Proverbs 31 (BOGWICC)
1 Nawa mawu a mfumu Lemueli wa ku Massa amene anamuphunzitsa amayi ake: 2 Nʼchiyani mwana wanga? Nʼchiyani mwana wa mʼmimba mwanga?Nʼchiyani iwe mwana wanga amene ndinachita kupempha ndi malumbiro? 3 Usapereke mphamvu yako kwa akazi.Usamayenda nawo amenewa popeza amawononga ngakhale mafumu. 4 Iwe Lemueli si choyenera kwa mafumu,mafumu sayenera kumwa vinyo.Olamulira asamalakalake chakumwa choledzeretsa 5 kuopa kuti akamwa adzayiwala malamulo a dziko,nayamba kukhotetsa zinthu zoyenera anthu osauka. 6 Perekani chakumwa choledzeretsa kwa amene ali pafupi kufa,vinyo kwa amene ali pa mavuto woopsa; 7 amwe kuti ayiwale umphawi wawoasakumbukirenso kuvutika kwawo. 8 Yankhula mʼmalo mwa amene sangathe kudziyankhulira okha.Uwayankhulire anthu onse osiyidwa pa zonse zowayenera. 9 Yankhula ndi kuweruza mwachilungamo.Uwateteze amphawi ndi osauka. 10 Kodi mkazi wangwiro angathe kumupeza ndani?Ndi wokwera mtengo kuposa miyala yamtengowapatali. 11 Mtima wa mwamuna wake umamukhulupirirandipo mwamunayo sasowa phindu. 12 Masiku onse a moyo wakemkaziyo amachitira mwamuna wake zabwino zokhazokha osati zoyipa. 13 Iye amafunafuna ubweya ndi thonje;amagwira ntchito ndi manja ake mwaufulu. 14 Iye ali ngati sitima zapamadzi za anthu amalonda,amakatenga chakudya chake kutali. 15 Iye amadzuka kusanache kwenikweni;ndi kuyamba kukonzera a pa banja pake chakudyandi kuwagawira ntchito atsikana ake antchito. 16 Iye amalingalira za munda ndi kuwugula;ndi ndalama zimene wazipeza amalima munda wamphesa. 17 Iye amavala zilimbenagwira ntchito mwamphamvu ndi manja ake. 18 Iye amaona kuti malonda ake ndi aphindu,choncho nyale yake sizima usiku wonse. 19 Iye amadzilukira thonjendipo yekha amagwira chowombera nsalu. 20 Iye amachitira chifundo anthu osaukandipo amapereka chithandizo kwa anthu osowa. 21 Iye saopa kuti banja lake lifa ndi kuzizira pa nyengo yachisanu;pakuti onse amakhala atavala zovala zofunda. 22 Iye amadzipangira yekha zoyala pa bedi pake;amavala zovala zabafuta ndi zapepo. 23 Mwamuna wake ndi wodziwika pa chipata cha mzinda,ndipo amakhala pakati pa akuluakulu a mʼdzikomo. 24 Iye amasoka nsalu zabafuta nazigulitsa;amaperekanso mipango kwa anthu amalonda. 25 Mphamvu ndi ulemu zimakhala ngati chovala chake;ndipo amaseka osaopa zamʼtsogolo. 26 Iye amayankhula mwanzeru,amaphunzitsa anthu mwachikondi. 27 Iye amayangʼanira makhalidwe a anthu a pa banja lakendipo sachita ulesi ndi pangʼono pomwe. 28 Ana ake amamunyadira ndipo amamutcha kuti wodala;ndipo mwamuna wake, amamuyamikira nʼkumati, 29 “Pali akazi ambiri amene achita zinthu zopambanakoma iwe umawaposa onsewa.” 30 Nkhope yachikoka ndi yonyenga, ndipo kukongola nʼkosakhalitsa;koma mkazi amene amaopa Yehova ayenera kutamandidwa. 31 Mupatseni mphotho chifukwa cha zimene iye wachitandipo ntchito zake zimutamande ku mabwalo.
