Proverbs 20 (BOGWICC)

1 Vinyo amachititsa munthu kukhala wonyoza ndipo chakumwa choledzeretsa chimachititsa munthu kukhala wolongolola;aliyense wosochera nazo zimenezi alibe nzeru. 2 Ukali wa mfumu uli ngati kubangula kwa mkango;amene amawuputa mkwiyowo amataya moyo wake. 3 Nʼchaulemu kwa munthu kupewa mikangano,koma chitsiru chilichonse chimafulumira kulongolola. 4 Munthu waulesi satipula mʼmunda pa nthawi yoyenera;kotero pa nthawi yokolola adzafunafuna zinthu koma sadzapeza kanthu kalikonse. 5 Zolinga za mtima wa munthu zili ngati madzi akuya,munthu womvetsa zinthu ndiye yekha angawatunge. 6 Anthu ambiri amayankhula za kukhulupirika kwawo,koma munthu wokhulupirika angamupeze ndani? 7 Munthu wolungama amakhala ndi makhalidwe abwino;odala ndi ana ake amene amatsanzira moyo wake. 8 Mfumu ikhala pa mpando wake wa chiweruzo,imapeta ndi maso ake anthu onse oyipa. 9 Ndani amene anganene kuti, “Ndawuyeretsa mtima wanga;ndilibe tchimo lililonse?” 10 Masikelo ndi miyeso ya zinthu imene ili yachinyengozonsezi Yehova zimamunyansa. 11 Ngakhale mwana amadziwika ndi zochita zake,ngati zochita zake zili zoyera ndi zoyenera. 12 Makutu amene amamva ndi maso amene amaona,zonsezi anazilenga ndi Yehova. 13 Usakonde tulo ungasauke;khala maso ndipo udzakhala ndi chakudya chambiri. 14 Munthu wogula chinthu amati, “Sichabwino, sichabwino.”Koma akagula nʼkuchokapo amayamba kudzitama. 15 Pali golide ndi miyala yamtengowapatali,koma milomo yoyankhula zanzeru ndi yamtengowapatali koposa zonsezi. 16 Utenge chovala cha munthu amene waperekera mlendo chikole;kuti chikhale chikole chako chifukwa waperekera chikole munthu wachilendo. 17 Chakudya chochipeza mwachinyengo chimukomera munthu,koma pa mapeto pake chimasanduka ngati mchenga mʼkamwa mwake. 18 Zokonzekera zimapindula utafunsira uphungu;ndipo usanamenye nkhondo yamba wapempha malangizo oyenera. 19 Amene amanka nanena miseche amawulula zachinsinsi.Choncho usamagwirizane naye munthu woyankhula zopusayo. 20 Ngati munthu atemberera abambo ake kapena amayi ake,moyo wake udzazimitsidwa ngati nyale mu mdima wandiweyani. 21 Cholowa chochipeza mofulumira poyamba,sichidzakhala dalitso pa mapeto pake. 22 Usanene kuti, “Ine ndidzabwezera choyipa chimenechi!”Dikira Yehova, ndipo Iye adzakupulumutsa. 23 Miyeso yosintha imamunyansa Yehova;ndipo masikelo onyenga si abwino. 24 Mayendedwe a munthu amawalamulira ndi Yehova,tsono munthu angadziwe bwanji njira yake? 25 Ndi msampha kwa munthu kuyankhula mofulumira kuti “Chinthu ichi nʼchopatulika kwa Yehova,”popeza mwina atha kusintha maganizo utalumbira kale. 26 Mfumu ya nzeru imapeta kwathunthuanthu oyipa. 27 Mpweya wa munthu uli ngati nyale ya Yehova;imafufuza ziwalo zake zonse zamʼkati. 28 Kukoma mtima ndi kukhulupirika ndizo zimasunga mfumu;chilungamo chimalimbikitsa mpando wake waufumu. 29 Ulemerero wa achinyamata uli mu mphamvu zawo,imvi ndi ulemerero wa anthu okalamba. 30 Mikwingwirima yopweteka ndiyo imachotsa zoyipa,ndipo mikwapulo ndiyo imachotsa zamʼkatikati mwa munthu.

