Numbers 36 (BOGWICC)
1 Atsogoleri a mabanja a fuko la Giliyadi, mwana wa Makiri, mwana wa Manase omwe anali ochokera ku fuko la ana a Yosefe anabwera ndi kuyankhula ndi Mose, atsogoleri ndi akuluakulu a mabanja a Aisraeli. 2 Iwo anati, “Pamene Yehova analamula mbuye wanga kuti apereke dziko ngati cholowa kwa Aisraeli mwa maere, anakulamulani inu kupereka cholowa cha mʼbale wathu Zelofehadi kwa ana ake aakazi. 3 Tsopano ngati akwatiwa ndi aamuna ochokera ku mafuko ena a mitundu ya Aisraeli, cholowa chawo chidzatengedwa kuchoka pa cholowa cha makolo athu ndipo adzachiwonjezera ku fuko limene akwatiwakolo. Ndipo gawo lina la cholowacho, lopatsidwa kwa ife lidzatengedwa. 4 Pamene chaka cha chikondwerero cha zaka makumi asanu, cha Aisraeli chafika, cholowa chawo chidzawonjezeredwa ku fuko limene iwo akwatiwako. Ndipo katundu wawo adzachotsedwa pa cholowa cha fuko la makolo athu.” 5 Tsono mwa lamulo la Yehova, Mose anapereka lamulo ili kwa Aisraeli: “Zimene ana a Yosefe akunena ndi zoona. 6 Izi ndi zimene Yehova akulamula kwa ana aakazi a Zelofehadi: Atha kukwatiwa ndi aliyense amene angakondweretsedwe naye koma zingakhale bwino atakwatiwa mʼfuko la abambo awo 7 kuti cholowa cha Israeli chisapite ku fuko lina, pakuti Mwisraeli aliyense ayenera kusunga cholowa cha fuko la makolo ake. 8 Mwana wamkazi aliyense amene adzalandira cholowa cha dziko la fuko lililonse la Israeli ayenera kukwatiwa ndi munthu wa fuko la abambo ake. 9 Cholowa chilichonse mu Israeli sichiyenera kupita ku fuko lina, popeza fuko lililonse la Israeli liyenera kusunga cholowa chimene linalandira.” 10 Choncho ana aakazi a Zelofehadi anachita monga Yehova analamulira Mose. 11 Ana aakazi a Zelofehadi amene ndi Mahila, Tiriza, Hogila, Milika ndi Nowa, anakwatiwa ndi asuweni awo a ku mbali ya abambo awo. 12 Anakwatiwa mʼmafuko a zidzukulu za Manase mwana wa Yosefe, ndipo cholowa chawo chinakhalabe mʼfuko la abambo awo. 13 Awa ndi malamulo ndi malangizo amene Yehova anapereka kwa Aisraeli kupyolera mwa Mose ku chigwa cha Mowabu mʼmbali mwa Yorodani, ku Yeriko.
In Other Versions
Numbers 36 in the ANGEFD
Numbers 36 in the ANTPNG2D
Numbers 36 in the AS21
Numbers 36 in the BAGH
Numbers 36 in the BBPNG
Numbers 36 in the BBT1E
Numbers 36 in the BDS
Numbers 36 in the BEV
Numbers 36 in the BHAD
Numbers 36 in the BIB
Numbers 36 in the BLPT
Numbers 36 in the BNT
Numbers 36 in the BNTABOOT
Numbers 36 in the BNTLV
Numbers 36 in the BOATCB
Numbers 36 in the BOATCB2
Numbers 36 in the BOBCV
Numbers 36 in the BOCNT
Numbers 36 in the BOECS
Numbers 36 in the BOHCB
Numbers 36 in the BOHCV
Numbers 36 in the BOHLNT
Numbers 36 in the BOHNTLTAL
Numbers 36 in the BOICB
Numbers 36 in the BOILNTAP
Numbers 36 in the BOITCV
Numbers 36 in the BOKCV
Numbers 36 in the BOKCV2
Numbers 36 in the BOKHWOG
Numbers 36 in the BOKSSV
Numbers 36 in the BOLCB
Numbers 36 in the BOLCB2
Numbers 36 in the BOMCV
Numbers 36 in the BONAV
Numbers 36 in the BONCB
Numbers 36 in the BONLT