In Other Versions
Proverbs 31 in the ANGEFD
Proverbs 31 in the ANTPNG2D
Proverbs 31 in the AS21
Proverbs 31 in the BAGH
Proverbs 31 in the BBPNG
Proverbs 31 in the BBT1E
Proverbs 31 in the BDS
Proverbs 31 in the BEV
Proverbs 31 in the BHAD
Proverbs 31 in the BIB
Proverbs 31 in the BLPT
Proverbs 31 in the BNT
Proverbs 31 in the BNTABOOT
Proverbs 31 in the BNTLV
Proverbs 31 in the BOATCB
Proverbs 31 in the BOATCB2
Proverbs 31 in the BOBCV
Proverbs 31 in the BOCNT
Proverbs 31 in the BOECS
Proverbs 31 in the BOHCB
Proverbs 31 in the BOHCV
Proverbs 31 in the BOHLNT
Proverbs 31 in the BOHNTLTAL
Proverbs 31 in the BOICB
Proverbs 31 in the BOILNTAP
Proverbs 31 in the BOITCV
Proverbs 31 in the BOKCV
Proverbs 31 in the BOKCV2
Proverbs 31 in the BOKHWOG
Proverbs 31 in the BOKSSV
Proverbs 31 in the BOLCB
Proverbs 31 in the BOLCB2
Proverbs 31 in the BOMCV
Proverbs 31 in the BONAV
Proverbs 31 in the BONCB
Proverbs 31 in the BONLT
Proverbs 31 in the BONUT2
Proverbs 31 in the BOPLNT
Proverbs 31 in the BOSCB
Proverbs 31 in the BOSNC
Proverbs 31 in the BOTLNT
Proverbs 31 in the BOVCB
Proverbs 31 in the BOYCB
Proverbs 31 in the BPBB
Proverbs 31 in the BPH
Proverbs 31 in the BSB
Proverbs 31 in the CCB
Proverbs 31 in the CUV
Proverbs 31 in the CUVS
Proverbs 31 in the DBT
Proverbs 31 in the DGDNT
Proverbs 31 in the DHNT
Proverbs 31 in the DNT
Proverbs 31 in the ELBE
Proverbs 31 in the EMTV
Proverbs 31 in the ESV
Proverbs 31 in the FBV
Proverbs 31 in the FEB
Proverbs 31 in the GGMNT
Proverbs 31 in the GNT
Proverbs 31 in the HARY
Proverbs 31 in the HNT
Proverbs 31 in the IRVA
Proverbs 31 in the IRVB
Proverbs 31 in the IRVG
Proverbs 31 in the IRVH
Proverbs 31 in the IRVK
Proverbs 31 in the IRVM
Proverbs 31 in the IRVM2
Proverbs 31 in the IRVO
Proverbs 31 in the IRVP
Proverbs 31 in the IRVT
Proverbs 31 in the IRVT2
Proverbs 31 in the IRVU
Proverbs 31 in the ISVN
Proverbs 31 in the JSNT
Proverbs 31 in the KAPI
Proverbs 31 in the KBT1ETNIK
Proverbs 31 in the KBV
Proverbs 31 in the KJV
Proverbs 31 in the KNFD
Proverbs 31 in the LBA
Proverbs 31 in the LBLA
Proverbs 31 in the LNT
Proverbs 31 in the LSV
Proverbs 31 in the MAAL
Proverbs 31 in the MBV
Proverbs 31 in the MBV2
Proverbs 31 in the MHNT
Proverbs 31 in the MKNFD
Proverbs 31 in the MNG
Proverbs 31 in the MNT
Proverbs 31 in the MNT2
Proverbs 31 in the MRS1T
Proverbs 31 in the NAA
Proverbs 31 in the NASB
Proverbs 31 in the NBLA
Proverbs 31 in the NBS
Proverbs 31 in the NBVTP
Proverbs 31 in the NET2
Proverbs 31 in the NIV11
Proverbs 31 in the NNT
Proverbs 31 in the NNT2
Proverbs 31 in the NNT3
Proverbs 31 in the PDDPT
Proverbs 31 in the PFNT
Proverbs 31 in the RMNT
Proverbs 31 in the SBIAS
Proverbs 31 in the SBIBS
Proverbs 31 in the SBIBS2
Proverbs 31 in the SBICS
Proverbs 31 in the SBIDS
Proverbs 31 in the SBIGS
Proverbs 31 in the SBIHS
Proverbs 31 in the SBIIS
Proverbs 31 in the SBIIS2
Proverbs 31 in the SBIIS3
Proverbs 31 in the SBIKS
Proverbs 31 in the SBIKS2
Proverbs 31 in the SBIMS
Proverbs 31 in the SBIOS
Proverbs 31 in the SBIPS
Proverbs 31 in the SBISS
Proverbs 31 in the SBITS
Proverbs 31 in the SBITS2
Proverbs 31 in the SBITS3
Proverbs 31 in the SBITS4
Proverbs 31 in the SBIUS
Proverbs 31 in the SBIVS
Proverbs 31 in the SBT
Proverbs 31 in the SBT1E
Proverbs 31 in the SCHL
Proverbs 31 in the SNT
Proverbs 31 in the SUSU
Proverbs 31 in the SUSU2
Proverbs 31 in the SYNO
Proverbs 31 in the TBIAOTANT
Proverbs 31 in the TBT1E
Proverbs 31 in the TBT1E2
Proverbs 31 in the TFTIP
Proverbs 31 in the TFTU
Proverbs 31 in the TGNTATF3T
Proverbs 31 in the THAI
Proverbs 31 in the TNFD
Proverbs 31 in the TNT
Proverbs 31 in the TNTIK
Proverbs 31 in the TNTIL
Proverbs 31 in the TNTIN
Proverbs 31 in the TNTIP
Proverbs 31 in the TNTIZ
Proverbs 31 in the TOMA
Proverbs 31 in the TTENT
Proverbs 31 in the UBG
Proverbs 31 in the UGV
Proverbs 31 in the UGV2
Proverbs 31 in the UGV3
Proverbs 31 in the VBL
Proverbs 31 in the VDCC
Proverbs 31 in the YALU
Proverbs 31 in the YAPE
Proverbs 31 in the YBVTP
Proverbs 31 in the ZBP