Numbers 4 (BOGWICC)

1 Yehova anati kwa Mose ndi Aaroni: 2 “Werengani Akohati omwe ndi gawo limodzi la Alevi monga mwa mafuko awo ndi mabanja awo. 3 Werengani amuna onse amene ali ndi zaka makumi atatu mpaka zaka makumi asanu amene amabwera kudzagwira ntchito mu tenti ya msonkhano. 4 “Ntchito ya Akohati mu tenti ya msonkhano ndi iyi: kusamalira zinthu zopatulika kwambiri. 5 Pamene anthu akusamuka pa msasa, Aaroni ndi ana ake aamuna azilowa mu tenti ndi kuchotsa chinsalu chotchingira ndi kuphimba nacho bokosi la umboni. 6 Ndipo azikuta bokosilo ndi zikopa za akatumbu ndi kuyala pamwamba pake nsalu ya mtundu wa thambo ndi kuyika mitengo yonyamulira mʼmalo mwake. 7 “Pa tebulo pamene pamakhala buledi wa ansembe aziyalapo nsalu ya mtundu wa thambo, ndipo aziyikapo mbale, mabeseni, zipande ndi mitsuko yoperekera nsembe yachakumwa. Aziyikaponso buledi wokhala pamenepo nthawi zonse. 8 Tsono pamwamba pa izi aziyalapo nsalu yofiira, ndi kuzikuta mʼzikopa za akatumbu ndi kuyika mitengo yonyamulira mʼmalo mwake. 9 “Azitenga nsalu ya mtundu wa thambo ndi kukutira choyikapo nyale, pamodzi ndi nyale zake, zopanira zake, zotengera zake ndi mitsuko yonse yosungiramo mafuta. 10 Kenaka achikulunge pamodzi ndi zipangizo zake zonse mʼzikopa za akatumbu ndi kuchiyika pa chonyamulira chake. 11 “Pamwamba pa guwa la golide aziyalapo nsalu ya mtundu wa thambo ndi kukutira ndi zikopa za akatumbu ndi kuyika mʼmalo mwake mitengo yonyamulira. 12 “Azitenga zipangizo zonse zogwiritsira ntchito ku malo wopatulika, azizikulunga mʼnsalu ya mtundu wa thambo, azizikuta ndi zikopa za akatumbu ndi kuziyika pa zonyamulira zake. 13 “Azichotsa phulusa la pa guwa lansembe lamkuwa ndi kuyalapo nsalu yapepo pamwamba pake. 14 Kenaka aziyikapo zipangizo zonse zogwiritsira ntchito potumikira pa guwa, kuphatikizapo miphika yowotchera nyama, mafoloko otengera nyama, zowolera phulusa ndi mbale zowazira magazi pa guwa lansembe ndipo pamwamba pake aziyalapo zikopa za akatumbu ndi kuziyika mʼzonyamulira zake. 15 “Aaroni ndi ana ake aamuna akamaliza kukutira ziwiya za ku malo wopatulika ndi zipangizo zopatulika zonse, ndipo akakonzeka kusamuka pamalopo, Akohati abwere kudzazinyamula koma asagwire zinthu zopatulikazo. Akatero adzafa. Izi ndizo zinthu zimene Akohati ayenera kunyamula mu tenti ya msonkhano. 16 “Eliezara mwana wa Aaroni, wansembe, aziyangʼanira mafuta a nyale, ndi lubani wa nsembe zofukiza, nsembe yaufa yoperekedwa nthawi zonse ndi mafuta odzozera. Aziyangʼaniranso chihema ndi zonse zili mʼmenemo, kuphatikizapo zida ndi ziwiya zonse zopatulika.” 17 Yehova anawuzanso Mose ndi Aaroni kuti, 18 “Onetsetsani kuti mabanja a fuko la Kohati asachotsedwe kwa Alevi. 19 Koma muziwachitira izi kuti asafe, akhalebe ndi moyo pamene ayandikira zinthu za ku malo wopatulika kwambiri: Aaroni ndi ana ake aamuna azipita ku malo wopatulika ndi kumamupatsa munthu aliyense ntchito yake ndi zimene ayenera kunyamula. 20 Koma Akohati asalowe kukaona zinthu zopatulika, ngakhale kanthawi pangʼono, chifukwa akatero adzafa.” 