Proverbs 16 (BOGWICC)
1 Zolinga za mu mtima ndi za munthu,koma kwa Yehova ndiye kumachokera yankho. 2 Zochita zonse za munthu zimaoneka zabwino pamaso pake,koma Yehova ndiye amasanthula zolinga zako. 3 Pereka ntchito zako zonse mʼmanja mwa Yehova,ndipo zolinga zako zidzachitikadi. 4 Yehova amachita zonse ndi cholinga chake,ngakhale anthu oyipa kuti aone tsiku latsoka. 5 Munthu aliyense wodzikuza amamunyansa Yehova.Koma dziwani izi: Iwo sadzakhala osalangidwa. 6 Chifukwa cha chikondi chosasinthika ndi kukhulupirika, munthu amakhululukidwa machimo ake;chifukwa cha kuopa Yehova munthu amapewa zoyipa. 7 Pamene makhalidwe a munthu akondweretsa Yehova,ngakhale adani ake amakhala naye mwa mtendere. 8 Kuli bwino kukhala ndi zinthu pangʼono zozipeza mwachilungamo,kusiyana ndi kukhala ndi zinthu zambiri zozipeza popanda chilungamo. 9 Mtima wa munthu umalingalira zochita,koma Yehova ndiye amakhazikitsa njira zake. 10 Mawu a mfumu ali ngati mawu ochokera kwa Mulungu;ndipo pakamwa pake sipalakwa poweruza mlandu. 11 Miyeso ndi masikelo achilungamo zimachokera kwa Yehova;miyala yonse yoyesera ya mʼthumba anayipanga ndi Yehova. 12 Kuchita zoyipa kumanyansa mafumu,pakuti chilungamo ndiye maziko a ufumu wake. 13 Mawu owona amakondweretsa mfumu.Iyo imakonda munthu woyankhula choonadi. 14 Ukali wa mfumu ndi mthenga wa imfa,koma munthu wanzeru amawupepesa ukaliwo. 15 Kuwala kwa nkhope ya mfumu kumapatsa moyo;ndipo kukoma mtima kwake kuli ngati mitambo ya mvula nthawi ya chilimwe. 16 Nʼkwabwino kwambiri kupeza nzeru kupambana golide.Kukhala womvetsa bwino zinthu nʼkwabwino kupambana ndi kukhala ndi siliva. 17 Msewu wa munthu wowongoka mtima umapewa zoyipa;wopenyetsetsa kumene akupita amasunga moyo wake. 18 Kunyada kumafikitsa ku chiwonongeko,ndipo munthu wodzikuza adzagwa. 19 Nʼkwabwino kukhala ndi mtima wodzichepetsa pakati pa anthu oponderezedwa,kusiyana ndi kugawana zolanda ndi anthu onyada. 20 Munthu womvera malangizo zinthu zimamuyendera bwino,ndipo wodala ndi amene amadalira Yehova. 21 A mtima wanzeru amatchedwa ozindikira zinthu,ndipo mawu ake okoma amawonjezera nzeru. 22 Kumvetsa zinthu ndi kasupe wa moyo kwa iwo amene ali nako,koma uchitsiru umabweretsa chilango kwa zitsiru. 23 Mtima wanzeru umathandiza munthu kuyankhula mwa nzeru,ndipo mawu ake amawonjezera nzeru. 24 Mawu okometsera ali ngati chisa cha njuchi,amakoma mu mtima ndipo amalimbitsa thupi. 25 Pali njira ina yooneka ngati yowongoka kwa munthukoma kumatsiriziro kwake ndi imfa. 26 Njala ya munthu wantchito imamuthandiza kulimbikira;njalayo imamukakamiza kuchitapo kanthu. 27 Munthu wopanda pake amakonzekera kuchita zoyipandipo mawu ake ali ngati moto wopsereza. 28 Munthu woyipa mtima amayambitsa mikangano,ndipo miseche imalekanitsa anthu okondana kwambiri. 29 Munthu wandewu amakopa mnansi wake,ndipo amamuyendetsa njira imene si yabwino. 30 Amene amatsinzinira maso ake amalingalira zinthu zokhota;amene amachita msunamo amakonzeka kuchita zoyipa. 31 Imvi zili ngati chipewa chaufumu chaulemerero;munthu amazipeza akakhala moyo wolungama. 32 Munthu wosapsa mtima msanga amaposa munthu wankhondo,munthu wowugwira mtima wake amaposa amene amalanda mzinda. 33 Maere amaponyedwa pa mfunga,koma ndiye Yehova amene amalongosola zonse.
