Numbers 3 (BOGWICC)

1 Iyi ndi mbiri ya banja la Aaroni ndi Mose pa nthawi yomwe Yehova anayankhula ndi Mose pa phiri la Sinai. 2 Mayina a ana aamuna a Aaroni anali Nadabu, woyamba kubadwa, Abihu, Eliezara ndi Itamara. 3 Amenewa ndi mayina a ana aamuna a Aaroni, ansembe odzozedwa omwe anapatulidwa kuti azitumikira ngati ansembe. 4 Koma Nadabu ndi Abihu, anagwa nafa pamaso pa Yehova pamene ankapereka nsembe ndi moto wachilendo pamaso pa Yehova mʼchipululu cha Sinai. Iwowo analibe ana aamuna. Choncho Eliezara ndi Itamara ndiwo amene ankatumikira ngati ansembe nthawi imene Aaroni abambo awo anali moyo. 5 Yehova anati kwa Mose, 6 “Bweretsa fuko la Levi ndipo ulipereke kwa Aaroni wansembe kuti lizimutumikira. 7 Azigwira ntchito yothandiza iyeyo ndi gulu lonse ku tenti ya msonkhano pogwira ntchito ya ku Chihema. 8 Azisamalira zipangizo zonse za mu tenti ya msonkhano, ndipo azigwirira ntchito Aisraeli potumikira mu tenti. 9 Pereka Alevi kwa Aaroni ndi kwa ana ake aamuna. Amenewa ndiwo Aisraeli amene aperekedwa kwa iye kwathunthu. 10 Usankhe Aaroni ndi ana ake aamuna kuti azitumikira pa ntchito ya unsembe. Koma wina aliyense woyandikira malo opatulika aphedwe.” 11 Yehova anawuzanso Mose kuti, 12 “Pakati pa Aisraeli onse ndatenga Alevi kulowa mʼmalo mwa mwana wamwamuna aliyense woyamba kubadwa kwa amayi a Chiisraeli. Alevi ndi anga, 13 pakuti ana onse oyamba kubadwa ndi anga. Nditakantha ana onse oyamba kubadwa mu Igupto, ndinadzipatulira ndekha mwana aliyense woyamba kubadwa mu Israeli, wa munthu ndi nyama. Azikhala anga. Ine ndine Yehova.” 14 Yehova anawuza Mose mʼchipululu cha Sinai kuti, 15 “Werenga Alevi monga mwa mabanja awo ndi mafuko awo. Werenga mwamuna aliyense kuyambira wa mwezi umodzi kapena kupitirirapo.” 16 Choncho Mose anawawerenga potsatira zomwe Yehova anamulamulira. 17 Mayina a ana aamuna a Levi ndi awa:Geresoni, Kohati ndi Merari. 18 Mayina a ana a Geresoni potsata mabanja awo ndi awa:Libini ndi Simei. 19 Ana a Kohati potsata mabanja awo ndi awa:Amramu, Izihari, Hebroni ndi Uzieli. 20 Ana a Merari potsata mabanja awo ndi awa:Mali ndi Musi.Amenewa ndiwo anali mabanja a Alevi monga mwa makolo awo. 21 Kwa Geresoni kunali banja la Alibini, banja la Asimei. Amenewa ndiwo anali mabanja a Ageresoni. 22 Chiwerengero cha amuna onse amene anawawerenga a mwezi umodzi kapena kupitirirapo chinali 7,500. 23 Mabanja a Ageresoni azimanga misasa yawo kumadzulo, kumbuyo kwa Chihema. 24 Mtsogoleri wa mabanja a Ageresoni anali Eliyasafu mwana wa Laeli. 25 Ntchito imene Ageresoni anapatsidwa ku tenti ya msonkhano inali yosamalira Chihema ndi tenti, pamodzi ndi zophimbira zake, katani ya pa khomo la ku tenti ya msonkhano, 26 ndi makatani wotchinga bwalo, katani ya pa chipata cholowera ku bwalo lozungulira Chihema ndi guwa lansembe, zingwe ndi zonse zokhudzana ndi ntchito yawo. 27 Kwa Kohati kunali mabanja a Amramu, Aizihara, Ahebroni ndi Auzieli. Awa ndiye anali mabanja a Akohati. 28 Chiwerengero cha amuna onse a mwezi umodzi kapena kupitirirapo chinali 8,600. Akohati ankagwira ntchito yosamalira malo wopatulika. 