21 Yehova anawuza Mose kuti, 22 “Werenganso Ageresoni monga mwa mabanja ndi mafuko awo. 23 Uwerenge amuna onse a zaka makumi atatu mpaka a zaka makumi asanu zakubadwa amene amabwera kudzatumikira ku tenti ya msonkhano. 24 “Ntchito ya mafuko a Ageresoni pamene akugwira ntchito ndi kunyamula katundu ndi iyi: 25 Azinyamula makatani a ku chihema, tenti ya msonkhano, zokutira zake ndi zokutira kunja za zikopa za akatumbu, makatani a pa khomo la ku tenti ya msonkhano, 26 makatani wotchingira bwalo lozungulira chihema ndi guwa, katani ya pa khomo, zingwe ndi zida zonse zimene zimagwiritsidwa ntchito mʼchihema. Ageresoni azichita zonse zofunika kuchitika ndi zinthu zimenezi. 27 Ntchito yawo yonse, kaya kunyamula kapena kugwira ntchito zina, achite Ageresoni motsogozedwa ndi Aaroni ndi ana ake aamuna. Uwagawire ntchito zonse zimene akuyenera kugwira. 28 Iyi ndiye ntchito ya fuko la Ageresoni ku tenti ya msonkhano. Ntchito zawo zichitike motsogozedwa ndi Itamara mwana wa wansembe Aaroni. 29 “Werenga Amerari monga mwa mafuko awo ndi mabanja awo. 30 Werenga amuna onse a zaka makumi atatu mpaka zaka makumi asanu zakubadwa amene akatumikire mu tenti ya msonkhano. 31 Ntchito yawo pamene azikatumikira mu tenti ya msonkhano ndi iyi: kunyamula matabwa a chihema, mitanda, mizati ndi matsinde, 32 ndiponso mizati yozungulira bwalo ndi matsinde ake, zikhomo za chihema, zingwe ndi zipangizo zake zonse ndiponso zonse zokhudzana ndi ntchito yake. Uwuze munthu aliyense chomwe ayenera kuchita. 33 Iyi ndiyo ntchito ya mafuko a Amerari pamene akugwira ntchito ku tenti ya msonkhano motsogozedwa ndi Itamara mwana wa wansembe Aaroni.” 34 Mose, Aaroni ndi atsogoleri a magulu a anthu anawerenga Akohati monga mwa mafuko ndi mabanja awo. 35 Aamuna onse a zaka makumi atatu mpaka makumi asanu amene anabwera kudzagwira ntchito ku tenti ya msonkhano, 36 atawawerenga mwa mafuko awo, anali 2,750. 37 Ichi chinali chiwerengero cha mafuko a Akohati onse omwe ankatumikira mu tenti ya msonkhano. Mose ndi Aaroni anawawerenga monga mwa lamulo la Yehova. 38 Ageresoni anawerengedwanso monga mwa mafuko ndi mabanja awo. 39 Amuna onse a zaka makumi atatu mpaka makumi asanu amene anabwera kudzagwira ntchito ku tenti ya msonkhano, 40 atawawerenga mwa mafuko ndi mabanja awo, anali 2,630. 41 Ichi chinali chiwerengero cha Ageresoni mwa mabanja awo amene ankatumikira ku tenti ya msonkhano. Mose ndi Aaroni anawawerenga monga mwa lamulo la Yehova. 42 Amerari anawawerenga monga mwa mafuko ndi mabanja awo. 43 Amuna onse kuyambira zaka makumi atatu mpaka makumi asanu amene anabwera kudzatumikira ntchito mu tenti ya msonkhano, 44 atawawerenga mwa mafuko ndi mabanja awo, anali 3,200. 45 Ichi ndicho chinali chiwerengero cha mabanja a Amerari. Mose ndi Aaroni anawawerenga monga momwe Yehova anawalamulira kudzera mwa Mose. 46 Kotero Mose, Aaroni ndi atsogoleri a Israeli anawerenga Alevi onse monga mwa mafuko ndi mabanja awo. 47 Aamuna onse a zaka makumi atatu mpaka zaka makumi asanu omwe anabwera kudzagwira ntchito yonyamula zinthu ku tenti ya msonkhano 48 analipo 8,580. 49 Aliyense anamupatsa ntchito ndi kumuwuza choti anyamule monga mwa lamulo la Yehova kudzera mwa Mose.Anawawerenga chomwechi potsata zimene Yehova analamula Mose.