In Other Versions
Proverbs 16 in the ANGEFD
Proverbs 16 in the ANTPNG2D
Proverbs 16 in the AS21
Proverbs 16 in the BAGH
Proverbs 16 in the BBPNG
Proverbs 16 in the BBT1E
Proverbs 16 in the BDS
Proverbs 16 in the BEV
Proverbs 16 in the BHAD
Proverbs 16 in the BIB
Proverbs 16 in the BLPT
Proverbs 16 in the BNT
Proverbs 16 in the BNTABOOT
Proverbs 16 in the BNTLV
Proverbs 16 in the BOATCB
Proverbs 16 in the BOATCB2
Proverbs 16 in the BOBCV
Proverbs 16 in the BOCNT
Proverbs 16 in the BOECS
Proverbs 16 in the BOHCB
Proverbs 16 in the BOHCV
Proverbs 16 in the BOHLNT
Proverbs 16 in the BOHNTLTAL
Proverbs 16 in the BOICB
Proverbs 16 in the BOILNTAP
Proverbs 16 in the BOITCV
Proverbs 16 in the BOKCV
Proverbs 16 in the BOKCV2
Proverbs 16 in the BOKHWOG
Proverbs 16 in the BOKSSV
Proverbs 16 in the BOLCB
Proverbs 16 in the BOLCB2
Proverbs 16 in the BOMCV
Proverbs 16 in the BONAV
Proverbs 16 in the BONCB
Proverbs 16 in the BONLT
Proverbs 16 in the BONUT2
Proverbs 16 in the BOPLNT
Proverbs 16 in the BOSCB
Proverbs 16 in the BOSNC
Proverbs 16 in the BOTLNT
Proverbs 16 in the BOVCB
Proverbs 16 in the BOYCB
Proverbs 16 in the BPBB
Proverbs 16 in the BPH
Proverbs 16 in the BSB
Proverbs 16 in the CCB
Proverbs 16 in the CUV
Proverbs 16 in the CUVS
Proverbs 16 in the DBT
Proverbs 16 in the DGDNT
Proverbs 16 in the DHNT
Proverbs 16 in the DNT
Proverbs 16 in the ELBE
Proverbs 16 in the EMTV
Proverbs 16 in the ESV
Proverbs 16 in the FBV
Proverbs 16 in the FEB
Proverbs 16 in the GGMNT
Proverbs 16 in the GNT
Proverbs 16 in the HARY
Proverbs 16 in the HNT
Proverbs 16 in the IRVA
Proverbs 16 in the IRVB
Proverbs 16 in the IRVG
Proverbs 16 in the IRVH
Proverbs 16 in the IRVK
Proverbs 16 in the IRVM
Proverbs 16 in the IRVM2
Proverbs 16 in the IRVO
Proverbs 16 in the IRVP
Proverbs 16 in the IRVT
Proverbs 16 in the IRVT2
Proverbs 16 in the IRVU
Proverbs 16 in the ISVN
Proverbs 16 in the JSNT
Proverbs 16 in the KAPI
Proverbs 16 in the KBT1ETNIK
Proverbs 16 in the KBV
Proverbs 16 in the KJV
Proverbs 16 in the KNFD
Proverbs 16 in the LBA
Proverbs 16 in the LBLA
Proverbs 16 in the LNT
Proverbs 16 in the LSV
Proverbs 16 in the MAAL
Proverbs 16 in the MBV
Proverbs 16 in the MBV2
Proverbs 16 in the MHNT
Proverbs 16 in the MKNFD
Proverbs 16 in the MNG
Proverbs 16 in the MNT
Proverbs 16 in the MNT2
Proverbs 16 in the MRS1T
Proverbs 16 in the NAA
Proverbs 16 in the NASB
Proverbs 16 in the NBLA
Proverbs 16 in the NBS
Proverbs 16 in the NBVTP
Proverbs 16 in the NET2
Proverbs 16 in the NIV11
Proverbs 16 in the NNT
Proverbs 16 in the NNT2
Proverbs 16 in the NNT3
Proverbs 16 in the PDDPT
Proverbs 16 in the PFNT
Proverbs 16 in the RMNT
Proverbs 16 in the SBIAS
Proverbs 16 in the SBIBS
Proverbs 16 in the SBIBS2
Proverbs 16 in the SBICS
Proverbs 16 in the SBIDS
Proverbs 16 in the SBIGS
Proverbs 16 in the SBIHS
Proverbs 16 in the SBIIS
Proverbs 16 in the SBIIS2
Proverbs 16 in the SBIIS3
Proverbs 16 in the SBIKS
Proverbs 16 in the SBIKS2
Proverbs 16 in the SBIMS
Proverbs 16 in the SBIOS
Proverbs 16 in the SBIPS
Proverbs 16 in the SBISS
Proverbs 16 in the SBITS
Proverbs 16 in the SBITS2
Proverbs 16 in the SBITS3
Proverbs 16 in the SBITS4
Proverbs 16 in the SBIUS
Proverbs 16 in the SBIVS
Proverbs 16 in the SBT
Proverbs 16 in the SBT1E
Proverbs 16 in the SCHL
Proverbs 16 in the SNT
Proverbs 16 in the SUSU
Proverbs 16 in the SUSU2
Proverbs 16 in the SYNO
Proverbs 16 in the TBIAOTANT
Proverbs 16 in the TBT1E
Proverbs 16 in the TBT1E2
Proverbs 16 in the TFTIP
Proverbs 16 in the TFTU
Proverbs 16 in the TGNTATF3T
Proverbs 16 in the THAI
Proverbs 16 in the TNFD
Proverbs 16 in the TNT
Proverbs 16 in the TNTIK
Proverbs 16 in the TNTIL
Proverbs 16 in the TNTIN
Proverbs 16 in the TNTIP
Proverbs 16 in the TNTIZ
Proverbs 16 in the TOMA
Proverbs 16 in the TTENT
Proverbs 16 in the UBG
Proverbs 16 in the UGV
Proverbs 16 in the UGV2
Proverbs 16 in the UGV3
Proverbs 16 in the VBL
Proverbs 16 in the VDCC
Proverbs 16 in the YALU
Proverbs 16 in the YAPE
Proverbs 16 in the YBVTP
Proverbs 16 in the ZBP