29 Mabanja a ana a Kohati ankamanga misasa yawo kummwera kwa Chihema. 30 Mtsogoleri wa magulu a mabanja a Kohati anali Elizafani mwana wa Uzieli. 31 Iwo ankagwira ntchito yosamalira Bokosi la Chipangano, tebulo, choyikapo nyale, maguwa, zipangizo za kumalo wopatulika zimene ansembe ankagwiritsa ntchito, katani, ndi zonse zomwe ankagwiritsa ntchito. 32 Mtsogoleri wamkulu wa Alevi anali Eliezara mwana wa Aaroni wansembe. Iye anasankhidwa kukhala woyangʼanira omwe ankasamalira malo wopatulika. 33 Kwa Merari kunali banja la Mali ndi banja la Musi. Amenewa ndiye anali mabanja a Amerari. 34 Chiwerengero cha amuna onse kuyambira a mwezi umodzi kapena kupitirirapo chinali 6,200. 35 Mtsogoleri wa magulu a mabanja a Amerari anali Zuriyeli mwana wa Abihaili. Iwo ankamanga misasa yawo kumpoto kwa Chihema. 36 Amerari anapatsidwa ntchito yosamalira mitengo ya chihema, nsichi zake, mizati yake, matsinde ake, ndi zida zake zonse, ndi zonse zomwe ankagwiritsa ntchito, 37 pamodzi ndi mizati yozungulira bwalo ndi matsinde ake, zikhomo za chihema ndi zingwe zake. 38 Mose ndi Aaroni ndi ana ake aamuna ankamanga misasa yawo kummawa kwa chihema, kuyangʼana kotulukira dzuwa, kutsogolo kwa tenti ya msonkhano. Anali ndi ntchito yosamalira malo wopatulika mʼmalo mwa Aisraeli. Aliyense woyandikira malo wopatulika ankayenera kuphedwa. 39 Alevi onse amene Mose ndi Aaroni anawawerenga potsatira lamulo la Yehova monga mwa magulu a mabanja awo, amuna onse kuyambira a mwezi umodzi kapena kupitirirapo anali 22,000. 40 Yehova anawuza Mose kuti, “Werenga ana onse aamuna oyamba kubadwa mu Israeli, omwe ali ndi mwezi umodzi kapena kupitirirapo ndipo ulembe mndandanda wa mayina awo. 41 Unditengere Alevi onse mʼmalo mwa ana oyamba kubadwa onse a Aisraeli, ndiponso ziweto zazimuna za Alevi mʼmalo mwa ziweto zonse zazimuna zoyamba kubadwa za Aisraeli. Ine ndine Yehova.” 42 Choncho Mose anawerenga ana aamuna onse oyamba kubadwa a Aisraeli monga momwe Yehova anamulamulira. 43 Chiwerengero chonse cha ana aamuna oyamba kubadwa kuyambira a mwezi umodzi kapena kupitirirapo chinali 22, 273. 44 Ndipo Yehova anawuzanso Mose kuti, 45 “Tenga Alevi mʼmalo mwa ana aamuna oyamba kubadwa onse a Aisraeli, ndiponso zoweta zonse za Alevi mʼmalo mwa zoweta za Aisraeli. Alevi ndi anga. Ine ndine Yehova. 46 Pofuna kuwombola ana aamuna 273 oyamba kubadwa a Aisraeli amene anaposa chiwerengero cha aamuna a fuko la Levi, 47 utenge masekeli asanu pa munthu aliyense. Masekeliwo akhale ofanana ndi masekeli a ku malo wopatulika, kumene sekeli imodzi imakwanira magera makumi awiri. 48 Ndalama zimenezi uzipereke kwa Aaroni ndi ana ake aamuna kuti ukhale mtengo woombolera Aisraeli woonjezerawo.” 49 Choncho Mose anatenga ndalama zowombolera zija kuchokera kwa Aisraeli amene chiwerengero chawo chinaposa chiwerengero cha omwe anawomboledwa ndi Alevi. 50 Anatenga masekeli a siliva okwana 1,365 molingana ndi masekeli a ku malo opatulika, kuchokera kwa ana aamuna oyamba kubadwa a Aisraeli. 51 Mose anapereka ndalama zowombolera zija kwa Aaroni ndi ana ake aamuna monga mwa mawu amene Yehova analamulira.