In Other Versions

Numbers 4 in the ANGEFD

Numbers 4 in the ANTPNG2D

Numbers 4 in the AS21

Numbers 4 in the BAGH

Numbers 4 in the BBPNG

Numbers 4 in the BBT1E

Numbers 4 in the BDS

Numbers 4 in the BEV

Numbers 4 in the BHAD

Numbers 4 in the BIB

Numbers 4 in the BLPT

Numbers 4 in the BNT

Numbers 4 in the BNTABOOT

Numbers 4 in the BNTLV

Numbers 4 in the BOATCB

Numbers 4 in the BOATCB2

Numbers 4 in the BOBCV

Numbers 4 in the BOCNT

Numbers 4 in the BOECS

Numbers 4 in the BOHCB

Numbers 4 in the BOHCV

Numbers 4 in the BOHLNT

Numbers 4 in the BOHNTLTAL

Numbers 4 in the BOICB

Numbers 4 in the BOILNTAP

Numbers 4 in the BOITCV

Numbers 4 in the BOKCV

Numbers 4 in the BOKCV2

Numbers 4 in the BOKHWOG

Numbers 4 in the BOKSSV

Numbers 4 in the BOLCB

Numbers 4 in the BOLCB2

Numbers 4 in the BOMCV

Numbers 4 in the BONAV

Numbers 4 in the BONCB

Numbers 4 in the BONLT

Numbers 4 in the BONUT2

Numbers 4 in the BOPLNT

Numbers 4 in the BOSCB

Numbers 4 in the BOSNC

Numbers 4 in the BOTLNT

Numbers 4 in the BOVCB

Numbers 4 in the BOYCB

Numbers 4 in the BPBB

Numbers 4 in the BPH

Numbers 4 in the BSB

Numbers 4 in the CCB

Numbers 4 in the CUV

Numbers 4 in the CUVS

Numbers 4 in the DBT

Numbers 4 in the DGDNT

Numbers 4 in the DHNT

Numbers 4 in the DNT

Numbers 4 in the ELBE

Numbers 4 in the EMTV

Numbers 4 in the ESV

Numbers 4 in the FBV

Numbers 4 in the FEB

Numbers 4 in the GGMNT

Numbers 4 in the GNT

Numbers 4 in the HARY

Numbers 4 in the HNT

Numbers 4 in the IRVA

Numbers 4 in the IRVB

Numbers 4 in the IRVG

Numbers 4 in the IRVH

Numbers 4 in the IRVK

Numbers 4 in the IRVM

Numbers 4 in the IRVM2

Numbers 4 in the IRVO

Numbers 4 in the IRVP

Numbers 4 in the IRVT

Numbers 4 in the IRVT2

Numbers 4 in the IRVU

Numbers 4 in the ISVN

Numbers 4 in the JSNT

Numbers 4 in the KAPI

Numbers 4 in the KBT1ETNIK

Numbers 4 in the KBV

Numbers 4 in the KJV

Numbers 4 in the KNFD

Numbers 4 in the LBA

Numbers 4 in the LBLA

Numbers 4 in the LNT

Numbers 4 in the LSV

Numbers 4 in the MAAL

Numbers 4 in the MBV

Numbers 4 in the MBV2

Numbers 4 in the MHNT

Numbers 4 in the MKNFD

Numbers 4 in the MNG

Numbers 4 in the MNT

Numbers 4 in the MNT2

Numbers 4 in the MRS1T

Numbers 4 in the NAA

Numbers 4 in the NASB

Numbers 4 in the NBLA

Numbers 4 in the NBS

Numbers 4 in the NBVTP

Numbers 4 in the NET2

Numbers 4 in the NIV11

Numbers 4 in the NNT

Numbers 4 in the NNT2

Numbers 4 in the NNT3

Numbers 4 in the PDDPT

Numbers 4 in the PFNT

Numbers 4 in the RMNT

Numbers 4 in the SBIAS

Numbers 4 in the SBIBS

Numbers 4 in the SBIBS2

Numbers 4 in the SBICS

Numbers 4 in the SBIDS

Numbers 4 in the SBIGS

Numbers 4 in the SBIHS

Numbers 4 in the SBIIS

Numbers 4 in the SBIIS2

Numbers 4 in the SBIIS3

Numbers 4 in the SBIKS

Numbers 4 in the SBIKS2

Numbers 4 in the SBIMS

Numbers 4 in the SBIOS

Numbers 4 in the SBIPS

Numbers 4 in the SBISS

Numbers 4 in the SBITS

Numbers 4 in the SBITS2

Numbers 4 in the SBITS3

Numbers 4 in the SBITS4

Numbers 4 in the SBIUS

Numbers 4 in the SBIVS

Numbers 4 in the SBT

Numbers 4 in the SBT1E

Numbers 4 in the SCHL

Numbers 4 in the SNT

Numbers 4 in the SUSU

Numbers 4 in the SUSU2

Numbers 4 in the SYNO

Numbers 4 in the TBIAOTANT

Numbers 4 in the TBT1E

Numbers 4 in the TBT1E2

Numbers 4 in the TFTIP

Numbers 4 in the TFTU

Numbers 4 in the TGNTATF3T

Numbers 4 in the THAI

Numbers 4 in the TNFD

Numbers 4 in the TNT

Numbers 4 in the TNTIK

Numbers 4 in the TNTIL

Numbers 4 in the TNTIN

Numbers 4 in the TNTIP

Numbers 4 in the TNTIZ

Numbers 4 in the TOMA

Numbers 4 in the TTENT

Numbers 4 in the UBG

Numbers 4 in the UGV

Numbers 4 in the UGV2

Numbers 4 in the UGV3

Numbers 4 in the VBL

Numbers 4 in the VDCC

Numbers 4 in the YALU

Numbers 4 in the YAPE

Numbers 4 in the YBVTP

Numbers 4 in the ZBP