aisraeli mʼchipululu. Atafika pa Yahazi anamenyana ndi Aisraeli. 24 Koma Aisraeli anamupha ndi kulanda dziko lake kuchokera ku Arinoni mpaka ku Yaboki, kulekezera mʼmalire a dziko la Aamoni, chifukwa malire a dziko la Aamoni anali otetezedwa. 25 Ndipo Aisraeli analanda mizinda yonse ya Aamori, nakhalamo kuphatikizapo Hesiboni ndi midzi yake yozungulira. 26 Hesiboni unali mzinda wa Sihoni mfumu ya Aamori, yemwe anamenyana ndi mfumu yakale ya dziko la Mowabu. Lonselo linakhala dziko lake mpaka ku Arinoni. 27 Nʼchifukwa chake alakatuli amati:“Bwerani ku Hesiboni, mzindawo umangidwenso;mzinda wa Sihoni ukhazikike. 28 “Moto unabuka ku Hesiboni,malawi a moto kuchokera mu mzinda wa Sihoni.Unanyeketsa Ari mzinda wa ku Mowabu,nzika za ku malo okwera a Arinoni. 29 Tsoka kwa iwe Mowabu!Mwawonongedwa inu anthu a ku Kemosi!Ana ake aamuna wawasandutsa ngati anthu othawathawandipo ana ake aakazi ngati akapolo,akapolo a Sihoni, mfumu ya Aamori. 30 “Koma ife tawagonjetsa;Hesiboni wawonongedwa mʼnjira monse mpaka kufika ku Diboni.Tawaphwasula mpaka ku mzinda wa Nofa,mzinda womwe umafika ku Medeba. 31 “Choncho Aisraeli anakhala mʼdziko la Aamori.” 32 Mose atatumiza azondi ku Yazeri, Aisraeliwo analanda midzi yozungulira ndi kuthamangitsa Aamori omwe ankakhala kumeneko. 33 Kenaka anabwerera, nadzera njira ya ku Basani. Choncho Ogi mfumu ya ku Basani ndi gulu lake lonse lankhondo anatuluka kukakumana nawo ndipo anamenyana nawo ku Ederi. 34 Yehova anati kwa Mose, “Usachite naye mantha pakuti ndamupereka mʼmanja mwako pamodzi ndi gulu lake lonse lankhondo ndi dziko lake lomwe. Ndipo uchite kwa iye zimene unachita Sihoni mfumu ya Aamori, amene ankalamulira ku Hesiboni.” 35 Choncho Aisraeli anapha Ogi pamodzi ndi ana ake aamuna ndi gulu lake lonse la nkhondo. Palibe ndi mmodzi yemwe amene anatsala wamoyo, ndipo analanda dziko lakelo.