In Other Versions

Numbers 3 in the ANGEFD

Numbers 3 in the ANTPNG2D

Numbers 3 in the AS21

Numbers 3 in the BAGH

Numbers 3 in the BBPNG

Numbers 3 in the BBT1E

Numbers 3 in the BDS

Numbers 3 in the BEV

Numbers 3 in the BHAD

Numbers 3 in the BIB

Numbers 3 in the BLPT

Numbers 3 in the BNT

Numbers 3 in the BNTABOOT

Numbers 3 in the BNTLV

Numbers 3 in the BOATCB

Numbers 3 in the BOATCB2

Numbers 3 in the BOBCV

Numbers 3 in the BOCNT

Numbers 3 in the BOECS

Numbers 3 in the BOHCB

Numbers 3 in the BOHCV

Numbers 3 in the BOHLNT

Numbers 3 in the BOHNTLTAL

Numbers 3 in the BOICB

Numbers 3 in the BOILNTAP

Numbers 3 in the BOITCV

Numbers 3 in the BOKCV

Numbers 3 in the BOKCV2

Numbers 3 in the BOKHWOG

Numbers 3 in the BOKSSV

Numbers 3 in the BOLCB

Numbers 3 in the BOLCB2

Numbers 3 in the BOMCV

Numbers 3 in the BONAV

Numbers 3 in the BONCB

Numbers 3 in the BONLT

Numbers 3 in the BONUT2

Numbers 3 in the BOPLNT

Numbers 3 in the BOSCB

Numbers 3 in the BOSNC

Numbers 3 in the BOTLNT

Numbers 3 in the BOVCB

Numbers 3 in the BOYCB

Numbers 3 in the BPBB

Numbers 3 in the BPH

Numbers 3 in the BSB

Numbers 3 in the CCB

Numbers 3 in the CUV

Numbers 3 in the CUVS

Numbers 3 in the DBT

Numbers 3 in the DGDNT

Numbers 3 in the DHNT

Numbers 3 in the DNT

Numbers 3 in the ELBE

Numbers 3 in the EMTV

Numbers 3 in the ESV

Numbers 3 in the FBV

Numbers 3 in the FEB

Numbers 3 in the GGMNT

Numbers 3 in the GNT

Numbers 3 in the HARY

Numbers 3 in the HNT

Numbers 3 in the IRVA

Numbers 3 in the IRVB

Numbers 3 in the IRVG

Numbers 3 in the IRVH

Numbers 3 in the IRVK

Numbers 3 in the IRVM

Numbers 3 in the IRVM2

Numbers 3 in the IRVO

Numbers 3 in the IRVP

Numbers 3 in the IRVT

Numbers 3 in the IRVT2

Numbers 3 in the IRVU

Numbers 3 in the ISVN

Numbers 3 in the JSNT

Numbers 3 in the KAPI

Numbers 3 in the KBT1ETNIK

Numbers 3 in the KBV

Numbers 3 in the KJV

Numbers 3 in the KNFD

Numbers 3 in the LBA

Numbers 3 in the LBLA

Numbers 3 in the LNT

Numbers 3 in the LSV

Numbers 3 in the MAAL

Numbers 3 in the MBV

Numbers 3 in the MBV2

Numbers 3 in the MHNT

Numbers 3 in the MKNFD

Numbers 3 in the MNG

Numbers 3 in the MNT

Numbers 3 in the MNT2

Numbers 3 in the MRS1T

Numbers 3 in the NAA

Numbers 3 in the NASB

Numbers 3 in the NBLA

Numbers 3 in the NBS

Numbers 3 in the NBVTP

Numbers 3 in the NET2

Numbers 3 in the NIV11

Numbers 3 in the NNT

Numbers 3 in the NNT2

Numbers 3 in the NNT3

Numbers 3 in the PDDPT

Numbers 3 in the PFNT

Numbers 3 in the RMNT

Numbers 3 in the SBIAS

Numbers 3 in the SBIBS

Numbers 3 in the SBIBS2

Numbers 3 in the SBICS

Numbers 3 in the SBIDS

Numbers 3 in the SBIGS

Numbers 3 in the SBIHS

Numbers 3 in the SBIIS

Numbers 3 in the SBIIS2

Numbers 3 in the SBIIS3

Numbers 3 in the SBIKS

Numbers 3 in the SBIKS2

Numbers 3 in the SBIMS

Numbers 3 in the SBIOS

Numbers 3 in the SBIPS

Numbers 3 in the SBISS

Numbers 3 in the SBITS

Numbers 3 in the SBITS2

Numbers 3 in the SBITS3

Numbers 3 in the SBITS4

Numbers 3 in the SBIUS

Numbers 3 in the SBIVS

Numbers 3 in the SBT

Numbers 3 in the SBT1E

Numbers 3 in the SCHL

Numbers 3 in the SNT

Numbers 3 in the SUSU

Numbers 3 in the SUSU2

Numbers 3 in the SYNO

Numbers 3 in the TBIAOTANT

Numbers 3 in the TBT1E

Numbers 3 in the TBT1E2

Numbers 3 in the TFTIP

Numbers 3 in the TFTU

Numbers 3 in the TGNTATF3T

Numbers 3 in the THAI

Numbers 3 in the TNFD

Numbers 3 in the TNT

Numbers 3 in the TNTIK

Numbers 3 in the TNTIL

Numbers 3 in the TNTIN

Numbers 3 in the TNTIP

Numbers 3 in the TNTIZ

Numbers 3 in the TOMA

Numbers 3 in the TTENT

Numbers 3 in the UBG

Numbers 3 in the UGV

Numbers 3 in the UGV2

Numbers 3 in the UGV3

Numbers 3 in the VBL

Numbers 3 in the VDCC

Numbers 3 in the YALU

Numbers 3 in the YAPE

Numbers 3 in the YBVTP

Numbers 3 in the ZBP