In Other Versions

Proverbs 20 in the ANGEFD

Proverbs 20 in the ANTPNG2D

Proverbs 20 in the AS21

Proverbs 20 in the BAGH

Proverbs 20 in the BBPNG

Proverbs 20 in the BBT1E

Proverbs 20 in the BDS

Proverbs 20 in the BEV

Proverbs 20 in the BHAD

Proverbs 20 in the BIB

Proverbs 20 in the BLPT

Proverbs 20 in the BNT

Proverbs 20 in the BNTABOOT

Proverbs 20 in the BNTLV

Proverbs 20 in the BOATCB

Proverbs 20 in the BOATCB2

Proverbs 20 in the BOBCV

Proverbs 20 in the BOCNT

Proverbs 20 in the BOECS

Proverbs 20 in the BOHCB

Proverbs 20 in the BOHCV

Proverbs 20 in the BOHLNT

Proverbs 20 in the BOHNTLTAL

Proverbs 20 in the BOICB

Proverbs 20 in the BOILNTAP

Proverbs 20 in the BOITCV

Proverbs 20 in the BOKCV

Proverbs 20 in the BOKCV2

Proverbs 20 in the BOKHWOG

Proverbs 20 in the BOKSSV

Proverbs 20 in the BOLCB

Proverbs 20 in the BOLCB2

Proverbs 20 in the BOMCV

Proverbs 20 in the BONAV

Proverbs 20 in the BONCB

Proverbs 20 in the BONLT

Proverbs 20 in the BONUT2

Proverbs 20 in the BOPLNT

Proverbs 20 in the BOSCB

Proverbs 20 in the BOSNC

Proverbs 20 in the BOTLNT

Proverbs 20 in the BOVCB

Proverbs 20 in the BOYCB

Proverbs 20 in the BPBB

Proverbs 20 in the BPH

Proverbs 20 in the BSB

Proverbs 20 in the CCB

Proverbs 20 in the CUV

Proverbs 20 in the CUVS

Proverbs 20 in the DBT

Proverbs 20 in the DGDNT

Proverbs 20 in the DHNT

Proverbs 20 in the DNT

Proverbs 20 in the ELBE

Proverbs 20 in the EMTV

Proverbs 20 in the ESV

Proverbs 20 in the FBV

Proverbs 20 in the FEB

Proverbs 20 in the GGMNT

Proverbs 20 in the GNT

Proverbs 20 in the HARY

Proverbs 20 in the HNT

Proverbs 20 in the IRVA

Proverbs 20 in the IRVB

Proverbs 20 in the IRVG

Proverbs 20 in the IRVH

Proverbs 20 in the IRVK

Proverbs 20 in the IRVM

Proverbs 20 in the IRVM2

Proverbs 20 in the IRVO

Proverbs 20 in the IRVP

Proverbs 20 in the IRVT

Proverbs 20 in the IRVT2

Proverbs 20 in the IRVU

Proverbs 20 in the ISVN

Proverbs 20 in the JSNT

Proverbs 20 in the KAPI

Proverbs 20 in the KBT1ETNIK

Proverbs 20 in the KBV

Proverbs 20 in the KJV

Proverbs 20 in the KNFD

Proverbs 20 in the LBA

Proverbs 20 in the LBLA

Proverbs 20 in the LNT

Proverbs 20 in the LSV

Proverbs 20 in the MAAL

Proverbs 20 in the MBV

Proverbs 20 in the MBV2

Proverbs 20 in the MHNT

Proverbs 20 in the MKNFD

Proverbs 20 in the MNG

Proverbs 20 in the MNT

Proverbs 20 in the MNT2

Proverbs 20 in the MRS1T

Proverbs 20 in the NAA

Proverbs 20 in the NASB

Proverbs 20 in the NBLA

Proverbs 20 in the NBS

Proverbs 20 in the NBVTP

Proverbs 20 in the NET2

Proverbs 20 in the NIV11

Proverbs 20 in the NNT

Proverbs 20 in the NNT2

Proverbs 20 in the NNT3

Proverbs 20 in the PDDPT

Proverbs 20 in the PFNT

Proverbs 20 in the RMNT

Proverbs 20 in the SBIAS

Proverbs 20 in the SBIBS

Proverbs 20 in the SBIBS2

Proverbs 20 in the SBICS

Proverbs 20 in the SBIDS

Proverbs 20 in the SBIGS

Proverbs 20 in the SBIHS

Proverbs 20 in the SBIIS

Proverbs 20 in the SBIIS2

Proverbs 20 in the SBIIS3

Proverbs 20 in the SBIKS

Proverbs 20 in the SBIKS2

Proverbs 20 in the SBIMS

Proverbs 20 in the SBIOS

Proverbs 20 in the SBIPS

Proverbs 20 in the SBISS

Proverbs 20 in the SBITS

Proverbs 20 in the SBITS2

Proverbs 20 in the SBITS3

Proverbs 20 in the SBITS4

Proverbs 20 in the SBIUS

Proverbs 20 in the SBIVS

Proverbs 20 in the SBT

Proverbs 20 in the SBT1E

Proverbs 20 in the SCHL

Proverbs 20 in the SNT

Proverbs 20 in the SUSU

Proverbs 20 in the SUSU2

Proverbs 20 in the SYNO

Proverbs 20 in the TBIAOTANT

Proverbs 20 in the TBT1E

Proverbs 20 in the TBT1E2

Proverbs 20 in the TFTIP

Proverbs 20 in the TFTU

Proverbs 20 in the TGNTATF3T

Proverbs 20 in the THAI

Proverbs 20 in the TNFD

Proverbs 20 in the TNT

Proverbs 20 in the TNTIK

Proverbs 20 in the TNTIL

Proverbs 20 in the TNTIN

Proverbs 20 in the TNTIP

Proverbs 20 in the TNTIZ

Proverbs 20 in the TOMA

Proverbs 20 in the TTENT

Proverbs 20 in the UBG

Proverbs 20 in the UGV

Proverbs 20 in the UGV2

Proverbs 20 in the UGV3

Proverbs 20 in the VBL

Proverbs 20 in the VDCC

Proverbs 20 in the YALU

Proverbs 20 in the YAPE

Proverbs 20 in the YBVTP

Proverbs 20 in the ZBP