In Other Versions

Numbers 21 in the ANGEFD

Numbers 21 in the ANTPNG2D

Numbers 21 in the AS21

Numbers 21 in the BAGH

Numbers 21 in the BBPNG

Numbers 21 in the BBT1E

Numbers 21 in the BDS

Numbers 21 in the BEV

Numbers 21 in the BHAD

Numbers 21 in the BIB

Numbers 21 in the BLPT

Numbers 21 in the BNT

Numbers 21 in the BNTABOOT

Numbers 21 in the BNTLV

Numbers 21 in the BOATCB

Numbers 21 in the BOATCB2

Numbers 21 in the BOBCV

Numbers 21 in the BOCNT

Numbers 21 in the BOECS

Numbers 21 in the BOHCB

Numbers 21 in the BOHCV

Numbers 21 in the BOHLNT

Numbers 21 in the BOHNTLTAL

Numbers 21 in the BOICB

Numbers 21 in the BOILNTAP

Numbers 21 in the BOITCV

Numbers 21 in the BOKCV

Numbers 21 in the BOKCV2

Numbers 21 in the BOKHWOG

Numbers 21 in the BOKSSV

Numbers 21 in the BOLCB

Numbers 21 in the BOLCB2

Numbers 21 in the BOMCV

Numbers 21 in the BONAV

Numbers 21 in the BONCB

Numbers 21 in the BONLT

Numbers 21 in the BONUT2

Numbers 21 in the BOPLNT

Numbers 21 in the BOSCB

Numbers 21 in the BOSNC

Numbers 21 in the BOTLNT

Numbers 21 in the BOVCB

Numbers 21 in the BOYCB

Numbers 21 in the BPBB

Numbers 21 in the BPH

Numbers 21 in the BSB

Numbers 21 in the CCB

Numbers 21 in the CUV

Numbers 21 in the CUVS

Numbers 21 in the DBT

Numbers 21 in the DGDNT

Numbers 21 in the DHNT

Numbers 21 in the DNT

Numbers 21 in the ELBE

Numbers 21 in the EMTV

Numbers 21 in the ESV

Numbers 21 in the FBV

Numbers 21 in the FEB

Numbers 21 in the GGMNT

Numbers 21 in the GNT

Numbers 21 in the HARY

Numbers 21 in the HNT

Numbers 21 in the IRVA

Numbers 21 in the IRVB

Numbers 21 in the IRVG

Numbers 21 in the IRVH

Numbers 21 in the IRVK

Numbers 21 in the IRVM

Numbers 21 in the IRVM2

Numbers 21 in the IRVO

Numbers 21 in the IRVP

Numbers 21 in the IRVT

Numbers 21 in the IRVT2

Numbers 21 in the IRVU

Numbers 21 in the ISVN

Numbers 21 in the JSNT

Numbers 21 in the KAPI

Numbers 21 in the KBT1ETNIK

Numbers 21 in the KBV

Numbers 21 in the KJV

Numbers 21 in the KNFD

Numbers 21 in the LBA

Numbers 21 in the LBLA

Numbers 21 in the LNT

Numbers 21 in the LSV

Numbers 21 in the MAAL

Numbers 21 in the MBV

Numbers 21 in the MBV2

Numbers 21 in the MHNT

Numbers 21 in the MKNFD

Numbers 21 in the MNG

Numbers 21 in the MNT

Numbers 21 in the MNT2

Numbers 21 in the MRS1T

Numbers 21 in the NAA

Numbers 21 in the NASB

Numbers 21 in the NBLA

Numbers 21 in the NBS

Numbers 21 in the NBVTP

Numbers 21 in the NET2

Numbers 21 in the NIV11

Numbers 21 in the NNT

Numbers 21 in the NNT2

Numbers 21 in the NNT3

Numbers 21 in the PDDPT

Numbers 21 in the PFNT

Numbers 21 in the RMNT

Numbers 21 in the SBIAS

Numbers 21 in the SBIBS

Numbers 21 in the SBIBS2

Numbers 21 in the SBICS

Numbers 21 in the SBIDS

Numbers 21 in the SBIGS

Numbers 21 in the SBIHS

Numbers 21 in the SBIIS

Numbers 21 in the SBIIS2

Numbers 21 in the SBIIS3

Numbers 21 in the SBIKS

Numbers 21 in the SBIKS2

Numbers 21 in the SBIMS

Numbers 21 in the SBIOS

Numbers 21 in the SBIPS

Numbers 21 in the SBISS

Numbers 21 in the SBITS

Numbers 21 in the SBITS2

Numbers 21 in the SBITS3

Numbers 21 in the SBITS4

Numbers 21 in the SBIUS

Numbers 21 in the SBIVS

Numbers 21 in the SBT

Numbers 21 in the SBT1E

Numbers 21 in the SCHL

Numbers 21 in the SNT

Numbers 21 in the SUSU

Numbers 21 in the SUSU2

Numbers 21 in the SYNO

Numbers 21 in the TBIAOTANT

Numbers 21 in the TBT1E

Numbers 21 in the TBT1E2

Numbers 21 in the TFTIP

Numbers 21 in the TFTU

Numbers 21 in the TGNTATF3T

Numbers 21 in the THAI

Numbers 21 in the TNFD

Numbers 21 in the TNT

Numbers 21 in the TNTIK

Numbers 21 in the TNTIL

Numbers 21 in the TNTIN

Numbers 21 in the TNTIP

Numbers 21 in the TNTIZ

Numbers 21 in the TOMA

Numbers 21 in the TTENT

Numbers 21 in the UBG

Numbers 21 in the UGV

Numbers 21 in the UGV2

Numbers 21 in the UGV3

Numbers 21 in the VBL

Numbers 21 in the VDCC

Numbers 21 in the YALU

Numbers 21 in the YAPE

Numbers 21 in the YBVTP

Numbers 21 in the ZBP