Numbers 36 in the BONUT2
Numbers 36 in the BOPLNT
Numbers 36 in the BOSCB
Numbers 36 in the BOSNC
Numbers 36 in the BOTLNT
Numbers 36 in the BOVCB
Numbers 36 in the BOYCB
Numbers 36 in the BPBB
Numbers 36 in the BPH
Numbers 36 in the BSB
Numbers 36 in the CCB
Numbers 36 in the CUV
Numbers 36 in the CUVS
Numbers 36 in the DBT
Numbers 36 in the DGDNT
Numbers 36 in the DHNT
Numbers 36 in the DNT
Numbers 36 in the ELBE
Numbers 36 in the EMTV
Numbers 36 in the ESV
Numbers 36 in the FBV
Numbers 36 in the FEB
Numbers 36 in the GGMNT
Numbers 36 in the GNT
Numbers 36 in the HARY
Numbers 36 in the HNT
Numbers 36 in the IRVA
Numbers 36 in the IRVB
Numbers 36 in the IRVG
Numbers 36 in the IRVH
Numbers 36 in the IRVK
Numbers 36 in the IRVM
Numbers 36 in the IRVM2
Numbers 36 in the IRVO
Numbers 36 in the IRVP
Numbers 36 in the IRVT
Numbers 36 in the IRVT2
Numbers 36 in the IRVU
Numbers 36 in the ISVN
Numbers 36 in the JSNT
Numbers 36 in the KAPI
Numbers 36 in the KBT1ETNIK
Numbers 36 in the KBV
Numbers 36 in the KJV
Numbers 36 in the KNFD
Numbers 36 in the LBA
Numbers 36 in the LBLA
Numbers 36 in the LNT
Numbers 36 in the LSV
Numbers 36 in the MAAL
Numbers 36 in the MBV
Numbers 36 in the MBV2
Numbers 36 in the MHNT
Numbers 36 in the MKNFD
Numbers 36 in the MNG
Numbers 36 in the MNT
Numbers 36 in the MNT2
Numbers 36 in the MRS1T
Numbers 36 in the NAA
Numbers 36 in the NASB
Numbers 36 in the NBLA
Numbers 36 in the NBS
Numbers 36 in the NBVTP
Numbers 36 in the NET2
Numbers 36 in the NIV11
Numbers 36 in the NNT
Numbers 36 in the NNT2
Numbers 36 in the NNT3
Numbers 36 in the PDDPT
Numbers 36 in the PFNT
Numbers 36 in the RMNT
Numbers 36 in the SBIAS
Numbers 36 in the SBIBS
Numbers 36 in the SBIBS2
Numbers 36 in the SBICS
Numbers 36 in the SBIDS
Numbers 36 in the SBIGS
Numbers 36 in the SBIHS
Numbers 36 in the SBIIS
Numbers 36 in the SBIIS2
Numbers 36 in the SBIIS3
Numbers 36 in the SBIKS
Numbers 36 in the SBIKS2
Numbers 36 in the SBIMS
Numbers 36 in the SBIOS
Numbers 36 in the SBIPS
Numbers 36 in the SBISS
Numbers 36 in the SBITS
Numbers 36 in the SBITS2
Numbers 36 in the SBITS3
Numbers 36 in the SBITS4
Numbers 36 in the SBIUS
Numbers 36 in the SBIVS
Numbers 36 in the SBT
Numbers 36 in the SBT1E
Numbers 36 in the SCHL
Numbers 36 in the SNT
Numbers 36 in the SUSU
Numbers 36 in the SUSU2
Numbers 36 in the SYNO
Numbers 36 in the TBIAOTANT
Numbers 36 in the TBT1E
Numbers 36 in the TBT1E2
Numbers 36 in the TFTIP
Numbers 36 in the TFTU
Numbers 36 in the TGNTATF3T
Numbers 36 in the THAI
Numbers 36 in the TNFD
Numbers 36 in the TNT
Numbers 36 in the TNTIK
Numbers 36 in the TNTIL
Numbers 36 in the TNTIN
Numbers 36 in the TNTIP
Numbers 36 in the TNTIZ
Numbers 36 in the TOMA
Numbers 36 in the TTENT
Numbers 36 in the UBG
Numbers 36 in the UGV
Numbers 36 in the UGV2
Numbers 36 in the UGV3
Numbers 36 in the VBL
Numbers 36 in the VDCC
Numbers 36 in the YALU
Numbers 36 in the YAPE
Numbers 36 in the YBVTP
Numbers 36 in the ZBP